Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g20 No. 3 tsamba 4-5
  • Muzidziwa Zoona Zake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzidziwa Zoona Zake
  • Galamukani!—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto Limene Limakhalapo
  • Mfundo ya M’Baibulo
  • Kodi Kudziwa Zoona Zake N’kothandiza Bwanji?
  • Zimene Mungachite
  • Kodi Muli Ndi Mtima Watsankho?
    Galamukani!—2020
  • Kodi Ndinu Wochitiridwa Tsankhu?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Tsankho Likuchitika Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Tsankho Lidzatha Liti?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—2020
g20 No. 3 tsamba 4-5
Azibambo awiri akuchita intavyu mayi wina yemwe akufuna kuyamba ntchito pakampani yopanga magalimoto. Mayiyo akuoneka wamantha.

Muzidziwa Zoona Zake

Vuto Limene Limakhalapo

Ambiri amachitira ena tsankho chifukwa sadziwa zolondola zokhudza anthuwo. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  • Anthu ena amene amalemba anzawo ntchito amaganiza kuti akazi sangagwire ntchito zofunika luso lapadera, mphamvu komanso kuganiza kwambiri.

  • M’zaka zapakati pa 500 ndi 1500 AD, ku Europe anthu ankanena kuti Ayuda amathira poizoni m’zitsime komanso kufalitsa matenda. Ndipo pa nthawi ya ulamuliro wachipani cha Nazi ku Germany, Ayuda anakumananso ndi vuto langati lomweli chifukwa anthu ankawanamizira kuti ndi omwe ankayambitsa mavuto azachuma m’dziko la Germany. Zochitika ziwiri zonsezi zinachititsa kuti Ayuda azisalidwa kwambiri ndipo tsankho limeneli likuchitikabe mpaka pano.

  • Ambiri amaganiza kuti munthu aliyense yemwe ndi wolumala sasangalala komanso amangokhala wolusa.

Anthu amene amakhulupirira zinthu zabodza ngati zimenezi, amapereka zitsanzo komanso maumboni awo otsimikizira kuti zimene amaganizazo ndi zoona. Ndipo amaona kuti aliyense amene amaganiza mosiyana ndi iwowo ndi wosazindikira.

Mfundo ya M’Baibulo

“Si bwino kuti munthu akhale wosadziwa zinthu.”​—MIYAMBO 19:2.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Ngati sitidziwa zolondola, tikhoza kuchita zinthu zolakwika. Tikamangokhulupirira zam’maluwa m’malo mofufuza zoona zake, tingayambe kumaona anthu ena molakwika.

Kodi Baibulo Limalimbikitsa Tsankho?

Anthu ena amanena kuti Baibulo limalimbikitsa tsankho. Koma kodi limanena zotani pa nkhani imeneyi?

  • Anthu onse ndi pachibale: “Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.”​—Machitidwe 17:26.

  • Mulungu alibe tsankho: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

  • Mulungu amaona mtima wa munthu, osati maonekedwe ake: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”​—1 Samueli 16:7.a

a Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.

Kodi Kudziwa Zoona Zake N’kothandiza Bwanji?

Kudziwa zolondola zokhudza anthu amtundu winawake kungatithandize kuti tisamangokhulupirira zinthu zabodza zomwe anthu ena amanena zokhudza anthuwo. Komanso tikangozindikira kuti zimene anthu ena amanena zokhudza mtundu winawake wa anthu ndi zabodza, timasiya kumangokhulupirira zinthu zoipa zimene tamva anthu ena akunena zokhudza anthuwo.

Zimene Zinachitikadi: Jovica (Balkans)

Jovica, yemwe tamutchula munkhani yapita ija, anakula akumva nkhani zoipa zokhudza anthu amtundu winawake omwe ankakhala m’dziko lawo. Ankamva nkhanizi kwa anthu am’dziko limene ankakhala, m’manyuzipepala komanso mapulogalamu a pa TV. Iye anati: “Tsankho linafika pondilowerera kwambiri moti mumtima mwanga ndinayamba kudana kwambiri ndi anthu amtundu umenewo. Koma ndinkaona kuti si kulakwa kumva choncho.

“Komabe pamene ndinalowa usilikali, ndinkakhala ndi anthu amenewa komanso ndinkagwira nawo ntchito chifukwa sindikanachitira mwina. M’kupita kwa nthawi, ndinayamba kuwadziwa bwino moti ndinafika pophunzira chinenero chawo komanso kumvetsera nyimbo zachikhalidwe chawo. Ndinkasangalala ndikamacheza nawo ndipo maganizo anga olakwika aja anasinthiratu. Komabe, mtima watsankho ukhoza kuyambiranso. Choncho ndimayesetsa kupeweratu kumvetsera nkhani zomwe zimanena zoipa zokhudza anthu amtunduwo. Komanso ndinasiya kuonera mafilimu ndi zisudzo zomwe zimanyoza anthu amenewa. Tsopano ndimazindikira kuti maganizo atsankho akhoza kukula mumtima mwa munthu n’kumuchititsa kuti azidana kwambiri ndi anthu osalakwa.”

Zimene Mungachite

  • Anthu akhoza kumanena kuti anthu a gulu linalake ali ndi khalidwe loipa. Komabe ndi bwino kumakumbukira kuti m’gulu limenelo muli anthu enanso ambirimbiri omwe alibe khalidwe loipalo.

  • Muzikumbukira kuti zikhoza kutheka kuti zimene mukudziwa zokhudza gulu la anthulo ndi zochepa.

  • Muziyesetsa kudziwa zolondola zokhudza anthuwo kuchokera kwa anthu komanso malo odalirika.

Anagonjetsa tsankho

Zithunzi: 1. Azibambo awiri akuyenda kwinaku akucheza. 2. Mmodzi wa azibambo aja akumwetulira ali limodzi ndi anzake ena.

Kodi n’chiyani chimene chinathandiza munthu wa Chiarabu komanso Myuda kusiya mtima watsankho?

Onerani vidiyo yakuti Kodi Chikondi Komanso Kukhulupirika Zidzagonjetsa Liti Chidani? Fufuzani mutu umenewu pa jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena