Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 1 tsamba 15
  • Mukhoza Kupeza Nzeru

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mukhoza Kupeza Nzeru
  • Galamukani!—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Akukupemphani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Nzeru Zimene Amapereka
  • Mukhoza Kupeza Nzeru za Mulungu
  • Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?
    Galamukani!—2015
  • Ndi Udindo Wanu Kusankha Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
  • Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 1 tsamba 15

Mukhoza Kupeza Nzeru

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Palembali, mawu akuti “anauziridwa” akutanthauza kuti Mulungu wamphamvuyonse anaika maganizo ake m’mitima ya anthu amene ankalemba Baibulo.

MFUNDO ZOKHUDZA BAIBULO

  • Chiwerengero cha mabuku.

    66

    Chiwerengero cha mabuku kapena zigawo zimene zili m’Baibulo.

  • Dzanja likulemba ndipo pamwamba pake pakuwala.

    40

    Amuna amene Mulungu anawagwiritsa ntchito polemba Baibulo.

  • Chithunzi chosonyeza nthawi.

    1513 B.C.E.

    Chaka chimene Baibulo linayamba kulembedwa, zomwe ndi zaka zoposa 3,500 zapitazo.

  • Zilembo za zilankhulo zosiyanasiyana.

    3,000+

    Zilankhulo zomwe Baibulo lonse lathunthu kapena mbali zake chabe limapezeka.

Mulungu Akukupemphani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Nzeru Zimene Amapereka

“Ine Yehova, ndine . . . amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”​—YESAYA 48:17, 18.

Muziona mawu a palembali kuti ndi zimene Mulungu akukupemphani kuchita. Iye amafuna kuti mukhale ndi mtendere wamumtima komanso muzisangalala mpaka kalekale, ndipo angakuthandizeni kupeza zinthu zimenezi.

Mukhoza Kupeza Nzeru za Mulungu

“M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenera ulalikidwe.”​—MALIKO 13:10.

“Uthenga wabwino” ukuphatikizapo malonjezo a Yehova oti adzathetsa mavuto, adzakonza dzikoli kuti likhale labwino komanso adzaukitsa okondedwa athu amene anamwalira. A Mboni za Yehova amalalikira uthenga wa m’Baibulo umenewu padziko lonse.

Nditayamba Kuwerenga Baibulo, Ndinasiya Kusokonezeka

“Kuyambira ndili mwana, sindinkamvetsa kuti Mlengi ndi ndani. Ndinkadabwa kuti, ‘Ndiye zingatheke bwanji kuti dziko lililonse likhale ndi mlengi komanso mulungu wawo?’ Choncho ndimasangalala ndi zimene Baibulo limanena pa Aroma 3:29 kuti ‘Mulungu woona ndi Mulungu wa anthu a mitundu yonse.’ Iye alinso ndi dzina lomwe ndi Yehova ndipo amafuna kuti ifeyo tikhale anzake.”​—Rakesh.

Rakesh.
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena