Mutu wa Buku Lino/Tsamba la Ofalitsa
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
Kuyang’ana Patsogola’pa M’Kuunika Kowala kwa Maulosi a Baibulo Amene Atsala Pang’ono Kukwaniritsidwa mu Mpangidwe wa Ulamuliro Umodzi Umene Udzakwaniritsa Zosowa ndi Zokhumba Zathu Zonse
“Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi; yimbirani ndi chilangizo. Mulungu ndiye Mfumu ya amitundu: Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera.”—Salmo 47:7, 8.
LOPEREKEDWA kwa Mulungu amene nthawi yake yachimwemwe yafika yakuti alowetse m’malo mwa ulamuliro waumunthu wosakaza’wo ndi wa iye mwini wokhala ndi boma lolungama limene anthu opsyinjika a mafuko onse aliyembekezera kwa nthawi yaitali.