Mutu wa Buku Lino/Tsamba la Ofalitsa
Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
Anthu kulikonse amafuna mtendere weniweni ndi chisungiko. Amalakalaka kupeza mpumulo ku mavuto ambiri amene amawasautsa. Kodi pali chothetsera mavutowa chosatha? Bukhu iri lafalitsidwa ndi chitsimikizo chakuti chiripo, ndi kuti mwamsanga mtendere weniweni ndi chisungiko zidzakhala zenizeni pa dziko lonse lapansi. Chiri chikhumbo chathu chowona mtima kuti mwa kuliwerenga mudzapeza chiyembekezo cholimba ndi chitsimikiziritso chosangalatsa mtima chonena za chimene chiri m’tsogolo kaamba ka onse amene amakonda chilungamo.
—Afalitsi