Mutu 5
Nkhani Imene Ikulowetsamo Inu
1. Kodi nchifukwa ninji anthu awona kukhala kovuta kuzindikira chifukwa chake Mulungu walola kuipa pakati pa anthu?
MOSASAMALA kanthu za chikhumbo cha onse cha mtendere ndi chisungiko, mbiri yamunthu yaipitsidwa ndi kukhetsa mwazi ndi zovulaza. Popeza kuti Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amanyansidwa ndi zinthu zoterozo, kodi nchifukwa ninji sanaletse mikhalidwe imeneyi kale lomwe? Ndithudi sikungakhale chifukwa cha kupanda chikondwerero. Baibulo, kudzanso kukongola kwa zinthu zopangidwa ndi Mulungu za padziko lapansi, zimapereka umboni wochuluka wa chikondi chake ndi nkhawa kaamba ka anthu. (1 Yohane 4:8) Chofunika kwambiri, ulemu wa dzina la Mulungu mwini ukulowetsedwamo, pakuti mikhalidwe imeneyi yachititsa anthu kumtonza. Pamenepa, kodi pakakhala chifukwa chotani, cha kupiririra kwake ndi zaka zikwi zambiri za kupanda mpumulo ndi chiwawa?
2. (a) Kodi nkuti m’Baibulo kumene timapeza chifukwa chake Mulungu walola mikhalidwe yoipa kwa nthawi yaitali? (b) Kodi nchiyani chimene chimapangitsa kukhala kwachiwonekere kuti cholembedwa cha Baibulo chonena za Adamu ndi Hava chiri chenicheni cha m’mbiri?
2 Yankho likupezeka m’cholembedwa Chabaibulo chonena za Adamu ndi Hava. Chimenechi sichiri chopeka chabe. Chiri chenicheni cha m’mbiri. Baibulo limapereka mbiri yokwanira ndi yatsatanetsatane ya mibadwo yoyambira m’zaka za zana loyamba za Nyengo Ino mpaka kukafika kwa anthu oyamba. (Luka 3:23-38; Genesis 5:1-32; 11:10-32) Monga makolo athu oyamba Adamu ndi Hava anali ndi chiyambukiro chenicheni pa ife. Ndipo chimene Baibulo limatiuza ponena za iwo chimatithandiza kuzindikira mikhalidwe imene imayambukira miyoyo yathu lerolino.
3. Kodi ndimakonzedwe amtundu wotani amene Mulungu anapangira anthu pachiyambi?
3 Baibulo limavumbula kuti makonzedwe onse a Mulungu kaamba ka anthu awiri oyamba anali abwino kwambiri. Iwo anali ndi chinthu chirichonse kaamba ka moyo wachimwemwe—malo okhala onga paki m’Edene, mitundu yambiri yosiyanasiyana ya zakudya, ntchito yokhutiritsa, chiyembekezo cha kuwona banja lawo likukula ndi kudzadza dziko lapansi ndi dalitso la Mlengi wawo. (Genesis 1:28, 29; 2:8, 9, 15) Kodi ndani amene moyenerera akanafuna zoposa apa?
4. (a) Pa kulengedwa kwawo, kodi anthu anali osiyana m’njira zotani ndi zolengedwa zina za padziko lapansi? (b) Kodi chitsogozo chofunikacho chinaperekedwera kwa iwo m’njira yotani?
4 Cholembedwa chouziridwa m’Genesis chimavumbula kuti anthu anali ndi malo antchito apadera padziko lapansi. Mosafanana ndi zinyama, iwo anali ndi mphamvu za kulingalira ndipo anapatsidwa ufulu wa kudzisankhira. Ndicho chifukwa chake iwo anapatsidwa mphamvu za kulingalira ndi kusankha. Kuti awatsogoze, Mulungu anaika mwa mwamuna ndi mkaziyo mphamvu ya chikumbumtima kotero kuti, monga anthu angwiro, chikhoterero chawo chanthawi zonse chikakhala kulinga ku zabwino. (Aroma 2:15) Kuphatikiza pa zonsezi, Mulungu anawauza chifukwa chake iwo anali ndi moyo, zimene iwo anayenera kuchita, ndi amene anawapatsa zinthu zonse zabwino zowazinga. (Genesis 1:28-30) Pamenepa, kodi tikufotokoza motani mikhalidwe yoipa imene iripo tsopanoyi?
5. (a) Kodi ndichofunika chosavuta chotani chimene Mulungu anaika pa anthu awiri oyamba, ndipo kaamba ka chifukwa chotani? (b) Kodi nchifukwa ninji ziyembekezo zawo za moyo wamtsogolo moyenerera zinalowetsedwamo?
5 Cholembedwa Chamalemba chimasonyeza kuti nkhani inabuka—imene ikulowetsamo aliyense wa ife lerolino. Iyo inachititsidwa ndi mikhalidwe imene inabuka pasanapite nthawi yaitali anthu awiri oyambirirawo atalengedwa. Mulungu anapatsa mwamuna ndi mkazi mwaŵi wa kusonyeza chiyamikiro chachikondi kwa Mlengi wawo mwa kumvera chofunika. Chofunikacho sichinali kanthu kalikonse kamene kakatanthauza kuti iwo anali ndi zikhoterero zoipa zimene zinafunikira kuletsedwa. Mmalo mwake, chinalowetsamo kanthu kamene mwa iko kokha kanali kachibadwa ndi koyenera—kudya chakudya. Monga momwe Mulungu anauzira mwamunayo kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wa kudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Chofunika chimenechi sichinalande aŵiri oyambirirawo kanthu kalikonse kofunika kaamba ka moyo. Iwo akanatha kudya mitengo ina yonse ya m’mundamo. Komabe ziyembekezo zawo za moyo zamtsogolo zinalowetsedwamodi, ndipo moyenerera choncho. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Iye amene anapempha kumvera anali Magwero enieniwo ndi Wochirikiza moyo wa munthu.
6. (a) Kodi makolo athu oyamba akanakhala ndi moyo kosatha ngati akanachita mogwirizana ndi chowonadi cha maziko chotani chonena za ulamuliro? (b) Kodi nchifukwa ninji iwo anayenera kusonkhezeredwa kumvera Mulungu?
6 Chifuno cha Mulungu sichinali chakuti munthu azifa. Palibe kutchulidwa kwa imfa kulikonse kumene kunapangidwa kwa Adamu ndi Hava kusiyapo kaamba ka kusamvera. Makolo athu oyambirira anali ndi chiyembekezo pamaso pawo cha kukhala ndi moyo kosatha m’malo awo okhala amtendere ndi onga paki. Kuti achifikire, kodi nchiyani chimene chinafunidwa kwa iwo? Iwo anafunikira kuzindikira kuti dziko lapansi pa limene iwo anakhala nla Uyo amene analipanga, ndi kuti, monga Mlengi, Mulungu moyenerera ali ndi ulamuliro pa chilengedwe chake. (Salmo 24:1, 10) Ndithudi Ameneyu, amene anapatsa munthu chirichonse chimene anafunikira, kuphatikizapo moyo weniweniwo, anafunikira kumvera pa chirichonse chimene anawapempha. Komabe, iye sanafune kuti kumvera kumeneku kukakamizidwe. Mmalo mwake, kunayenera kuchokera m’mitima yofunitsitsa, yosonkhezeredwa ndi chikondi. (1 Yohane 5:3) Koma makolo athu aumunthu oyamba analephera kusonyeza chikondi chotero. Kodi zimenezi zinachitika motani?
Chiyambi cha Kutsutsa Ulamuliro wa Mulungu
7. (a) Mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, kodi nkuti kumene kukana ulamuliro wa Mulungu kunayambira? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kukhulupirira malo amizimu?
7 Baibulo limasonyeza kuti kutsutsa ulamuliro wa Mulungu choyamba kunayamba, osati padziko lapansi, koma m’malo osawoneka ndi maso aumunthu. Kodi ife, mofanana ndi ambiri, tiyenera kukaikira kukhalako kwa malo oterowo chifukwa chokha chakuti sitingathe kuwawona? Eya, mphamvu yokoka singathe kuwonedwa, ngakhalenso mphepo. Komabe ziyambukiro zake ziri zenizeni kwambiri. Choteronso, ziyambukiro za malo osawoneka zingathe kuwonedwa. Ngakhale kuti “Mulungu ndiye mzimu,” ntchito zake zachilengedwe zingathe kuwonedwa motizinga monse. Ngati tikhulupirira mwa iye, tiri okakamizika kukhulupirira malo amizimu. (Yohane 4:24; Aroma 1:20) Koma kodi palinso anthu ena amene amakhala m’malowo?
8. Kodi angelo ndianthu amtundu wotani?
8 Mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, mamiliyoni ambiri a anthu amizimu, angelo, analengedwa munthu asanalengedwe. (Yobu 38:4, 7; Salmo 103:20; Danieli 7:10) Onsewa analengedwa ali angwiro; popanda zikhoterero zoipa. Komabe, mofanana ndi cholengedwa cha pambuyo pake cha Mulungu, munthu, iwo anapatsidwa ufulu wa kudzisankhira. Chifukwa chake iwo akanasankha njira ya kukhulupirika kapena ya kusakhulupirika kulinga kwa Mulungu.
9, 10. (a) Kodi nzotheka motani kuti cholengedwa chauzimu changwiro chikhale ndi lingaliro lokhoterera ku kuchita choipa? (b) Chotero, kodi ndimotani mmene mmodzi wa angelo anakhalira Satana?
9 Koma funso lofunsidwa ndi anthu ambiri ndilakuti: Monga zolengedwa zangwiro, kodi ndimotani, mmene aliyense wa iwo akanakhaliradi wokhoterera ku kuchita cholakwa? Eya, kodi ndinthawi zingati m’miyoyo ya ife eni mmene mikhalidwe imabuka yotichititsa kuyang’anizana ndi zothekera zolekanalekana—zina zabwino, zina zoipa? Kukhala ndi luntha la kuzindikira kuthekera kwa zoipa mwa iko kokha sikumatipangitsa kukhala oipa, kodi kumatero? Funso lenileni nlakuti: Kodi tidzasumika kuti maganizo ndi mtima wathu? Ngati tiwasumika pamalingaliro ovulaza, tingasonkhezedwere kukulitsa chikhumbo choipa m’mitima yathu. Chikhumbo chotero potsirizira pake chikatisonkhezera kuchita machitidwe olakwa. Zungulirezungulire wowononga ameneyu anafotokozedwa ndi mlembi Wabaibulo Yakobo kuti: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iyemwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo, ndipo uchimo utakula msinkhu, ubala imfa.”—Yakobo 1:14, 15.
10 Malemba amavumbula kuti ichi chinachitika kwa mmodzi wa ana auzimu a Mulungu. Iye ananyengedwa ndi zikhumbo za iye mwini. Iye anawona kuthekera mwa zolengedwa zaumunthu za Mulungu. Kodi iwo angagonjere kwa iye mmalo mwa kugonjera kwa Mulungu? Mwachiwonekere iye anayamba kulalakala pafupifupi kulandira mbali ya kulambira kumene kunali kwa Mulungu. (Luka 4:5-8) Pochita mogwirizana ndi chikhumbo chake, iye anakhala wotsutsa Mulungu. Chifukwa cha chimenecho iye akutchedwa Satana m’Baibulo, limene litanthauza Wotsutsa.—Yobu 1:6.
11. Kodi pali maziko abwino otani okhulupiririra kuti Satana alikodi?
11 M’zaka zino za zana la20 za kukhulupirira zinthu zowoneka, kukhulupirira kuti pali munthu wamzimu Satana sikofala. Komano, kodi kulingalira kofala kunayamba kwakhalapo chitsogozo chotsimikizirika ku chowonadi? Pakati pa awo amene amafufuza matenda, panthawi ina kunali kosafala kukhulupirira kuti tizilombo topatsa nthenda tosawoneka tinali nakatande. Koma tsopano chisonkhezero chake nchodziŵika bwino lomwe. Ndithudi, pamenepa, kusafala kwa kanthu kena sikumatanthauza kuti iko kanganyalanyazidwe. Yesu Kristu mwiniyo anachokera kumalo auzimu ndipo chotero akanatha kulankhula mwaukumu ponena za moyo kumeneko. Iye motsimikizirika anadziŵikitsa Satana kukhala munthu wamzimu woipa. (Yohane 8:23; Luka 13:16; 22:31) Kuli kokha mwa kupenda kukhalako kwa mdani wauzimu ameneyu kuti kungakhale kotheka kuzindikira mmene mikhalidwe yoipa yotere inayambira padziko lapansi lino.
12. Kodi Satana analankhula motani ndi mkaziyo Hava, ndipo chifukwa ninji mwanjirayo?
12 Cholembedwa chouziridwa m’Genesis mutu 3, chimalongosola mmene Satana anapitirizira m’kuyesa kukhutiritsa chikhumbo chake choipa. M’munda wa Edene iye anafikira mkaziyo Hava mwa mkhalidwe umene unabisa kudziŵika kwake kwenikweni. Iye anagwiritsira ntchito chinyama chowonedwa nthawi zonse ndi anthu awiriwa—njoka. Mwachiwonekere pogwiritsira ntchito chimene tikatcha kulankhulira kutseri kwa kanthu kena, anapangitsa kuwonekera ngati kuti mawu ake anachokera mwa cholengedwa chimenechi. Mkhalidwe wake wochenjera mwachibadwa unayenerana bwino lomwe ndi lingaliro limene Satana anafuna kusonyeza.—Genesis 3:1; Chivumbulutso 12:9.
13. Kodi Satana ananena chiyani kwa Hava, ndipo limodzi ndi cholinga chowonekera bwino chotani?
13 Mmalo mwa kulamula mwachindunji kuti mkaziyo ayang’ane kwa iye monga wolamulira wake, Satana choyamba anafuna kuika chikaikiro m’maganizo mwake, akumamfunsa kuti: “Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Kwenikweni, iye anali kunena kuti: ‘Nzomvetsa chisoni kuti Mulungu wanena kuti musadye zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu.’ Mwa ichi iye anapereka lingaliro lakuti mwinamwake Mulungu anali kukaniza kanthu kena kabwino. Hava anayankha mwa kugwira mawu chiletso cha Mulungu, chimene chinalowetsamo mtengo umodzi wokha, kudzanso kutchula kuti chilango cha kusamvera chinali imfa. Pamenepo, Satana anayesa kuchepetsa kulemekeza kwake lamulo la Mulungu, akumati: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:1-5) Mutayang’anizana ndi mkhalidwe woterowo, kodi inu mukanachitanji?
14. (a) Kodi nchifukwa ninji Hava anagonjera kwa Satana? (b) Kodi Adamu anachitanji?
14 Hava anadzilola kukopedwa ndi chikhumbo chadyera. Anadya chimene Mulungu anakaniza. Pambuyo pake, mwakukakamiza kwake, mwamuna wake Adamu nayenso anadya. Anasankha kugwirizana ndi mkaziyo mmalo mwa Mlengi wake. (Genesis 3:6; 1 Timoteo 2:14) Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo chake?
15. Chotero, pamenepa, kodi nchiyani chimene chachititsa upandu ndi chiwawa, kudzanso matenda ndi imfa, zimene zawoneka pa kukhalapo konse kwa anthu?
15 Banja lonse la anthu linalowetsedwa muuchimo ndi kupanda ungwiro. Adamu ndi Hava tsopano sakanatha kupereka kwa ana awo ungwiro umene iwo poyamba anali nawo. Monga momwe kwakhalira kuti makope opangidwa kuchokera ku kanthu kena kanthenya onse amakhala anthenya imodzimodziyo, chotero ana awo onse anabadwira mu uchimo, ndi chikhoterero chobadwa nacho chakuchita dyera. (Genesis 8:21) Chikhoterero chimenechi, chitasiyidwa chosaletsedwa, chatsogolera ku zoipa zimene zachotsa mtendere ndi chisungiko mwa anthu. Chiri cholowa cha uchimo chimenechi chimenenso chachititsa matenda ndi imfa.—Aroma 5:12.
Nkhani Zodzutsidwa
16, 17. (a) Kuti tizindikire chifukwa chake Mulungu wapirira ndi mkhalidwe umenewu kwanthawi yaitali kwambiri, kodi tiyenera kuzindikira chiyani? (b) Kodi nchiyani kwenikweni chimene chiri nkhani imene inadzutsidwayo?
16 Mothandizidwa ndi maumboni amenewa, maganizo athu akubwerera ku funso la chifukwa chake Mulungu wapilirira ndi mkhalidwewu, akumaulola kukula mpaka pamene wafikapa. Chiri chifukwa cha nkhani yaikulu imene inadzutsidwa ndi chiyambukiro chake pa chilengedwe chonse. Kodi zimenezi ziri choncho motani?
17 Mwachigomeko chake chakuti lamulo la Mulungu kwa Adamu ndi Hava silinali labwino kwa iwo ndi mwa kutsutsa chotulukapo cholongosoledwa ndi Mulungu cha kusamvera, Satana anali kukaikira ulamuliro wa Mulungu. Ayi, iye sanakaikire chenicheni chakuti Mulungu ali wolamulira. Mmalo mwake, nkhani imene Satana anadzutsa inasumikidwa pa kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova ndi kulungama kwa njira Zake. Mwachinyengo, Satana ananena kuti zikawayendera bwino mwa kuchita moima pawokha, kudzipangira zosankha mmalo mwakugonjera ku chitsogozo cha Mulungu. (Genesis 3:4, 5) Komabe, kwenikweni, mwa kuchita choncho iwo akakhala akutsatira chitsogozo cha mdani wa Mulungu.
18. (a) Kodi ndinkhani ina iti imene inaloŵetsedwamo, ndipo kodi imeneyi yasonyezedwa pati m’Baibulo? (b) Kodi ndimotani mmene nkhani imeneyi ikuloŵetseramo ifeyo?
18 Nkhani ina inalowetsedwamo. Popeza kuti zolengedwa za Mulungu zimenezi zinampandukira mu Edenemo, kodi zinazo zikanachitanji? Pambuyo pake m’masiku a munthuyo Yobu, Satana mwapoyera ananena kuti awo amene amatumikira Yehova amatero, osati chifukwa cha kukonda Mulungu ndi ulamuliro wake kulikonse, koma mwadyera, chifukwa chakuti Mulungu amawapatsa chinthu chirichonse. Satana anapereka lingaliro lakuti palibe amene angachirikize mokhulupirika ulamuliro wa Yehova atapsinjika. Chotero kukhulupirika ndi umphumphu wa cholengedwa chanzeru chirichonse kumwamba ndi padziko lapansi zinakaikiridwa. Motero nkhaniyo ikuphatikizapo inu.—Yobu 1:8-12; 2:4, 5.
19, 20. Mwa kusawononga opandukawo nthawi yomweyo, kodi ndimwaŵi wotani umene Yehova anapereka kwa zolengedwa zake, ponse paŵiri zauzimu ndi zaumunthu?
19 Poyanganizana ndi chitokoso choterocho, kodi Yehova akanachitanji? Iye mosavuta akanawononga Satana ndi Adamu ndi Hava. Kumeneko kukanasonyeza mphamvu yaufumu ya Yehova. Koma kodi kukanayankha mafunso amene tsopano anadzutsidwa m’maganizo mwa zolengedwa zonse za Mulungu zimene zinawona zochitika zimenezi? Mtendere wamuyaya ndi chisungiko zachilengedwe chaponseponse zinafunikiritsa kuti mafunso amenewa ayankhidwe kotheratu, komalizira. Ndiponso, umphumphu ndi kukhulupirika kwa zolengedwa zanzeru zonse za Mulungu zinakaikiridwa. Ngati izo zinamkonda, zikafuna kudziyankhira chinenezo chonama chimenecho. Yehova anazipatsa mwaŵi wa kuchita chimenecho kumene. Ndiponso, mwa kulola Adamu ndi Hava kubala ana (ngakhale ali opanda ungwiro), Mulungu akatetezera kusoloka kwa banja laumunthu—banja limene lafikira kulowetsamo tonsefe amene tiri ndi moyo lerolino. Kumeneku kukapatsa mbadwa zimenezi mwaŵi wa kudzisankhira kuti kaya zikamvera ulamuliro wa Mulungu kapena ayi. Chosankha chimenecho ndicho chimene tsopano chikuyang’anizana nanu!
20 Chotero, mmalo mwa kupereka chilango cha imfa panthawi yomweyo, Yehova analola opandukawo kukhalako kwakanthawi. Adamu ndi Hava anathamangitsidwa m’Edene, kukafa zaka chikwi zisanathe. (Genesis 5:5; yerekezerani ndi Genesis 2:17 ndi 2 Petro 3:8.) Satana anayeneranso kuwonongedwa m’nthawi yokwanira, monga ngati kuti anali njoka imene mutu wake waphwanyidwa.—Genesis 3:15; Aroma 16:20.
Chimene Kupita Kwanthawi Kwavumbula
21, 22. (a) Ponena za ulamuliro, kodi Satana ndi anthu akhala akuchitanji mkati mwa nthawi yololedwa ndi ndi Mulungu (b) Kodi nchiyani chimene mbiri ya anthu imasonyeza ponena za boma limene limayesayesa kunyalanyaza Mulungu?
21 Kodi nchiyani chimene chatuluka m’kutokosa kuyenera kwa ulamuliro wa Mulungu? Kodi munthu wadzipindulitsa mwa kuyesayesa kuyendetsa zochita zake? Anthu aloledwa kuyesa mtundu uliwonse wolingaliridwa wa boma. Yehova sanaimike zoyesayesa za anthu mofulumira kwambiri zotulukapo zokwanira zisanawonedwe. Ngakhale zaka zana limodzi zapitazo zikanakhala nthawi yofulumirirapo kwambiri. Munthu anali kungoloŵa kumene mu “nyengo ya luso lazopangapanga” ndipo anali kungoyamba kumene kunena zochuluka ponena za zimene iye akachita.
22 Koma kodi pangafunike zaka zina zana limodzi kuti tiwone chimene chidzakhala chotulukapo cha njira yamunthu ya kusadalira pa Mulungu? Ngakhale amuna otchuka m’mbali za boma ndi sayansi akuvomereza kuti dziko lapansi likuyang’anizana ndi upandu waukulu kwambiri wa chiwonongeko. Ndithudi Mulungu safunikira kulola chiwonongeko chotheratu mmalo mwakuti atsimikizire kulephera kotheratu kwa ulamuliro wa munthu wa kudzilamulira. Pokhala ndi umboni wa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi wochitira umboni chimene chimachitika pamene boma linyalanyaza Mulungu, sikunganenedwe konse kuti panalibe nthawi yokwanira yokonzera ulamuliro wamunthu. Maumboni akusonyeza kuti palibe boma lirilonse losadalira pa Mulungu limene lingathe kudzetsa mtendere weniweni ndi chisungiko kwa anthu onse.
23. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitika posachedwapa kulambulira njira ulamuliro wolungama wa dziko lapansi wokhala m’manja mwa Mwana wa Mulungu?
23 Monga momwe tidzawonera pambuyo pake, nthawi yaitali pasadakhale ndipo mosaphonyetsa nthawi Yehova Mulungu anasonyeza mbadwo wina umene ukamuwona akuchotsa chipanduko chonse chotsutsana ndi ufumu wake waumulungu m’chilengedwe chonse. Sikokha kuti anthu oipa akawonongedwa koma kuti Satana ndi ziwanda zake akabindikiritsidwa monga ngati m’mphompho, osakhoza kusonkhezera zochita kaya za anthu kapena za angelo. Chimenechi chidzalambulira njira ulamuliro wolungama wa dziko lapansi ndi boma la Mwana wa Mulungu. Mkati mwa nyengo yazaka chikwi, boma limenelo lidzachotsa zivulazo zonse zochititsidwa ndi ulamuliro wamunthu wadyera wa zaka zikwi zambiri. Lidzabwezeretsa dziko lapansili ku kukongola kwaparadaiso ndi kubwezeretsanso anthu omvera kuungwiro umene unali mu Edene.—Chivumbulutso 20:1, 2; 21:1-5; 1 Akorinto 15:25, 26.
24. (a) Kodi nchifukwa ninji Satana ndi ziwanda zake adzamasulidwa pamapeto a zaka chikwi? (b) Kodi chotulukapo chidzakhala chotani?
24 Baibulo limafotokoza kuti pamapeto aulamuliro wa zaka chikwi umenewo Satana ndi ziwanda zake adzamasulidwa kukubindikiritsidwa kwawo kwa kanthawi. Chifukwa ninji? Kuti onse okhala ndi moyo panthawiyo akhale ndi mwaŵi wodzisonyeza kukhala okhulupirika kuulamuliro waufumu wa Yehova. Ziŵerengero zankhaninkhani zidzakhala zitatuluka m’chiukiriro. Kwa ambiri a iwo umenewu udzakhala mwaŵi wawo woyamba wa kusonyeza kukonda kwawo Mulungu pansi pa chiyeso. Nkhaniyo idzakhala yofanana ndi ija imene inadzutsidwa mu Edene—kuti kaya iwo adzachirikiza ulamuliro wa Yehova mwa kumvera mokhulupirika. Ofuna kuimira kumodzi ndi mdani wa Mulungu ndi ziwanda zake m’zoyesayesa zirizonse zimene amenewa apanga kudodometsanso mtendere wachilengedwe chaponseponse cha Mulungu adzakhala aufulu kupanga chosankha chimenecho. Koma mwakukana motero boma lopangidwa ndi Mulungu iwo adzayenerera chiwonongeko. Ndipo panthawi iyi chidzadza mwadzidzidzi, monga ngati ndi moto wochokera kumwamba. Opanduka onse, auzimu ndi aumunthu, panthawiyo adzakhala atawonongedwa kunthawi zonse.—Chivumbulutso 20:7-10.
25, 26. Kodi ndimotani mmene kuyendetsa zinthu kwa Yehova kwakhalira kopindulitsa kwa aliyense wa ife?
25 Zowona, kwazaka zikwi zambiri anthu akumana ndi mavuto ochuluka. Koma chimenechi chinali chifukwa cha chosankha cha makolo athu oyambirira, osati cha Mulungu. Mulungu wapirira chitonzo ndipo walekerera zinthu zonyansa kwa iye kwanthawi yonseyi. Koma Mulungu, kwa amene ‘zaka chikwi ziri ngati tsiku limodzi,’ ali wokhoza kuwona zinthu zikali patali kwambiri ndipo kumeneku kumapindulitsa zolengedwa zake. Monga momwe mtumwi wouziridwa akulembera kuti: “[Yehova] sazengeleza nalo lonjezano [lake], monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike ku kulapa.” (2 Petro 3:8, 9) Pakadapanda kuleza mtima kwa Mulungu ndi chipiriro, palibe yense wa ife lerolino akanakhala ndi mwaŵi ulionse wa chipulumutso.
26 Komabe, sitiyenera kunena kuti mkati mwa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapitazo mbali ya Mulungu yakhala kokha yopanda chochita. Ayi, iye sanangolekerera kokha kuipa, kupititsa nthawi ndi kusachitapo kanthu iye mwini. Monga momwe tidzawonera, maumboni akusonyeza zosiyana ndi zimenezo.
[Chithunzi patsamba 51]
Satana ananena kuti atayesedwa anthu onse akaswa umphumphu ndi kuchita mosadalira Mulungu