Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tp mutu 10 tsamba 108-116
  • Kodi Mukufunitsitsa Kuyang’anizana ndi Chowonadi m’Moyo Wanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukufunitsitsa Kuyang’anizana ndi Chowonadi m’Moyo Wanu?
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunika kwa Uphungu ndi Mwambo
  • “Lankhulani Zowona Yense ndi Mnzake”
  • Mulungu amasamalira Awo Amene Amagwiritsira Ntchito Chowonadi
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
  • Chitani Zinthu Zonse Moona Mtima
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kutsanzira Mulungu wa Choonadi
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Muzichita Zinthu Zonse Mwachilungamo
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
tp mutu 10 tsamba 108-116

Mutu 10

Kodi Mukufunitsitsa Kuyang’anizana ndi Chowonadi m’Moyo Wanu?

1, 2. (a) Kodi chowonadi chingatipindulitse motani? (b) Kodi inu mumakhulupilira chiyani kukhala magwero enieni ku amene mtendere weniweni ndi chisungiko zidzachokera?

KUDZIŴA chowonadi kungakhale kopindulitsa kwambiri. Chitagwiritsiridwa ntchito mwanzeru, icho chingakhoze kukutetezerani ku upandu kapena kutayikiridwa ndi kuthandizira chimwemwe chanu ndi chisungiko. Izi ziri choncho makamaka ponena za chowonadi chonena za chimene chiri mtsogolo mwa mbadwo uno.

2 Mothandizidwa ndi zimene zaperekedwa m’bukhu lino, inu mungavomereze kuti munthu sangadzetse mtendere weniweni ndi chisungiko. Mungazindikire kuti chimene Baibulo limanena ndicho chowonadi—kuti Mulungu yekha, kupyolera mwa Ufumu wake, angathetse mavuto oyang’anizana ndi anthu. Pamenepo kodi sikungakhale kwanzeru kulinganiza njira yanu ya moyo mogwirizana ndi zimene inu mukudziwa tsopano kukhala chowonadi? (Yakobo 1:22) Kodi kumeneko kumaloŵetsamo chiyani?

3. Kodi masinthidwe amene munthu ayenera kupanga m’moyo wake ngati afuna kupulumutsidwa ndi Mulungu kulowa m’Dongosolo Lolungama la Mulungu ngofunika motani?

3 Baibulo limapereka miyezo yakutiyakuti imene iyenera kufikiridwa ndi awo amene Mulungu adzawavomereza kukhala mbali ya Dongosolo lake Latsopano lolungama. Miyezo imeneyi imafunikira masinthidwe tsopano m’moyo wa aliyense amene akufuna kukhala ndi moyo panthawiyo. Nzowona, kuti mwalingaliro la munthu, njira ya moyo yamakono yamunthu aliyense simalingaliridwa kukhala yoipa. Komabe, ndi miyezo Yabaibulo kumaphatikizapo lingaliro latsopano kotheratu ponena za moyo. Ndicho chifukwa chake Aroma 12:2, NW, amati: “Lekani kufanizitsidwa ndi dongosolo iri la zinthu, koma khalani osandulizidwa mwa kusintha maganizo anu, kuti mukadzitsimikizire chifuniro cha Mulungu chabwino ndi chokondweretsa ndi changwiro.”

4. Ngati titi ‘tiyendedi m’njira ya chowonadi,’ kodi tiyenera kutsimikiza choyenera ndi cholakwa pamaziko otani?

4 Kusanduliza koteroko kudzayambukira mmene timatsimikizirira chimene chiri cholungama ndi cholakwa. Kalelo tingakhale titadalira pa malingaliro a ena kapena kukhazikitsa miyezo ya ife eni. Koma tsopano tikuzindikira kuti linali lingaliro lenileni limeneli limene linachititsa Adamu ndi Hava kukana Mulungu kukhala Wolamulira wawo, ndi zotulukapo zowononga. Ngati tifuna chivomerezo cha Mulungu, tiyenera kuyang’ana kwa iye kaamba ka miyezo yowona ya chimene chiri cholungama ndi chimene chiri cholakwa. Miyezo imeneyo njopezeka mosavuta m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Monga momwe Salmo 119:151 limanenera kuti: ‘Malamulo ake onse ndiwo chowonadi.’ Chifukwa cha chimenecho, kugwirizana nawo kumatanthauza ‘kuyenda m’njira ya chowonadi.’ (Salmo 86:11) Kodi chimenecho sindicho chimene mufuna kuchita?

Kufunika kwa Uphungu ndi Mwambo

5. (a) Ngati titi tipange masinthidwe m’miyoyo yathu, kodi ndichowonadi chotani chonena za ife eni chimene tiyenera kukhala ofunitsitsa kuyang’anizana nacho? (b) Kodi nchiyani chimene kaŵirikaŵiri chimalepheretsa anthu kuvomera cholakwa, ndipo limodzi ndi choturukapo chotani?

5 Ngati munthu ati apange masinthidwe m’moyo wake, ayenera kuwona kuti pali kufunika kwake. “Palibe munthu wosachimwa,” limatero Baibulo. (1 Mafumu 8:46) Komabe anthu ambiri ali osafunitsitsa kuvomereza zolakwa. Chifukwa ninji? Kunyada ndiko kumene kumawapinga. Mmalo mwa kuvomereza modzichepetsa cholakwa chawo, iwo kaŵirikaŵiri amapaka ena thayo. Kutereku kumangoipitsa kwambiri vutolo.

6. Kodi ndikumagwero otani kumene tiyenera kuyang’anako kaamba ka mwambo, ndipo chifukwa ninji?

6 Vuto lalikulu mofananamo ndilo lakuti tiri opanda ungwiro ndipo sitimazindikira nthawi zonse njira yoyenera kuitsatira. Tingathedi kunyengeka kuganizira kuti njira yovulazayo njabwino kwambiri. (Miyambo 16:25) Chotero tifunikira mwambo wochokera kumagwero apamwamba kwambiri koposa munthu ngati titi tichite mogwirizanadi ndi ubwino wa ife eni kudzanso uja wa anthu anzathu. Miyambo 3:11 imatchula Magwero amenewo kuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova.”

7. (a) Kodi ndimotani mmene mwambo wochokera kwa Yehova umatifikira? (b) Kodi kuvomereza ndi kugwiritsira ntchito kwathu mwambo umenewu kumasonyezanji ponena za ife?

7 Kodi ndimotani mmene Yehova amaperekera mwambo umenewo? Mwanjira ya Mawu ake, Baibulo Loyera. Chotero pamene tiŵerenga Baibulo, kapena kusonyezedwa ndi wokhulupilira mnzathu, ndi kumva mwanjira ina yake kuti tikupereŵera, tikulandira mwambo wa Mulungu. Mwakulandira mwambo umenewu monga woyenera ndi kuchitapo kanthu kuulabadira, timatsimikizira kuti tikuyang’anizana ndi chowonadi. Tikuvomereza kuyenera kwa Mulungu kwa kutipatsa chitsogozo ndipo tikusonyeza kuti tiri mtundu wa anthu amene iye amawafuna m’Dongosolo lake Latsopano. Inde, moyo wathu umadalira pakulabadira mwambo wa Mulungu!—Miyambo 4:13.

8. (a) Kodi nchifukwa ninji tikakhala tikudzivulaza kwenikweni ngati tinanyengezera kulandira mwambo koma sitinasinthe kwenikweni njira zathu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kotonthoza kudziŵa kuti Yehova amatiwona kuli konse kumene tiri?

8 Ndithudi ngati titi tipindule ndi mwambo wa Mulungu, ife tiyenera kukhala owona mtima kwa ife eni. Sikukatichitira ubwino uliwonse kungonyengezera pamene tikuwonedwa ndi ena, ndiyeno kubwerera ku njira zathu zoyambilira pamene sakutiwona. Kuchita kwathu monyenga kukangogodomalitsa zikumbumtima zathu. Ndipo ngakhale ngati anthu angayang’ane pa ife mosirira, sitinganyenge Mlengi. Miyambo 15:3 ikutiuza kuti: “Maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.” Kudziwa kuti Yehova akuwona kuyenera kutiletsa kuchita cholakwa. Panthawi imodzimodziyo tingapeze chilimbikitso m’chitsimikiziro chakuti iye amayang’ana mwachiyanjo ‘pa abwino.’

“Lankhulani Zowona Yense ndi Mnzake”

9. (a) Pamene pafika pakulankhula chowonadi, kodi nchiyani chimene chimalandiridwa kukhala chozoloŵereka m’dziko? Chifukwa ninji? (b) Chotero, ngati munthu ati ‘aleke kufanizitsidwa ndi dongosolo iri lazinthu,’ kodi ndikusintha kotani kumene kukufunika?

9 Ngakhale kuli kwakuti samadzinenera kukhala akutsatira Baibulo mwathithithi, anthu ambiri lerolino samadzilingalira kukhala osawona mtima. Koma kodi pali angati amene mosasintha amalankhula chowonadi? Kaŵirikaŵiri anthu ochuluka amabisa chowonadi kapena amalankhula kokha zimene iwo akhulupilira kuti zidzapititsa patsogolo zolinga za iwo eni. Ngakhale kuli kwakuti kumeneku kumalingaliridwa kukhala kwa chizolowezi m’dziko, kumeneku sikumakupangitsa kukhala koyenera. Dziko lamtundu wa anthu lokhala pa udani ndi Mulungu “ligona mwa woipayo.” “Woipa” ameneyo Satana Mdyerekezi, ndiye “atate wa bodza.” Kunama kunayamba ndi iye. (1 Yohane 5:19; Yohane 8:44) Chotero sikuyenera kudabwitsa munthu ngati apeza kuti iye afunikira kupanga kusintha kwakukulu m’nkhani yakunena zowona ngati iye ati ‘aleke kufanizitsidwa ndi dongosolo iri lazinthu.’

10. Kodi ndimotani mmene kusiyiranasiyirana koipa kwakusawona mtima kumawonongera mtendere weniweni ndi chisungiko?

10 Pali chifukwa chabwino chokhalira wowona mtima. Palibe chirichonse chimene chimawononga mtendere ndi chisungiko kuposa kulephera kukhala wowona mtima nthawi zonse—panyumba, pantchito kapena bizinesi, m’kusangulutsa, ndi m’kucheza. Pamene anthu sasunga mapangano awo, pamene anamiza kapena kunyenga, palibe aliyense amapindula. Kaŵirikaŵiri okwangwanutsidwawo amapsa mtima ndi kukwiya. Kuphatikiza pa zitsenderezo za malingaliro ndi maganizo, kusawona mtima kungachititse chivulazo chakuthupi ndipo ngakhale imfa. Mwachitsanzo, zinthu zosapangika bwino, zipangizo zoipa, ndi kunena monyenga zachititsa ngozi zoipa kwambiri. Munthu amene amaganiza kuti akupindula ndi kusawona mtima kwake panthawi imodzimodziyo akuluza mwakusawona mtima kwa ena. Iye, nayenso, amalipira mitengo yokwera kwambiri ya zinthu ndi mautumiki chifukwa chakuti ponse paŵiri ogwira ntchito ndi ogula zinthu omwe amaba. Motero kusawona mtima kumadzetsa kusiyiranasiyirana koipa. Pamene anthu ambiri akudyera anzawo masuku pamutu, kugwiritsidwa mwala, chiwawa, kuvulazika, ndipo ngakhale imfa zimachuluka.

11. Kodi Yehova amalingalira motani kusawona mtima ndi kunama?

11 Chifukwa cha zipatso zoipa zimenezo, sikuli kodabwitsa kuti pakati pa zinthu zimene “Yehova amada” pali kunama, kulumbira zonama, miyeso yonyenga ndi milingo yonyenga. (Miyambo 6:16-19, NW; 20:23) Onama mwachizoloŵezi sadzakhala ndi mbali iriyonse m’madalitsa amene Mulungu wasungira awo omkonda. (Chivumbulutso 21:8) Kodi zimenezi sindizo zimene tikanaziyembekezera kwa Mulungu wolungama? Ngati Mulungu akanati apitirizebe kulekerera awo ofuna kupindula mwachinyengo molima pamsana anansi awo, kodi ndimotani mmene munthu aliyense akanawonera kukhala wosungika m’Dongosolo lake Latsopano?

12, 13. (a) Kodi Baibulo lenilenilo limanenanji ponena za kulankhula zowona? (b) Kodi kuwona mtima kwathu kuli ndi chochita chotani ponena za kuti kaya tingatumikire Yehova monga mboni zake?

12 Chifukwa cha chimenecho Baibulo silimalankhula mopeputsa pamene limalangiza kuti: “Nenani chowonadi yense ndi mnzake.” (Zekariya 8:16; Aefeso 4:25) Ponena za malonjezo kapena mapangano, “Inde,” wathu ayenera kutanthauza Inde, ndi “Iyai” wathu, Iyai. (Yakobo 5:12) Ngati tifuna kuimira “Yehova, Mulungu wa chowonadi,” tiyenera kukhala osasintha polankhula chowonadi. (Salmo 31:5) Ngati munthu sanena chowonadi, sangapeze ulemu wa Mulungu kapena wa anthu anzake. Ndiponso iye sangaimire Mulungu monga mmodzi wa Mboni Zake. Wamasalmo anati: “Kwa woipa Mulungu anena, Uli nawo chiyani Malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako? Pakamwa pako mpochita zochimwa, ndipo lilime lako likonza chinyengo.”—Salmo 50:16, 19.

13 Koma ena angafunse kuti: Kodi munthu anganene chowonadi ndi kukhala wowona mtima ndipo nakhalabe ndi moyo m’dziko lino? Kodi iye ‘angapeze chipambano’ m’bizinesi popanda kuchita chimene munthu wina aliyense akuchita?

Mulungu amasamalira Awo Amene Amagwiritsira Ntchito Chowonadi

14. Kodi Baibulo limatithandiza motani kuzindikira kuti nkotheka kudzipezera zosoŵa m’dziko iri popanda kukhala wosawona mtima?

14 Kunena kuti munthu sangathe kudzipezera zofunika za moyo popanda kukhala wosawona mtima kukakhala kunena kuti Mulungu samasamalira awo amene amamkonda. Komatu izi nzosemphana ndi chimene atumiki a Yehova akumana nacho kwazaka zikwi zambiri. (Ahebri 13:5, 6) Wamasalmo Davide ananena kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zirinkupempha chakudya.” (Salmo 37:25) Chimenechi sichikutanthauza kuti anthu olungama samakumana ndi zovuta kapena nthawi zovuta. Davide iyemwini anakakamizidwa kwakanthawi kukhala monga wothamangitsidwa m’chitaganya. Koma anali ndi zofunika za moyo.

15. Kodi Yesu ananenanji ponena za chikondwerero cha Mulungu m’kupeza kwathu zinthu zakuthupi kuti zichirikize moyo?

15 Chokondweretsa cha kulambira kowona sindicho phindu lakuthupi. Komabe, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti kuli koyenera kupemphera kwa Mulungu kaamba ka dalitso Lake pazoyesayesa zawo zakupeza “tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.” (Luka 11:2, 3) Akumavomereza kufunikira kwawo zofunika za moyo, iye anatsimikizira ophunzira kuti: “Atate wanu wakumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo.” Koma iye anawalimbikitsa kuti: “Muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:25-34) Kodi mumakhulupilira zimenezo? Ngati ziri choncho, simudzaloŵa m’chiyeso cha kunyalanyaza miyezo yolungama ya Mulungu kokha chifukwa chakuti anthu ena akutero. Mmalo mwake, mudzazindikira nzeru ya zimene zalembedwa pa 1 Timoteo 6:6-8, pamene pamati: “Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenga kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”

16. Kodi ndimotani mmene kugwiritsira ntchito kwathu malamulo amakhalidwe abwino Amalemba amenewa kungatitetezerere?

16 Kutsatira chilangizo chimenechi kumafunikira lingaliro limene liri losiyaniratu ndi limene liri lofala m’dziko lerolino. Kumeneku, kukulowetsedwamonso, mu ‘kusintha maganizo athu.’ Kukhutira ndi zofunika za moyo kumatiletsa kupanga kulondola kufunafuna ndalama ndi zinthu zakuthupi kukhala cholinga chachikulu m’moyo ndi kupewa kuloŵa m’chiyeso chakudyera masuku anthu ena kuti tizipeze. (Miyambo 28:20; Mateyu 6:24; 1 Timoteo 6:9, 10) Awo amene amapanga chuma kukhala cholinga chawo angalingalire kuti chimenechi chimaimira chisungiko ndi chimwemwe. Koma mmalomwake kuli monga momwe Baibulo limanenera kuti “wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.” (Mlaliki 5:10) Awo amene ali ndi zambiri amafuna zambiri. Kaŵirikaŵiri iwo amataikiridwa ndi thanzi lawo ndi moyo wawo wabanja kuti azipeze. Mmalo mwakukhala osungika, iwo amakhala owopa kuluza zimene iwo ali nazo.

17. (a) Pamene munthu aika mtima wake pakufunafuna chuma chakuthupi, kodi iye akunyalanyaza chowonadi chiti? (b) Kodi pali umboni wotani wakuti nkoyenera m’tsiku lathu kugwiritsira ntchito malamulo akhalidwe labwino onena zakukhala owona mtima ndi kunena zowona m’kupeza zosoŵa?

17 Munthu amene amathamangitsa chuma sakuchita mogwirizana ndi chenicheni chonga chimene Yesu ananena kuti, “chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Kuli bwino kwambiri kuika chikhulupiliro m’kukhoza kwa Mulungu m’kugawira atumiki ake. M’maiko oposa 200 pakati pa Mboni za Yehova mamiliyoni angapo pali umboni weniweni wakuti Mulungu amagawira zofunika zotero. Pansi pa mipangidwe yonse yaboma ndipo mu mtundu uliwonse wantchito yovomerezedwa, Mboni za mafuko onse ndi ziyambi ziri zokhoza kukhala ndi miyoyo yachimwemwe, limodzi ndi kugawiridwa kwa zosoŵa zawo. Chikhulupiliro chawo mkukhoza kwa Mulungu kwa kugaŵira, ngakhale pamene kuwona mtima kumawonekera kukhala kosawapindulitsa chafupidwa. Izo zapindula ulemu wa anthu anzawo ndipo kaŵirikaŵiri zimasankhidwa kukhala zolembedwa ntchito chifukwa chakuti anthu akali kufunabe kugwira ntchito ndi anthu amene ali okhulupirika. Koma chimene chiri chofunika kwambiri chiri chakuti olungama amasangalala ndi chikumbumtima choyera chifukwa cha kuwona mtima kwawo.

18, 19. (a) Kodi nchifukwa ninji anthu ameneŵa asintha miyoyo yawo kuti igwirizane ndi miyezo ya Mulungu? (b) Kodi Mulungu akufunafuna anthu amtundu wotani kuti awapulumutse kuloŵa m’Dongosolo lake Latsopano?

18 Asanakhale Mboni za Yehova, iwo anali oyenerana ndi chitsanzo chadziko kumlingo wokulirapo kapena wocheperapo. Koma kuphunzira Baibulo ndi kugwirizana ndi chowonadi chake zinawachititsa kusiya machitachita oipa. Iwo tsopano akuyesayesa mwamphamvu kusonyeza “chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.” (Tito 2:10) Nthawi zonse sikunakhale kosavuta kwa iwo kuyang’anizana ndi chowonadi ndi kupanga masinthidwe m’moyo wawo. Koma kukonda chowonadi kwawathandiza kuchita mogwirizana nacho.

19 Kodi inu mumakonda chowonadi mofananamo? Ngati mumatero, inu ndinu munthuyo amene Mulungu akumfunafuna kuti ampulumutse wamoyo kuloŵa m’Dongosolo lake Latsopano. Kuti muvomerezedwe ndi Mulungu, inu muyenera ‘kulambira mu mzimu ndi chowonadi.” (Yohane 4:24) Kumeneku kudzakusonyezani kukhala wosiyana ndi dziko lokuzingani. Palinso njira zina m’zimene muyenera kukhala ŵosiyana ndi dziko ngati muti mukondweretse Yehova. Kodi zimenezi nziti?

[Chithunzi patsamba 113]

Kodi munthu angakhale wolankhula chowonadi ndi wowona mtima napulumukabe m’zandalama m’dziko lino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena