Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 40
  • Phunziro m’Chifundo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunziro m’Chifundo
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro M’chifundo
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Anawaphunzitsa Kukhululukira Ena
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yesu Anakadya Chakudya ku Nyumba kwa Simoni ku Betaniya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 40

Mutu 40

Phunziro m’Chifundo

YESU angakhale adakali ku Naini, kumene posachedwapa anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye, kapena mwinamwake akucheza mumzinda wapafupipo. Mfarisi wina wotchedwa Simoni akukhumba kupenyetsetsa munthu amene akuchita ntchito zapaderayo. Chotero iye akuitana Yesu kudzadya naye.

Polingalira chochitikacho monga mwaŵi wa kuchitira umboni kwa amene alipo, Yesu akuvomereza chiitanocho, monga momwedi wavomerezera ziitano zina za kukadya ndi okhometsa msonkho ndi ochimwa. Komabe, pamene akuloŵa m’nyumba ya Simoni, Yesu sakulandiridwa motenthedwa maganizo kumene kaŵirikaŵiri kumapatsidwa kwa alendo.

Mapazi ovekedwa ndi nkhwaŵira amatentha ndi kuda chifukwa cha kuyenda m’misewu ya fumbi, ndipo uli mchitidwe wozolowereka wa kulandira alendo kusambitsa mapazi awo ndi madzi ozizira. Koma mapazi a Yesu sakusambitsidwa pamene afika. Iye sakulandiridwanso mwakupsopsonedwa, umene uli mwambo wofala. Ndipo mafuta a mwambo wa kulandira alendo sakuperekedwa kaamba ka tsitsi lake.

Mkati mwa nthaŵi ya chakudya, pamene alendo akuseyama pagome, mwakachetechete mkazi wina wosaitanidwa aloŵa m’chipindacho. Iye ngwodziŵika mumzindawo kuti ngwamoyo wa makhalidwe achiwerewere. Mwachiwonekere iye wamva ziphunzitso za Yesu, kuphatikizapo za chiitano chake kaamba ka ‘awo onse amene ali othodwa kudza kwa iye kaamba ka mpumulo.’ Ndipo pokhala wosonkhezeredwa maganizo kwambiri ndi zimene wawona ndi kumva, iye tsopano wafunafuna Yesu.

Mkaziyo akumka kumbuyo kwa Yesu pagomepo ndi kugwada pamapazi ake. Pamene misozi yake ikugwera pamapazi ake, iye akuipukuta ndi tsitsi lake. Iye akutenganso mafuta onunkhira m’chotengera chake, ndipo pamene apsopsonetsa mwachikondi mapazi ake, atsanulira mafutawo pamapaziwo. Simoni akuyang’ana moipidwa. “Akadakhala mneneri uyu,” iye akulingalira motero, “akanazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza iye, chifukwa ali wochimwa.”

Podziŵa kuganiza kwake, Yesu akuti: “Simoni, ndiri ndi kanthu kakunena kwa iwe.”

“Mphunzitsi nenani,” iye akuyankha motero.

“Munthu wokongoletsa ndalama anali nawo amangaŵa aŵiri,” Yesu akuyamba motero. “Mmodziyo anali ndi mangaŵa ake marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu. Popeza analibe chobwezera iwo, anawakhululukira onsewo aŵiri. Chotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?”

“Ndiyesa kuti,” akutero Simoni, mwinamwake ndi lingaliro lamphwayi pafunso lowonekera kukhala losafunikira, “iye amene anamkhululukira zoposa.”

“Waweruza bwino,” Yesu akutero. Ndiyeno potembenukira kwa mkaziyo, akuti kwa Simoni: “Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinaloŵa m’nyumba yako; sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma mkazi uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake. Sunandipatse mpsompsono wachibwenzi; koma uyu sanaleka kumpsompsonetsa mapazi anga, chiloŵere ine muno. Sunadzodza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.”

Motero mkaziyo wapereka umboni wa kulapa kochokera pansi pamtima kaamba ka makhalidwe ake apapitapo a chisembwere. Chotero Yesu akumaliza kuti: “Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, machimo ake, ndiwo ambiri akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene amakhululukira pang’ono, iye akonda pang’ono.”

Yesu sakuloleza konse kapena kulekelera chisembwere. Mmalomwake, chochitika chimenechi chimavumbula kuzindikira kwake kwa chifundo kaamba ka anthu amene amapanga zophophonya m’moyo komano amene amasonyeza kuti ali achisoni kaamba ka zimenezi ndipo motero kudza kwa Kristu kaamba ka mpumulo. Pogaŵira mpumulo weniweni kwa mkaziyo, Yesu akuti: “Machimo ako akhululukidwa. . . . Chikhulupiliro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.” Luka 7:36-50; Mateyu 11:28-30.

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akulandiridwira ndi womchereza wake, Simoni?

▪ Kodi ndani amene akufunafuna Yesu, ndipo chifukwa ninji?

▪ Kodi ndichitsanzo chotani chimene Yesu akupereka, ndipo kodi iye akuchigwiritsira ntchito motani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena