Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 41
  • Phata la Mkangano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phata la Mkangano
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu—Maziko a Kusagwirizana
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Yesu Ankazitenga Kuti Mphamvu Zochitira Zozizwitsa?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • “Nthaŵi Yonse Palibe Munthu Analankhula Chotero”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Phunzirani kwa Ine”
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 41

Mutu 41

Phata la Mkangano

MWAMSANGA atachezetsedwa kunyumba ya Simoni, Yesu akuyamba ulendo wachiŵiri waulaliki wa ku Galileya. Paulendo wake wapapitapo m’deralo, anatsagana ndi ophunzira ake oyambirira, Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane. Koma tsopano atumwi 12, ndiponso akazi ena, akutsagana naye. Ameneŵa akuphatikizapo Mariya Magadalene, Susana, ndi Yohana, amene mwamuna wake ali mdindo wa Mfumu Herode.

Pamene liŵiro la utumiki wa Yesu likuwonjezereka, mkangano wonena za ntchito yake nawonso ukutero. Pali munthu wina wogwidwa chiŵanda, amenenso ali wakhungu ndi wosakhoza kulankhula, akufika naye kwa Yesu. Pamene Yesu amchiritsa, kotero kuti wamasuka kukugwidwa ndi chiŵanda ndipo akutha kulankhula ndi kuwona, makamuwo akuzizwa. Iwo akuyamba kunena kuti: “Uyu si Mwana wa Davide kodi?”

Makamu akusonkhana m’ziŵerengero zazikulu mozinga nyumba imene Yesu akukhala kwakuti iye ndi ophunzira ake satha ngakhale kudya chakudya. Kuwonjezera pa awo amene akuganiza kuti iye angakhale “Mwana wa Davide” wolonjezedwayo, pali alembi ndi Afarisi amene adza kuchokera ku Yerusalemu kudzamchitira mwano. Pamene achibale a Yesu akumva za chipolowe chokhudza Yesu, iwo akufika kudzamgwira. Kaamba ka chifukwa chotani?

Eya, ngakhale abale ake enieni a Yesu sakukhulupilirabe kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu. Ndiponso, phokoso la anthu ndi udani zimene iye wachititsa nzosiyana kotheratu ndi Yesu amene iwo amadziŵa pamene iye anali kukula m’Nazarete. Chifukwa cha chimenecho, iwo akukhulupilira kuti kanthu kena kalakwika kwambiri ndi Yesu mwamaganizo. ‘Wasokonezeka maganizo,’ iwo akugamula motero, ndipo akufuna kumgwira ndi kumka naye.

Komabe umboni wachiwonekere ngwakuti Yesu wachiritsa munthu wogwidwa chiŵanda. Alembi ndi Afarisiwo akudziŵa kuti sangakane zenizeni za chimenechi. Chotero kuti achitire chipongwe Yesu iwo akuuza anthu kuti: “Uyu samatulutsa ziŵanda koma ndi mphamvu yake ya Beelzebule, mkulu wa ziŵanda.”

Podziŵa kuganiza kwawo, Yesu akutembenukira kwa alembi ndi Afarisi nati: “Ufumu uliwonse wogaŵanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uliwonse kapena banja logaŵanika pa lokha silidzakhala, ndipo ngati Satana, amatulutsa Satana, iye agaŵanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake?”

Ndilingaliro losapita m’mbali chotani nanga limenelo! Popeza kuti Afarisi amadzinenera kuti anthu okhala pakati pawo achotsa ziŵanda, Yesu akufunsanso kuti: “Ngati ine ndimatulutsa ziŵanda ndi mphamvu yake ya Beelzebule, ana anu amatulutsa ndi mphamvu ya yani?” Mwamawu ŵena, chinenezo chawo pa Yesu chiyeneranso kugwira ntchito pa iwo monganso pa iye. Pamenepo Yesu akuchenjeza kuti: “Koma ngati ine ndimatulutsa ziŵanda ndi mphamvu yake ya mzimu wa Mulungu, pomwepo ufumu wa Mulungu unafika pa inu.

Pochitira chitsanzo kuti kutulutsa kwake ziŵanda kuli umboni wa mphamvu yake kuposa Satana, Yesu akunena kuti: “Akhoza bwanji munthu kuloŵa m’banja la munthu wolimba ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? ndipo pamenepo adzafunkha za m’banja lake. Iye wosakhala pamodzi ndi ine akana ine, ndi iye wosasonkhanitsa amwazamwaza.” Mwachiwonekere Afarisiwo ngotsutsana ndi Yesu, akumadzisonyeza kukhala atumiki a Satana. Iwo akumwaza Aisrayeli kuwachotsa kwa iye.

Potsirizira, Yesu akuchenjeza otsutsa ausatanawo kuti ‘kuchitira mwano mzimu sikudzakhululukidwa.’ Iye akufotokoza kuti: “Aliyense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene aliyense anganenere Mzimu Woyera zoipa, sadzakhululukidwa nthaŵi ino kapena irinkudzayo.” Alembi ndi Afarisiwo apalamula mlandu wa tchimo losakhululukiridwa limenelo mwa kugwirizanitsa mwachipongwe ndi Satana zinthu zimene kwenikweni ziri kugwira ntchito kozizwitsa kwa mzimu woyera wa Mulungu. Mateyu 12:22-32; Marko 3:19-30; Yohane 7:5.

▪ Kodi ndimotani mmene ulendo wachiŵiri wa Yesu wa ku Galileya uliri wosiyana ndi woyamba?

▪ Kodi nchifukwa ninji achibale akuthupi a Yesu akuyesayesa kumgwira?

▪ Kodi ndimotani mmene Afarisi akuyesera kuchitira mwano zozizwitsa za Yesu, ndipo kodi Yesu akuwatsutsa motani?

▪ Kodi Afarisiwo ali ndi liwongo lanji, ndipo chifukwa ninji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena