Mutu 67
Alephera Kumgwira
PAMENE Phwando la Misasalo liri kuchitika, atsogoleri achipembedzo akutumiza maofesala apolisi kukagwira Yesu. Iye sakuyesa kubisala. Mmalomwake, Yesu akupitirizabe kuphunzitsa poyera, akumati: “Katsala kanthaŵi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma ine. Mudzafunafuna ine, osandipeza; ndipo pomwe ndiri ine, inu simungathe kudzapo.”
Ayudawo sakumvetsetsa, akufunsana kuti: “Adzamka kuti uyu kuti ife sitikampeza iye? kodi adzamuka kwa Ahelene obalalikawo, ndi kuphunzitsa Ahelene? Mawu aŵa amene ananena ndichiyani? Mudzandifunafuna osandipeza ine: ndipo pomwe ndiri ine, inu simungathe kudzapo?” Indedi, Yesu, akulankhula za imfa yake yoyandikirayo ndi chiukiliro kumka kumoyo wakumwamba, kumene adani ake sangatsatire.
Tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi lomalizira la phwandolo likufika. Mmaŵa uliwonse wa phwandolo, wansembe watsanulira madzi, omwe anawatunga m’Thamanda la Siloamu, kotero kuti akutsikira kutsinde kwa guwa lansembe. Mwachiwonekere kukumbutsa anthu za dzoma la tsiku ndi tsiku limeneli, Yesu akufuula kuti: “Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa ine, namwe. Iye wokhulupilira ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka mkati mwake.”
Kwenikweni, Yesu panopa akulankhula za zotulukapo zazikulu pamene mzimu woyera ukatsanuliridwa. Chaka chotsatiracho kutsanulira mzimu woyera kumeneku kukuchitika pa Pentekoste. Kumeneko, mitsinje ya madzi a moyo ikuyenda tawatawa pamene ophunzira 120 ayamba kutumikira anthu. Koma kufikira panthaŵiyo, palibe mzimu m’lingaliro lakuti palibe aliyense wa ophunzira Akristu amene ali wodzozedwa ndi mzimu woyera ndi kuitanidwira kumoyo wakumwamba.
Polabadira kuchiphunzitso cha Yesu, ena ayamba kunena kuti: “Mneneriyo ndi uyu ndithu,” mwachiwonekere akumasonyeza za mneneri wamkulu koposa Mose amene analonjezedwa kudza. Ena akuti: “Uyu ndi Kristu.” Koma ena akuti: “Kodi Kristu adza kutuluka m’Galileya? Kodi sichinati chilembo kuti Kristu adza kutuluka mwa mbewu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?”
Chotero pakukhala magaŵano pakati pa khamulo. Ena akufuna kuti Yesu amangidwe, koma palibe ndi mmodzi yemwe akumgwira. Pamene maofesala apolisi abwerera alibe Yesu, akulu ansembe ndi Afarisi akufunsa kuti: “Simunamtenga iye bwanji?”
“Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero,” maofesalawo akuyankha motero.
Atakwiya, atsogoleri achipembedzowo akuyamba kuwanyodola, kuwalalatira, ndi kuwatcha maina amwano. Iwo akuwaseka nati: “Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupilira iye, kapena wa Afarisi, koma khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembeleredwa.”
Pakumva izi, Nikodemo, Mfarisi ndi wolamulira wa Ayuda (ndiko kuti, chiŵalo cha Sanhedrin), akuyesera kulankhula mochirikiza Yesu. Mungakumbukire kuti zaka ziŵiri ndi theka zapitazo, Nikodemo anadza kwa Yesu usiku ndi kusonyeza chikhulupiliro mwa iye. Tsopano Nikodemo akuti: “Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?”
Afarisiwo akukwiyitsidwa mowonjezerekadi powona kuti mmodzi wa iwo akutchinjiriza Yesu. “Kodi iwenso uli wotuluka m’Galileya?” iwo akutero moseleula. “Santhula, nuuwone kuti m’Galileya sanauka mneneri.”
Ngakhale kuti Malemba samanena mwachindunji kuti mneneri akachokera ku Galileya, iwo amasonya kwa Kristu kukhala akuchokera kumeneko, akumati “kuŵala kwakukulu,” kukawoneka m’derali. Ndiponso, Yesu anabadwira m’Betelehemu, ndipo anali mbadwa ya Davide. Pamene kuli kwakuti mwinamwake Afarisiwo akudziŵa zimenezi, ayenera kukhala ndi thayo la kufalitsa malingaliro olakwika amene anthu nawo ponena za Yesu. Yohane 7:32-52; Yesaya 9:1, 2; Mateyu 4:13-17.
▪ Kodi nchiyani chikuchitika mmaŵa ulionse wa phwandolo, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu angasonyezere zimenezi?
▪ Kodi nchifukwa ninji maofesala akulephera kugwira Yesu, ndipo kodi atsogoleri achipembedzo akulabadira motani?
▪ Kodi Nikodemo ndani, kodi malingaliro ake ngotani kulinga kwa Yesu, ndipo kodi akuchitiridwa motani ndi Afarisi anzake?
▪ Kodi pali umboni wotani wakuti Kristu akachokera ku Galileya?