Mutu 68
Kuphunzitsa Kowonjezereka Patsiku la Chisanu ndi Chiŵiri
TSIKU lomalizira la Phwando la Misasa, tsiku la chisanu ndi chiŵiri likadali mkati. Yesu akuphunzitsa m’chipinda cha kachisi chotchedwa ‘nyumba ya chuma.’ Mwachiwonekere ili ndigawo lotchedwa Bwalo la Akazi kumene kuli mabokosi amene anthu amaponyamo zopereka zawo.
Usiku uliwonse mkati mwa phwandolo, pamakhala kuunika kwapadera mmalo a kachisi ameneŵa. Zoikapo nyali zazikulu zinayi zimaimikidwa munomo, chirichonse chokhala ndi zotengera zazikulu zinayi zodzazidwa ndi mafuta. Kuunika kochokera m’nyali zimenezi, zoyaka ndi mafuta a m’zotengera 16 kumeneku, nkoŵala mokwanira kuunikira malo aakulu ozungulira pausiku. Zimene Yesu tsopano akunena mwina zingakumbutse omvetsera ake za chisonyezero ichi. “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi,” Yesu akutero. “Iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.”
Afarisiwo akutsutsa kuti: “Muchita umboni wa inu nokha; umboni wanu suuli wowona.”
Poyankha Yesu akuti: “Ndingakhale ndichita umboni wa ine ndekha umboni wanga uli wowona; chifukwa ndidziŵa kumene ndinachokera ndi kumene ndikumukako; koma inu simudziŵa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.” Iye akuwonjezera kuti: “Ine ndine wakuchita umboni wa ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma ine achita umboni wa ine.”
“Ali kuti atate wanu?” Afarisiwo akufuna kudziŵa.
Yesu akuyankha kuti: “Simudziŵa kapena ine, kapena Atate wanga; mukadadziŵa ine, mukadadziŵanso Atate wanga.” Ngakhale kuti Afarisi akufunabe kuti Yesu amangidwe, palibe akumgwira.
“Ndimuka ine,” Yesu akutero kachiŵirinso. “Kumene ndimukako ine, simudziŵa kudza inu.”
Pakumva izi Ayudawo ayamba kudabwa kuti: “Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, kumene ndimukako ine, simudziŵa inu kudza?”
“Inu ndinu ochokera pansi,” Yesu akufotokoza motero. “Ine ndine wochokera kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindiri ine wa dziko lino lapansi.” Iye akuwonjezeranso kuti: “Ngati simukhulupilira kuti ine ndine, mudzafa m’machimo anu.”
Inde Yesu, akusonya ku kukhalapo kwake asanakhale munthu ndi kukhala kwake Mesiya wolonjezedwa, kapena Kristu. Komabe, iwo akufunsa, mosakayikira mwachipongwe kwambiri kuti: “Ndinu yani?”
Poyang’anizana ndi kukana kwawo, Yesu akuyankha kuti: “Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.” Komabe akupitiriza kuti: “Koma wondituma ine ali wowona; ndipo zimene ndazimva kwa iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.” Yesu akupitirizabe kuti: “Pamene mutadzamkweza Mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi. Ndipo wondituma ine ali ndi ine; sanandisiye ine pandekha; chifukwa ndichita ine zimene zimkondweretsa iye nthaŵi zonse.”
Pamene Yesu akunena zinthu izi, ambiri akumkhulupilira. Kwa iwowa iye akuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.”
“Tiri mbewu ya Abrahamu,” otsutsa ake akudodometsa, “ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthaŵi iriyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa aufulu?”
Ngakhale kuti Ayudawo kaŵirikaŵiri akhala pansi pa ulamuliro wachilendo, iwo samavomereza wotsendereza aliyense kukhala mbuye wawo. Amakana kutchedwa akapolo. Koma Yesu akusonyeza kuti iwo alidi akapolo. Mwanjira yotani? “Indetu, indetu, ndinena kwa inu,” Yesu akutero, “kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.”
Kukana kuvomereza ukapolo wawo kuuchimo kukuika Ayudawo m’malo angozi. “Koma kapolo sakhala m’nyumba nthaŵi yonse,” Yesu akufotokoza motero. “Mwana ndiye akhala nthaŵi yonse.” Popeza kuti kapolo alibe zoyenera za choloŵa, angakhale paupandu wa kuchotsedwa ntchito panthaŵi iriyonse. Kokha mwana wobadwira kapena woleredwadi m’banjamo amakhala “nthaŵi yonse,” ndiko kuti, malinga ngati ali moyo.
“Chifukwa chake ngati mwana adzakuyesani inu aufulu,” Yesu akupitiriza, “mudzakhala mfulu ndithu.” Motero, chowonadi chomasula anthu ndicho chowonadi chonena za Mwanayo, Yesu Kristu. Kuli kokha kudzera mwa nsembe ya moyo wake waumunthu wangwiro kuti aliyense angathe kumasulidwa kuuchimo wa imfa. Yohane 8:12-36.
▪ Kodi nkuti kumene Yesu akuphunzitsa patsiku la chisanu ndi chiŵiri? Kodi nchiyani chikuchitika usiku kumeneko, ndipo kodi chimenechi chikugwirizana motani ndi chiphunzitso cha Yesu?
▪ Kodi Yesu akunenanji ponena za chiyambi chake, ndipo kodi zimenezi ziyenera kuvumbulanji ponena za iye monga munthu?
▪ Kodi Ayudawo ali akapolo mwanjira yotani, koma kodi ndichowonadi chotani chimene chidzawamasula?