Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 71
  • Afarisi Akana Dala Kukhulupirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Afarisi Akana Dala Kukhulupirira
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Kusakhulupirira Kouma Khosi kwa Afarisi
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Anachiritsa Munthu Amene Anabadwa Wosaona
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuchiritsa Munthu Wosawona Chibadwire
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 71

Mutu 71

Afarisi Akana Dala Kukhulupirira

MAKOLO a yemwe kale anali wakhungu wopemphapemphayo akuwopa ataitanidwira pamaso pa Afarisiwo. Iwo akudziŵa kuti kwatsimikiziridwa kuti aliyense wosonyeza chikhulupiliro mwa Yesu adzachotsedwa m’sunagoge. Kudulidwa koteroko m’chiyanjano ndi ena m’chitaganya kungabweretse vuto lalikulu, makamaka pabanja losauka. Motero makolowo akuchita mochenjera.

“Kodi uyu ndimwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosawona?” Afarisiwo akufunsa motero. “Ndipo apenya bwanji tsopano?”

“Tidziŵa kuti uyu ndimwana wathu, ndi kuti anabadwa wosawona,” makolowo akutsimikizira motero. “Koma sitidziŵa umo apenyera tsopano; kapena sitimdziŵa amene anamtsegulira pamaso pake.” Ndithudi mwana wawo ayenera kukhala atawauza zonse zimene zinachitika, koma mochenjera makolowo akuti: “Mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.”

Chifukwa chake, Afarisiwo akuitananso munthuyo. Panthaŵi inoyo akuyesa kumuwopseza mwa kusonyeza kuti asonkhanitsa umboni wotsutsa Yesu. “Lemekeza Mulungu,” iwo akulamula motero. “Tidziŵa kuti munthuyo ali wochimwa.”

Munthu amene anali wosawona poyambayo sakukana kuneneza kwawo, akumati: “Ngati ali wochimwa, sindidziŵa.” Koma akuwonjezera kuti: “Chinthu chimodzi ndichidziŵa, pokhala ndinali wosawona, tsopano ndipenya.”

Poyesa kupeza cholakwa muumboni wake, Afarisiwo akufunsanso kuti: “Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji?”

“Ndinakuuzani kale,” munthuyo akudandaula motero, “ndipo simunamva; mufuna kumvanso bwanji?” Mowazazira, akufunsa kuti: “Kodi inunso mufuna kukhala akuphunzira ake?”

Yankholi likukwiyitsa Afarisiwo. “Ndiwe wophunzira wa iyeyu,” iwo akumlalatira, “ife ndife akuphunzira a Mose. Tidziŵa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziŵa kumene achokera ameneyo.”

Posonyeza kudabwa, wopemphapempha wodzichepetsayo akuyankha kuti: “Pakuti chozizwitsa chiri mmenemo, kuti inu simudziŵa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.” Kodi ndilingaliro lotani limene liyenera kupezedwa m’zimenezi? Wopemphapemphayo akusonyeza mfundo yovomerezeka: “Tidziŵa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo. Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegula maso munthu wosawona chibadwire.” Motero, kugamula kuyenera kukhala kwachiwonekere: “Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.”

Afarisiwo alibe mawu otsutsa lingaliro lachiwonekere, ndi lomvekera bwino limenelo. Iwo atsutsidwa, ndipo motero iwo akulalatira munthuyo kuti: “Wabadwa iwe konse m’zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi?” Pamenepo, iwo akutayira munthuyo kunja, mwachiwonekere kumchotsa m’sunagoge.

Pamene Yesu adziŵa zimene iwo achita, akufunafuna munthuyo ndi kumfunsa kuti: “Kodi ukhulupilira Mwana wa Mulungu?”

Poyankha, yemwe kale anali wopemphapempha wosawonayo akufunsa kuti: “Ndani iye, Ambuye, kuti ndimkhulupilire iye?”

“Wakulankhula ndi iwe ndiiyeyo,” Yesu akuyankha motero.

Nthaŵi yomweyo, munthuyo akugwada pamaso pa Yesu ndi kunena kuti: “Ndikhulupilira, Ambuye.”

Kenako Yesu akufotokoza kuti: “Kudzaŵeruza ndadza ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osawona.”

Pomva zimenezo, Afarisi omvetserawo akufunsa kuti: “Kodi ifenso ndife osawona?” Ngati iwo akanavomereza kuti ali osawona mwamaganizo, pakanakhala chodzikhululukira pa kutsutsana kwawo ndi Yesu. Monga momwe Yesu akuwauzira kuti: “Mukadakhala osawona simukadakhala nalo tchimo.” Komabe, iwo akuumilira mouma khosi kuti sali akhungu ndipo safunikira kuunikiridwa kwauzimu kulikonse. Chotero Yesu akuti: “Tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.” Yohane 9:19-41.

▪ Kodi nchifukwa ninji makolo a amene kale anali wosawona wopemphapempha akuwopa poitanidwa ndi Afarisi, ndipo chotero iwo akuyankha motani mochenjera?

▪ Kodi ndimotani mmene Afarisi akuyesera kuwopseza munthu amene kale anali wosawona?

▪ Kodi ndilingaliro lotsutsa lanzeru lachiwonekere lotani la munthuyo limene likukwiyitsa Afarisiwo?

▪ Kodi nchifukwa ninji Afarisiwo alibe chodzikhululukira kaamba ka chitsutso chawo kwa Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena