Mutu 70
Kuchiritsa Munthu Wosawona Chibadwire
PAMENE Ayudawo akuyesera kuponya miyala Yesu, iye sakuchoka mu Yerusalemu. Pambuyo pake, pa Sabata, iye ndi ophunzira ake akuyenda mumzindamo pamene awona munthu wina wakhungu chibadwire. Ophunzirawo akufunsa Yesu kuti: “Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosawona?”
Mwinamwake ophunzirawo akukhulupilira kuti, monga mmene arabi ena amachitira, munthu angachimwe ali m’mimba mwa amake. Koma Yesu akuyankha kuti: “Sanachimwa ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikawonetsedwe mwa iye.” Kusawona kwa munthuyo sikuli chotulukapo cha cholakwika chinachake kapena tchimo lochitidwa kaya ndi munthuyo kapena makolo ake. Uchimo wa munthu woyamba Adamu unachititsa anthu onse kukhala opanda ungwiro, ndipo motero kukhala mikhole ku kulemala monga kubadwa wosawona. Kulemalaku mwa munthuyu tsopano kukupereka mpata kwa Yesu kuti awonetsere ntchito za Mulungu.
Yesu akugogomezera kufulumira kwa kuchita ntchito zimenezi. “Tiyenera kugwira ntchito za iye wondituma ine, pokhala pali masana,” iye akutero. “Ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito. Pakukhala ine m’dziko lapansi, ndiri kuunika kwa dziko lapansi.” Mwamsanga imfa ya Yesu idzamuika mumdima wamanda kumene sadzachita kanthu kalikonse. Pakali pano, iye ali magwero akuunika kudziko.
Atalankhula zimenezi, Yesu akulavulira pansi nakanda thope ndi mate. Iye akuliika pamaso a munthu wosawonayo nati kwa iye: “Muka, kasambe m’thamanda la Siloamu.” Munthuyo akumvera. Ndipo pamene atero, iye angathe kuwona! Iye akusangalala chotani nanga pobwerera, akuwona kwanthaŵi yoyamba m’moyo wake!
Anansi ndi ena amene amamdziŵa akuzizwa. “Kodi suuyu uja wokhala ndi kupemphapempha?” akufunsa motero. “Ndiyeyu,” ena akuyankha motero. Koma ena sakukhulupilira zimenezi: “Iyayi, koma afanana naye.” Komabe munthuyo akuti: “Ndine amene.”
“Nanga maso ako anatseguka bwanji?” anthuwo akufuna kudziŵa.
“Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m’maso mwanga, nati kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo mmene ndinasamba ndinapenya.”
“Ali kuti iyeyo?” iwo akufunsa motero.
Iye akuyankha kuti: “Sindidziŵa.”
Tsopano anthuwo akupereka munthu anali wosawonayo kwa atsogoleri achipembedzo, Afarisi. Awa nawonso akuyamba kumfunsa mmene anayambira kuwona. “Anapaka thope m’maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya,” akufotokoza motero munthuyo.
Ndithudi, Afarisiwo ayenera kusangalala ndi wopemphapempha wochiritsidwayo! Koma mmalomwake, iwo akukana Yesu. “Munthu uyu sachokera kwa Mulungu,” iwo akutero. Kodi akuneneranji izi? “Chifukwa sasunga Sabata.” Ndipo komabe Afarisi ena akudabwa kuti: “Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere?” Chotero pali magaŵano pakati pawo.
Chifukwa chake, iwo akufunsa munthuyo kuti: “Iwe unenanji za iye, popeza anakutsegulira maso ako?”
“Ali mneneri,” iye akuyankha motero.
Afarisiwo akukana kukhulupilira zimenezi. Iwo ali okhutiritsidwa kuti payenera kukhala kugwirizana kwina kwamtseri pakati pa Yesu ndi munthuyu kuti apusitse anthu. Chotero kuti athetse nkhaniyo, iwo akuitana makolo a wopemphapemphayo kuti awafunse. Yohane 8:59; 9:1-18.
▪ Kodi nchiyani chimene chiri chochititsa kusawona kwa munthuyo, ndipo kodi sichiri chiyani?
▪ Kodi nchiyani chiri usiku umene munthu sangagwire ntchito?
▪ Pamene munthuyo wachiritsidwa, kodi awo omdziŵa akuchita motani?
▪ Kodi Afarisiwo ali ogaŵikana motani pankhani ya kuchiritsidwa kwa munthuyo?