Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 73
  • Msamariya Wachifundo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msamariya Wachifundo
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Msamariya Waunansi
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Msamariya Apezeka Kuti Ndiye Mnansi Wabwino
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mnansi Wabwino
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 73

Mutu 73

Msamariya Wachifundo

MWINAMWAKE Yesu ali pafupi ndi Betaniya, mudzi wokhala pamtunda wa makilomitala pafupifupi atatu kuchokera ku Yerusalemu. Mwamuna wina amene ali katswiri pa Chilamulo cha Mose akufika kwa iye ndi funso, akumafunsa kuti: “Mphunzitsi, ndidzaloŵe m’moyo wosatha ndi kuchita chiyani?”

Yesu akuzindikira kuti mwamunayo, loyala, sakufunsira kudziŵa, mmalomwake, akufuna kumuyesa. Cholinga cha loyalayo chingakhale cha kuchititsa Yesu kuyankha mwanjira imene idzakhumudwitsa malingaliro a Ayuda. Motero Yesu achititsa loyalayo kudziyankhira iye mwini, akumamfunsa kuti: “M’Chilamulo mulembedwa chiyani? Uŵerenga bwanji?”

Poyankha, loyalayo, akumasonyeza nzeru zapadera, akugwira mawu m’malamulo a Mulungu pa Deuteronomo 6:5 ndi Levitiko 19:18, akumati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.”

“Wayankha bwino,” Yesu akuyankha motero. “Chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.”

Komabe, loyalayo, sakukhutira. Yankho la Yesu siliri lolunjika mokwanira kwa iye. Iye akufuna chitsimikizo kuchokera kwa Yesu chakuti malingaliro ake ali olondola ndi kuti ndicho chifukwa chake iye ali wolungama pochita ndi ena. Chifukwa cha chimenecho, iye akufunsa kuti: “Ndipo mnansi wanga ndani?”

Ayuda amakhulupilira kuti liwu lakuti “mnansi” limagwira ntchito kokha kwa Ayuda anzawo, monga momwe mawu apambuyo ndi apatsogolo pa Levitiko 19:18 amawonekera kukhala akusonyezera. Kwenikweni, pambuyo pake ngakhale mtumwi Petro anati: “Mudziŵa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wamtundu wina.” Chotero loyalayo, ndipo mwinamwake ophunzira a Yesu nawonso, amakhulupilira kuti iwo ali olungama ngati achita kwa Myuda mnzawo mokoma mtima, popeza kuti, m’malingaliro awo, osakhala Ayuda saali kwenikweni anansi awo.

Kodi Yesu angawongolere motani lingaliro lawo, popanda kukhumudwitsa omvetsera ake? Iye akuwasimbira za nkhani ina yake, mwinamwake yozikidwa pachochitika chenicheni. “Munthu wina [Myuda],” Yesu akufotokoza motero, “anatsika kuchokera ku Yerusalemu kumka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.”

“Ndipo kudangotero,” Yesu akupitirizira, “kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuwona iye anapita mbali ina. Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuwona, anapita mbali ina. Koma Msamariya wina ali paulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuwona, anagwidwa chifundo.”

Ansembe ambiri ndi othandiza awo Achilevi a pakachisi amakhala mu Yeriko, mtunda wa makilomitala 23 pamsewu wowopsa wotsika mamitala 900 kuchokera kukachisi m’Yerusalemu kumene amatumikira. Wansembe ndi Mlevi akayembekezeredwa kuthandiza Myuda mnzawo wovutikayo. Koma iwo sakutero. Mmalomwake, Msamariya ndiye akutero. Ayuda amada Asamariya kwambiri kwakuti posachedwapa ananyoza Yesu ndi mawu oipa mwa kumutcha kuti “Msamariya.”

Kodi Msamariyayo akuchitanji kuthandiza Myuda ameneyo? “Anadza pali iye,” Yesu akutero, “namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye panyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira. Ndipo m’maŵa mwake anatulutsa malupiya atheka aŵiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Musungire iye, ndipo chirichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe.”

Atatsiriza nkhaniyo, Yesu akufunsa loyalayo kuti: “Uti wa aŵa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?”

Posamva bwino kaamba ka chiyamikiro chirichonse cholunjikitsidwa pa Msamariya, loyalayo akungoyankha kuti: “Iye wakumchitira chifundo.”

“Pita, nuchite iwe momwemo,” Yesu akumaliza motero.

Yesu akanati auze loyalayo mwachindunji kuti osakhala Ayuda analinso anansi ake, sikokha kuti mwamunayo akanakana kuvomereza zimenezi komanso unyinji wa omvetsera ukanakhala kumbali yake pokambitsirana ndi Yesu. Komabe, nkhani yowona yamoyo imeneyi, inakupangitsa kukhala kwachiwonekere mwa njira yosatsutsika kuti anansi athu amaphatikizapo anthu ena kuwonjezera pa anthu a fuko lathu ndi mtundu. Ndinjira yophunzitsa yozizwitsa chotani nanga imene Yesu ali nayo! Luka 10:25-37; Machitidwe 10:28; Yohane 4:9; 8:48.

▪ Kodi loyala akufunsa mafunso otani kwa Yesu, ndipo mwachiwonekere kodi chifuno chake nchotani m’kufunsako?

▪ Kodi Ayuda amakhulupilira ayani kukhala anansi awo, ndipo kodi pali chifukwa chotani chokhulupililira kuti ngakhale ophunzirawo ali ndi lingaliro lofananalo?

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akuperekera lingaliro lolondola kotero kuti loyalayo sakhoza kulitsutsa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena