Mutu 74
Uphungu kwa Marita, ndi Chilangizo pa Pemphero
MKATI mwa uminisitala wa Yesu mu Yudeya, iye akuloŵa m’mudzi wa Betaniya. Kunoko ndikumene Marita, Mariya, ndi mlongo wawo Lazaro amakhala. Mwinamwake Yesu anakumana ndi atatuwa kuchiyambiyambi kwa uminisitala wake ndipo chotero ali kale bwenzi lawo lapafupi. Mulimonse mmene zingakhalire, Yesu tsopano akupita kunyumba kwa Marita ndipo akulandiridwa naye.
Marita ali wofunitsitsa kupereka kwa Yesu zabwino koposa zomwe ali nazo. Ndithudi, uli ulemu waukulu kuchezeredwa panyumba yamunthuwe ndi Mesiya wolonjezedwayo! Chotero Marita akutanganitsidwa m’kukonzekera chakudya chabwino koposa ndi kusamalira zochitika zina zambiri zolinganizidwa kuchititsa kucheza kwa Yesu kukhala kosangalatsa mowonjezereka ndi kuti apeze bwino.
Kumbali ina, mchwemwali wa Marita Mariya akukhala pansi pamapazi a Yesu namvetsera kwa iye. Pambuyo pakanthaŵi, Marita akufika nati kwa Yesu: “Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.”
Koma Yesu akukana kunena chirichonse kwa Mariya. Mmalomwake, akupereka uphungu kwa Marita pokhala wodera nkhaŵa mopambanitsa ndi zinthu zakuthupi. “Marita, Marita,” iye akumdzudzula mokoma mtima, “uda nkhaŵa nuvutika ndi zinthu zambiri; koma chisoŵeka chinthu chimodzi.” Yesu akunena kuti sikofunika kuthera nthaŵi yochuluka kukonzekera mitundu yambiri ya chakudya. Chakudya cha mtundu umodzi chokha nchokwanira.
Malingaliro a Maritawo ngabwino; iye akufuna kukhala wolandira alendo wochereza. Komabe, mwa kudera nkhaŵa kwake kumakonzedwe a zinthu zakuthupi, iye akutayikiridwa ndi mwaŵi wa kulandira malangizo achindunji kuchokera kwa Mwana wa Mulungu mwini! Chotero Yesu akumaliza ndi kuti: “Pakuti Mariya anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.”
Pambuyo pake, pachochitika china, wophunzira wina akufunsa Yesu kuti: “Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.” Nkwachiwonekere kuti wophunzira ameneyu padalibe pafupifupi chaka chimodzi ndi theka poyambirirapo pamene Yesu anapereka pemphero lachitsanzo mu Ulaliki wake wa pa Phiri. Chotero Yesu akubwereza malangizo ake komano napitiriza kupereka fanizo kugogomezera kufunika kwa kuchita khama m’pemphero.
“Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake,” Yesu akuyamba motero, “nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu; popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo, ndipo ndiribe chompatsa; ndipo iyeyu wamkatimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa? Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zirizonse azisoŵa.”
Mwakuyerekezera kumeneku Yesu sakutanthauza kuti Yehova Mulungu ali wosafuna kuyankha mapempho, monga mmene bwenzilo linaliri m’nkhani yake. Ayi, koma iye akuchitira fanizo kuti ngati bwenzi losafunalo lidzalabadira kumapempho akhama, kuli koposa chotani nanga ndi Atate wathu wakumwamba! Chotero Yesu akupitiriza kuti: “Ndipo ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.”
Ndiyeno Yesu akusonyeza za atate aumunthu, opanda ungwiro ndi ochimwa, kuti: “Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? kapena nsomba, nadzamninkha njoka mmalo mwa nsomba? kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye?” Ndithudi, ndichilimbikitso chosonkhezera chotani nanga chimene Yesu akupereka kukhala akhama m’pemphero. Luka 10:38–11:13.
▪ Kodi nchifukwa ninji Marita akupanga makonzedwe aakulu motero kaamba ka Yesu?
▪ Kodi Mariya akuchitanji, ndipo nchifukwa ninji Yesu akumuyamikira mmalo mwa Marita?
▪ Kodi nchiyani chikusonkhezera Yesu kubwereza malangizo pa pemphero?
▪ Kodi Yesu akuchitira fanizo motani kufunika kwa kukhala akhama m’pemphero?