Mutu 75
Magwero a Chimwemwe
MKATI mwa uminisitala wake m’Galileya, Yesu anachita zozizwitsa, ndipo tsopano iye akubwereza zimenezi m’Yudeya. Mwachitsanzo, iye akuchotsa chiŵanda mwa mwamuna wina chimene chamletsa kulankhula. Makamu a anthu akuzizwa, koma osuliza akuutsa chitsutso chofanana ndi cha m’Galileya. “Ndi Beelzebule mkulu wa ziŵanda amatulutsa ziŵanda,” iwo akutero. Ena akufuna umboni wokulira kuchokera kwa Yesu ponena za amene iye ali, ndipo akumyesa mwa kumpempha chizindikiro chochokera kumwamba.
Podziŵa zimene iwo akulingalira, Yesu akupereka yankho lofananalo kwa osuliza ake m’Yudeya longa limene anapereka kwa a ku Galileya aja. Iye akunena kuti ufumu uliwonse wogaŵanika mwa iwo wokha udzagwa. “Ndiponso,” iye akufunsa, “ngati Satana agaŵanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake?” Iye akusonyeza kaimidwe kaupandu ka osuliza ake mwa kunena kuti: “Ngati ine nditulutsa ziŵanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafikira inu.”
Awo amene akuwona zozizwitsa za Yesu ayenera kulabadira mofanana ndi awo amene anachita motero zaka mazana ambiri zapitazo pamene Mose anachita chozizwitsa. Iwo anadzuma kuti: “Chala cha Mulungu ichi.” Chinalinso “chala cha Mulungu” chimene chinazokota Malamulo Khumi pamagome a miyala. Ndipo “chala cha Mulungu”—mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito—ndicho chikutheketsa Yesu kuchotsa ziŵanda ndi kuchiritsa odwala. Chotero Ufumu wa Mulungu wafikiradi osulizawa, popeza kuti Yesu, Mfumu yolinganizidwa ya Ufumuwo, iri pakati pawo pomwepo.
Pamenepo Yesu akufotokoza fanizo kuti mphamvu yake ya kuchotsa ziŵanda iri umboni wa ulamuliro wake pa Satana, monga momwedi pamene munthu wamphamvu kwambiri amadzera nagonjetsa munthu wokonzekeretsedwa bwino ndi zida wolonda nyumba yake yaufumu. Iye akubwerezanso fanizo limene anasimba mu Galileya lonena za mzimu wonyansa. Mzimuwo ukusiya munthuyo, koma pamene munthuyo sakudzaza malo opanda kanthuwo ndi zinthu zabwino, mzimuwo ukubwereranso ndi ina isanu ndi iŵiri, ndipo mkhalidwe wa munthuyo ukufikira kukhala woipa kwambiri koposa poyamba.
Adakali chimvetserere kuziphunzitsozi, mkazi wina wa m’khamulo akusonkhezereka kufuula kuti: “Yodala mimba imene idakubalani, ndi maŵere amene munayamwa.” Popeza kuti chikhumbo cha mkazi aliyense Wachiyuda ndicho cha kukhala amayi wa mneneri ndipo makamaka Mesiya, nkomvekera bwino kuti mkaziyu akunena zimenezi. Mwachiwonekere iye analingalira kuti Mariya akanakhala wachimwemwe mwapadera chifukwa cha kukhala amayi ŵa Yesu.
Komabe, Yesu mwamsanga akuwongolera mkaziyo ponena za magwero owona a chimwemwe. “Inde,” iye akuyankha motero, “koma odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.” Yesu sanapereke konse lingaliro lakuti amayi ŵake, Mariya akayenera kupatsidwa ulemu wapadera. Mmalomwake, iye anasonyeza kuti chimwemwe chowona chimapezeka m’kukhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, osati m’migwirizano ina iriyonse yakuthupi kapena zimene iye wakwaniritsa.
Monga mmene anachitira m’Galileya, Yesu akupitirizanso kudzudzula anthu a m’Yudeya kaamba ka kupempha chizindikiro chakumwamba. Iye akuwauza kuti palibe chizindikiro chimene chidzaperekedwa kusiyapo chizindikiro cha Yona. Yona anakhala chizindikiro ponse paŵiri mwa masiku ake atatu m’chinsomba ndi mwa kulalikira kwake kolimba mtima, kumene kunachititsa Anineve kusonkhezeredwa ku kulapa. “Ndipo wonani,” Yesu akutero, “wakuposa Yona ali pano.” Mofananamo, Mfumukazi ya ku Seba inazizwa ndi nzeru ya Solomo. “Ndipo wonani!” Yesu akuteronso, “woposa Solomo ali pano.”
Yesu akufotokoza kuti pamene munthu ayatsa nyali, samayiika m’chipinda chapansi kapena mumtsuko koma pachoikapo nyali kotero kuti anthu athe kuwona kuunika. Mwinamwake iye akuyerekezera kuti kuphunzitsa ndi kuchita zozizwitsa pamaso pa anthu ouma khosi ameneŵa mwa omvetsera ake nkofanana ndi kubisa kuunika kwa nyali. Maso a omvetsera oterowo saali akumodzi, kapena owona bwino, chotero chifuno cha zozizwitsa sichikukwaniritsidwa.
Yesu wangochotsa kumene chiŵanda ndipo wachititsa munthu wosalankhula kulankhula. Zimenezi ziyenera kusonkhezera anthu okhala ndi maso opanda chinyengo, kapena owona bwino, kutamanda chochitika chaulemerero chimenechi ndi kulengeza mbiri yabwino! Komabe, limodzi ndi otsutsa ameneŵa, zimenezi sindizo zimene zikuchitika. Chotero Yesu akumaliza kuti: “Potero yang’anira kuunika kuli mwa iwe kungakhale mdima. Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake la mdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuŵala kwake ikuunikira iwe.” Luka 11:14:36; Eksodo 8:18, 19; 31:18; Mateyu 12:22, 28.
▪ Kodi nchiyani chimene chiri chilabadiro cha kuchiritsa munthu kwa Yesu?
▪ Kodi nchiyani chimene chiri “chala cha Mulungu,” ndipo kodi ndimotani mmene Ufumu wa Mulungu wafikira omvetsera a Yesu?
▪ Kodi magwero a chimwemwe chowona nchiyani?
▪ Kodi munthu angakhale ndi diso lakumodzi motani?