Mutu 90
Chiyembekezo cha Chiukiriro
POTSIRIZA pake Yesu akufika ku miraga ya Betaniya, mudzi wokhala pafupifupi makilomitala atatu kuchokera ku Yerusalemu. Pangopita masiku ochepekera okha imfa ya Lazaro ndi kuikidwa zitachitika. Alongo ake Mariya ndi Marita akali kulirabe, ndipo ambiri adza kunyumba kwawo kudzawatonthoza.
Pamene akulira, munthu wina akuuza Marita kuti Yesu akubwera. Chotero akuchoka mofulumira kukamchingamira, mwachiwonekere popanda kuuza mchemwali wake. Atafika kwa Yesu, Marita akubwereza zimene iye ndi mchemwali wake ayenera kukhala atanena nthaŵi zambiri mkati mwa masiku anayi apitawo kuti: “Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.”
Komabe, Marita, akusonyeza chiyembekezo ndipo akupereka lingaliro lakuti Yesu angachitebe kanthu kena kwa mbale wake. “Ndidziŵa kuti zinthu zirizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu,” iye akutero.
“Mlongo wako adzauka,” Yesu akulonjeza motero.
Marita akuzindikira kuti Yesu akulankhula za chiukiriro cha padziko lapansi cha mtsogolo, chimene Abrahamu ndi atumiki enanso a Mulungu anayang’anira mtsogolo. Chotero akuyankha kuti: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.”
Komabe, Yesu akupereka chiyembekezo cha chitonthozo cha nthaŵi yomweyo, akumayankha kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” Iye akukumbutsa Marita kuti Mulungu wampatsa ulamuliro pa imfa, akumati: “Wokhulupilira ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupilira ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.”
Yesu sakupereka lingaliro kwa Marita lakuti anthu okhulupirika panthaŵiyo sadzafa konse. Ayi, koma mfundo imene iye akumveketsa njakuti kusonyeza chikhulupiriro mwa iye kungatsogolere kumoyo wosatha. Moyo wotero udzalandiridwa ndi anthu ambiri monga chotulukapo cha kuukitsidwa kwawo patsiku lomaliza. Koma ena amene ali okhulupirika adzapulumuka mapeto a dongosolo lino la zinthu padziko lapansi, ndipo kwa amenewa mawu a Yesu adzakhala owona m’lingaliro lenileni. Iwo sadzafa konse! Pambuyo pa mawu ochititsa nthumanzi amenewa, Yesu akufunsa Marita kuti, “Kodi ukhulupirira ichi?”
“Inde Ambuye,” iye akuyankha motero. “Ndakhulupirira ine kuti inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m’dziko lapansi.”
Pamenepo Marita akubwerera msanga kukaitana mchemwali wake, akumamuuza mtseri kuti: “Wafika mphunzitsi, akuitana iwe.” Mwamsanga Mariya akuchoka panyumbapo. Pamene ena akumuwona akupita, akumtsatira, akumalingalira kuti iye akupita kumanda achikumbukirowo.
Pofika kwa Yesu, Mariya akugwa pamapazi nalira. “Ambuye, mukadakhala kuno inu, mlongo wanga sakadamwalira,” iye akutero. Yesu akuvutika maganizo kwambiri pamene awona kuti Mariya ndi khamu la anthu omtsatira akulira. “Mwamuika iye kuti?” iye akufunsa.
“Ambuye, tiyeni mukawone,” iwo akuyankha.
Yesu nayenso akulira, akumachititsa Ayudawo kunena kuti: “Tawonani, anamkondadi!”
Ena akukumbukira kuti Yesu, panthaŵi ya Phwando la Misasa miyezi yochepekera yapitayo isanakhale, anali atachiritsa mnyamata wina wosawona chibadwire, ndipo iwo akufunsa kuti: “Kodi uyu wotsegulira maso wosawona uja, sanakhoza kodi kuchita kuti sakadafa ameneyunso?” Yohane 5:21; 6:40; 9:1-7; 11:17-37.
▪ Kodi ndiliti pamene Yesu potsirizira akufika pafupi ndi Betaniya, ndipo kodi ndimkhalidwe wotani umene uli kumeneko?
▪ Kodi ndimaziko otani amene Marita ali nawo akukhulupirira chiukiriro?
▪ Kodi Yesu akuyambukiridwa motani ndi imfa ya Lazaro?