Mutu 91
Pamene Lazaro Aukitsidwa
YESU, limodzi ndi omperekeza, tsopano akufika pamanda achikumbukiro a Lazaro. Kwenikweni, iwo ndiwo phanga lokhala ndi mwala woikidwa pakhomo. “Chotsani mwala,” Yesu akutero.
Marita akutsutsa, wosazindikirabe zimene Yesu akufuna kuchita. “Ambuye,” iye akutero, “adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anayi.”
Koma Yesu akufunsa kuti: “Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzawona ulemerero wa Mulungu?”
Chotero mwalawo ukuchotsedwa. Pamenepo Yesu akukweza maso ake napemphera kuti: “Atate, ndiyamika inu kuti munamva ine. Koma ndadziŵa ine kuti mumandimva ine nthaŵi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti inu munandituma ine.” Yesu akupemphera poyera chotero kuti anthu adziŵe kuti zimene ali pafupi kuchita zidzachitidwa mwa mphamvu yolandiridwa kuchokera kwa Mulungu. Ndiyeno akufuula ndi mawu aakulu kuti: “Lazaro, tuluka!”
Pamenepo, Lazaro akutuluka. Manja ake ndi miyendo zikali chikulungidwire ndi nsalu zakumanda, ndipo nkhope yake njozingidwa ndi mlezo. “M’masuleni iye, ndipo mlekeni amuke,” Yesu akutero.
Powona chozizwitsa ichi, Ayuda ambiri amene anadza kudzatonthoza Mariya ndi Marita akukhulupirira Yesu. Komabe, ena, akuchoka kukauza Afarisi zimene zachitika. Mwamsanga Afarisiwo ndi akulu ansembe akulinganiza kuchita msonkhano wabwalo lalikulu la Ayuda, la Sanhedrin.
Sanhedrin imaphatikizapo mkulu wa ansembe wapanthaŵiyo, Kayafa, ndiponso Afarisi, ndi Asaduki, akulu ansembe, ndi amene kale anali akulu ansembe. Ameneŵa akudandaula kuti: “Titani ife? chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. Ngati timleka iye kotero, onse adzakhulupilira iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.”
Ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo akuvomereza kuti Yesu ‘amachita zizindikiro zambiri’ chinthu chimodzi chokha chimene iwo akudera nacho nkhaŵa ndicho malo awo antchito ndi ulamuliro. Kuukitsidwa kwa Lazaro ndiko, nkhonya yaikulu kwambiri, kwa Asaduki, popeza kuti sakhulupirira chiukiriro.
Kayafa, amene mwinamwake ali Msaduki, tsopano akulankhula momvekera, kuti: “Simudziŵa kanthu konse inu, kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usawonongedwe.”
Mulungu anasonkhezera Kayafa kunena izi, popeza kuti mtumwi Yohane pambuyo pake analemba kuti: “Koma ichi [Kayafa] sananena kwa iye yekha.” Chimene kwenikweni Kayafa anatanthauza chinali chakuti Yesu ayenera kuphedwa kuti Amlepheretse kululuza mowonjezereka malo awo antchito ndi chisonkhezero. Komabe, malinga ndi kunena kwa Yohane, ‘Kayafa analosera kuti Yesu analinganizidwiratu kufera osati mtundu wokhawo, koma kuti ana a Mulungu asonkhanitsidwe pamodzi.’ Ndipo, ndithudi, ichi chiri chifuno cha Mulungu kuti Mwana wake afe monga dipo la onse.
Pamenepo Kayafa akupeza chipambano m’kusonkhezera Sanhedrin kuchita chiwembu cha kupha Yesu. Koma Yesu, mwinamwake podziŵa za chiwembucho kudzera kwa Nikodemo, chiŵalo cha Sanhedrin amene ali waubwenzi kwa iye, akuchoka kumalowo. Yohane 11:38-54.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akupemphera poyera asanaukitse Lazaro?
▪ Kodi ndimotani mmene awo amene anawona chiukiriro chimenechi akulabadirira?
▪ Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuipa kwa ziŵalo za Sanhedrin?
▪ Kodi cholinga cha Kayafa chinali chotani, koma kodi Mulungu anamgwiritsira ntchito kulosera chiyani?