‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Kodi nthawi zina mumaona kuti simukudziwa zoyenera kuchita ndipo mukufunika munthu woti akuthandizeni? Aliyense akufunika kutsogoleredwa ndi Yesu Khristu chifukwa ndi Mtsogoleri amene Mulungu anatipatsa. Yesu anati: “Ine ndine m’busa wabwino, nkhosa zanga ndimazidziwa ndipo nazonso zimandidziwa.” (Yohane 10:14) Kodi M’busa Wabwino ameneyu mumamudziwadi? Kodi mumadziwa makhalidwe ake, uthenga wake, ntchito imene ankagwira mwakhama ndiponso chikondi chake? Bukuli likuthandizani kuti mumudziwe bwino kwambiri Yesu ndiponso kuti muzimutsatira mosamala kwambiri.