Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yc phunziro 13 tsamba 28-29
  • Timoteyo Ankafuna Kuthandiza Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timoteyo Ankafuna Kuthandiza Anthu
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Yofanana
  • Timoteyo Anali Wokonzeka Komanso Wofunitsitsa Kutumikira
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Paulo, Sila ndi Timoteyo
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Timoteo—‘Mwana Weniweni m’Chikhulupiriro’
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Mwana Wanga Wokondedwa Ndi Wokhulupirika Mwa Ambuye”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Phunzitsani Ana Anu
yc phunziro 13 tsamba 28-29
Amayi ake a Timoteyo a Yunike komanso agogo ake a Loisi akuphunzitsa Timoteyo za Yehova

PHUNZIRO 13

Timoteyo Ankafuna Kuthandiza Anthu

Timoteyo anali mnyamata yemwe ankakonda kuthandiza anthu. Iye anayenda malo ambirimbiri kuti azithandiza anthu ndipo zimenezi zinapangitsa kuti azikhala moyo wosangalala. Kodi ungakonde kudziwa zimene ankachita?—

Agogo komanso amayi ake a Timoteyo ankamuphunzitsa za Yehova

Timoteyo anakulira mumzinda wina, dzina lake Lusitara. Ali mwana, agogo ake, omwe dzina lawo linali Loisi, ndi mayi ake, omwe dzina lawo linali Yunike, ankamuphunzitsa za Yehova. Timoteyo atakula ankafuna kuthandiza anthu ena kuti nawonso adziwe za Yehova.

Timoteyo adakali mnyamata, Paulo anamupempha kuti aziyenda naye limodzi pokalalikira kumadera ena ndipo anavomera. Iye anali wokonzeka kupita kulikonse kuti akathandize anthu.

Timoteyo anapita ndi Paulo ku mzinda wina, dzina lake Tesalonika, womwe unali ku Makedoniya. Pa ulendowu, anafunika kuyenda pansi mtunda wautali kenako n’kukwera bwato. Atafika kumeneko, anathandiza anthu ambiri kudziwa za Yehova. Koma anthu ena anawakwiyira ndipo ankafuna kuwamenya. Choncho Paulo ndi Timoteyo anachoka n’kumakalalikira kwina.

Timoteyo ndi Timoteyo ali pa ulendo wapamadzi

Timoteyo ankakhala mosangalala

Pambuyo pa miyezi ingapo, Paulo anamupempha Timoteyo kuti abwerere ku Tesalonika kukaona mmene abale akumeneko alili. Timoteyo anafunika kulimba mtima kuti apitenso kumzinda woopsawo. Koma Timoteyo anapitabe chifukwa ankadera nkhawa abale a mumzindawo. Pamene ankabwerera kwa Paulo anabwera ndi uthenga wabwino. Anamuuza kuti abale a ku Tesalonika ali bwino komanso zinthu zikuwayendera bwino mwauzimu.

Timoteyo anagwira ntchito limodzi ndi Paulo kwa zaka zambiri. Pa nthawi ina Paulo analemba kuti panalibe munthu wina wabwino kuposa Timoteyo, amene angamutumize kukalimbikitsa mipingo. Timoteyo ankakonda Yehova komanso anthu.

Kodi iweyo umakonda anthu ndipo umafuna kuwathandiza kudziwa za Yehova?— Ngati umatero udzakhala wosangalala kwambiri ngati Timoteyo.

WERENGANI MAVESI AWA

  • 2 Timoteyo 1:5; 3:15

  • Machitidwe 16:1-5; 17:1-10

  • 1 Atesalonika 3:2-7

  • Afilipi 2:19-22

MAFUNSO:

  • Kodi Timoteyo anakulira kuti?

  • Kodi Timoteyo ankafuna kuyenda ndi Paulo? N’chifukwa chiyani wayankha choncho?

  • N’chifukwa chiyani Timoteyo anapitanso ku Tesalonika?

  • Kodi iweyo ungatani kuti ukhale ndi moyo wosangalala ngati Timoteyo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena