Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 1
  • Kuchita Chidwi ndi Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchita Chidwi ndi Anthu
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Kukambirana Mwachibadwa
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Mmene Mungayambire Kucheza ndi Anthu Kuti Muwalalikire Mwamwayi
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 1

ULENDO WOYAMBA

Yesu akucheza ndi mayi pachitsime.

Yohane 4:6-9

PHUNZIRO 1

Kuchita Chidwi ndi Anthu

Mfundo yaikulu: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”—1 Akor. 13:4, 5.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu akucheza ndi mayi pachitsime.

VIDIYO: Yesu Anakumana ndi Mayi Wina pa Chitsime

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 4:6-9. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Yesu anadziwa zotani zokhudza mayiyo asanayambe kucheza naye?

  2. Yesu anati: “Mundipatseko madzi akumwa mayi.” N’chifukwa chiyani imeneyi inali njira yabwino yoyamba kukambirana naye?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Zikhoza kutiyendera bwino kwambiri tikamakambirana ndi anthu nkhani yomwe angachite nayo chidwi.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzikhala okonzeka kusintha. Musamakakamire kuti muyambe kukambirana ndi munthu nkhani yokhayo yomwe mwakonzekera. Mungayambe ndi kukambirana nkhani ina yomwe ili m’kamwam’kamwa. Dzifunseni kuti:

  1. ‘Kodi munyuzi mwalembedwa nkhani yanji?’

  2. ‘Kodi maneba anga, anzanga a kuntchito kapena anzanga a kusukulu akulankhula zotani?’

4. Muzichita chidwi. Dzifunseni kuti:

  1. ‘Kodi munthuyu akutani? Kodi angakhale kuti akuganiza chiyani?’

  2. ‘Kodi zomwe wavala, mmene akuonekera kapena mmene pakhomo pake palili zikundiuza chiyani zokhudza chikhalidwe chake komanso zomwe amakhulupirira?’

  3. ‘Kodi ino ndi nthawi yabwino yoti ndicheze naye?’

5. Muzimvetsera.

  1. Musamalankhule kwambiri.

  2. Muzimupatsa mpata wofotokoza maganizo ake. Ngati ndi zotheka, mukhoza kumufunsa mafunso.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mat. 7:12; 1 Akor. 9:20-23; Afil. 2:4; Yak. 1:19

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena