Kodi Mudzamamatira ku Chowonadi?
NGATIMWAYAMBA kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, funso lalikulu limene muyenera kayankha ku chikwaniritso chanu liri lakuti, Kodi ichi ndi chowonadi? Ngati mupeza kuti icho chiri, kodi mudzamamatira ku icho? Mafunso ofananawo anayang’anizana ndi anthu mu masiku a Yesu Kristu ndi atumwi ake.
Pamene atumwi analalikira ponena za Yesu, kodi ndimotani mmene anthu anachitira? Chabwino, mbiri yonena za Ufumu wa Kristu, zozizwitsa zake, nsembe yake ya dipo, kuukitsidwa kwake kwa akufa, ndi moyo wosatha zinamveka bwino, ndipo ambiri analandira zomwe anamva monga chowonadi. Koma ochulukira sanatero. M’chenicheni, gulu la Akristu la nthawi imeneyo “linaneneredwa” konsekonse. (Machitidwe 28:22) Chotero kulandira chowonadi chimene ophunzira a Yesu analalikira kunatanthauza kutsutsanandi kawonedwe kofala ndi kukumanizana ndi chitsutso. Anthu okondwerera chotero anayenera kutsimikizira ku chikwaniritso cha iwo eni kuti ziphunzitso Zachikristu zinali chowonadi. Pokhapo ndipo pamene iwo akanatenga kaimidwe kamphamvu.
Pamene Paulo ndi Barnaba anachezera Antiokeya mu Asia Minor, anthu ambiri anamvetsera ku uthenga wawo ndi chikondwerero chenicheni. Mbiri ya Baibulo imati: “Ndipo pa kuturuka iwo anapempha kuti alankhule nawonso mawu awa Sabata likudzalo. Ndipo Sabata linalo anasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mawu a Mulungu.” (Machitidwe13:42, 44) Koma chikondwerero choyambirira chimenechi chinazilala mu unyinji wa anthu pamene anamva otsutsamwa maganizo akutsutsana ndi atumwi.
Versi 45 ya Machitidwe mutu 13 limati: “Koma Ayuda pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndiPaulo, nachita mwano.” Kenaka versi 50 likupitiriza kunena kuti: “Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnaba, ndipo anawapitikitsa iwo m’malire awo.” Anthu okondwerera anayenera kuchita chosankha kaya kupitiriza kumvetsera kwa otsatira a Yesu mosasamala kanthu za chitsutso. Iwo anayenera kaya kuvomereza zomwe anamva monga chowonadi kapena kutseka makutu awo ku icho.
Chitsutso Lerolino
Monga mmene Akristu anatsutsidwira mu zana loyamba C.E. choteronso pali otsutsa lerolino omwe amayesa kutseka makutu a anthu okondwerera ku chowonadi cha Malemba chimene Mboni za Yehova zikuphunzitsa. Mabwenzi, anansi, ndi atsogoleri achipembedzo kawirikawiri amayesa mosaphula kanthu kukhwethemula okondwerera kuchoka ku kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Popanda chitsimikizo cha Malemba, otsutsawo amawombanitsa zimene amaphunzitsa ndi kupanga zinenezo za bodza.
Kodi nchiyani chimene anthu okondwerera ayenera kuchita? Kodi iwo ayenera kulola mawu a otsutsa kutseka maganizo awo ndi makutu awo monga mmene anachita ena ku Antiokeya? Kapena kodi ayenera kutsimikizira iwo eni kuchokera mu Baibulo kuti kaya zimene akuphunzira ziri chowonadi kapena ayi?
Anthu ovomereza mu mzinda wa Bereya anayamikiridwa chifukwa iwo anasanthula Malemba kuwona ngati zimene Paulo anawauza zinali zowonadi. Pamene anapeza kuti iye analankhula chowonadi, iwo anatenga kaimidwe ka nji kulinga ku icho. Tikuuzidwa kuti: “[Anthu aku Bereya] anali mfulu kuposa a muTesalonika, popeza analandira mawu ndikufunitsitsa kwa mtima wonse, nasanthula Malemba masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.”—Machitidwe 17:10, 11.
Anthu aku Bereya sanalole mawu a otsutsa kutseka malingaliro awo ku mbiri yabwino. M’malo mwake, iwo anasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kutsimikizira kuti zinthu zimene anali kumva zinali zowonadi. Iwo anapeza chuma chamtengo wapatali ndipo iwo sanali okonzekera kulola otsutsa kuwachotsa iwo ku icho. Kodi imeneyi siingakhale njira yanzeru kuitenga m’chigwirizano ndi mbiri yabwino yofananayo imene Mboni za Yehova zikulalikira lerolino?
Chifukwa Chimene Ena Amatsutsira
Nthawi zina otsutsa ali anansi adyera omwe inu mumakonda ndi kuwalemekeza, ndipo mumakhala ndi chifukwa chirichonse chakukhulupirira kuti iwo ali owona mtima mu chikondwerero cha umoyo wanu. Koma mukafunikira kulingalira ndi chifukwa ninji iwo akutsutsa ku kuphunzira kwanu Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kodi iwo ali ndi chitsimikiziro cholimba cha Malemba chakuti chimene mukuphunzira sichiri chowonadi? Kapena kodi chitsutso chawo chiri chifukwa cha zimene ena anawauza iwo? Kodi iwo alibe chidziwitso choyenerera ponena za zimene Mboni zimaphunzitsa? Ambiri amene anatsutsa Yesu anachita tero mwaumbuli ponena za zimene iye anaphunzitsa ndipo chifukwa anakhulupirira zinenezo zabodza za otsutsa.
Pamene Yesu anali kulenjekeka pa mtengo wozunzirapo, anthu omupitirira “anamchitira mwano, napukusa mitu yawo nanena, ‘Ha! iwe wakupasula kachisi, ndi kummanga masiku atatu, udzipulumutse mwini, nutsike pamtengo wozunzirapo.’ Moteronso ansembe akulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena: ‘Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha! Atsike tsopano pamtengo wozunzirapo, Kristu Mfumu ya Israyeli, kuti tiwone, ndi kukhulupirira.’ ” (Marko15:29-32) Kodi nchiyani chomwe chinali chifukwa kaamba ka khalidwe loipa limeneli?
Anthuwo anali atalola kawonedwe kawo ka Yesu kukhala katawongoleredwa ndi atsogoleri achipembedzo omwe anamuda iye chifukwa iye anawavumbulutsa iwo monga aphunzitsi onyenga amene kachitidwe kawo sikanali m’chigwirizano ndi zolalikira zawo za kukhala oimira Mulungu wowona. Ndi kuona mtima, Yesu ananena kwa iwo: “Mulumphira nji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu? Onyenga inu, Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, ‘anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo, koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.’”—Mateyu 15:3, 7-9.
Atsogoleri achipembedzo anamuda Yesu kwambiri ndi chowonadi chimene iye anaphunzitsa kotero kuti iwo anapangana kumupha iye ndi kupanga kuyesetsa kuli konse kuwatembenuza anthu motsutsana ndi iye. Lerolino, atsogoleri ambiri achipembedzo amatsutsa Mboni za Yehova ndi mphamvu yofananayo. Ndipo monga momwe zinaliri ndi Akristu oyambirira, Mboni “zimaneneredwa” kuli konse. Koma kodi chiri chanzeru kulola chitsutso chofala chimenechi kuwongolera kalingaliridwe kanu?
Chowonadi chofananacho cha Baibulo ponena za Ufumu wa Mulungu umene Yesu ndi atumwi ake analalikira chiri kulalikidwa lerolino ndi Mboni za Yehova. Mazana a zikwi za anthu kuzungulira padziko lonse lapansi akulandira mbiri yabwino imeneyi mosasamala kanthu za chitsutso champhamvu ndi mabwenzi, anansi, ndi atsogoleri achipembedzo. Awo amene akulandira uthenga wa Ufumu atsimikizira ku chikwaniritso chawo kuti icho chiri chowonadi, ndipo ali otsimikizira kuchigwiritsitsa icho.
Chotero ndi chifukwa ninji kuti muyenera kukhala ngati awo a mu zana loyamba omwe analola ena kuwatembenuza iwo kuchoka ku chowonadi cha m’Malemba chopatsa moyo chomwe chinabwera kwa iwo kudzera mwa otsatira osayanjidwa a Yesu Kristu? M’malo mwake, pitirizani kuphunzira Baibulo ndi Mboni, kugwiritsira ntchito Mawu olembedwa a Mulungu kutsimikizira ku chikwaniritso chanu kuti chimene mukuphunzira chiridi chowonadi. (Yohane 8:32) Ndipo ndi thandizo la Mulungu mamatirani ku chowonadi.