Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 2/1 tsamba 21
  • Kuumirira mu Ntchito Yawo ya Umulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuumirira mu Ntchito Yawo ya Umulungu
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Mbiri Yabwino Kuchokera ku Norway
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Iwo Anasintha Njira Yawo ya Moyo
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhosa za Yesu Zimva Mawu Ake
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 2/1 tsamba 21

Ripoti la Olengeza Ufumu

Kuumirira mu Ntchito Yawo ya Umulungu

MBONI ZA YEHOVA zimatenga mosamalitsa ntchito yawo ya umulungu yolalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 9:16; Machitidwe 20:26, 27) Okwatirana mu France anaimva mphamvu ya ntchito imeneyi kufikira aliyense ndi mbiri yabwino. Mu gawo lawo munali hositelo yomwe inali kusunga othaŵa nkhondo za ndale zadziko ndi ogwira ntchito achichepere ochokera ku maiko ena. Okwatiranawa akulongosola kuti: “Sitinadziŵe mmene tikanaloŵera mkatimo koma kokha ngati tinaitanidwa ndi wina yemwe anali kukhala mmenemo. Tinalingalira za kugwirizana ndi anthu kunja ndipo mwinamwake kupeza chiitano cha kuwachezera iwo mkati. Mwamuna wachichepere mofunitsitsa analandira magazini ndi kufunsa kuti adzachezeredwe.

“Tinachezera mwamuna wachichepere ameneyu, ndipo phunziro linayambidwa mwamsanga. Nthaŵi iriyonse bwenzi lake linalipo, koma bwenzilo silinanene liwu lirilonse. Pamene, tinali pamapeto a phunziro lachiŵiri, tinafunsa ngati iyenso angakonde kuphunzira zowonjezereka ponena za Mawu a Mulungu, iye anayankha kuti: ‘Nkulekeranji?’ Chotero phunziro lachiŵiri linayambidwa. Tinawaitana iwo ku misonkhano kuyambira pa chiyambi, ndipo iwo sanaphonyepo ndi umodzi womwe kuyambira pamenepo. Kupita kwawo patsogolo kunali kuwonekera kwambiri, makamaka pa hositeloyo, kumene iwo mwamsanga anayamba kulankhula ponena za zinthu zimene anali kuphunzira, kutulukapo m’kuyambitsidwa kwa phunziro lachitatu ndi okwatiranawo. Tsiku lina gulu lonselo linali pa khomo, lokonzekera kunyamuka kaamba ka misonkhano, pamene bwenzi linasankha kupita limodzi. Iye anatenthedwa maganizo ndipo anafuna kuti bwenzi lake lalimuna liphunzire ponena za zonsezo. Onse anayamba kuphunzira.

“Kufikira pa nthaŵiyo maphunziro asanu anali kutsogozedwa. Lirilonse linali ngati msonkhano! Aliyense anapezekapo pa phunziro la aliyense, ndipo achatsopano analowamonso. Iwo onse analankhula ponena za chowonadi, ndipo monga chotulukapo chake, phunziro lachisanu ndi chimodzi linayambidwa ndi mwamuna wina, yemwe anayamba kupezeka pa misonkhano ndi kuchitira umboni kwa bwenzi lake lachikazi.

“Ndithudi, zonsezi zinali umboni wozizwitsa mu hositeloyo. Sichinali chopepuka kwa anthu achichepere amenewa kuvala umunthu watsopano. Iwo anayenera kuleka kusuta, uchidakwa, chiwawa, mkhalidwe wachisembwere, ndi mayanjano oipa. Satana anawona ku icho kuti mabwenzi awo akale anayesera kutsekereza kupita patsogolo kwawo, kuwanyenga iwo kuti asute fodya kapena kukhala ndi mapwando a phokoso. Mmodzi wa amuna okondwererawa anatomera mkazi yemwe anali mbali ya gulu la chipembedzo. Iye anayesera kumchotsa kuchoka ku chowonadi. Komabe, iye kenaka anayamba kuphunzira ndipo kuyambira pamenepo wapanga kupita patsogolo kwabwino.

“Mogwirizana ndi mbiri ya posachedwapa,” akusimba okwatiranawo, “mmodzi wa amuna achicheperewa anapita kundende kaamba ka kaimidwe kake kauchete. M’nyengo yochepera pa chaka chimodzi, asanu ndi mmodzi ena anabatizidwa, asanu a amene mwamsanga analoŵa mu utumiki wa upainiya wothandizira. Pa gulu lonselo, asanu ndi mmodzi tsopano ali apainiya okhazikika, okhala ndi ntchito yaupainiya wapadera monga chonulirapo chawo.”

Ndi molemera chotani nanga mmene okwatirana amenewa afupidwira kaamba ka kuumirira kwawo kuchita ntchito yawo yaumulungu kufunafuna kaamba ka onga nkhosa! Ndithudi Yehova wadalitsa zoyesayesa zawo zokhulupirika. Pamene kuli kwakuti sitingakhale ndi zokumana nazo zowonekera zoterozo, nthaŵi zonse timafuna kuchita mokhulupirika ntchito yathu yaumulungu ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.​—Mateyu 24:14.

[Chithunzi patsamba 21]

Okwatiranawo mu France limodzi ndi apainiya okhazikika asanu ndi mmodzi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena