Ripoti la Olengeza Ufumu
Zokumana Nazo Kuchokera ku Tuvalu
MBIRI yabwino ya Ufumu ikulalikidwa m’zisumbu zokongola za Tuvalu, Kum’mwera kwa Pacific, ndipo umboni wabwino waperekedwa ngakhale kwa anthu a malo apamwamba. Mbale wa ku Australia ndi mkazi wake yemwe akutumikira m’ntchito yoyendayenda ku Tuvalu akutiuza ife za zokumana nazo zake:
“Mkazi wanga ndi ine tinaitanidwa kupezekapo pa chakudya panyumba ya Nduna Yaikulu ya Tuvalu. Chochitikacho chinali ulendo wa Nduna Yowona za Nkhani za Kunja ya Austrailia. Mkati mwa chakudyacho, mkazi wanga ndi ine tinali ndi mwaŵi wabwino wakuchitira umboni kwa onse aŵiri nduna ya Australia ndi mkazi wake. Pamene anali kutidziŵikitsa ife, Nduna Yaikulyyo inatchula ponena za ntchito yosangalatsa imene Mboni za Yehova zikuchita mu Tuvalu, makamaka ponena za kutembenuza kwa mabukhu athu m’chinenero cha chiTuvalu. ‘Ndiri ndi makope a zofalitisdwa zawo zonse m’laibulale yanga, ndipo ziri zabwino koposa!’ iye anatero. Onse aŵiri ndunayo ndi mkazi wake anali osangalatsidwa kumva za kupita patsogolo kwa ntchito yathu mu Tuvalu.
“Pambuyo pake m’madzulo, tinapezeka pa zosangulutsa za kumaloko za kavinidwe ka kumaloko. Pambuyo pake Governor General wa Tuvalu anatifikira ife ndi kutchula kuti Mboni zina zinali zitachezera kunyumba kwake mlungu wapita ndipo zinasiya makope ena a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Iye anawona kumbuyo kwa imodzi ya magaziniwo kulengeza kaamba ka New World Translation of the Holy Scriptures ndipo anafuna kudziŵa mmene angapezere imodzi kumaloko. Tinanena kuti mwachimwemwe tidzampatsa iye kope. Sande yotsatira, ndinapita kunyumba kwake ndi Baibulolo, ndipo tinali ndi kukambitsirana kwabwino kwa chifupifupi ora limodzi. Iye anatchula kukulira kumene iye akuyamikirira ntchito yathu ndi zofalitsidwa. M’chenicheni, pamene tinafika kunyumba kwake, mkazi wake anali kuŵerenga bukhu la Kukhala ndi Moyo Kosatha m’chi Tuvalu. Chotero tinali achimwemwe kukhala okhoza kuchitira umboni kwa ena ‘omwe ali m’malo apamwamba.’”—1 Timoteo 2:1-4.
Pa chochitika china Nduna Yaikulu ya Tuvalu inachezera Zisumbu za Solomon. Gulu la anthu a chiTuvalu omwe amakhala kumeneko anapanga phwando ku ulemerero wake. Pakati pa awo oitanidwa ku phwandolo panali miongo mmodzi, yemwe anasimba chokumana nacho chotsatirachi:
“Pamapeto pa phwandolo, Nduna Yaikuluyo inalola mwaŵi wa kufunsa mafunso ponena za zochitika za posachedwa mu Tuvalu. Funso limodzi lomwe linafunsidwa linali lakuti, ‘Kodi pali zipembedzo zirizonse zatsopano mu Tuvalu?’ Nduna Yaikuluyo inayankha kuti ‘pali zipembedzo zina zatsopano zomwe zavomerezedwa mu Tuvalu koma chimodzi chokha chabwino.’ Pamene anafunsidwa kuti nchiti chimenecho, iye anayankha kuti, ‘Mboni za Yehova.’
“Aliyense anadabwitsidwa ndi yankho lake, ndipo funso lodziŵikiratu linabuka kuti nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri ‘chipembedzo chimodzi chokha chabwino.’ Iye ananena kuti: ‘Chifukwa apasitala athu amakhala kunyumba tsiku lonse ndikungoimba belu pa ma Sande kaamba ka ife kuti tipite ndi kukamvetsera iwo. Koma Mboni za Yehova m’chenicheni zimabwera kwa inu, ndipo ngakhale kuti simugapite ku tchalitchi, izo zidzakuphunzitsani ponena za Baibulo m’nyumba mwanu mwenimweni.’”
Chotero, ngakhale kuti ena angasulize utumiki wathu wa kukhomo ndi khomo, mwachidziŵikire ena amayamikira kutenga kwathu uthengawo kunyumba zawo zenizeni—Machitidwe 5:42.