Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 8/1 tsamba 23-26
  • ‘Zingwe Zoyesera Zandigwera Mondikomera’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Zingwe Zoyesera Zandigwera Mondikomera’
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuleredwa Kwauzimu
  • Chikondwerero Mkati mwa Chiletso
  • Mmene Ndinakhalire Wandende
  • Ufulu​—Koma Nkhondo Zowonjezereka
  • Moyo m’Dziko Latsopano
  • Ndi M’nzanga wa mu Ukwati
  • “Mondikomera”
  • Ndadalitsidwa Moyo Wanga Wonse Chifukwa Chosankha Bwino Zochita
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Yehova Ndiye Pothaŵirapo Panga ndi Mphamvu Yanga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Chifundo Chanu Chiposa Moyo”
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yehova Anandiphunzitsa Kuchita Chifuniro Chake
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 8/1 tsamba 23-26

‘Zingwe Zoyesera Zandigwera Mondikomera’

Monga momwe yasimbidwira ndi D. H. MacLean

PAMENEPO ndinakhala, ora pambuyo pa ora, ndi mmodzi wa Royal Canadian Mounted Police pambali panga. Ndinali wandende wake. Tinali kupita ku msasa wandende pa Mtsinje wa Chalk, Ontario, Canada, ndipo chinawoneka ngati kuti ulendo wa makilomita 2,400 wa pa sitimawo sudzatha.

Munali mu 1944, ndipo Nkhondo ya Dziko II inali pachimake. Koma nchiyani chimene ndinali kuchita pano pa ulendo wa kundende? Chabwino, mokulira chinali chifukwa cha chimene Atate anandiphunzitsa ine kuyambira ku ubwana kunka mtsogolo. Iwo nthaŵi zonse anali kutha kukambitsirana kulikonse kosamalitsa ndi ine mwakugwiritsira ntchito ku moyo wawo weniweni mawu a wamasalmo: “Zinwe zoyesera zandigwera mondikomera.” Kenaka iwo anali kundisonkhezera ine kukalamira kaamba ka chokumana nacho chofanacho.​—Masalmo 16:6.

Kuleredwa Kwauzimu

Zinthu zimene Atate anawona pamene anali kutumikira kwa zaka zinayi monga mkulu wa gulu lankhondo mkati mwa Nkhondo ya Dziko I, makamaka zimene anawona za mkhalidwe wachinyengo wa atsogoleri a chimpedzo, zinawakwiitsa. Chotero, mu 1920, pamene Wophunzira Baibulo wotenthedwa maganizo analongosola yankho la Mulungu ku mavuto a dziko, zowonadi za Baibulo zinakantha chingwe chovomereza mu mtima mwa Atate. Amayi nawonso anatenga chikondwerero ndi kukhala mtumiki wodzipereka wa Yehova. Chotero, mlongo wanga Kay ndi ine tinali ndi mwaŵi wa kuleredwa mwauzimu.

M’kupita kwanthaŵi, Atate angulitsa bizinesi yawo, ndipo iwo ndi Amayi, anayamba kuyendayenda ku mzinda ndi mzinda mu ntchito yolalikira ya nthaŵi zonse. Chotero, mkati mwa chaka cha sukulu cha 1928, pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi chimodzi ndipo Kay anali ndi zisanu ndi zitatu, tinalowetsedwa m’masukulu osiyanasiyana asanu ndi atatu! Tinapitiriza njira ya moyo woyendayenda imeneyi kwa miyezi 18 yotsatira. Koma pamene chinafikira kukhala chovuta mowonjezereka kupereka chisamaliro choyenera ku maphunziro athu, makolo anga anagula malo omwetsera mafuta ndi garaji imene kumbali kwake kunali sitolo yogulitsira zakudya. Mosasamala kanthu za chimenecho, miyezi 18 ya upainiya imeneyi inasiya chisindikizo chosatha pa mlongo wanga ndi ine.

Nyumba yathu pafupi ndi Halifax, Nova Scotia, nthaŵi zonse inali nyumba yotseguka kaamba ka apainiya ndi oyang’anira oyendayenda. Atate anali oolowa manja ndi othandiza kwa awo ofuna kukonzedwa kwa magalimoto kapena mbali zapadera, pamene Amayi anasamalira kaamba ka zosowa za panyumba za alendo athu ambiri. Ndiri ndi zikumbukiro zowonekera za zokumana nazo zolimbikitsa chikhulupiriro zokambidwa ndi antchito a nthaŵi zonse amenewo. Ndingakumbukirenso nthaŵi imene ndinali ndi zaka 18 zakubadwa ndipo mmodzi wa abale oyendayenda anaditana ine kutsagana naye kwa milungu itatu pamene anachezera mipingo yapafupipo. Mwaŵi wosayembekezereka umenewo unakhalirirabe wosindikizidwa m’maganizo anga.

Chikondwerero Mkati mwa Chiletso

Mu 1940, pamene ndinali kokha 17, maulamuliro mu Canada analengeza kukhala lopanda lamulo “Gulu la Mboni za Yehova,” ndipo ntchito yolengeza ya Mbonizo inaletsedwa. Nsanja ya Olonda inali kusindikizidwa mwakabisira m’nyumba yathu, ndipo kuchokera kumeneko inagawiridwa m’chigawo chonse cha Nova Scotia. Ndimakumbukira chikondwerero pamene onyamula zinthu anafika mkati mwa usiku ndi mastencil ndi zoperekedwa za mapepala ndi inki.

Mkati mwa mbali ya kumayambiiro ya chiletsocho, tinagawanamo monga banja m’kugawira kwa mtundu wonse kwa pakati pa usiku kwa kabukhu kapadera kokhala ndi mutu wakuti End of Nazism. Ndiyenera kuvomereza kuti mtima wanga unali kugunda pamene ndinatuluka m’galimoto mumdima wa usiku wa chifunga umenewo. Atate anapereka malangizo a mwamsanga, omvekera. Kenaka tinasiyana ndipo aliyense anapita njira yosiyana.

Mungalingalire kudera nkhaŵa kwathu pamene Kay sanabwerere ku galimoto panthaŵi yomwe tinavomerezana. Pambuyo pa kuyembekezera koposa ora limodzi, panalibe china chirichonse chomwe tikanachita koma kupita kunyumba. Ku mpumulo wathu wokulira, iye anali kumeneko, akuyembekezera modera nkhaŵa kaamba ka ife. Iye anali anatengedwa ndi apolisi koma osati kaamba ka kugawira mabukhu oletsedwa. Wapolisi wamwamuna anali anamuwona iye ndi kudabwa kuti nchiyani chimene mtsikana wa zaka za pakati pa 13 ndi 19 wokongola anali kuchita yekha m’makwalala a Halifax m’maora oyambirira a m’mawa wozizira wa nyengo yachisanu. Chotero pamene anapereka kumuyendetsa iye kunyumba, Kay anavomereza​—timabukhu take tonse tinali tinagawiridwa kale. Ndawalayo inali chipambano chachikulu ndipo inapeza kufalitsidwa kokulira mu Canada monse.

Mmene Ndinakhalire Wandende

Pambuyo pa kumaliza sukulu yapamwamba mu 1941, ndinagwira ntchito ya ku dziko kwa chifupifupi zaka ziŵiri. Kenaka ndinapezeka pa msonkhano wachigawo mu United States, kumene ndinakumana ndi Milton Bartlett, mpainiya wachangu wa msinkhu wanga. Kutenthedwa maganizo kwake kaamba ka chowonadi ndi chimwemwe chowonekeratu m’kuchita upainiya zinali mokulira zonsonkhezera m’kusankha kwanga kusiya ntchito ya ku dziko ndi kulowa mu utumiki wa nthaŵi zonse mu March 1943.

Popeza chiletsocho chinali chidakali champhamvu, kulalikira Baibulo kunyumba ndi nyumba kunali mokulira maseŵera a mphaka ndi khoswe ndi apolisi. Pagawo latsopano mu Charlottetown, Chisumbu cha Prince Edward, ndinali wodera nkhaŵa mokulira kupita mu utumiki ndi kuwona chivomerezo cha anthu kotero kuti ndinaiwala kulemba keyala ya malo anga ogonako.

Ndinali nditachezera kokha nyumba zoŵerengeka pamene ndinafikiridwa ndi wapolisi, yemwe anafufuza m’chola changa ndi kundimanga. Popeza sindikanapereka keyala, ndinathera m’ndende, kumene ndinasungidwa osalankhulidwa kwa masiku anayi. Mwamwaŵi, mwana wamkazi wa Mboni mu mpingo anamva mkulu wa apolisi akulankhula za Mboni yachichepere yomwe wio anali kuisunga, ndipo ichi chinatsogolera ku kumangidwa kwanga ndiri kunja ndi abalewo.

Kuzengedwa mlandu kwanga kunaimitsidwa kwa miyezi ingapo, ndipo chotero ndinapitiriza mu utumiki wa kukhomo ndi khomo. Kenaka ndinapatsidwa gawo lina, ku Glace Bay, Nova Scotia. Miyezi ingapo pambuyo pake, ndinalandira zisamani zokapezeka m’bwalo lamilandu kubwerera mu Charlottetown. Ndinakonzekera mwaluso kaamba ka mlandu wanga, ndikumayembekezera kupereka umboni wamphamvu wa utumiki wanga.

Woweruzayo anakhutiritsidwa kuti ndinafikira ziyeneretso zonse za kukhala mtumiki wa chimpembedzo. Iye anawonjezera, ngakhale kuli tero, kuti unali mwambo kutumiza Mboni za Yehova ku misasa ya ndende m’chigwirizano ndi malamulo a mautumiki a mtundu. Mmenemo ndi mmene ndinafikira kukhala pa sitima imeneyo kupita ku msasa wa ndende pa Mtsinje wa Chalk, Ontario. Mkati mwa zaka ziŵiri zotsatira, ndinatumizidwa ku misasa itatu yosiyana.

Ufulu​—Koma Nkhondo Zowonjezereka

Ndinamasulidwa mu 1946 ndi kuyambanso upainiya pa Glace Bay. Ndi chiletso chitachotsedwa pa Mboni za Yehova, tinalinso aufulu kuchita ntchito yathu mu Canada ndi chinjirizo la lamulo. Kupatulidwa kumodzi kunali gawo lolankhula chiFrench la Chikatolika la Quebec, kumene chizunzo cha chipembedzo chinali chokulira. Mwakutero inayambika yomwe inadzafikira kutchedwa Nkhondo ya Quebec.

Pa Sande, November 3, 1946, msonkhano wapadera unakonzedwa mu Montreal, wopezedwapo ndi prezidenti wa Watch Tower Society ndi ena kuchokera ku malikulu a Brooklyn. Katrakiti ka moto Quebec’s Burning Hate for God and Christ and Freedom Is the Shame of All Canada kanatulutsidwa, ndipo programu ya kugawira kwa mtundu wonse inandandalitsidwa. Apainiya anaitanidwa kulemba chifunsiro kaamba ka kalasi yotsatira ya Gileadi kukalandira maphunziro owakonzekeretsa iwo kutsatira pa ndawala yapadera imeneyi mu Quebec. Ndinalemba chifunsiro ndipo mkati mwa miyezi yoŵerengeka ndinalandira chiitano ku kalasi yachisanu ndi chinayi ya Gileadi.

Moyo m’Dziko Latsopano

Popeza ndinadzimva kukhala woyenerera kubwerera ku Quebec, ndinadabwitsidwa kotheratu pamene, pa kumaliza maphunziro, ndinagawiridwa monga woyang’anira wadera mu Ontario, Canada, kukachezera mipingo yolankhula Chingelezi kumeneko. Komabe ichi sichinali chirichonse kuyerekeza ndi chozizwitsa chomwe chinabwera miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake pamene ndinalandira kalata yochokera ku Sosaite yomwe inali ndi gawo la kupita ku Australia.

Kumeneko m’dziko latsopano limenelo, gawo langa loyamba linali kutumikira dera lokwaniritsa boma lonse la Kumadzulo kwa Australia, la ukulu wa makilomita 2,528,000 m’mbali zonse zinayi! Dera lina la kumayambiriro lomwe ndinatumikira m’mbali ya pakati ya Australia linaphatikiza malo akunja otchedwa William Creek. Mboni yokha kumeneko inali kuyendetsa sitolo yopereka zinthu pamalo oima sitima. Tsiku lina ndinadabwitsidwa kuwona khamu la ngamila likuyendetsedwa ndi maAborigine a ku Australia pang’onopang’ono likuima pafupi ndi sitoloyo. Iwo anabwera kudzagula zinthu. Kukambitsiranako kunali kotere:

Wogula: Ndikufuna nsapato.

Mwini sitolo: Zazikulu kapena zazing’ono?

Wogula: Zazikulu.

Ndi chimenecho kugulitsanako kunatha, ndipo wogulayo anatuluka m’sitoloyo kukakweza nsapato zake zatsopano pa ngamila yake. Wina analowa.

Wogula: Ndikufuna dresi kaamba ka lubra (liwu la chiAboriginal kaamba ka mkazi).

Mwini sitolo: Wamkulu kapena wowonda?

Wogula: Wowonda.

Dresilo linatulutsidwa, kulipiridwa, ndipo kuponyedwa m’chola kuti likwezedwe pa ngamila yoyembekezerayo.

Ndi M’nzanga wa mu Ukwati

Zaka zitatu pambuyo pa kufika mu Australia, ndinakwatira mtsikana wokongola wa ku Brisbane, wotchedwa June Dobson. Pamapeto pa ukwati wathu, tinachita upainiya kwa chaka chimodzi tisanaitanidwe kubwerera mu ntchito yoyendayenda, choyamba mu ntchito ya dera, kenaka mu ntchito ya gawo.

Pamene ndinali wosakwatira, ndinatumikira mbali zambiri za kunja pa njinga yamoto. Komabe, tsopano ndi mkazi wanga ndi ine tinayenda pa galimoto. Msewu wodutsa Chigwa chopanda anthu cha Nullarbor, kumene kutentha mwachisawawa kumakwera kuposa 46° sentigradi, unali wosaikidwa tara kwa makilomita 1,200 ndipo unali ndi fumbi lopereka. Ilo linkawuluka, kotero kuti galimotoyo inawoneka ngati speedboat ikumayenda kupyola m’madzi. Mosamalitsa tinatseka zitseko zonse ndi mazenera ndi masking tepi kuti fumbi loipalo lisalowe mkati. Ichi chinapangitsa kutentha mkati mwa galimotoyo kukwera modabwitsa, koma kwa chifupifupi icho chinatipulumutsa ife ku kukhala okutidwa ndi m’chenga ndi fumbi.

Mkati mwa zaka zathu za ntchito ya chigawo, tinadutsadutsa kontinenti ya Australia kwanthaŵi ndi nthaŵi, kuchezera unyinji wa matauni ndi mizinda ndi kutumikira misonkhano ya dera m’makhazikitsidwe aliwonse othekera. Pamene tinayamba ntchito ya gawo mu 1953, panali kokha chigawo chimodzi mu Australia. Tsopano pali asanu.

Mu 1960 chiitano chosayembekezereka chinabwera kwa ife​—kutumikira pa Beteli ya Sydney mu Strathfield. Kusiyana ku ntchito yoyendayenda kunali kokulira, koma m’kupita kwanthaŵi ndinakhala wozolowerana ndi ntchito ya pa desiki. Mwamsanga, ngakhale kuli tero, tinali kale m’chodabwitsa china. Pambuyo pa kutumikira kwa miyezi 18 pa Beteli, June ndi ine tinalandira chiitano kupezeka pa maphunziro aposachedwa a miyezi 10 pa Sukulu ya Gileadi.

M’kusiyanitsa ndi kuphunzira kwanga kwapapitapo kwa pa Gileadi pa South Lansing, New York, nthaŵi ino tinali mu Brooklyn pa malikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova. Pa kumaliza maphunziro, tingawiridwa kubwerera ku Australia, kachiŵirinso ku ntchito yoyendayenda. Tinatumikira m’gawo limenelo kufikira 1981, pamene tinaitanidwanso kubwerera ku Sydney Beteli. Kumeneko tinali okhoza kugawana mu ntchito yokulira ya kusamutsa ofesi ya nthambi yonse, fakitale, ndi banja la Beteli kuchokera ku Strathfield kupita ku malo omangidwa chatsopano pa Ingleburn, chifupifupi makilomita 48 kuchokera pakati pa Sydney.

“Mondikomera”

Pano ntchito yanga ya pa desiki ya utumiki iri chisangalatso cha tsiku ndi tsiku. Kudziŵa mwaumwini ambiri a abale ndi alongo kuchokera ku mbali zonse za kontinentiyi chifukwa cha zaka mu ntchito ya gawo, ndiri ndi lingaliro la kukhala pamenepo ndi oyang’anira a madera pamene maripoti awo amabwera mlungu uliwonse. Maripoti a oyang’anira a zigawo amandipititsa ine mkati mwa malo a za masaŵera ndi Maholo Osonkhanira ndi mkhalidwe wonse wa msonkhano wadera. Ndi banja la Beteli la oposa 110, lokhala m’malo a kumudzi pang’ono ochotsedwa kwambiri ku phokoso ndi kuipitsa kwa mzinda, mkazi wanga ndi ine ndimamva kuti moyo pa Beteli uli ndithudi “motikomera.”

Pa tsiku limodzi la kumapeto kwa ngululu mu May 1984, m’gwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi, H. V. Mouritz, mwakachetechete anandiuza ine kuti ndalandira kuikidwa kuchokera ku Bungwe Lolamulira kutumikira monga chiwalo cha Komiti ya Nthambi ya Australia. Malingaliro anga masana amenewo anali mokulira ofanana ndi mmene analiri mu 1947 pamene ndinaŵerenga kalata yondigawira ine kutumikira m’dziko losangalatsa limeneli kunsi kumeneko.

Kubwereramo m’zaka zanga za moyo 65 m’gulu la Yehova kuli kumva kukwaniritsidwa kwaumwini kwa Masalmo 16:6. Ndithudi, “zingwe zoyesera” zagwa “mondikomera” kwambiri. Ngati ndinayenera kukonzanso moyo wanga, mopanda chikaikiro ndikanasankha njira yomwe ndaitenga. Sipangakhale zotulukapo zosangalatsa zoposa​—popanda chokumana nacho chopatsa mphotho chowonjezereka.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena