Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 3/15 tsamba 26-29
  • Kulengeza Ufumu mu Malaysia Yosiyanasiyana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulengeza Ufumu mu Malaysia Yosiyanasiyana
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Kukumana ndi Chitokoso cha Chipembedzo
  • Kuchita Ndi Zinenero ndi Miyambo
  • Mu “Land of the Headhunters”
  • ‘Wam’ng’ono Akhala Chikwi’
Nsanja ya Olonda—1989
w89 3/15 tsamba 26-29

Kulengeza Ufumu mu Malaysia Yosiyanasiyana

MASIKITI ndi nyumba zapambali zopakidwa golidi, tiakachisi ndi zimango zoloŵerapo, matchalitchi ndi nsanja, maziggurat a kachisi okometsedwa ndi mafano owumba. Iyi ndiyo Malaysia, dziko kumene zipembedzo zinayi zazikulu zadziko zimakumana. Nzika zake 16,000,000 ali aMalay, aChina, Amwenye, aEurasia, aIban, aKadazan, ndi mafuko angapo a dzikolo. Mwinamwake palibe kusiyana kokulira koteroko m’chipembedzo, mikhalidwe, mwambo, fuko, ndi chinenero kumene kungapezedwe kwina kulikonse.

Yokhala kokha kumpoto kwa equator mu South China Sea, Malaysia iri yopangidwa ndi zigawo ziŵiri za dziko: kachisumbu kamene kankatchedwa Malaya kumadzulo ndi boma la Sabah ndi Sarawak pa chisumbu cha Borneo kum’mawa. Kuchokera ku malo a zidikha a ku gombe, kupyola m’nkhalango zochindikala, kaŵirikaŵiri zosayandeka, kufika ku nsonga za mapiri atali​—kuphatikizapo Phiri la Kinabalu mu Sabah la utali wa mamita 4,101​—dzikolo liri losiyanasiyana monga mmene aliri anthu ake ndi mikhalidwe yawo ya kumalo.

Ndi mkati mwa malo a mkhalidwe umenewo mmene Mboni za Yehova zikuyesayesa kulalikira “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Kodi amakhoza bwanji kufikira anthu, ndi zinenero zosiyanasiyana, miyambo, ndi malingaliro a chipembedzo? Kodi chiri chotani kulalikira uthenga wa Ufumu m’dziko limeneli? Pamwamba pa zonse, kodi ndi chiyani chimene Mboni zakhala zokhoza kukwaniritsa?

Kukumana ndi Chitokoso cha Chipembedzo

Kufikira anthu a mikhalidwe ya chipembedzo yosiyanasiyana, ofalitsa a mbiri yabwino ayenera kuphunzira kusiyanitsa nyumba ya m’Silamu kuchokera ku ya m’Hindu, banja ya Chibuda kapena chiTao kuchokera ku ya Chiprotesitanti kapena ya Chikatolika. Ndimotani mmene ichi chingachitidwire?

Pali zisonyezero zowonekera bwino. Mwachitsanzo, guwa lofiira mowala liri chizindikiro cha nyumba ya chiTao kapena Chibuda monga mmene fano lowumba la Mariya kapena Yesu liri chizindikiro cha nyumba ya Mkatolika. Zozindikiritsa mofananamo ziri masamba a mango za nyumba za Chihindu kapena malemba Achiluya ochokera m’Koran olembedwa poloŵera m’nyumba za Chisilamu.

Kuzindikira mkhalidwe wakumbuyo wa chipembedzo wa mwininyumba chiri chinthu chimodzi; kumpangitsa iye kukhala wokondwerera m’mbiri yabwino chiri chinthu china. Kuyankha kwa nthaŵi zonse, kaŵirikaŵiri mu msanganizo wa chiChina, chiMalay, ndi Chingelezi, kuli kwakuti: “Semua agama sama lah.” Kumeneku kumatsatiridwa ndi, “Pepani, sindiri wokondwerera.” Ndi kumwetulira kwakukulu, mwininyumba wangokuwuzani kuti akulingalira kuti zipembedzo zonse ziri zofanana ndi kuti sali wokondweretsedwa.

Ambiri a anthu a ku Malaysia obadwa Abuda, a Taoist, kapena Ahindu akokedwa ndi kutembenuka kwa mwamsanga koperekedwa ndi mamishoni a Chikristu cha Dziko ndipo iwo aloŵa ku zipatuko zosiyasiyana za Chiprotesitanti. Okakamizidwa ndi atsogoleri a chipembedzo awo, ambiri a iwo atseka makutu awo ku mbiri yabwino. Chikhalirechobe, dzina lalikulu la Yehova ndi chifuno zikulengezedwa mopitirizabe m’dziko losiyanasiyana limeneli.

Chifukwa cha kuleza mtima ndi kumvetsetsa kwa Mboni za Yehova, anthu ambiri owona mtima akuvomereza moyanja ku uthenga wabwino wa Ufumu. Mwachitsanzo, lingalirani Patrick, amene kale anali wosuta fodya wokhala ndi tsitsi lalitali, losapesedwa. Iye anaphunzitsidwa m’maseŵera omenyana a chiChina ndipo anakhala wachiwawa pamene anatokosedwa. Ngankhale kuti analibe chifuno m’moyo, iye anakhudzidwa ndi mawu akuti “sipadzakhalanso imfa,” amene wofalitsa wa Ufumu anaŵerenga kwa iye kuchokera pa Chibvumbulutso 21:4. Chotero Patrick analandira phunziro la Baibulo. Wokondweretsedwa ndi chowonadi cha m’Malemba chimene iye anali kuphunzira, iye mwamsanga anayamba kuchilongosola kwa amayi ake, ponse paŵiri mwa kutumiza makalata ndi mwaumwini pamene anabwerera kumudzi. Koma amayi ake anali otsutsa kwambiri.

Tsiku lina, Patrick ndi amayi ake anali kulanga mbale wake wam’ng’ono, nayenso katswiri wa karate. Pamene mbaleyo anayamba kumenya ndi kubanthula, amayi ake anadabwitsidwa kuwona kuti Patrick sanabwezere koma anakhala wa bata. Amayi akewo anakondweretsedwa mu chimene mwana wawo anali kupunzira chimene chinali ndi mphamvu yosintha yoteroyo. Amayi ake anapanga kupita patsogolo kwamsanga ndipo anabatizidwa mkati mwa kokha miyezi isanu ndi umodzi. Amayi akewo, nawonso, anachitira umboni kwa amayi awo a zaka 73 zakubadwa, m’Buda wokhulupirira. Mayi ameneyu nayenso anayamikira chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha. Ngakhale anali osadziŵa kuŵerenga ndi kulemba, iwo anayamba kuphunzira bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, akuloweza zirembo za chiChina zambiri monga mmene anathera. Tsopano nawonso ali wofalitsa wa mbiri yabwino.

Kuchita Ndi Zinenero ndi Miyambo

Kuti achite ndi mkhalidwe wa zinenero zambiri, chola cholongedwa bwino ndi mabukhu ambiri chiri chofunikira polalikira kuchokera kunyumba ndi nyumba. Koma chimenechi sichimathetsa vutolo nthaŵi zonse.

Mwachitsanzo, kukhala m’China ndi kukhala ndi mabukhu a chiChina sikumatanthauza kuti Mboni idzakhoza kukambitsirana ndi mwininyumba wa chiChina. Kodi iwo amalankhula mawu ofanana? Ngati Mboniyo ndi m’Hokkien ndipo mwininyumba ndi m’Canton, chimenechi chikakhala vuto. Popeza kuti katchulidwe ka mawu ka chiChina kali kofanana mkamvekedwe, kusiyana kochepera kwa katchulidwe ka mawu kungapereke uthenga wosiyana kotheratu. Kuchitira chitsanzo: Chinali choposa kusangalatsa pamene mlongo wa chipainiya wolankhula chiHokkien anayenda m’malo a chiCanton akuwuza anthu kuti iye anali “wophunzira wopenga” pamene iye anafuna kunena kuti anali “wophunzira wa Baibulo.”

Ngakhale pamene liwu loyenera ligwiritsiridwa ntchito, ilo silingatanthauze chinthu chimodzimodzi kwa aliyense. Pokhala m’chitaganya cha mafuko ambiri, anthu a chiMalaysia ali mwachisawawa a thayo ndipo osamalira kusalakwira aliyense. Chiri chovuta mwapadera kaamba ka iwo kunena kuti ayi kwa alendo. Chotero, wina amaphunzira kukhala wosakondweretsedwa mopambanitsa pamene mwininyumba anena kuti inde ku kuitanira kukhala ndi phunziro la Baibulo kapena kupita ku misonkhano ya Chikristu. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti chimenechi sichikutanthauza kuti iye akulandira chirichonse. Chimatenga nthaŵi ndi kuzoloŵera kugamulapo amene ali okondweretsedwa kwenikweni.

Malaysia iri pakati pa maiko okhala ndi chiŵerengero chochulukira koposa cha matchuthi ndi mapwando a chipembedzo. Izi ziri nthaŵi pamene anthu ali otanganitsidwa kuchezera anthu ndi achibale. Mboni za ku Malaysia nazonso zimawonjezera liwiro la machitachita awo kugwiritsira ntchito matchuthi oterowo kulengeza mbiri yabwino. Koma iwo ayenera kuchita tero ndi kuchenjera ndi kumvetsetsa ngati ati akhale ndi zotulukapo zabwino.

Chaka Chatsopano cha chiChina liri kokha tsiku loterolo. Kuti atsimikizire kupita patsogolo kaamba ka nthaŵi yonse ya chaka, a Taoist amakhulupirira kuyamba chaka chatsopano ndi mawu okoma mtima ndi machitidwe abwino. Pa tsiku limenelo, Mboni ikapeŵa kugwiritsira ntchito mawu onga “imfa,” “matenda,” ndi “chowawitsa.” M’malomwake, iye akawumirira pa nkhani za chimwemwe, zonga ngati “kukhala kwa nthaŵi zonse mu umoyo wabwino ndi mtendere wosatha ndi chipambano m’dziko latsopano.” Tchuthi chimenechi siiri nthaŵi yokumbutsa anthu za matsoka awo.

Mu “Land of the Headhunters”

Popeza kuti “khamu lalikulu” liri lopangidwa ndi anthu “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” sitingathe kuleka kuganiza za mafuko ambiri a mwambo a ku East Malaysia. (Chibvumbulutso 7:9) Chiri chotenthetsa maganizo kuwona kuti chiŵerengero chowonjezereka cha anthu a ku Sarawak​—pa nthaŵi ina lodziŵika kukhala Land of the Headhunters​—akuvomereza ku uthenga wa Ufumu.

Mwachitsanzo, zaka zinayi zapita mu tauni ya mafuta ya kugombe ya Miri, mu Sarawak, munali kokha ofalitsa a Ufumu atatu. Lerolino, ambiri akusonyeza chikondwerero m’kuphunzira ponena za Baibulo. Mlongo wachipainiya amachitira ripoti maphunziro a Baibulo 17, ena a ophunzira ake iwo eni akutsogoza maphunziro ndi anthu okondwerera ena. Muli tsopano mpingo wopita patsogolo mu tauni yaing’ono ya Miri.

Mbali yodziŵika mwapadera ya anthu a chiIban a ku Sarawak iri nyumba yaitali. Chimango chachitali chimenechi pa mizati chiri chomangidwa ndi mitengo yolimba ndi masamba a mtengo wa kanjedza. Kaŵirikaŵiri chomangidwa m’mphepete mwa mtsinje pothera nkhalango, chimakhala ndi mzera wa nyumba zokhalamo kuchokera pa 30 kufika ku 40 kapena kuposapo zoyang’anizana motsatira khonde lapakati lopitamo. Yochulukira ya ntchito yathu yolalikira imachitidwa mu mtundu umenewo wa gawo.

Pa chochitika china, nkhani ya Baibulo pa nkhani yakuti “Nchiyembekezo Chotani kaamba ka Akufa?” inafunikira kuperekedwa pa imodzi ya nyumba zazitali zimenezi. Tuai rumah, kapena nyakwawa, anasonkhanitsa anthu onse ku ruai, kapena holo ya pakati. Aliyense anamvetsera modzichepetsa ndipo mwa bata langwiro kufikira nkhaniyo inatha. Kenaka, mwamuna wina anafunsa kuti: “Ndimotani mmene akufa angakhalire osadziŵa kanthu?” wina anawumirira kuti abwino anali kale m’mwamba ndipo oipa mu helo wotentha. Koma ena anapeza chiyembekezo cha kukhala kosatha m’paradaiso pa dziko lapansi kukhala chosangalatsa ndipo anafuna kudziŵa zowonjezereka. Chinali kokha monga mmene Paulo analankhulira kwa Atene pa Areopagi.​—Machitidwe 17:32-34.

M’nyumba yaitali ina munakhala Juing Insoll, m’Iban wa zaka 72 zakubadwa yemwe anali wa Tchalitchi cha Anglican. Monga wachichepere, iye anali wodabwitsidwa ndi mafunso onga awa: Ndimotani mmene Mulungu wachikondi akazunzira akufa kwamuyaya mu helo wotentha? Ngati Mulungu aliko, nchifukwa ninji kuli chisalungamo chochuluka motero? Palibe aliyense ankakhoza kumpatsa mayankho okhutiritsa. Tsiku lina bwenzi lake lochokera ku mzinda linapeza kope la bukhu lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Akuwona kuti ilo lingakhoze kuyankha mafunso a Juing, bwenzilo linamubwereka iye bukhulo. Chinali chisangalalo chotani nanga kaamba ka Juing! Pomalizira, pambuyo pa zaka 60 za kufufuza, iye anachipeza chowonadi ponena za Mulungu!

Juing anali wogamulapo kupeza kope la bukhulo kaamba ka iyemwini. Iye anayenda makilomita 240 kupita ku Kuching, mzinda waukulu wa Sarawak, ndi kufufuza malo ogulitsira mabukhu. Panalibe ngakhale chizindikiro cha bukhulo. Usiku umenewo, m’nyumba ya wachibale, anamva kuti wachibale wina anali ndi kope. Iye anatsogozedwa ku Nyumba ya Ufumu ya kumaloko ndi kugula zofalitsidwa zosiyanasiyana na 15 zobwerera nazo kunyumba yake yaitali.

Pambuyo pa kuŵerenga nkhani zonsezo, Juing anabwereranso mu mzinda, akufunsira kuti abatizidwe. Akulu anamwetulira ndi kupukusa mitu yawo. Ku kudabwitsidwa kwawo, ngakhale kuli tero, mwamsanga iwo anapeza kuti iye anali woyeneretsedwa mokwanira. Chotero, iye anabatizidwa! Atabwerera m’nyumba yaitaliyo, ndipo ndi mabukhu a Baibulo owonjezereka, Juing anayamba kuphunzitsa kwa achinansi ake. Poyamba, iye anadabwa chifukwa chimene mabwenzi ake sanalandire chowonadi mwamsanga pambuyo pa kuŵerenga mabukhuwo. Koma mwamsanga anazindikira kuti iye anayenera kuphunzira nawo Baibulo. Ripoti la utumiki wa m’munda la Juing linali nthaŵi zonse mu mkhalidwe wa diary (bukhu lolembamo zochitika za tsiku ndi tsiku)!

Kuchokera ku tauni yakutali ya Lahad Datu mu boma la Sabah kunabwera ripoti iri: Mkazi wachichepere wokwatiwa ndi ana atatu anaphunzira chowonadi kupyolera m’phunziro la Baibulo lochitidwa mwa kulemba makalata ndi mlongo wina mu Kota Kinabalu, mzinda waukulu wa bomalo. M’kupita kwa nthaŵi, mkaziyo anagamulapo kubatizidwa pa msonkhano wadera. Mkati mwa nkhani ya ubatizo, ngakhale kuli tero, mwamuna wake analowa mkati ndi kulamula kuti mkaziyo abwerere naye kunyumba.

Atabwerera kunyumba, mwamunayo anayesa kupanga malamulo koma popanda chipambano. Pomalizira, iye anafuula kuti: “Tsopano, chimene ukufuna nchiyani?” “Ndifuna kubatizidwa,” mkazi wake anayankha tero. “Kodi chimenecho chiri chofunikira kwambiri kwa iwe?” mwamunayo anafunsa. “Inde, chiri chochitika chofunika koposa m’moyo wanga.” “Chabwino!” mwamunayo anavomereza pomalizira. “Itana mkulu wako. Ndidzamanga dziŵe losambiramo kaamba ka iwe kuti ubatizidwe pompano.”

Mowona ku mawu ake, chimenecho ndicho chimene mwamunayo anachita. Ndipo mkazi wake anabatizidwa mkati mwa kuchezera kwa woyang’anira wakera kotsatira​—mu dziŵe losambiramo limene mwamuna wake anamanga kaamba iye! Koma kodi nchiyani chimene chinapatsa mlongoyo kugamulapo koteroko? Chabwino, ngakhale kuti anali wakutali, iye mokhazikika anakonzekera nkhani zonse kaama ka misonkhano yosiyanasiyana. Ngati anaphonya konse “msonkhano” uliwonse, iye anadzimva ngati anaphonya chakudya. Mlongo ameneyo tsopano akuphunzitsa ana ake ndi kutsogoza maphunziro a Baibulo apanyumba atatu.

‘Wam’ng’ono Akhala Chikwi’

Ntchito ya Ufumu mu Malaysia inatsegulidwa ndi Alfred ndi Thelma Wicke, amene anapita kumeneko kuchokera ku Australia mu 1939. Utumiki wawo wa umishonale wokhulupirika wafutukuka kufikira ku chifupifupi zaka 50, ndipo ndimodabwitsa chotani nanga mmene Yehova wadalitsira zoyesayesa zawo! Chiyambire kukhazikitsidwa kwa ofesi ya nthambi mu Penang mu 1972, ndi Mbale Wicke monga woyang’anira nthambi, ntchito yolakikira mu Malaysia yawonjezera liŵiro. Pa nthaŵi imeneyo, panali ofalitsa a Ufumu 207. Zaka khumi pambuyo pake, chiŵerengerocho chinawonjezeka katatu. Chotero, mu July 1983, nthambiyo inasamutsidwira ku Klang, mzinda wa kudoko pafupi ndi mzinda waukulu wa chigwirizano cha maboma, Kuala Lumpur. Malo a nthambi atsopano ali ndi mzera wa zimango zitatu za nyumba ziŵiri zosanjikana, zoyenerera bwino ku zosowa za nthaŵi ino. (Onani tsamba 26.)

Zaka zoŵerengeka zapita, kuyesayesa kwamphamvu kunachitidwa kupereka uthenga wa Ufumu kwa anthu owonjezereka olankhula chiChina ndi chiTamil. Tsopano, pambali pa mipingo iŵiri ya chiChina, pali magulu a chiChina ndi a chiTamil m’mipingo ina ingapo ndiponso ndi gulu lopita patsogolo la chiJapan la anthu chifupifupi 20.

Mkati mwa gawo lonselo, muli tsopano mipingo 20, ndi ofalitsa a Ufumu chifupifupi 900. Ichi chimapereka chiŵerengero cha wofalitsa mmodzi ku chifupifupi anthu 18,500. Chotero kudakali ntchito yochuluka yofunika kuchitidwa. Monga chisonyezero cha kuthekera kaamba ka kukula, anthu 2,633 anabwera ku phwando la Chikumbutso la 1988. Mboni za chiMalaysia zinasangalatsidwa ndi ichi, ndipo owonjezereka akukalamira kaamba ka utumiki wa nthaŵi zonse. Inde, Mboni za Yehova mu Malaysia zikuyang’ana kutsogolo mufunitsitsa kufikira chiŵerengero cha ofalitsa 1,000. Amakumbukira bwino lonjezo la Yehova: “Wam’ng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.”​—Yesaya 60:22.

[Mapu patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

THAILAND

MALAYSIA

Penang

Kuala Lumpur

Klang

Singapore

MALAY PENINSULA

SUMATRA

EQUATOR

South China Sea

PHILIPPINES

SABAH

Kota Kinabalu

Mt. Kinabalu

Lahad Datu

BRUNEI

Miri

MALAYSIA

SARAWAK

Kuching

BORNEO

600 Km

400 MI

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena