Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 3/1 tsamba 26-29
  • Kugwa kwa Babulo kufalitsidwa mu Japan

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwa kwa Babulo kufalitsidwa mu Japan
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Japan Adzikonzekeretsa
  • Utumiki wa Upainiya Wothandizira
  • Tsiku la Ntchito Lapadera
  • Umboni wa M’khwalala
  • Kugaŵira Magazine
  • Ukulu Woposa Wamphamvu
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 3/1 tsamba 26-29

Kugwa kwa Babulo kufalitsidwa mu Japan

“IYE wagwa! Babulo Wamkulu wagwa, iye amene anapangitsa mitundu yonse kumwako ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake!” Chilengezo chaungelo chodzutsa maganizo chimenecho chinamvedwa kwa nthaŵi yoyamba ndi mtumwi Yohane kumbuyoko m’zaka za zana loyamba za Nyengo Yathu ino. Komabe, mkati mwa nthaŵi yathu, mu “tsiku la Ambuye,” icho chalengezedwanso ndi Mboni Zachikristu za Yehova chikumamvedwa ndi mtundu wonse wa anthu.​—Chibvumbulutso 1:10; 14:8, NW.

Babulo Wamkulu ali dongosolo la dziko lonse la chipembedzo chonyenga, lokhala ndi Dziko Lachikristu monga mbali yaliŵongo koposa. Kupyola “nthaŵi yachimaliziro” yonse, ziweruzo za Yehova motsutsana naye zafalitsidwa molimba mtima ndi Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse. (Danieli 12:4) Mwachitsanzo, makope a Nsanja ya Olonda a April ndi May a chaka chatha anali ndi nkhani zamphamvu zovumbula liŵongo la chipembedzo chonyenga ndi chiwonongeko chake chikudzacho. Makope oposa pa 50 miliyoni a magazine amenewo anagaŵiridwa dziko lonse​—chilengezo champhamvudi cha kugwa kwa Babulo Wamkulu!

Japan Adzikonzekeretsa

Chitsanzo cha chisangalalo cha Mboni za Yehova kaamba ka makope apadera amenewo chinawonedwa mu Japan, amene ali mzati wa mbali ya Babulo Wamkulu ya Chishinto-Buda. Mu Japan kope la Utumiki Wathu Waufumu la December 1988 linadziŵitsa mipingo za ndawala yapadera ya utumiki wakumunda yokonzekeretsedwa kaamba ka miyezi ya April ndi May 1989. Ziitano zochirikiza ntchito yamagazine yapadera imeneyi zinapita m’makope otsatizana a Utumiki Wathu Waufumu, kupyoleranso m’makalata ku mipingo ndi mabungwe a akulu.

Chivomerezo chinali chachikulu. Ndi thandizo la Yehova, mkati mwa miyezi iŵiri imeneyo ya chaka chatha, Japan analandira umboni woposa ndi kalelonse.

Utumiki wa Upainiya Wothandizira

Chilengezo cha m’December 1988 chinaphatikizapo mawu awa: “Tikukulimbikitsani kukhala ndi chonulirapo cha kusangalala ndi upainiya wothandizira mkati mwa April ndi May, makamaka April.” Lingaliro limeneli linabwerezedwa m’kope la Utumiki Wathu Waufumu wa February 1989, umene unasonkhezera abale ‘kusintha ndandanda zawo za tsiku ndi tsiku kotero kuti akhale aminisitala odzipatulira ambiri monga mmene kukathekera akalembetse monga apainiya othandizira mu April.’

Mbonizo zinatenga zikumbutso zimenezi mosamalitsa. Chotulukapo? Chiŵerengero chapamwamba cha nthaŵi yonse cha apainiya othandizira. Mu March 1989 chiŵerengero cha apainiya othandizira chinali chitafika kale pa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha 24,115. Koma mu April chiŵerengero chimenecho chinaŵirikiza chifupifupi kaŵiri kufika pa 41,055. Kuyesayesa kochititsadi chidwi!

M’mipingo yambiri, onse kapena ofalitsa ambiri anakhala ndi phande m’mbali zosiyanasiyana za utumiki wanthaŵi zonse m’nthaŵi ya miyezi iŵiri ya ntchito yapaderayo. Izi kaŵirikaŵiri zinatenga kulinganiza kochulukira. Mkazi wina wapanyumba anakaikira ngati akanakhoza kukhala ndi phande, popeza amakhala chifupifupi mamita 900 kukwera m’mapiri kumene zoyendera machepa. Mosasamala kanthu za zimenezo, iye anafunadi kuchita upainiya wothandizira. Chotero akulu anapanga makonzedwe a kumthandiza ndi zoyendera, ndipo iye, limodzi ndi ofalitsa ena onse mumpingomo, anasangalala ndi mwezi waupainiya.

Utsogoleri wabwino wa akulu unachitiridwa chitsanzo mu Mpingo wa Otsuka wa ofalitsa 77, m’Osaka Prefecture, Mzinda wa Takatsuki, kumene akulu onse ndi atumiki otumikira anali pakati pa 73 amene anakhala ndi phande m’mitundu ya utumiki waupainiya. Awo ochita upainiya anaphatikizaponso ofalitsa obatizidwa achichepere onse omapitabe ku sukulu. Mzimu waupainiya wosonyezedwa ndi Mboni zachichepere zimenezi unali wofananadi ndi uja wowonedwa m’mipingo yambiri. Mwachitsanzo, pa azaka zapakati pa 13 ndi 19 okwanira 23 mu Mpingo wa Heiwadai mu Tokyo Prefecture, 11 ali apainiya okhazikika, ndipo 11 anachita upainiya wothandizira mu April. Mu mpingo umenewo, chiwonkhetso cha ofalitsa 93 anachita upainiya m’mwezi umodzimodziwo.

Tsiku la Ntchito Lapadera

Kope la March la Utumiki Wathu Waufumu Wachijapan linalimbikitsa abale ndi mawu awa: “Ntchito ya magazine yachirikizidwa osati pa Loŵeruka lachiŵiri ndi lachinayi pokha komanso pa Loŵeruka lirilonse la mwezi. Changu chimene abale akuchisonyeza nchoyamikirika. Mu April ntchito ya magazine yandandalitsidwa kaamba ka Loŵeruka lirilonse, koma chonde pangani kuyesayesa kwapadera kupatula April 8 monga tsiku la magazine kotero kuti aliyense angakhale ndi phande mu ntchito ya magazine pa tsikulo. Kuti chenjezo limveketsedwe kwa onse amene adzamvetsera, nkofunikira kugaŵira makope apanthaŵi yake ameneŵa mofalikira.”​—Yesaya 61:2; Chibvumbulutso 18:4, 5.

Mu February Utumiki Wathu Waufumu Wachijapan unali utagogomezera ntchito yofunika imeneyi. Uwo unati: “Pa Loŵeruka lachiŵiri, April 8, lolani kuti Mboni ya Yehova iriyonse mu Japan​—tsopano zoposa pa chiŵerengero cha 130,000​—ikhale ndi phande m’ntchito ya magazine.” Akulu analimbikitsidwa kundandalitsa ntchito za magazine zosiyanasiyana kukwaniritsa tsiku lonse kotero kuti ambiri monga kungathekere angatengemo mbali. Tikuyamikira chivomerezo chabwino cha akulu ndi chilikizo la mtima wonse la ofalitsa ena onse, tsikulo linalidi lachipambano chachikulu. Tinganene kuti pa tsikulo kumveka kwa kulengeza ziweruzo za Yehova motsutsana ndi Babulo Wamkulu kunafika pachimake mu Japan.

Mwachitsanzo, mu Mpingo wa Ushioda mu Mzinda wa Yokohama, akulu anapanga makonzedwe a utumiki umene ukapitirizabe kwa maola 13, kuyamba 7:00 a.m. mpaka 8:00 p.m. Zophatikizidwamo zinali nyengo ziŵiri za umboni wa m’khwalala, limodzinso ndi nthaŵi zochezera anthu amene sanali panyumba ndi za umboni wanthaŵi zonse wa kunyumba ndi nyumba. Ofalitsa ambiri anali okhoza kukhala ndi phande mu imodzi kapena kuposapo ya mbali zokonzedwa za utumiki, ndipo ambiri anagaŵanamo chifupifupi m’mbali iriyonse ya ntchito yokonzekeretsedwa.

Utumiki wopita patsogolo unakonzedwanso mu Mpingo wa Jonan, Mzinda wa Fukuoka. Kumeneko, makonzedwe anapangidwa okuta maola kuchokera pa 8:00 a.m. mpaka 9:00 p.m., ndi kupuma kwakufupi kokha masana. Zophatikizidwamo zinali nthaŵi za umboni wa kunyumba ndi nyumba, kufikira gawo la bizinezi ndi malo ogulako zinthu, ndi kufika kumene sanakambitsirane ndi wina aliyense pa maulendo apita. Mboni zina mu mpingo umenewo zinachitira lipoti maola ofika ku asanu ndi atatu a ntchito yolalikira pa tsikulo!

Chivomerezo cha mtima wonse cha abale chinawonedwa mu Wakayama Prefecture, kumene ofalitsa onse 55 mu Mpingo wa Kainan anakhala ndi phande m’tsiku la ntchito lapadera. Mlongo wina kumeneko, mpainiya wokhazikika, anakhala ndi mwana pa April 7. Kodi chimenecho chinamletsa kuchita umboni pa April 8? Ayi. Iye anagaŵira magazinewo m’chipatala mwenimwenimo! Kusonyeza mzimu wofananawo, mbale wa ku Osaka Prefecture anakakamizidwa kusamalira nkhani pa malo antchito yake yakuthupi pa April 8. Kodi ndimotani mmene akanakhalira ndi phande mu ntchito yapadera? Iye anapanga malo a ntchito yake yakuthupi kukhala gawo lake ndipo anapeza masabuskripishoni asanu.

Mlongo wina mu Saitama Prefecture analakalaka kukhala ndi phande mu ntchito yapadera ya tsikulo, koma anali ndi ulendo wa makilomita chifupifupi 1,280 kupita ku Mzinda wa Asahikawa ndi mwamuna wake wosakhulupirira. Komabe, iye sanaleke. Mu Asahikawa, iye anapita ku sitesheni ya sitima ndi ana ake aang’ono aŵiri, ndipo kumeneko, panja pa sitesheniyo, anapeza chimene anayembekezera: gulu la ofalitsa ochokera ku mpingo wa kumaloko ali mu utumiki wakumunda. Iye anakhoza kugawana nawo m’ntchito ya tsikulo.

Umboni wa M’khwalala

Utumiki Wathu Waufumu Wachijapan unalimbikitsa makamaka akulu kupanga makonzedwe a umboni wa m’khwalala kaamba ka April 8, ndipo chimenechi chinakhala mbali yaikulu ya tsiku lapadera limenelo. Monga zinachitikira, kunagwa mvula yaikulu dziko lonselo, koma chimenechi sichinafooketse chisangalalo cha abale. Ambiri a iwo anasonyeza mzimu wonga uja wowonedwa mwa alongo atatu olemala mu Mpingo wa Minamata, Kumamoto Prefecture. Mosasamala kanthu za misinkhu yawo​—65, 80, ndi 85​—iwo sanawope mphepo yoipayo ndipo anali chilimbikitso chabwino ku mpingo wonse; iwo anakokanso chisamaliro cha opita m’njira ambiri.

Pamene ankachita umboni wa m’khwalala, mlongo wina wa Mpingo wa West mu Mzinda wa Kashiwa anafunsa mwamuna wina kuti: “Kodi munamvapo za Babulo Wamkulu?” Pamene anamgaŵira makope a magazine a April, mwamunayo anati, “Sindiri wokondweretsedwa” ndi kupita. Komabe, pamene anafika podutsira njanji ndi kuima, iye anali kung’ung’udza yekha kuti, “Kodi Babulo Wamkulu nchiyani?” Mbale wina yemwe ankachita utumiki wa m’khwalala chapafupi anamumva iye nayendera limodzi naye m’njiramo, akulongosola chimene Babulo Wamkulu ali. Mwamunayo analandira magazinewo.

Mipingo ina inali isanachitepo umboni wa m’khwalala. Koma chiyambire pa April 8, iwo aupanga kukhala mbali yokhazikika ya ntchito yawo. Ndipo nzosadabwitsa! Umboni wa m’khwalala uli njira yachipambano kwambiri yopezera anthu amene mwanthaŵi zonse safikirika. Mlongo wina mu Mzinda wa Naha, Okinawa, anali mu umboni wa m’khwalala kunja kwa nyumba ya maofesi amene Mboni za Yehova siziloledwa kuloŵa ndi chifuno chochitira umboni. Iye anagaŵira magazine 12 mu ola limodzi mwakufikira aja oloŵa ndi otuluka m’nyumbayo.

Mlongo wina mu Mzinda wa Muroran, Hokkaido, anali mu umboni wa m’khwalala kunja kwa masitolo aakulu mkati mwa mzinda. Iye anauza mwamuna amene analandira magazine kuti: “Ngati mungafune kuphunzira zowonjezereka, tingakuchezereni m’nyumba mwanu.” Mwanunayo anampatsa adresi yake, nambala ya foni, mapu yotsogoza kunyumba kwake, ndi nthaŵi zimene akapezeka panyumba! Mlungu wotsatira, iye ndi mbale anamchezera ndikupeza kuti ankakhala m’nyumba imene inali yotsekeredwa ku maulendo anthaŵi zonse autumiki a Mboni za Yehova. Mwamuna wachichepereyo anakhutiritsidwa ndi kuŵerenga kwake Baibulo kwaumwini kuti Dziko Lachikristu linalibe chiyanjo cha Mulungu. Iye ankafunafuna Chikristu chowona ndipo anali wachimwemwe kuyamba phunziro Labaibulo lapanyumba lokhazikika.

Wofalitsa wina mu Mzinda wa Kawasaki anagawanamo mu umboni wa m’khwalala pa masana a April 8. Pamapeto a nthaŵi imene anaipatula, analankhula kwa munthu mmodzi womalizira, mkazi wachichepere yemwe anati anali anaphunzirapo Baibulo ndi Mboni za Yehova. Koma anayang’anizana ndi chitsutso kuchokera kwa makolo ake ndipo pambuyo pake anapita ku yunivesiti ndi kusamukira mu nyumba yogonamo yapasukulupo. Chotero iye analeka phunziro lake. Komabe, tiyamikira umboni wa m’khwalala, iye mwachisangalalo anayambanso phunziro lake Labaibulo ndipo akupezeka kale ku misonkhano.

Kugaŵira Magazine

Monga chotulukapo cha ambiri chotero ochirikiza ntchito yapadera, kugaŵira magazine​—makamaka okhala ndi mauthenga a chiweruzo motsutsana ndi Babulo Wamkulu​—kunali kwakukulu. Wofalitsa wamumpingo mu Osaka Prefecture anagaŵira magazine 205 mu April. Mu Mpingo wa East, Mzinda wa Kagoshima, ofalitsa 14 aliyense anagaŵira magazine oposa zana limodzi, pamene kuli kwakuti gulu lakutali la ofalitsa 12 mu Tauni ya Ogawa, Ibaraki Prefecture, anagaŵira chiwonkhetso cha magazine 1,388 mkati mwa April.

Ndithudi, mu Japan monse, magazine 3,293,266 anagaŵiridwa mu April wa chaka chatha​—92 peresenti kuposa April wa 1988! Ndi mwamphamvu chotani nanga mmene uthenga wa chiweruzo cha Yehova unalengezedwera motsutsana ndi Babulo Wamkulu!

Ukulu Woposa Wamphamvu

Motsimikizirika, mofanana ndi m’mbali zonse za dziko, Mboni za Yehova mu Japan zinali zotsimikiza ndi zachangu mu ngululu ya 1989. Zokumana nazo zawo zinapereka umboni wowonekera wakuti Yehova anadalitsa changu chawo ndi kuchirikiza zoyesayesa zawo kufalitsa ziweruzo zake motsutsana ndi chipembedzo chonyenga. Kwa ena, sizinali zosavuta kutengamo mbali; mosasamala kanthu za zimenezo, iwo anali ofunitsitsa, ndipo Yehova anadalitsa changu chawo. Ambiri amakhala m’gawo limene limagwiridwamo ntchito mobwerezabwereza, koma iwo anasonyeza mzimu umodzimodzi wa kufulumiza ndi chisangalalo mofanana ndi abale awo m’malo ena. M’zochitika zonse, mawu a Yesaya anatsimikizira kukhala owona: “Iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.”​—Yesaya 40:29.

Mosakaikira zokumana nazo zawo zinawakumbutsa mawu a mtumwi Paulo akuti: “Koma tiri nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.” (2 Akorinto 4:7) Inde, pamene munthu aika utumiki Wachikristu, “chuma ichi,” m’malo oyamba m’moyo wake, amakhala ndi “ukulu woposa wamphamvu” wopatsidwa ndi Mulungu. Lolani kuti Yehova apitirizebe kugwiritsira atumiki ake mu Japan ndi m’maiko ena onse kupereka umboni wotheratu mapeto asanafike.​—Mateyu 24:14.

Chaka chino, makope a April ndi May a Nsanja ya Olonda adzasonyeza mpambo wapachikuto pa mitu yakuti “Kodi Ndani Adzatsogolera Mtundu wa Anthu ku Mtendere?” “Mtendere wa Dziko Lonse​—Kodi Udzatanthauzanjidi?” “Mamiliyoni Akufa Tsopano Adzakhalanso ndi Moyo,” ndi “Harmagedo​—Liti?” Bwanji osapanga makonzedwe a kugaŵana chidziŵitsochi ndi anansi anu? Khalani otsimikiziridwa kuti ambiri monga mmene kungathekere akudziŵitsidwa za mbiri yabwino yozizwitsa imene Mulungu wasunga m’Baibulo kaamba ka tsiku lathu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena