Sierra Leone—Kufukula “Madiamond” Ake Amtengo Koposa
M’CHAKA cha 1462, gulu la amalinyero Achipwitikizi opanda mantha anatsikira ku gombe la Kumadzulo kwa Africa mpaka pamalo a mtunda wa makilomita 890 kumpoto kwa equator. Iwo sanawopsyezedwe ndi nthano za nyanja ya mdima yodzala ndi zirombo zowopsya yolingaliridwa kukhala kum’mwera kwa Morocco. Ndiponso, iwo sanalandire chikhulupiriro chofala chakuti dzuŵa linatentha kwambiri kufupi ndi equator chakuti nyanja inaŵira.
Mongadi mmene amalinyerowo anayembekezerera, zombo zawo zamatabwa sizinakolere moto, sanawonenso zirombo zopanda mitu zam’nthanozo. Mmalomwake, iwo anapeza mchenga woyera wokongola wapagombe ndipo kutsogolo kwake kunali mapiri aatali obiriŵira, okutidwa ndi nkhalango. Ndipo pamene mvula ya ku malo otenthawo inasefukira panthaka ndi mphenzi kung’anima kumwamba, bingu linagunda ndi kulilima m’mapirimo ngati kubangula kwa chirombo chinachake chachikulukulu. Mosangalatsa, anthu oyenda panyanjawo anatcha malowo Sierra Leone—“Mapiri a Mkango”!
Pamene zaka zinapita, anthu anadziŵa kuti kulemera kwa Sierra Leone sikunali kukongola kokha. Panalinso miyala yamtengo wapatali: chitsulo, chiziro, rutile, chromite, platinum, ndi golidi. Koma kufikira 1930 palibe amene anadziŵa zimenezi kuchititsa mbali yadziko yazamalonda kuzindikira kadziko kakang’onoka. Madiamond anapezedwa! Ngale zamtengo wake zimenezi zinatsimikizira kukhala zambirimbiri, nizikopa zikwizikwi za ofufuza.
Ena atoladi madiamond pamwamba penipeni panthaka. Mkazi wina anatola diamond yaikulu pamene ankachapa zovala zake mu mfuleni. Mwamuna wina anafukula ngale yokwanira 153-carat pamene ankabzala chimungulu m’munda. Komabe, kwakukulukulu, kupeza miyala yamtengo wapatali imeneyi kwafuna kuyesayesa kwakukulu. Mwachitsanzo, madiamond ena amakhala pansi zedi m’nthaka, osomekedwa m’mwala winawake wotchedwa kimberlite. Kuwafuna iwo kumaloŵetsamo kukumba, kutentha kwamphamvu, kuphwanya, ndi kusankha. Kumafunanso luso, chidziŵitso, ndi kuleza mtima.
Pamene kuli kwakuti ntchito zokulira za kukumba diamond zikupitirizabe mpaka lerolino, kufufuza kwa miyala yamtengo wake ya mtundu wosiyana—madiamond auzimu a mtengo wopambana koposa—kwakhala kukuchitika mu Sierra Leone chiyambire 1915. M’chaka chimenecho, mwamuna wotchedwa Alfred Joseph anachoka mu Barbados natenga ulendo wopita ku dziko limeneli pa sitima yapamadzi. Kunoko iye anayamba ntchito “yofunafuna,” osati madiamond, koma anthu amene anakhumba kutumikira Mulungu wowona “mumzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:24) Kufufuza kumeneku kunachitidwa m’njira yofanana monga kuja kochitidwa ndi Akristu am’zaka za zana loyamba—“pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.” (Machitidwe 20:20) Zaka zisanu ndi ziŵiri pambuyo pake, William R. Brown, wochokera ku West Indies anadzagwirizana ndi Alfred Joseph m’ntchito imeneyi.
Podzafika kumapeto kwa 1923, mpingo waung’ono unakhazikitsidwa mu likulu, Freetown. Mpingo umenewo unaphatikizapo obatizidwa chatsopano 14. Lerolino, anthu 632 m’mipingo 30 akukhala ndi phande mokangalika m’ntchito yolalikira monga Mboni za Yehova. Zoyesayesa zawo zakupeza ndi kufukula zimene zingatchedwe madiamond auzimu amtengo wapatali a Sierra Leone zapitirizabe kukhala zachipambano mokulira.
Ofufuza Chowonadi Okangalika
Ophunzira ena atsopano a Yesu Kristu atsimikizira kukhala ngati madiamond otoledwa mosavuta pamwamba pa nthaka. Iwo afunafuna Mboni za Yehova mokangalika. Mmodzi wa ameneŵa anali wokonza tsitsi wotchedwa Joan. Mkaziyu anatumiza lamya ku malikulu a Mboni a kumaloko mu Freetown ndi kupempha phunziro la Baibulo.
Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Joan kutumiza lamyayo? “Sindikukumbukira m’nthaŵi ya moyo wanga pamene sindinafunefune Mulungu,” iye akutero. “Kuyambira paubwana, ndagwirizana ndi matchalitchi ambiri ndi magulu achipembedzo koma sindinapeze chikhutiritso chauzimu.
“Chifupifupi zaka khumi zapitazo, ndinadziŵa za Mboni, koma popanda chifukwa chirichonse, ndinakhala ndi lingaliro lakuti anthuwa anayenera kupeŵedwa kotheratu. Pamene bwenzi la banja linakhala Mboni, ndinalembetsa magazine a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndinatero kungofuna kumkondweretsa iye; sindinaganizire za kuwaŵerenga mpang’ono pomwe. Kwenikwenidi, ndinawagwiritsira ntchito kuyeretsa mazenera! Kenaka kunabwera Awake! imene inagwira maganizo anga. Nkhani yapachikuto inali pa kufunika kwathu kwa chikondi. [September 22, 1986] Ndinaiŵerenga ndipo ndinasangalatsidwa kwenikweni. Anali magazine amenewo amene anandisonkhezera kupempha phunziro la Baibulo.” Joan anapanga kupita patsogolo kofulumira ndipo mwamsanga anakhala Mboni ya Yehova yobatizidwa.
Munthu wina amene anafuna ndi kuchipeza chowonadi anali mwamuna wachichepere wotchedwa Manso. Iye anafuna kukhala wansembe ndipo anapita ku seminale. Koma pamene anawona chinyengo cha aziphunzitsi ake, anakhumudwitsidwa ndi kuleka. Chotsatira, Manso anayamba kupezeka ku misonkhano ya zipembedzo zina. Tsiku lina pamene anali panjira kukachezera amalume ake, anawona bukhu lofalitsidwa ndi Watch Tower Society—Is the Bible Really the Word of God? Ilo linali pansi m’madzi amatope. Popeza kuti mutu wake unasangalatsa Manso, iye anavuula bukhulo, kuliumika, ndi kuliŵerenga. Siichi nanga chowonadi chomwe ankafunafuna! Bukhulo linalimbikitsa aŵerengi kupezeka pa misonkhano ku Nyumba Yaufumu yakumaloko. Chotero Manso anapita, nayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni, ndipo mwamsanga anabatizidwa. Tsopano akutumikira monga mlaliki wachipainiya wanthaŵi zonse!
Kuvomereza ku Thandizo Loleza Mtima
Komabe, ophunzira ena atsopano, atsimikizira kukhala ngati madiamond otsekeredwa mkatikati mwa mwala. Kuyesayesa kwenikweni kwakhala kofunika “kuwafukula.” Donald, mkulu Wachikristu, akukumbukira kuleza mtima kumene kunafunikira kuthandiza mkazi wotchedwa Martha. Iye akulongosola kuti: “Ngakhale kuti anavomera kuphunzira, iye nthaŵi zonse ankatipangitsa kudikira kwanthaŵi yaitali tisanayambe kuphunzira. Nthaŵi zina iye ankayamba dala ntchito zina zimene zikanachitidwa pasadakhale. Ndiyeno ankatipempha kudikira kufikira atazimaliza. Nthaŵi zina tinadikirira koposa ola limodzi. Iye anayembekezera kuti tikakhumudwitsidwa ndi kupita, koma mlungu uliwonse tinayesera kuphunzirako zochepa zokha zokhutiritsa. Chotulukapo? M’kupita kwa nthaŵi chiyamikiro chake chinakula.
“Vuto lina linali kutengera Martha ku misonkhano. Ndinali kubweretsa Mboni zina ku phunziro lake la Baibulo kotero kuti akadzimve womasuka pamene akabwera ku Nyumba Yaufumu. Koma zidamtengera nthaŵi yaitali ndithu chakuti pamene anabwera pomalizira pake, iye anadziŵadi mpingo wonse!” Kuleza mtima kunafupidwa. Martha tsopano ngwobatizidwa ndipo ali ndi kaimidwe kabwino mumpingo.
Pius poyamba anakana chowonadi. Podzafika nthaŵi imene amishonale aŵiri okwatirana anayamba phunziro la Baibulo ndi iye, Pius anali m’ma 70, anali chiŵalo cholimba cha chipani cha ndale zadziko, ndipo anali msungi chuma wa tchalitchi chake. Amishonalewo anati: “Iye anatsutsa kwamtu wagalu nsonga iriyonse imene tinakambitsirana.” “Mlungu uliwonse iye anayamba modekha, koma mwapang’nopang’ono ankapsya mtima. Inali nkhondo yeniyeni mlungu uliwonse, ndipo kaŵirikaŵiri tinafuna kusiya mokhumudwitsidwa ndi kumleka. Chinthu chachikulu chimene chinkatibwezerabe kwa iye chinali chakuti nthaŵi zonse iye anakonzekera phunzirolo kotheratu.
“Pambuyo pa chifupifupi chaka chimodzi cha zimenezi, Pius ananena kuti anaganiza za kupanga kufufuza kwa pa yekha. Popeza kuti iye anali mphunzitsi woleka ntchito pokwanitsa zaka zake, anadziŵa kupanga kufufuza. Tsiku lirilonse kwa milungu iŵiri, anakwera phiri kupita ku laibulale ya pa yunivesiti, kumene anadziloŵetsa m’kuŵerenga ndemanga za Baibulo ndi mabuku ena olozerako. Pambuyo pake analengeza kuti: ‘Tsopano ndakhutiritsidwa kuti zonse zimene mwakhala mukundiuza nzowona. Mulungu sali Utatu, kulibe moto wa helo, ndipo moyo suli wosafa. Ngakhale anthu ena m’tchalitchi changa akuvomereza zimenezi kukhaladi tero.’ Pambuyo pa zimenezo, Pius anapanga kupita patsogolo kwamwamsanga, akuchoka ponse paŵiri m’ndale zadziko ndi tchalitchi. Pambuyo pobatizidwa, anatumikira monga mpainiya wothandizira, akumathera maola 60 mwezi uliwonse m’ntchito yolalikira, kaŵirikaŵiri monga mmene anakhozera kufikira imfa yake mu 1987.
“Chinthu chimodzi chimene sitinadziŵe kwa nthaŵi yaitali,” akukumbukira tero amishonale amene anaphunzitsa Pius, “chinali chakuti amake anayanjanapo ndi Mboni za Yehova. Iye anakumbukira kupezeka ku misonkhano limodzi nawo pamene adali wang’ono. Koma iwo atamwalira, iye anadzisankhira njira yakeyake. Pambuyo pa ubatizo wake, Pius ananena kuti: ‘Chisoni changa chokha nchakuti amayi anga sangandiwone tsopano.’ Kenaka nkhope yake inasangalala, nawonjezera kuti: ‘Koma adzandiwona m’dziko latsopano!’”
Kufikira lerolino, kufufuza madiamond ndi kufufuza ophunzira kukupitirizabe. Kusatsa kwa malonda kumanyadira kuti: “madiamond akhala kosatha.” Chikhalirechobe, mwini ngale yokongola yoteroyo samasangalala nayo kosatha chifukwa chakuti pambali pa makonzedwe a Mulungu a chipulumutso, imfa ndiyo mathedwe a anthu onse ochimwa. (Yohane 3:16, 17) Motero ntchito ya Mboni za Yehova mu Sierra Leone ikututa chuma cha mtengo wopambana kutalitali ndi madiamond wamba: atumiki a Mulungu ndi ophunzira a Yesu Kristu! Ndipo Mawu a Yehova akulonjeza kuti: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”—1 Yohane 2:17.
[Mapu/Zithunzi pamasamba 22, 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Zithunzi]
Pakati pa malo monga awa, olengeza Ufumu amapeza madiamond auzimu mu Sierra Leone