Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 3/15 tsamba 30
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Cholinga Chadyera
  • Olephera Lottery
  • Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?
    Galamukani!—1991
  • Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 3/15 tsamba 30

Chidziŵitso pa Nyuzi

Cholinga Chadyera

Mwamsanga pambuyo poyamba kulamulira mu 1933, wolamulira Wachinazi Adolf Hitler anapangana pangano ndi Tchalitchi Chachikatolika. Pangano limeneli linampatsa Hitler mphamvu yoletsa kusankhidwa kwa mabishipu a ku Germany mosinthanitsa ndi mwaŵi wina woperekedwa ku tchalitchi. Koma kodi ndi iti ya mbali ziŵirizo imene inayenera kupindula koposa? Bukhu lanazonse latsopano la ku France Lachikatolika likukpereka yankho lachindunji ku funso limeneli.

“Papa Pius XI mwiniwakeyo . . . anachilingalira kukhala chofunika koposa kutsimikizira kuchinjirizidwa kwa tchalitchi cha ku Germany mwakupanga pangano. Zimenezi zinakambitsiridwa pakati pa April ndi July 1933. Ngakhale kuti poyambapo zinayanja Tchalitchi Chachikatolika, kwenikwenidi pangano limeneli linali chipambano kwa Hitler, popeza kuti linapereka kuzindikirika kwa ulamuliro wake. Kuwonjezerapo, popeza kuti nthaŵi zambiri Hitler ankaliphwanya, papayo anapatsidwa mlandu wokhwethemula zikumbumtima Zachikatolika ndi kuchotsera abishopu mphamvu mwakupanga pangano lopusa.”

Lerolino, makamaka mu France ndi Germany, Tchalitchi Chachikatolika chimasulizidwa mwapoyera chifukwa chogonjeretsa ulamuliro wake mkati mwa ulamuliro Wachinazi. Mavuto ameneŵa amayamba pamene atsogoleri atchalitchi amalephera kulabadira mawu ndi chitsanzo cha Yesu Kristu, yemwe ananena za atsatiri ake owona kuti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Zowona, kugonjera koteroko kochitidwa ndi atsogoleri atchalitchi kwakometsera chiyanjo cha mbali ya ndale zadziko, koma kodi zimenezi zachitanji ku unansi wawo ndi Mulungu? Pamene ankalembera Akristu anzake, Yakobo, wophunzira wa Yesu anachenjeza kuti: “Ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu.”​—Yakobo 4:4.

Olephera Lottery

Mwaŵi wakupambana kwanu lottery uli mamiliyoni 14 kwa umodzi. Komabe, mamiliyoni a anthu amaseŵera mokhazikika malottery olipiriridwa ndi boma, ikusimba motero The Globe and Mail, nyuzipepala ya ku Canada. Kufufuza kukusonyeza kuti malottery alibe chisonkhezero china choposa chiyembekezo cha kupata jackpot, chimene kaŵirikaŵiri chimasonkhezeredwa ndi kusatsa kumene kumasumika “pa mphotho ndi kuipa kwa kulephera kugula tikiti.” Popeza kuti cholinga cha lottery chiri kupeza phindu ndi kutulutsa opambana oŵerengeka, olipirira amapanga misampha yatsiku ndi tsiku “m’chiyembekezo chakukhazikitsa zogula zachizoloŵezi.”

Kodi zimenezi zikuthandiza? Inde! Akumasimba m’magazine a American Health pa kuwonjezeka kwa kutchova njuga pakati pa a zaka zapakati pa 13 ndi 19, Dr. Durand Jacobs akusonya ku maLottery kukhala chiyambi chawo cha kutchova njuga “chifukwa ngwotchipa, ofikirika ndipo amachirikizidwa kukhala abwino.” Iye akuwonjezera kuti: “Lottery iri Kumata Phula kumene kumatsogolera achichepere m’mitundu ina yoipa ya mkhalidwe wa kutchove njuga.” Bukhu lina la ku Canada lonena za kutchova njuga kokakamiza likuti: “Aliyense amene angayesera kukuuzani kuti malottery sali kutchova njuga akuchita monga chitsiru kapena n’zitsiru. . . . Tikutaya mazana a mamiliyoni a madola pa malottery m’chiyembekezo chopata chinachake. Iko kuli kutchova njuga.”

Malottery amachirikiza chikondi cha pa ndalama. Dr. Marvin Steinberg, prezidenti wa Connecticut Council on Compulsive Gambling, ananena kuti a zaka zapakati pa 13 ndi 19 otchova njuga ovutitsa amagwiritsira ntchito ndalama zawo za chakudya chamasana, ndalama zobedwa, ndipo ngakhale kuba m’sitolo kuti achirikize chizoloŵezi chawo cha kutchova njuga. Owonadi ali mawu a mtumwi Paulo: “Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, . . . adzipyoza ndi zowawa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena