Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 4/1 tsamba 10
  • “Onse Okhala Mmanda Achikumbukiro”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Onse Okhala Mmanda Achikumbukiro”
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Amasamala za Inu
    Nsanja ya Olonda—1996
  • ‘Mitembo Yambiri ya Anthu Oyera Mtima Inauka’
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • “New World Translation”—Yaukatswiri ndi Yowona
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 4/1 tsamba 10

“Onse Okhala Mmanda Achikumbukiro”

KODI mungathe kutsimikizira kuti unyinji wa akufa adzakhalanso ndi moyo? Inde, popeza Yesu anati: “Musazizwe ndi ichi, chifukwa ikudza nthaŵi imene onse ali mmanda achikumbukiro adzamva mawu ake nadzatulukamo.” (Yhane 5:28, 29, NW) Tawonani mawuwo “manda achikumbukiro,” amene amapezeka kokha mu New World Translation. Amatikumbutsa za kufunika kwa chikumbukiro cha Mulungu m’chiukiriro.

Kodi nchifukwa ninji mawu ozoloŵereka akuti, “manda,” sakugwiritsiridwa ntchito? Chifukwa chakuti Yesu sanagwiritsire ntchito zochuluka za liwu Lachigriki lakuti taʹphos, limene limatanthauza “manda” kapena “msitu.” Ndithudi, sionse amene adamwalira anaikidwa m’manda enieni, kapena taʹphoi. Komabe, awo amene Mulungu adzaukitsa m’chiukiriro ali m’chikumbukiro chake. Zimenezi zasonyezedwa ndi kugwiritsira ntchito kwa Yesu mumpangidwe wa zochuluka wa mne·meiʹon, mawu amene ali ogwirizana kwambiri ndi Achigriki amene kwakukulukulu amatanthauza “kukumbukira.” (Mateyu 16:9; Marko 8:18) Greek-English Lexicon yolembedwa ndi H. G. Liddell ndi R. Scott imatembenuza mne·meiʹon kukhala “cholembapo cha chikumbutso, chokumbukirira, mbiri ya munthu kapena chinthu, . . . manda, . . . kŵirikaŵiri, chokumbutsira.”

Motero, New World Translation imasiyanitsa pakati pa mawuwo taʹphos ndi mne·meiʹon. Kulinso kokondweretsa kuwona kuti matembenuzidwe ambiri a Baibulo mofananamo amagwiritsira ntchito mawu osiyana aŵiri pa Mateyu 23:29 pamene mawu aŵiri onsewo Achigriki amapezeka. Revised Standard Version imamasulira mawuwo motere: “Mumamanga manda [mpangidwe wa taʹphos] a aneneri ndi kukometsera zikumbukiro [mpangidwe wa mne·meiʹon] za olungama.”

Mlengi wa munthu samaiwala zitsanzo za moyo wa anthu mamiliyoni zikwi zambiri amene anakhalapo ndi moyo. (Salmo 139:16; 147:4; Mateyu 10:30) M’nthaŵi yake yokwanira, iye adzakumbukira awo okhala “mmanda achikumbukiro” ndikuwabwezeretseranso ku moyo padziko lapansi loyeretsedwa. Tiri olimbikitsidwa ndi otonthozedwa chotani nanga pakudziŵa kuti chikumbukiro changwiro cha Mulungu sichingalephere!​—Chivumbulutso 20:11-13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena