Mawu a Mulungu ndi Chowonadi
“Patulani iwo m’chowonadi; mawu anu ndi chowonadi.”—YOHANE 17:17.
1. Kodi wamasalmo Wachihebri analilingalira motani Baibulo, koma kodi ambiri amalilingalira motani lerolino?
“MAWU anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuwunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Anatero wamasalmo Wachihebri. Lerolino pali ochepekera okha amene ali ndi ulemu wotero kaamba ka Mawu a Mulungu. Mzaka za zana la 20 lino, Mawu a Mulungu akupezeka mumpangidwe wolembedwa monga Baibulo Lopatulika. Ilo lamasulidwira ndi kugaŵiridwa m’zinenero zambiri kuposa bukhu lina lirilonse m’mbiri. Komabe, ambiri amakana kulivomereza monga nyali ya mapazi awo. Ngakhale awo odzinenera kukhala Akristu, kwakukulukulu, amasankha kulondola malingaliro a iwo eni mmalo mwa kulola Baibulo kuunikira njira yawo.—2 Timoteo 3:5.
2, 3. Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimaliwonera Baibulo, ndipo ndi mapindu otani amene zimenezi zaŵabweretsera?
2 Mosiyana kwambiri, ife amene tiri Mboni za Yehova timavomerezana ndi wamasalmo. Kwa ife, Baibulo ndilo chitsogozo choperekedwa ndi Mulungu. Tidziŵa kuti “lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” (2 Timoteo 3:16) Mosiyana ndi ambiri lerolino, sitimafuna kuyesezera nkhani ya makhalidwe abwino ndi kudzisungira. Tidziŵa chimene chiri cholungama chifukwa chakuti Baibulo limatiuza.
3 Zimenezi zatibweretsera mapindu okulira. Tafikira pakudziŵa Yehova, ndipo taphunzira zifuno zake zazikulu kaamba ka dziko lapansi ndi anthu, chotero tiri ndi chidaliro chakuti mtsogolo mwabwino muli mothekera kwa ife ndi mabanja athu. Timavomerezana kotheratu ndi wamasalmo amene anati: “Ha ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiliramo ine tsiku lonse. Malamulo anu andipatsa nzeru ya kuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire.”—Salmo 119:97, 98.
Kuchitira Umboni Mwamakhalidwe
4. Kodi kuzindikira Baibulo kukhala Mawu a Mulungu kumaika thayo lotani pa ife?
4 Chifukwa chake, tiri ndi chifukwa chabwino cha kuvomerezanira ndi mawu a Yesu olunjikitsidwa kwa Atate wake akuti: “Mawu anu ndi chowonadi.” (Yohane 17:17) Koma kuvomereza chowonadi chimenechi kumaika thayo pa ife. Tiyenera kuthandiza ena kuzindikira kuti Mawu a Mulungu ndiwo chowonadi. Mwanjira iyi iwonso adzakhoza kusangalala ndi madalitso amene timakumana nawo. Kodi tingawathandize motani mwanjirayo? Choyamba, tiyenera kupanga kuyesayesa kulikonse kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo m’miyoyo yathu ya tsiku ndi tsiku. Mwanjirayo, anthu owona mtima adzawona kuti njira Yabaibulo iri yabwinodi koposa.
5. Kodi ndi uphungu wotani umene Petro anapereka wonena za kuchitira umboni mwa kudzisungira kwathu?
5 Imeneyi inali mfundo yaikulu ya uphungu wa mtumwi Petro kwa akazi Achikristu amene amuna awo anali osakhulupirira. Iye anati kwa iwo: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe popanda mawu mwa mayendedwe a akazi.” (1 Petro 3:1) Linalinso lamulo lamakhalidwe abwinolo kutseri kwa uphungu wake kwa Akristu onse—amuna, akazi, ndi ana—pamene anati: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuwona ntchito zanu zabwino, tsiku la kuyang’anira.”—1 Petro 2:12; 3:16.
Nzeru Yopambana Yabaibulo
6. Kodi Petro akutithandiza motani kuwona kuti tiyenera kuthandiza ena kuzindikira Baibulo?
6 Ndiponso, Akristu angathe kuthandiza ena kuzindikira Baibulo ngati achita monga momwenso Petro analangizira kuti: “Mumpatulikitse ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Aminisitala Achikristu ayenera kukhala okhoza kutetezera Baibulo ndikulongosolera ena kuti ndilo Mawu a Mulungu. Kodi angatero motani?
7. Kodi ndi chenicheni chotani chonena za Baibulo chimasonyeza kuti liyenera kukhala Mawu a Mulungu?
7 Mfundo imodzi yokopa ikupezeka m’bukhu la Miyambo. Mmenemo timaŵerenga kuti: “Mwananga ukalandira mawu anga, ndikusunga malamulo anga; kutchera makutu ako ku nzeru . . . udzazindikira kuwopa Yehova ndikum’dziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka mkamwa mwake.” (Miyambo 2:1-6) Nzeru ya Mulungu mwini imapezeka m’masamba a Baibulo. Pamene munthu wowona mtima awona nzeru yakuya imeneyo, sangalephere kuzindikira kuti Baibulo liri loposa kukhala chabe mawu a munthu.
8, 9. Kodi ndimotani mmene uphungu wa Baibulo wonena za kusunga lingaliro lokhazikika la kupeza chuma wasonyezedwera kukhala wolondola?
8 Talingalirani zitsanzo zochepekera. Lerolino, kaŵirikaŵiri chipambano m’moyo chimapimidwa ndi ziyeneretso zachuma. Pamene munthuyo ali wopata zambiri, ndi pamenenso amalingaliridwa kukhala wachipambano kwambiri. Komabe, Baibulo, limachenjeza motsutsana ndi kuika chigogomezero chopambanitsa pa zinthu za kuthupi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitaiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:9, 10; yerekezerani ndi Mateyu 6:24.
9 Zokumana nazo zasonyeza mmene chenjezo limeneli liriri loyenerera. Katswiri wa nthenda zamaganizo wotchuka anati: “Kukhala Na. 1 ndi kukhupuka sikumakupangitsani kukhala wa chikwanekwane, wokhutira, kulemekezedwa kapena kukondedwa mowona mtima.” Inde, kaŵirikaŵiri awo amene amawonongera nyonga zawo zonse kulondola chuma amatsirizira m’kukhala achisoni ndi ogwiritsidwa mwala. Pamene kuli kwakuti Malemba, amavomereza phindu la ndalama, amasonya kanthu kena kofunika kwambiri: “Nzeru ichinjiriza monga ndalama zichinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.”—Mlaliki 7:12.
10. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulabadira uphungu wa Baibulo wa kuchenjera ndi mayanjano athu?
10 Baibulo liri ndi malangizo ambiri otere. Lina ndi iri: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma m’nzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Nayonso mfundoyi yatsimikizira kukhala yowona mwa zokumana nazo. Chitsenderezo cha atsamwali chalowetsa achichepere muuchidakwa, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala, ndi chisembwere. Aliyense amene amayanjana ndi wolankhula motukwana potsirizira pake amadzipeza kukhala wogwiritsira ntchito molakwa kulankhula konyansa kofananako. Ambiri amabera abwana awo chifukwa chakuti ‘aliyense akuchita motero.’ Zowona, monga momwe Baibulo limanenera kuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33.
11. Kodi ndimotani mmene mafufuzidwe a nthenda za maganizo anasonyezera nzeru ya kulondola Lamulo Lamakhalidwe Abwino?
11 Umodzi wa uphungu wotchuka koposa wa m’Baibulo ndiwo wotchedwa kuti Lamulo la Makhalidwe Abwino: “Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Ngati anthu akanatsatira lamulo iri, dziko likanakhala malo abwinodi kwambiri. Komabe ngakhale kuti anthu samatsatira lamulo iri, kulibwino kuti inu monga munthu mutero. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tinapangidwa kusamalira ena ndi kuwadera nkhaŵa. (Machitidwe 20:35) Mafufuzidwe anthenda zamaganizo ochitidwa mu United States ofuna kudziŵa mmene anthu anachitira pamene anathandiza ena anafikira chosankha ichi: “Pamenepa, kukuwonekera kuti kudera nkhawa ndi ena kuli kwakukulukulu mbali ya chibadwidwe cha anthu monga momwe kuliri kudzidera nkhaŵa.”—Mateyu 22:39.
Uphungu wa Baibulo—Ngwanzeru Mwapadera
12. Kodi n’chinthu chimodzi chiti chimene chimapangitsa Baibulo kukhala lapadera?
12 Ndithudi, lerolino, pali magwero ambiri auphungu kunja kwa Baibulo. Manyuzipepala amakhala ndi madanga auphungu, ndipo mmasitolo amabuku muli modzala ndi mabuku akudzithandiza. Kuwonjezera apa, pali akatswiri a nthenda za maganizo, akatswiri opereka uphungu, ndi ena amene amapereka uphungu m’nkhani zosiyanasiyana. Koma Baibulo liri lapadera m’mbali zokwanira zitatu. Yoyamba, uphungu wake nthaŵi zonse ngwopindulitsa. Suli konse nthanthi wamba, ndipo sumativulaza konse. Aliyense wotsatira uphungu wa Baibulo afunikira kuvomerezana ndi wamasalmo pamene anati kwa Mulungu m’pemphero: “Mboni zanu zivomerezeka ndithu.”—Salmo 93:5.
13. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza Baibulo kukhala lapamwamba kwambiri kuposa nzeru yochokera kwa anthu?
13 Yachiŵiri, Baibulo lapambana chiyeso cha kupita kwanthaŵi. (1 Petro 1:25; Yesaya 40:8) Uphungu wochokera kumagwero aumunthu ngwokhoza kusinthidwa momvetsa manyazi, ndipo kaŵirikaŵiri umene uli wotchuka chaka chimodzi umasulizidwa chotsatiracho. Komabe, ngakhale kuti Baibulo linamalizidwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, likali chikhalirebe ndiuphungu wanzeru koposa wonse wopezeka, ndipo mawu ake amagwiritsiridwa ntchito kulikonse. Amagwira ntchito nzotulukapo zofanana kaya tikukhala ku Afirika, ku Asia, Kummwera kapena Kumpoto kwa Amerika, ku Ulaya, kapena m’zisumbu zanyanja.
14. Kodi uphungu wa Mawu a Mulungu umaposa mwanjira iti?
14 Yotsirizira, uphungu wosiyanasiyana wa Baibulo ngwosayerekezereka. Mwambi wa Baibulo umati: “Yehova apatsa nzeru,” ndipo mosasamala kanthu za vuto kapena chosankha chimene tiyang’anizana nacho, m’Baibulo muli nzeru imene imatithandiza kuchithetsa. (Miyambo 2:6) Ana, achichepere, makolo, okalamba, olembedwa ntchito, olemba ntchito, olamulira, onse amapeza kuti nzeru ya m’Baibulo imagwira ntchito kwa iwo. (Miyambo 4:11) Ngakhale pamene tiyang’anizana ndi mikhalidwe imene inali yosadziŵika m’nthaŵi ya Yesu ndi atumwi ake, Baibulo limatipatsa uphungu umene umagwira ntchito. Mwachitsanzo, Kalelo m’zaka za zana loyamba, kusuta fodya kunali kosadziŵika ku Middle East. Lerolino, nkofalikira. Komabe, aliyense amene amalabadira uphungu wa Baibulo wakupewa “kulamulidwa [kapena kutsogozedwa] nacho chimodzi” ndi kusunga chiyero kuchokera ku “chodetsa chonse cha thupi ndi chamzimu” adzapewa chizolowezi chimenechi, chimene chiri ponse paŵiri chomwerereketsa ndi chowononga thanzi.—1 Akorinto 6:12; 2 Akorinto 7:1.
Kaamba ka Ubwino Wathu Wosatha
15. Kodi nchifukwa ninji ambiri amanena kuti Baibulo nlachikale?
15 Ndithudi, ambiri amanena kuti Baibulo nlachikale ndipo nlosayenerera m’zaka za zana la 20 lino. Komabe, mwachiwonekere chifukwa chake nchakuti Baibulo silimanena zimene amafuna kuti amve. Kutsatira uphungu Wamalemba kumatibweretsera mapindu osatha, koma kaŵirikaŵiri pamafunikira kuleza mtima, kudzilanga, ndi kudzimana—mikhalidwe imene iri yosatchuka m’dziko limene limatilimbikitsa kufunafuna chikondwerero cha nthaŵi yomweyo.—Miyambo 1:1-3.
16, 17. Kodi ndi miyezo yapamwamba m’zakugonana yotani imene Baibulo limakhazikitsa, ndipo kodi yanyalanyazidwa motani m’nthaŵi zamakono?
16 Tatengani nkhani ya chisembwere cha kugonana. Miyezo Yamalemba njankhokera kwambiri. Malo okha ololeza kugonana ndiwo muukwati, ndipo maunansi otere aliwonse kunja kwa ukwati ngoletsedwa. Timaŵerenga kuti: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna . . . sadzalowa ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Ndiponso, kwa Akristu Baibulo limawauza kukwatirana ndi munthu mmodzi, mwamuna mmodzi kaamba ka mkazi mmodzi. (1 Timoteo 3:2) Ndipo pamene kuli kwakuti pali zochitika zopambanitsa kumene chisudzulo kapena chilekaniro zingaloledwe, Baibulo limanena kuti kaŵirikaŵiri chomangira chaukwati nchamoyo wonse. Yesu mwiniyo anati: “Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzakhala thupi limodzi . . . chotero kuti salinso aŵiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi cimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:4-6, 9; 1 Akorinto 7:12-16.
17 Lerolino, miyezo imeneyi ikunyalanyazidwa kwambiri. Zizoloŵezi za kusadziletsa za kugonana zikulekeleredwa. Kugonana pakati pa achichepere oyendera limodzi kumawonedwa kukhala kosalakwa. Kukhalira pamodzi popanda kulembetsa ukwati kumavomerezedwa. Pakati pa okwatirana mwalamulo, kugonana kunja kwa ukwatiwo kochitidwa ndi aliyense wa iwo nkozolowereka. Ndipo chisudzulo chakhala mliri wa chawola m’dziko lamakono lino. Komabe, miyezo yofewa imeneyi, sinabweretse chimwemwe. Zoturukapo zoipa zatsimikizira kuti ndiiko komwe Baibulo linalondola pakuumirira gwagwagwa pamiyezo yamakhalidwe abwino.
18, 19. Kodi nchiyani chimene chatulukapo m’kunyalanyazidwa kofalikira kwa miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino?
18 Magazine a Ladies’ Home Journal anati: “Chigogomezero pakugonana chimene chinafalikira mma 60 ndi 70 chadzetsa osati chimwemwe chosatha kwa anthu koma chisoni chachikulu chaumunthu.” Panopa “chisoni chachikulu chaumunthu” chikuphatikizapo ana ovutitsidwa ndi chisudzulo chamakolo ndi akulu okanthidwa ndi kupweteka kwa maganizo. Chimaphatikizaponso kuwonjezereka kwa mabanja a kholo limodzi ndi mliri wa chawola wa asungwana achichepere mbeta amene ali ndi makanda pamene iwo eni sanatuluke konse muubwana. Ndiponso, chimaphatikizapo mliri wa chawola cha nthenda zopatsirana mwa kugonana, monga ngati mathudza akumpheto, chizonono, chindoko, kalamudiya, ndi AIDS.
19 Kaamba ka zonsezi, profesala wa sosholoji anati: “Mwinamwake tiri okula mokwanira kulingalira kuti kaya sikukatipindulitsa bwino kwambiri kuchilikiza lamulo loletsa osakwatirana limene liri loyanjidwa koposa ku zosowa za nzika zathu ndi kuyenerera kwawo kwa kupeza ufulu: ufulu kumatenda, ufulu kumimba zosafunika.” Molondola Baibulo limati: “Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukila kubodza.” (Salmo 40:4) Odalira nzeru ya Baibulo samanyengedwa ndi mabodza a onyozera Baibulo ndikunena kuti kudzisungira kosadziletsa kwambiri kumadzetsa chimwemwe. Miyezo yanzeru ya Baibulo, ngati iri yankhokera, imapindulitsa koposa.
Zothetsa Nzeru Zovuta M’moyo
20. Kodi ndi malamulo amakhalidwe abwino otani a Baibulo amene atsimikizira kukhala othandiza kwa oyang’anizana ndi umphaŵi wa ndiwe yani m’miyoyo yawo?
20 Nzeru ya Baibulo imatithandizanso kusamalira zothetsa nzeru zovuta zimene timayang’anizana nazo mmoyo. Mwachitsanzo, mmaiko ambiri, muli Akristu okhala ndi moyo muumphaŵi waukulu, ndi wadzawoneni. Komabe iwo amathana ndi umphaŵi wawo napezabe chimwemwe. Motani? Mwakutsatira Mawu ouziridwa a Mulungu. Iwo amalabadira mwamphamvu mawu otonthoza a Salmo 55:22 akuti: “Umsenzetse Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakugwiriziza.” Iwo amadalira pa Mulungu kaamba ka nyonga ya kupilira. Ndiyeno amagwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo napewa zizolowezi zovulaza, ndi zowawanya, monga kusuta fodya ndi uchidakwa. Iwo ngokangalika, monga momwe Baibulo limavomerezera, ndipo chotero iwo kaŵirikaŵiri amapeza zimene angadyetse mabanja awo pamene anthu a manja lende kapena otaya mtima amalephera. (Miyambo 6:6-11; 10:26) Ndiponso, iwo amalabadira chenjezo la Baibulo lakuti: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa.” (Salmo 37:1) Iwo samatembenukira ku kuchova juga kapena ku machitachita aupandu, monga ngati kugulitsa mankhwala ogodomalitsa. Zinthu zimenezi zingapereke “zothetsera” zofulumira za mavuto awo, koma zipatso zake za nthaŵi yaitali nzoŵaŵa.
21, 22. (a) Kodi ndimotani mmene mkazi wina Wachikristu anapezera chithandizo ndi chitonthozo m’Baibulo? (b) Kodi ndi umboni wina wotani wonena za Baibulo umatithandiza kuzindikira kuti ndilo Mawu a Mulungu?
21 Kodi kulondola Baibulo kumathandizadi awo amene ali aumphaŵi kwambiri? Inde, monga momwe zokumana nazo zambirimbiri, zimatsimikizirira. Mkristu wina wamasiye mu Asia akulemba kuti: “Ngakhale kuti ndine mphaŵi, sindimakwiya kapena kuipidwa. Chowonadi cha Baibulo chimandidzaza ndi lingaliro lotsimikizirika.” Iye akusimba kuti lonjezo lodziŵika loperekedwa ndi Yesu lakwaniritsidwa kwa iye. Yesu anati: “Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezeredwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Iye akuchitira umboni kuti mwa kuika utumiki wake kwa Mulungu poyamba m’moyo wake, iye nthaŵi zonse amalandira mwanjira zosiyanasiyana zofunika, za kuthupi za moyo. Ndipo utumiki wake Wachikristu umampatsa ulemu ndi chonulirapo mmoyo zimene zimapangitsa umphaŵi wake kukhala wopiririka.
22 Ndithudi, kuya kwa nzeru zake kumasonyeza kuti Baibulo liridi Mawu a Mulungu. Palibe bukhu lotulutsidwa ndi anthu chabe likakhoza kufola mbali zosiyanasiyana za moyo ndi kukhala laluntha kwambiri ndi kukhalabe lolondola mosaphonyetsa. Koma pali mbali ina yonena za Baibulo imene imasonyeza kukhala kwake lochokera kwa Mulungu. Liri ndi mphamvu ya kusintha anthu kukhala abwino kwambiri. Tidzakambitsirana mfundoyi m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi Mboni za Yehova nzodalitsidwa mwanjira iti mwakuvomereza kwawo Baibulo monga Mawu a Mulungu?
◻ Monga okhulupirira Mawu a Mulungu, kodi ndi thayo lotani limene tiri nalo, ndipo kodi kudzisungira kwathu kungatithandize bwanji kusungilira thayo limeneli?
◻ Kodi nchiyani chimene chimapangitsa uphungu wa nzeru wa Baibulo kukhala wapamwamba koposa uphungu wa anthu?
◻ Kodi nziti zimene ziri zitsanzo zina zosonyeza kuya kwa nzeru ya Baibulo?