Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 7/1 tsamba 14-15
  • “Nyumba Iyi Njanu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Nyumba Iyi Njanu”
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Kufutukula Mofulumira Chotere?
  • Nsembe ndi Kupereka Kowoloŵa Manja
  • Tsiku Lopereka
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 7/1 tsamba 14-15

“Nyumba Iyi Njanu”

“NYUMBA iyi njanu​—taiwonjezera.” Mawu awa analongosola mwachidule moyenerera chotani nanga malingaliro a omwe adangomaliza ntchito yamphamvu ya zaka ziŵiri pa ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ya ku Australia! Mawuwa analunjikitsidwa kwa Yehova Mulungu, ndipo anali mbali ya nyimbo yopangidwira chochitika chapadera. Chochitika chotani? Kuperekedwa kwa kufutukula kwatsopano kwa nyumba ya Beteli ndi fakitale.

Kufutukula Mofulumira Chotere?

Modabwitsa, zaka zochepera pa zisanu ndi ziŵiri kumayambiriro, kupereka kofananaku kunachitika kwa nyumba ya Beteli yomangidwa chatsopano panthaŵiyo mu Ingleburn, kum’mwera koma chakumadzulo kwa Sydney, Australia. Kodi nchifukwa ninji kufutukula kowonjezereka kunafunikira mofulumira chotere?

Chifukwa nchakuti, chiŵerengero cha Mboni mu Australia chakula kuchokera pa ochepera pa 32,000 mu 1981 kufika ku chiŵerengero chapamwamba cha 51,152 mu October wa 1989, ndipo ichi chinafulumiza kuwonjezera ogwira ntchito pa Beteli. Kuwonjezera apa, panali kuwonjezeka kochititsa nthumanzi m’chiŵerengero cha mabuku amene Australia inatumiza ku nthambi zina. Pakali pano, Australia imapanga mabuku m’zinenero 37 zosiyanasiyana kutumikira zosowa za Fiji, Indonesia, Papua New Guinea, New Caledonia, New Zealand, Solomon Islands, Tahiti, Vanuatu, Niue, Western Samoa, Tonga, Tuvalu, ndi Wallis Islands, limodzinso ndi Australia. Ndicho chifukwa chake, banja la Beteli lawonjezeka mofulumira kufikira ziŵalo 164.

Kuti apeze malo a banja lomakulali, kuchiyambiyambi kwa 1987 kufutukulidwa kwa ofesi ya nyumba zosanja zitatu kunamalizidwa, kupereka malo a ofesi ofunidwa koposa. Chotsatira, Bungwe Lolamulira linavomereza kumangidwa kwa fakitale ya nyumba zosanja zitatu yowonjezeredwa ndi kufutukulidwa kwa nyumba zogonamo zosanja zisanu. Mu January 1988 ntchito inayambika kuwonjezera fakitale yatsopano, yomwe ikapereka ukulu wa malo okwanira mamita 3,600 m’mbali zonse zinayi. Miyezi ingapo pambuyo pake, ntchito inayambika pa nyumba yogonamo, yomwe ikapereka zipinda zogonamo 51 zowonjezereka.

Nsembe ndi Kupereka Kowoloŵa Manja

Ziitano zinatumizidwa ku mipingo ya m’dziko lonselo zoitana antchito aufulu omwe akakhala mbali ya “banja lomanga” kwa zaka ziŵiri. Yankho la izi linali lochititsa chidwi, ndipo antchito aufulu oyeneretsedwa ntchito zonse anayankha kwadzawoneni. Mafomu ofunsira oposa 700 analandiridwa, ndipo m’nyengo yomangayo, chiwonkhetso cha antchito aufulu 270 anabwera ndi kudzagwira ntchito pa projekitiyo kwa nyengo zochokera pa milungu iŵiri kufika pafupifupi zaka ziŵiri.

Mboni ina inali ndi bizinesi yogwiritsira ntchito makatapila m’boma lakumpoto la Queensland. Iye anagulitsa mbali ina ya bizinesi yake, ndipo iye ndi mkazi wake anakhala mbali ya banja lomangalo kuchokera pachiyambiyambi. Iye anagula katapila yaikulu yokumba ndipo anachita ntchito yambiri yokumba pansi yofunikira popanda kulipiritsa Sosaite. Pamene kukumba kwakukulu kunamalizidwa, iye anagulitsa makinawo ndikukhalirira kugwira ntchito m’mbali zina za kumangako. Ichi nchitsanzo chimodzi chokha cha mzimu wabwino, wodzipereka kotheratu wosonyezedwa ndi onse paprojekiti yonseyo.

Mboni zinapereka kugwiritsiridwa ntchito kwa makina osanganiza konkiri yokhoza kudzaza mtunda wa mamita 3,300 m’mbali zitatu za konkiri yofunikira pa nyumba zosanja zisanu ndi zitatu m’nyumba ziŵiri. Ena anapereka ziwiya zofunikira kupanga matanki atatu osungira madzi a konkiri a malita 22,000, ndipo Mboni zogwira ntchito pa fakitalepo zinadzipereka zokha kupanga matanki osungira madziwo.

Kunena zowona, siantchito aufulu onse amene anali aluso la zopangapanga. Ndithudi, amuna achichepere ambiri anaphunzira maluso atsopano pamalopo. Ambiri anakhala omanga nyumba aluso kwambiri pamene anathandizira kuika njerwa zokwanira theka la miliyoni zofunikira kaamba ka projekitiyo. Ena anaphunzira kuika mapale m’makoma ndi pansi, ndipo pamilungu yoŵerengeka yokha, mlongo wina anakhala waluso kwenikweni m’kumamatiza mapepala a m’makoma.

Tsiku Lopereka

Tsiku lopereka, Loŵeruka, November 25, 1989, linali lowala ndipo ladzuŵa​—tsiku labwino kwambiri, la kothera kwa nyengo ya ngululu. Nyumba yosanja yachiŵiri ya fakitale yatsopano yowonjezeredwayo inali itayeretsedwa ndikuipanga nyumba yosonkhanira programu yoperekayo. Wailesi yakanema yowonetsa zinthu zochitika pamtunda waung’ono inalumikizidwa m’magawo ena a chipinda cha fakitale ndi chamabuku, holo ya Beteli, ndi chipinda chodyera cha Beteli. Ichi chinapereka malo abwino okhalamo anthu oposa 3,000.

Chifukwa chakuti malo anali ochepera, obatizidwa kwa zaka 40 okha ngomwe anaitanidwa kukapezekako, limodzi ndi alendo a ziŵalo za banja la Beteli ndi lomanga. Zakumwa zozizira zinaliko mmawa, ndipo chakudya chokoma chinaperekedwa pamasana. Pa 9:00 m’mawa, msonkhano wa chaka ndi chaka wa Watchtower Society ya ku Australia unachitidwa, ndipo ziŵalo zonse 21 za chigwirizano cha ku Australia zinapezekapo. Pamene tsatanetsatane walamulo anasamaliridwa, ena anaitanidwa kumsonkhanowo, ndipo onse anasangalatsidwa kumva nkhani ya Theodore Jaracz wa Bungwe Lolamulira.

Pa 1:45 m’madzulo, nyimbo Zaufumu zoimbidwa kwa mphindi 15 zinatsegulira programu yakuperekayo. Osonkhana anali okondwa kumva malipoti, zochitika zosangalatsa, zokumana nazo, ndi ndemanga zochokera ku ziŵalo zitatu za Bungwe Lolamulira zopezekapo. Mwa awa, Carey Barber ndi Daniel Sydlik unali ulendo wawo woyamba wonka kudzikoli. Mbale Barber analankhula pamutu wakuti “Kututa Ndiko Mapeto Ambadwo,” pamene Mbale Sydlik anasamalira mutu wakuti “Achimwemwe Ndi Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova.” Mbale Jaracz, yemwe ankatumikira nthambi ya Australia monga woyang’anira woyendera nthambi, anapereka nkhani yopereka.

Mbali yosangalatsa ya programuyo inali kuimbidwa kwa nyimbo yokhala ndi mavesi anayi nkhani yoperekayo isanaperekedwe. Nyimboyo yozikidwa pa mawu a Yesaya pa Yesaya 60:22, mutu wake unali wakuti “Wamng’ono Wakhala Chikwi.” Mmawu ake chiyamikiro chinaperekedwa kwa Yehova kuti antchito aufulu ambiri anali ndi mwaŵi wa kuwonjezera ‘kunyumba yake’ m’mbali iyi ya munda wadziko.

[Zithunzi patsamba 15]

Nyumba yowonjezeredwa yatsopano ku nyumba yosindikizira ya Watch Tower ku Ingleburn, N.S.W., Australia

C. Barber

T. Jaracz

D. Sydlik

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena