Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 8/15 tsamba 24-28
  • Kugwira Ntchito ya Mulungu M’njira ya Mulungu mu Nigeria

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwira Ntchito ya Mulungu M’njira ya Mulungu mu Nigeria
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Kufutukuka Kofulumira
  • Zikumbukiro za Kumanga
  • Kuzindikiridwa Kwalamulo
  • Tsiku Lopereka
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 8/15 tsamba 24-28

Kugwira Ntchito ya Mulungu M’njira ya Mulungu mu Nigeria

KANALI kawonekedwe kokongola. Miulu yaikulu ya mitanda yachitsulo​—pafupifupi makilogramu theka la miliyoni a iyi​—anaikidwa pa doko la Houston, Texas, yodzala ponsepo. Wolonga katundu padoko anali ndi ntchito ya kufufuza mtokoma waukuluwo woti utumizidwe. Pamene ankagwira ntchito, iye anadabwitsidwa kuwona kuti wonsewo unalembedwa kuti “Watchtower,” (Nsanja ya Olonda). Pambuyo pake iye anafikira mwamuna amene anali woyang’anira mtokomawo namufunsa kuti: “Nanga nsanja ya olondayi idzakhala yaitali motani?”

Pamenepo wolonga katundu padokoyu anazindikira kuti zitsulozo sizikapangidwa nsanja ya olonda yeniyeni. Mmalo mwake, zinkatumizidwa ku Igieduma, Nigeria, kumene zikagwiritsiridwa ntchito kumangira nyumba yanthambi yatsopano ya Watch Tower Society​—kwenikweni mzinda waung’ono pakati pa nkhalango ya Afirika.

Zaka zisanu ndi chimodzi zapitazo malo a pa Igieduma poyamba analidi nkhalango yosapitika ya mitengo ya mpira. Tsopano malowo ngosamaliridwa ndipo ngokongola; ali ndi maluŵa, madimba, ndipo ngakhale paki yokhala ndi kasenye! Komabe, cha kunsi kwake kunaikidwa nyumba yosindikizira yaikulu kuposa malo onse omwe anamangidwapo nthambi yakale mu Lagos. Mkati mwa fakitaleyo, makina osindikizira atatu amagwira ntchito, imodzi njokhoza kusindikiza magazine 17,000 pa ola limodzi. Nyumba yogonamo ingakhalidwe ndi anthu oposa 400. Nyumba yosamaliramo zautumiki ili ndi chipinda chodyeramo chachikulu ndi kitchini limodzinso ndi mosamalira okalamba ndi ofesi ya odwala mano. Pali magwero a pawokha operekera madzi ndi dongosolo lotaila zoipa. Nyumba yamagetsi yosamaliridwa ndi kompyuta imatumiza magetsi. Pali Nyumba Yaufumu, nyumba ya ofesi, ndi dipatimenti ya ozima moto. Uku inu mudzapezakonso misewu ndi magetsi a mkhwalala. Nkosadabwitsa kuti anthu amatcha nyumba ya Beteli pa Igieduma kuti ndi mzinda. Ndipo iyi inamangidwa ndi antchito aufulu okhaokha ndi kuchilikizidwa mwa ndalama ndi zopereka zosakakamiza.

Kufutukuka Kofulumira

Pamene kuli kwakuti Beteli iyi njaikulu koposa mu Nigeria, sindiyo yoyamba. Yoyambirira inakhazikitsidwa ndi Mbale William R. Brown, amene anasamukira ku Lagos mu 1930 ndi mkazi wake ndi mwana wamkazi. Zipinda zambiri zochitidwa lendi zimene anakhalamo zinatumikira monga likulu la nthambi ya Sosaite ya Kumadzulo kwa Afirika, imene panthaŵiyo inasamalira ntchito ya Ufumu mu Nigeria, Ghana, ndi Sierra Leone. Panthaŵiyo, munali ofalitsa okangalika asanu ndi aŵiri okha a mbiri yabwino mu Nigeria.

Bible Brown, monga mmene anadziŵidwira mofala, anali mlaliki wamphamvu ndi wolimba mtima wa mbiri yabwino. Pokhala wosakhutiritsidwa ndi kukhala pansi kwa nthaŵi yaitali mumpando mu ofesi, iye anachezera dzikolo mwa kugwiritsira ntchito galimoto ndi sitima, akumapereka nkhani zapoyera ndi kugaŵira mabuku ambiri.

Pamene uthenga wamphamvu wa Ufumu unazika mizu mmalingaliro ndi mitima ya anthu ovomereza, anthu ambiri anakhala alengezi achangu a Ufumu. Zaka khumi zomwe zinatsatira zinali ngati nyengo ya m’zaka za zana loyamba m’Yerusalemu pamene ‘mawu a Mulungu anakula; ndipo chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu.’ (Machitidwe 6:7) Podzafika mu 1940 chiŵerengero cha atamandi achangu a Yehova mu Nigeria chinakwera kuchokera pa 7 kunka ku 1,051!

‘Wamng’ono anasanduka chikwi,’ komatu ichi chinali chiyambi chokha. (Yesaya 60:22) Mu 1947 Sosaite inatumiza amishonale atatu ophunzitsidwa ku Gileadi kunka ku Lagos. Mmodzi wa awa, Anthony Attwood, adakali wokangalikabe m’ntchito yake. Iye akukumbukira Beteli ya panthaŵiyo motere: “Inali nyumba yokhala pamwamba pa sitolo ya nsapato. Munali zipinda zogona zitatu, chipinda chopumulira/​ofesi, ndi chipinda chodyera. Mbale ndi Mlongo Brown ndi banja lawo anatenga zipinda zogonamo ziŵiri, ndipo amishonale atatufe tinapapatizana m’chipinda chachitatu chogona. Munali malo okwanira makama atatu a munthu mmodzi ndi kachipinda koikamo zovala kopangidwira m’khoma.”

Kufunikira zipinda zowonjezereka kunatisonkhezera kusamukira ku nyumba ya zipinda zosanja zitatu mu 1948. Panthaŵiyi chiŵerengero cha ofalitsa mu Nigeria chinafikira 6,825. Zaka zisanu ndi zitatu pambuyo pake, chiŵerengerochi chinali chinawonjezeka kuwirikiza katatu, motero Beteli inasamutsidwiranso ku Shomolu, Lagos. Kumeneko, kwa nthaŵi yoyamba mu Nigeria, Sosaite inadzimangira Nyumba yake ya Beteli, nyumba ya zipinda zisanu ndi zitatu zogonamo ya pa malo a mahekitala oposa theka. Boma la kumaloko linatcha msewuwo dzina lakuti Watch Tower Street. Mdimba munamera mitengo yambiri, kuphatikizapo mitengo ya ngole limodzinso ndi citrus, breadfruit, avokado, ndi mango. Koma zoposa zaka 33 zotsatira, nyumba zinawonjezeredwa ndi kufutukulidwa. Koma podzafika pakati pa ma 1970, nyumba zinadzala pafupifupi malo onsewo. Kusamuka kunafunikiranso.

Zikumbukiro za Kumanga

Choyamba, malo a mtunda wa mahekitala 31 anapezedwa pa Otta, kumpoto kwa Lagos. Koma mavuto anapitirizabe kutsekereza kupita patsogolo. Pomalizira pake, kunawonekera kuti kusamukila kumeneko sikunali chifuniro cha Yehova. Chotsatira kufunafuna malo kunafutukudwira kumbali ya kumwera ya dzikolo, ndipo mu 1983 Sosaite inapeza malo a mahekitala 57 pa Igieduma, mu Boma la Bendel.

M’zaka zotsatira zisanu ndi chimodzi, njoka za nsato ndi mamba zinachokapo pamene abale ndi makina amphamvu anasamukirapo. Chitokoso chachikulu pantchitoyo chinali chakuti kunali kovuta, kapena pafupifupi kosatheka, kugula ziwiya zambiri ndi zinthu zomangira m’dzikomo. Thandizo lochokera kunja linafunikira. Chotero gulu la Mboni mu United States linapemphedwa kukafunafuna, kugula, ndi kutumiza zinthuzo. Terry Dean, mgwirizanitsi wa kugwira ntchito kwamphamvuku, akusimba motere: “Chimene chinapangitsa projekitiyo kupanga mbiri chinali chakuti pafupifupi chirichonse chinafunikira kutumizidwa. Abale ku Nigeria anatiuza kuti zinthu zomangira zimene anali nazo unali mchenga, simenti, ndi madzi basi!”

Kunali kwabwino kuti zomangira zazikuluzi zinalipo, popeza kuti ntchito yomangayo inatenga matani 7,500 a simenti, matani 55,000 a mchenga, ndi matani 35,000 a dothi. Mitengo yambiri inaliponso. Komabe, m’zaka zisanu zotsatira, makilogalamu mamiliyoni anayi ndi theka a zinthu zomangira zinatumizidwa kuchokera ku United States, zokwanira kudzaza mabokosi otumizira 347, omwe atandandalikidwa angafikire pamtunda wa makilomita 3.5!

Nthambi zina zinathandiziranso ndi zinthu. Mangalande anatumiza dongosolo lonse la zamagetsi, kuphatikizapo makina otulutsira magetsi asanu ndi imodzi aakulu. Sweden inathandizira crane yaitali, matrakita, matrakita okumbira, galimoto, zipangizo, ziwiya za m’kitchini, ndi dongosolo la lukanelukane lotumizira mafoni. Pamene sitolo yogulitsa zipangizo inaikidwa pa selu, abale a ku Sweden anaigula ndi kutumiza zinthu zonsezo ku Nigeria. Zinthu zokha za m’sitoloyo zimene sanatumize zinali mafosholo a chipale chofeŵa​—omwe ngopindulitsa kwenikweni mu Sweden kuposa mu Afirika!

Ndithudi, Mboni za kumaloko zinathandiziranso molingana ndi mphamvu zawo. Anthu oposa 125,000 anasonyeza kuchilikiza kwawo projekitiyo mwa kubwera ku nyumbayo pa kumangidwa kwakeko. Ambiri anathandizira ndalama. Chothandizira chimodzi cha 20 cents (U.S.) chinachokera kwa mnyamata wa zaka zisanu ndi ziŵiri. Kodi ndalamazo anazipeza kuti? Atate wake anampatsa chilazi kuti aphike ndikudya; mmalo mwake mnyamatayo anachisunga ndikuchifesa mnyengo yake. Pambuyo pake iye anatuta chilazi chakecho, nachigulitsa, ndi kuthandizira ndalamayo ku projekiti ya ku Igieduma.

Mboni zina za Yehova zinathandizira maluso awo, ngakhale kuphunzitsa ena kuzolowera maluso a kumanga. Ambiri, okwanira 500 panthaŵi imodzi, anathandizira mphamvu zawo, akumavutika padzuwa lotentha ndi mvula kuti atsirize ntchitoyo. Mwachitsanzo, lingalirani ntchito yokha yophatikizidwa pomanga mpanda wozungulira nyumbayo. M’miyezi isanu ndi iŵiri imene inatheredwa pomaliza mpanda wa pafupifupi makilomita atatuwu, abalewo anapanga ndikuumba njerwa za konkiri zokwanira 57,000! Mbale wina anaseka motere: “Chomwe chinandipangitsa ine kupitirizabe chinali kuwona miimba yambiri yomauluka mmwamba ikumandiyembekezera ine kuchitapo kanthu!” Zowonadi, mofanana ndi anthu ena zikwi zambiri omwe anathandizira kupita patsogolo kwa ku Igieduma, iye anasonkhezeredwa ndi kuchilikizidwa ndi mzimu wa Yehova.

Kuzindikiridwa Kwalamulo

Akuluakulu a boma anagwirizana kuchilikiza ntchitoyo. Ofesi ya Prezidenti inagamulapo kuti zinthu zomangira zonse zowodedwa kunja zisalipiridwe misonkho. Akuluakulu a kumaloko analeka kulipiritsa misonkho ya chitukuko ndi ya kuvomereza mapulani. Msonkho wochepa wa kumanga wokha ngomwe unafunikira. Nthaŵi ina, pamene panali mkangano wokhudza malo, Omo N’oba, kapena mfumu, ya dera lonselo analoŵereramo ndi kulamulira motere: “Ntchitoyi siiyenera kuletsedwa chifukwa chakuti iyi ndi ntchito ya Mulungu.”

Kunena kuti projekiti iyi inachilikizidwa ndi Mulungu kunazindikiridwa ndi ena osakhala Mboni za Yehova. Pamene kampani ya ku Amereka inatumiza zitsulo zomangira garaji, iwo anatumizanso mmodzi wa anthu awo, Mkatolika, kukathandiza kuimanga. M’milungu iŵiri ya kukhala kwake mu Igieduma, iye anawona ngati anali kunyumba kwake, akumathadi kutchula antchito anzake ndi dzina lakuti mbale ndi mlongo. Pamene anabwerera kumudzi, iye analembera ofesi yathu ya ku Nigeria motere: “Sindinasangalalepo ndi ntchito kwambiri chotere monga pamene ndinali kwanuko kuchita ntchito ya Mulungu m’njira ya Mulungu.”

Tsiku Lopereka

Pa January 20, 1990, nyumba yokongolayi ya Beteli inaperekedwa kwa Yehova Mulungu, amene mzimu wake unali ndi thayo la kuimaliza. Ochezera anachokera m’madera onse a Nigeria, ngakhale kuti ziitano zinalekezera kwa omwe anali obatizidwa kwa pafupifupi zaka 35 kapena omwe anathera zaka zokwanira 20 muuminisitala wa nthaŵi zonse. Alongo anavala maadresi aatali, okongola ndi mipango ya kumutu yofanana, ndipo abale ambiri anavala miinjiro ya mu Afirika yabwino kwabasi. Oitanidwa onse, 4,209 kuchokera m’maiko 29 anapezeka pa kuperekako. Pakati pa awa panali pafupifupi amishonale 80, ambiri a awa anachokera ku maiko ena a Kumadzulo kwa Afirika. M’programuyo munaphatikizidwa malipoti osimbidwa ndi nthumwi zochokera m’nthambi zisanu zodzacheza, omwe anagogomezera umodzi wa chifuno ndi kumvana komwe kulipo pakati pa anthu a Yehova. Malonje olembedwa ndi matelegramu anachokera kwa abale a m’maiko 21, kuphatikizapo uthenga wochititsa chidwi wochokera kwa “abale ndi alongo 400 a ku Moscow, Soviet Union.”

Ziŵalo ziŵiri za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova mu Brooklyn, New York, zinaliponso. Albert Schroeder anapereka nkhani yokhala ndi mutu wakuti “Chomwe Chikuyembekezeredwa Nkupezedwa Wokhulupirika,” akumagogomezera kufunika kwa kupitiriza kukhala wokhulupirika kwa anthu a Mulungu. (1 Akorinto 4:2) Nkhani yopereka inaperekedwa ndi Lyman Swingle, yemwe anafotokoza kumangidwa kwa kachisi yaulemerero ya m’tsiku la Solomo. Ngakhale kuti kachisiyo inachilikizidwa ndi kuvomerezedwa ndi Mulungu, Yehova anachimveketsa kuti chomwe chinali chofunika koposa kuposa nyumbayo chinali kukhulupirika ndi chimvero cha anthu ake odzipereka. Mwanjirayi Mbale Swingle anasonyeza kuti nyumba yokongola ya nthambi pa Igieduma siinali mapeto mwa iyo yokha koma chochititsira kupititsa patsogolo kulambira kowona.

Patsiku lotsatira, misonkhano yapadera yokhudza kuperekedwa inachitika m’mizinda itatu ya Nigeria. Anthu oposa 60,000 anapezeka pa iyi.

M’nthaŵi zakale, pamene anthu olankhula chinenero cha Edo cha ku Nigeria anabwera kudzalemekeza mfumu, panali mapwando ndi kusangalala kwambiri. Igieduma (yomwe poyambapo inali ugie dunai) inali liwu logwiritsiridwa ntchito kufotokoza mapeto achipambano a msonkhano wosangalatsawo. Kwa anthu a Yehova omwe anapezeka patsiku loperekalo kudzalemekeza Mfumu ya Chilengedwe Chonse, Yehova Mulungu, mawu ochepa akakhala okwanira. Kwa ofalitsa a Ufumu 139,150 mu Nigeria, liwu lakuti “Igieduma” imawakumbutsa malo kumene kumachokera chitsogozo ndi uphungu wateokratiki, limodzinso ndi zinthu zosindikizidwa zimene zidzawathandiza kupitiriza kuchita ntchito ya Mulungu m’njira ya Mulungu mu Nigeria.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

1. Nyumba yogonamo

2. Nyumba Yaufumu

3. Nyumba Yosamalira Utumiki

4. Ofesi

5. Fakitale

6. Garaji

7. Nyumba yoperekera magetsi

[Zithunzi patsamba 26]

Mbale ndi Mlongo Brown kutsogolo kwa ofesi yanthambi m’ma 1940

Pofikira alendo pa fakitale panthambi yatsopano

Chipinda cha pa Beteli

[Zithunzi patsamba 27]

Makina osindikiza mitundu iŵiri panthaŵi imodzi

Kulonga mabuku

Nyumba Yaufumu

Dipatimenti Yautumiki

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena