Chidziŵitso pa Nyuzi
Kuulula Liŵongo Lawo Lamwazi
“Tinaitcha nkhondoyo [Nkhondo Yadziko ya II] kukhala nkhondo yopatulika ndipo tinatumiza anthu kumabwalo ankhondo,” anavomereza motero Shingen Hosokawa, mlembi wamkulu wa Kagulu Kampatuko ka Otani ka ku Japan ka Ofesi ya Kachisi Yadziko Lachibuda Lenileni Loyera. “Sitingachitire mwina koma kugwidwa ndi manyazi pamaso pa Buddha wopatulika.” Pa “Mwambo Wokumbukira Onse Akufa pa Nkhondo” wochitidwa posachedwapa, zaka 45 pambuyo pa kutha kwa Nkhondo Yadziko ya II, kagulu kampatukoko, kokhala ndi akhulupiriri oposa mamiliyoni asanu, kanavomereza thayo lake “m’kugwirizana mofunitsitsa mu [zoyesayesa zankhondo za] Nkhondo Yadziko ya II.” “Palibe gulu lina lirilonse lamwambo Lachibuda limene linafotokoza momvekera thayo lake lenileni lankhondo pa mwambo wachipembedzo,” inafotokoza motero Asahi Shimbun.
Komabe, kodi zipembedzo zambiri kwabasi siziyenera “kugwidwa ndi manyazi” kaamba ka kusonkhezera amuna achichepere ake ambiri kupita kunkhondo? Mogwirizana ndi Kodansha Encyclopedia of Japan, pafupifupi zipembedzo zonse Zachibuda, “Chikristu,” ndi Chishinto m’Japan zinapanga Chigwirizano Chachipembedzo mu 1941 “kuti zipereke chilikizo lauzimu kwa mtunduwo m’nthaŵi yankhondo.”
Mosadabwitsa, polozera ku ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga kukhala ‘Babulo Wamkulu,’ Baibulo limati: “Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa . . . onse amene anaphedwa padziko.” (Chibvumbulutso 18:2, 24) Kodi Yehova Mulungu, Mpatsi wa moyo wa anthu, adzaŵerengera anthu achipembedzowo kaamba ka liŵongo lamwazi? Mutu umodzimodziwo wa Chibvumbulutso ukufotokoza mwafanizo zimene zidzachitika kwa Babulo Wamkulu, ukumati: ‘Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso.’—Chibvumbulutso 18:21.
Kuperewera kwa Ansembe
Magulu ampatuko Achibuda m’Japan akuvutitsidwa maganizo ndi vuto la makachisi olekedwa. Anansi okhala pafupi ndi akachisi opanda ansembe akutsutsa ku kuyendayenda kwa alova pamalo a kachisiwo limodzinso ndi ngozi ya moto. Kagulu kampatuko Kachibuda ka Zen Myoshinji kanasankha kulaka vutolo kaya mwakuchotsa akachisiwo kapena kuwaphatikiza ndi amene ali pafupi. Akachisi oposa 20 peresenti pa akachisi 3,500 a kagulu kampatuko ka Myoshinji m’Japan monse amakhala mwina alibe wansembe wokhala pamalopo kapena kungotumikiridwa ndi ansembe ochokera ku akachisi apafupipo.
Kodi nchifukwa ninji pali vutoli? “Kagulu kampatukoko kakupeza vuto la kupeza olowa m’malo ansembe oleka ntchito,” ikufotokoza motero The Daily Yomiuri, “ndipo ansembe achichepere akukana kutumizidwa ku akachisi amene ali kumalo kumene kulibe anthu ambiri.” Kagulu kampatukoko kayesera kuphunzitsa anthu oleka ntchito zina kukhala ansembe koma aleka kale kakonzedweko. Ngakhale kuti Myoshinji ikunena kuti “iyi sinyengo imene chiŵerengero cha akachisi amene alipo chiri umboni wa mphamvu,” nchosakanika kuti chisonkhezero chawo chikutha mphamvu.
Mosangalatsa, bukhu Labaibulo la Chibvumbulutso likuneneratu kuti madzi a Firate, pomwe dongosolo ladziko lonse lachipembedzo—‘Babulo Wamkulu’—wakhala, ‘adzaphwa.’ (Chibvumbulutso 16:12; 18:2, 9, 11) Kodi madziwo akuimiranji? “Madziwo udawaona . . . ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.” (Chibvumbulutso 17:15) Kuphwa kwa “madziwo,” kapena achilikizi, mowonekera kukuchitika m’ufumu wa Kum’mawa wa Babulo Wamkulu.
Yankho Langwiro
“Ziwopsyezo zomakantha zimene tikuyang’anizana nazo tsopano . . . ziri ndi mphamvu kwenikweni kwakuti pokhapo ngati kachitidwe kozibweza kayambika tsopano, mosapeŵeka izo zidzatsogolera ku zotulukapo zosakaza chuma ndi kugwa kwa magulu amayanjano ndi andale,” ikufotokoza motero Worldwatch Institute, yozikidwa mu Washington, D.C., U.S.A. Lipoti lapachaka la chaka chatha la gululi linachenjeza kuti mphepo yakupha yotentha, chilala, ndi zigumula zinali kokha zowoneratu za masoka owopsya omwe adzagwera dziko lapansi lowonongedwa kaleli. Madera osonyezedwa m’lipotilo kaamba ka chisamaliro chamwamsanga anaphatikizapo kuchepetsa chiŵerengero cha anthu, kuchuluka kwa mphamvu, kudzalanso nkhalango, ndi kuchinjiliza njala. Komabe, gululo likuti ‘kakonzedwe ka kuchitapo kanthu mwamsanga ka dziko lonse’ ndi ‘masinthidwe aakulu m’dongosolo la khalidwe la anthu’ zikufunikira kuti tipeze zotulukapo zabwino.
Kodi tingayembekezere kuwona kakonzedwe ka dziko lonse kamene kadzabweretsa masinthidwe aakulu m’nthaŵi yathu? Inde, koma osati kupyolera m’zoyesayesa za munthu aliyense kapena gulu la anthu. Nchifukwa ninji ayi? Chifukwa chakuti mneneri Yeremiya analemba motere zaka mazana ambiri apitawo: ‘Njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’ M’malo mwake, Baibulo limalonjeza kuti Yehova Mulungu ‘adzaononga iwo akuononga dziko’ ndipo “adzalungamitsa zinthu” kuti zipindulitse nzika za dziko lapansi.—Yeremiya 10:23; Chibvumbulutso 11:18; Mika 4:3, 4, NW.