Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/15 tsamba 15-20
  • Chikondi Chenicheni Chimafupa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi Chenicheni Chimafupa
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo Chathu Chabwino Koposa
  • Chitsanzo Chabwino cha Yesu
  • Chitsanzo cha Paulo
  • Chikondi Chenicheni Chimafupa m’Masiku Athu
  • Chikondi Chenicheni ndi Uminisitala Wathu
  • Chofupa m’Njira Zina
  • Kulani M’chikondi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • ‘Chachikulu cha Izi Ndicho Chikondi’
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Pitirizani Kusonyeza Chikondi”
    Yandikirani Yehova
  • Kondani Mulungu Amene Amakukondani
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/15 tsamba 15-20

Chikondi Chenicheni Chimafupa

‘Pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.’​—AHEBRI 6:10.

1, 2. Kodi nchifukwa ninji chikondi chenicheni chiri chofupa kwa ife mwaumwini?

CHIKONDI chopanda dyera ndicho chachikulu koposa, chopambana, mkhalidwe wamtengo wapatali kwenikweni umene tingausonyeze. Chikondichi (m’Chigiriki, a·gaʹpe) nthaŵi zonse chimafuna kuti ife tichite zambiri. Koma chifukwa chakuti tinalengedwa ndi Mulungu wa chiweruzo chachilungamo ndi chikondi, timapeza kuti chikondi chopanda dyera chimafupadi. Kodi nchifukwa ninji izi ziri tero?

2 Chifukwa chimodzi chonenera kuti chikondi chenicheni chimafupa chimaphatikizapo lamulo lonena za kuvomereza kwathupi zochitika m’maganizo, chiyambukiro cha maganizo ndi malingaliro pamatupi athu. Katswiri wina wanena motere pa kupsinjika: “‘Kukonda mnansi wako’ ndiko magwero operekedwa a zamankhwala a chitetezo kwenikweni.” Inde, ‘wachifundo achitira moyo wake zokoma.’ (Miyambo 11:17) Mawu otsatirawa ali ndi tanthauzo lofanana: ‘Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.’​—Miyambo 11:25; yerekezerani ndi Luka 6:38.

3. Kodi Mulungu amachita motani kuchipangitsa chikondi chenicheni kukhala chofupa?

3 Chikondi chimafupanso chifukwa chakuti Mulungu amafupa mopanda dyera. Timaŵerenga kuti: ‘Wochitira waumphaŵi chifundo abwereka Yehova; [Mulungu] adzambwezera chokoma chakecho.’ (Miyambo 19:17) Mboni za Yehova zimachita mogwirizana ndi mawuwa pamene zilengeza mbiri yabwino Yaufumu wa Mulungu. Iwo amadziŵa kuti ‘Mulungu sali wosalungama kuti aiwale ntchito zawo ndi chikondi chimene anachisonyeza ku dzina lake.’​—Ahebri 6:10.

Chitsanzo Chathu Chabwino Koposa

4. Kodi ndani amene amapereka chitsanzo chabwino koposa chakuti chikondi chenicheni chimafupa, ndipo kodi iye wachita bwanji motero?

4 Kodi ndani yemwe amasonyeza chitsanzo chabwino koposa chakuti chikondi chenicheni chimafupa? Eya, icho chikusonyezedwa osati ndi munthu wina aliyense kuposa Mulungu mwiniyo! Iye ‘anakonda dziko lapansi [la anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha.’ (Yohane 3:16) Kupereka Mwana wake kotero kuti ovomereza nsembe ya dipo akhale ndi moyo wosatha kunamuwonongeradi zambiri Yehova, ndipo ichi chimasonyezadi kuti iye ali ndi zonse ziŵiri chikondi ndi chifundo. Ichi chasonyezedwanso ndi chenicheni chakuti ‘m’mazunzo onse a Israyeli m’Igupto, iye anazunzidwa.’ (Yesaya 63:9) Ayenera kukhala anazunzidwa kwakukulu chotani nanga Yehova kuwona Mwana wake pamtengo wozunzirapo ndikumumva akulira kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”​—Mateyu 27:46.

5. Kodi chachitika nchiyani chifukwa chakuti Mulungu anakonda anthu kwambiri kwakuti anapereka Mwana wake monga nsembe?

5 Kodi Yehova anakupeza kusonyeza kwake kwa chikondi chenicheniku kukhala kofupa? Iye anaterodi. Mwapadera, linali yankho lamphamvu chotani nanga limene Mulungu anali wokhoza kuyankha Mdyerekezi chifukwa chakuti Yesu anatsimikizira kukhala wokhulupirika mosasamala kanthu za chirichonse chimene Satana anali wokhoza kuchita kwa iye! (Miyambo 27:11) Kwenikweni, zomwe Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa kuchotsera dzina la Yehova chitonzo, kukhazikitsa Paradaiso padziko lapansili, ndikupatsa anthu mamiliyoni ambiri moyo wosatha zidzachitika chifukwa chakuti Mulungu anakonda anthu kwambiri kwakuti anapereka munthu wapamtima pake kukhala nsembe.

Chitsanzo Chabwino cha Yesu

6. Kodi chikondi chinamsonkhezera Yesu kuchitanji?

6 Chitsanzo china chabwino chotsimikizira kuti chikondi chenicheni chimafupa ncha Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. Iye amawakonda Atate wake wakumwamba, ndipo chikondi chimenecho chasonkhezera Yesu kuchita chifuniro cha Yehova m’mavuto aliwonse. (Yohane 14:31; Afilipi 2:5-8) Yesu anapitirizabe kusonyeza chikondi chake kwa Mulungu chinkana kuti kuchita teroko nthaŵi zina kunafunikiritsa kuti iye afikire Atate wake “ndi kulira kwakukulu ndi misozi.”​—Ahebri 5:7.

7. Kodi ndim’njira yotani mmene Yesu wapezera chikondi chenicheni kukhala chofupa?

7 Kodi Yesu anafupidwa ndi chikondi chodzipereka nsembe choterocho? Iye anaterodi! Tangoganizirani za chisangalalo chimene anapeza kuchokera m’zinthu zabwino zonse zimene anazichita m’nthaŵi yauminisitala wake wa zaka zitatu ndi theka. Iye anawathandiza chotani nanga anthu mwauzimu ndi kuthupi! Kuposa zonse, mwakusonyeza kuti munthu wangwiro angasungebe mwangwiro umphumphu kwa Mulungu mosasamala kanthu za zirizonse zimene Satana akabweretsa motsutsana naye, Yesu anakhutiritsidwa ndikutsimikizira kwake Mdyerekezi kukhala wabodza. Kuwonjezera apa, monga mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, Yesu analandira mfupo yaikulu ya moyo wosafa pamene anaukitsidwira kumoyo wa kumwamba. (Aroma 6:9; Afilipi 2:9-11; 1 Timoteo 6:15, 16; Ahebri 1:3, 4) Ndipo pali mwaŵi wabwino chotani nanga umene ukumuyembekezera pa Armagedo ndi m’kulamulira kwake kwa Zaka Chikwi, pamene Paradaiso adzabwezeretsedwa kudziko lapansi ndi pamene anthu mamiliyoni zikwi zambiri adzaukitsidwa kwa akufa! (Luka 23:43) Palibe kukaikira kuti Yesu watsimikizira kuti chikondi chenicheni chimafupa.

Chitsanzo cha Paulo

8. Kodi nchiti chinali chokumana nacho cha Paulo chifukwa cha chikondi chake chenicheni kaamba ka Mulungu ndi kaamba ka anthu anzake?

8 Mtumwi Petro anamfunsapo Yesu kuti: ‘Onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?’ Mwapang’ono, Yesu anayankha kuti: ‘Onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.’ (Mateyu 19:27-29) Tiri nachonso chitsanzo chabwino kwambiri cha ichi mwa mtumwi Paulo, amene anasangalala ndi madalitso ambiri, monga mmene zalembedwera makamaka ndi Luka m’bukhu la Machitidwe. Chikondi chenicheni cha Mulungu ndi munthu mnzake chinachititsa Paulo kuleka ntchito yake monga m’Farisi wolemekezedwa. Taganiziraninso zimene Paulo anapirira nazo mwakumenyedwa, zochitika zapafupi imfa, ngozi, ndi kubindikiritsidwa​—zonsezo chifukwa cha chikondi chenicheni cha Mulungu ndi utumiki Wake wopatulika.​—2 Akorinto 11:23-27.

9. Kodi Paulo anafupidwa motani kaamba ka kusonyeza chikondi chenicheni?

9 Kodi Yehova anamfupa Paulo kaamba ka kukhala kwake chitsanzo chabwino choterocho m’kusonyeza chikondi chenicheni? Eya, tangolingalirani mmene uminisitala wa Paulo unaliri wobala zipatso. Iye anali wokhoza kukhazikitsa mipingo yambirimbiri Yachikristu. Ndipo ha, ndi zozizwitsa zotani nanga zimene Mulungu anampatsa mphamvu kuti azichite! (Machitidwe 19:11, 12) Paulo analinso ndi mwaŵi wa kulandira masomphenya osakhala aumunthu ndikulemba makalata 14 omwe tsopano ndiwo mbali ya Malemba Achikristu Achigiriki. Kuti afupidwe nazo zonsezi, mphotho ya moyo wosafa kumwamba inapatsidwa kwa iye. (1 Akorinto 15:53, 54; 2 Akorinto 12:1-7; 2 Timoteo 4:7, 8) Paulo anapezadi kuti Mulungu amafupa chikondi chenicheni.

Chikondi Chenicheni Chimafupa m’Masiku Athu

10. Kodi kukhala wophunzira wa Yesu ndi kusonyeza chikondi chathu kaamba ka Yehova kungatitaikiritse chiyani?

10 Mofananamo Mboni za Yehova lerolino zapeza kuti chikondi chenicheni chimafupa. Kusonyeza chikondi chathu kaamba ka Yehova mwa kukhala ndi kaimidwe kathu kumbali yake ndikukhala ophunzira a Yesu kungatiwonongeredi miyoyo yathu monga osunga umphumphu. (Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 2:10.) Ndicho chifukwa chake Yesu anati tiyenera kupenda zotaika. Koma sitimachita zimenezo kuti titsimikizire kaya ngati kukhala wophunzira kumafupa kapena ayi. Mmalomwake, timatero m’malo mwakuti tidzikonzekere tokha kulipira mtengo uliwonse umene kukhala wophunzira kudzafuna.​—Luka 14:28.

11. Kodi nchifukwa ninji anthu ena amalephera kudzipereka okha kwa Mulungu?

11 Lerolino, anthu ambiri​—mosakaikira mamiliyoni ambiri​—amakhulupirira uthenga umene Mboni za Yehova zimaŵabweretsera kuchokera m’Mawu a Mulungu. Koma amazengereza osadzipereka okha kwa Mulungu ndikubatizidwa. Kodi ichi chingakhale chifukwa chakuti akusoŵeka chikondi chenicheni cha Mulungu chimene ena ali nacho? Anthu ambiri amalephera kutenga masitepe a kudzipereka ndi ubatizo chifukwa chakuti amafuna kukhala okondedwabe ndi mnzawo wa muukwati wosakhulupirira. Ena samayandikira kwa Mulungu chifukwa chakuti ali ndi mkhalidwe wamaganizo wa mwamuna wamalonda amene anauza Mboni ina kuti: “Ndimakonda tchimo.” Ndithudi, anthu oterowo samayamikira zinthu zonse zimene Mulungu ndi Kristu awachitira.

12. Kodi magazini ano anenanji chimene chimagogomezera mfupo za chidziŵitso chimene chimatikokera chifupi ndi Mulungu m’chikondi chenicheni?

12 Ngati tiri nacho chiyamikiro chenicheni kaamba ka zonse zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu atichitira, tidzachisonyeza ichi mwa kukhala ofunitsitsa kulipira mtengo uliwonse umene kuteroko kumafuna kuti titumikire Atate wathu wakumwamba ndikukhala m’modzi wa ophunzira a Yesu. Chifukwa cha chikondi chenicheni cha Mulungu, amuna ndi akazi a mikhalidwe yonse ya moyo​—amuna achipambano m’zamalonda, ngwazi zotchuka m’zamaseŵera, ndi ena otero​—asinthanitsa ntchito zodzifunirazo ndi uminisitala Wachikristu, monga mmene anachitira mtumwi Paulo. Ndipo mfupo za kudziŵa ndi kutumikira Mulungu sakadziloŵetsa mmalo ndi chinthu chirichonse. Pamfundoyi, The Watch Tower nthaŵi ina inati: “Nthaŵi zina tinafusa kuti, Kodi ndi abale angati amene angafune kugulitsa Chowonadi chimene ali nacho ndi madola chikwi chimodzi? Sipananyamulidwe dzanja ndilimodzi lomwe! Kodi ndani amene angavomere ndi madola zikwi khumi? Panalibenso! Kodi ndani amene angavomere madola miliyoni imodzi? Kodi ndani angavomere kupatsidwa dziko lonse kusinthanitsa ndi zimene amadziŵa ponena za munthu Waumulungu ndi Makonzedwe Aumulungu? Panalibe ndi m’modzi yense! Kenaka tinati, Mabwenzi okondedwanu, sindinu khamu la anthu osakhutiritsidwa. Ngati mukulingalira kuti ndinu olemera kwambiri kwakuti simungasinthanitse chidziŵitso chanu cha Mulungu ndi chinthu chirichonse, ndiko kuti mukulingalira kuti ndinu olemera monga mmene tikulingalirira ife.” (December 15, 1914, tsamba 377) Inde, chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi zifuno zake zimatikokera chifupi kwa iye m’chikondi chenicheni chimene chimafupadi.

13. Kodi phunziro laumwini tiyenera kuliwona motani?

13 Ngati timamukonda Mulungu, tidzakalamira kudziŵa ndi kuchita chifuniro chake. (1 Yohane 5:3) Tidzailingalira mosamalitsa phunziro laumwini, pemphero, ndi kupezeka pamisonkhano Yachikristu. Zonsezi zimafunikira kudzipereka nsembe, popeza kuti ntchitozi zimafunikira kuwononga nthaŵi, nyonga, ndi chuma china. Tingafunikire kusankha pakati pa kupenyerera programu ya pawailesi yakanema ndi kudziloŵetsa m’phunziro laumwini Labaibulo. Komatu timakhala amphamvu chotani nanga mwauzimu, timakhala mboni zokhoza chotani nanga kwa ena, ndipo timapatamo zochuluka chotani nanga m’misonkhano Yachikristu titatenga phunziro loterolo mosamalitsa ndikuikhazikitsira nthaŵi yokwanira!​—Salmo 1:1-3.

14. Kodi pemphero ndi unansi wabwino ndi Yehova Mulungu nzofunika motani?

14 Kodi timasangalala kulankhula mokhazikika kwa Atate wathu wakumwamba mwa ‘kulimbikira m’pemphero’? (Aroma 12:12) Kapena kodi kaŵirikaŵiri timakhala otanganitsidwa kwambiri kuchita nawo zolungama mwaŵi wa mtengo wapataliwu? ‘Kupemphera mosaleka’ ndiko njira yofunika ya kulimbitsira unansi wathu ndi Yehova Mulungu. (1 Atesalonika 5:17) Ndipo palibe chirichonse kuposa unansi wathu ndi Yehova chimene chingatithandize titayang’anizana ndi ziyeso. Kodi chinatheketsa Yosefe kutsutsa mkazi wa Potifa nchiyani? Ndipo kodi nchifukwa ninji Daniele sanaleke kupemphera pamene chilamulo cha Amedi ndi Aperisiya chinamletsa kupemphera kwa Yehova? (Genesis 39:7-16; Danieli 6:4-11) Eya, unali unansi wabwino ndi Mulungu umene unathandiza amuna amenewo kulakika, mongadi mmene udzatithandiziranso ife kutero!

15. Kodi misonkhano Yachikristu tiyenera kuilingalira motani, ndipo nchifukwa ninji?

15 Kenaka, kodi timapezekapo mosamalitsa chotani pamisonkhano yathu isanu ya mlungu ndi mlungu? Kodi timalola kutopa, kudwala pang’ono kwathupi, kapena kusacha bwino kwa kunja kusokoneza thayo lathu la kusaleka kusonkhana pamodzi ndi akhulupiriri anzathu? (Ahebri 10:24, 25) Makanika wina wa ku Amereka wolandira malipiro abwino anawona kuti ntchito yake inadodometsa mobwerezabwereza kupezeka kwake pamisonkhano Yachikristu. Chotero iye anasintha ntchito yake, akumataikiridwa chuma chambiri kotero kuti akhale wokhoza kupezeka pamisonkhano yonse yampingo mokhazikika. Misonkhano yathu imatitheketsa kusangalala ndi kupatsana chilimbikitso ndi kulimbitsana chikhulupiriro. (Aroma 1:11, 12) M’nkhani zonsezi, kodi sitimapeza kuti “iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta”? (2 Akorinto 9:6) Inde, kusonyeza chikondi chenicheni m’njira zoterozo kumafupa kwenikweni.

Chikondi Chenicheni ndi Uminisitala Wathu

16. Kodi chingatulukepo nchiyani pamene chikondi chitisonkhezera kuchitira umboni mwamwaŵi?

16 Chikondi chimatisonkhezera kulalikira mbiri yabwino monga anthu a Yehova. Mwachitsanzo, icho chimatifulumiza kudziloŵetsa m’kuchitira umboni wamwamwaŵi. Tinganyalanyaze kuchitira umboni mwamwaŵi, koma chikondi chidzatisonkhezera kulankhula. Ndithudi, chikondi chidzatichititsa kuganizira za njira zochenjera zoyambira kukambitsirana ndipo kenaka kuzilunjikitsira ku Ufumu. Kuti tifotokoze mwafanizo: M’ndege, mkulu Wachikristu nthaŵi ina anakhala pafupi ndi wansembe wa Roma Katolika. Choyamba, mkuluyo anamufunsa wansembeyo funso labwino. Komabe, podzafika nthaŵi imene wansembeyo anatuluka m’ndegemo, chikondwerero chake chinamsonkhezera kutenga mabuku athu aŵiri. Chinali chotulukapo chabwino chotani nanga cha kuchitira umboni wamwamwaŵi!

17, 18. Kodi chikondi chidzatisonkhezera kuchitanji kulinga ku uminisitala Wachikristu?

17 Chikondi chenicheni chimatisonkhezera kukhalamo ndi phande mokhazikika m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba ndi ntchito zina za uminisitala Wachikristu. Kuchuluka kumene tidzakhala tikukambirana Baibulo, tidzalemekeza nako Yehova Mulungu ndipo tidzathandiza onga nkhosa kukhala panjira yonkera ku moyo wosatha. (Yerekezerani ndi Mateyu 7:13, 14.) Ngakhale ngati tiri osakhoza kukambitsirana Baibulo, zoyesayesa zathu sizidzakhala zachabe. Kupezekapo kwathu kwenikweniko panyumba za anthu kumatumikira monga umboni, ndipo ife enife timapindula nawo uminisitalawo, popeza kuti sitingalengeze zowonadi za Baibulo popanda kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Zowonadi, pamafunikira kudzichepetsa kuti munthu apite kunyumba ndi nyumba, ‘kuchita zonse chifukwa cha uthenga wabwino kuti akakhale woyanjana ndi ena.’ (1 Akorinto 9:19-23) Koma chifukwa cha chikondi kaamba ka Mulungu ndi anthu anzathu, timapanga kuyesayesa ndipo timafupidwa ndi madalitso olemerera.​—Miyambo 10:22.

18 Pamafunikiranso chikondi chenicheni kuti atumiki a Yehova akhale otsimikiza za kupanga maulendo obwereza kwa anthu okondwerera m’chowonadi cha Baibulo. Kutsogoza maphunziro Abaibulo mlungu ndi mlungu ndi mwezi ndi mwezi ndicho chisonyezero cha chikondi cha Mulungu ndi anansi, popeza kuti ntchitoyi imafuna kuti tiwononge nthaŵi, kuyesayesa, ndi chuma chakuthupi. (Marko 12:28-31) Komabe, pamene tiwona m’modzi wa ophunzira Baibulowa akubatizidwa ndipo mwinamwake kulowa muuminisitala wa nthaŵi zonse, kodi sitimakhutiritsidwa kuti chikondi chenicheni chimafupa?​—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 3:1-3.

19. Kodi pali unansi wotani pakati pa chikondi ndi utumiki wa nthaŵi zonse?

19 Chikondi chopanda dyera chimatisonkhezera kuti tipereke nsembe chuma chakuthupi kaamba ka utumiki wa nthaŵi zonse ngati nkotheka kwa ife kugawanamo m’ntchito yoteroyo. Zikwizikwi za Mboni zingachitire umboni kuti kusonyeza chikondi chawo kuutali umenewo kwakhala kofupa kwenikweni. Ngati mkhalidwe ukulolani kugawana muuminisitala wa nthaŵi zonse komano simumaugwira mwaŵiwo, inu simukudziŵadi madalitso amene mukuphonya.​—Yerekezerani ndi Marko 10:29, 30.

Chofupa m’Njira Zina

20. Kodi chikondi chimatithandiza motani kukhala okhululukira?

20 Njira ina imene chikondi chenicheni chimafupira njakuti chimatithandiza kukhala wokhululukira. Inde, chikondi ‘sichilingirira zoipa.’ Kwenikweni, ‘chikondi chikwirira zonse.’ (1 Akorinto 13:5; 1 Petro 4:8) Kunena kuti “zonse” kumatanthauza kuti machimowo ngambiri, kodi sitero? Ndipo kumafupa chotani nanga kukhala wokhululukira! Mutakhululukira, ichi chimapangitsa munthuwe ndi amene anakuchimwirani kumva bwino. Koma chofunika kwenikweni ndicho mfundo yakuti pokhapo ngati tinakhululukira kale otichimwira, sitingamuyembekezere Yehova kutikhululukira.​—Mateyu 6:12; 18:23-35.

21. Kodi chikondi chenicheni chidzatithandiza motani kukhala ogonjera?

21 Kuwonjezera apa, chikondi chenicheni chimafupa chifukwa chakuti chimatithandiza kukhala ogonjera. Ngati timamukonda Yehova, tidzadzichepetsa pansi pa dzanja lake lamphamvu. (1 Petro 5:6) Kumukonda kwathu kudzatifulumizanso kugonjera chiwiya chake chosankhika, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Ichi chimaphatikizapo kukhala wogonjera kwa otsogolera mumpingo. Kuchita ichi kumadzetsa mfupo chifukwa kulephera kwathu kuchita tero ‘sikukatipindulitsa.’ (Mateyu 24:45-47; Ahebri 13:17) Ndithudi, lamulo lamakhalidwe abwinoli la kukhala ogonjera limagwiranso ntchito mkati mwa banja. Njira yotereyi njodzetsa mfupo chifukwa chakuti imapititsa patsogolo chisangalalo, mtendere, ndi chigwirizano cha m’banja ndikutipatsanso chikhutiritso chimene chimachokera m’kudziŵa kwathu kuti tikukondweretsa Mulungu.​—Aefeso 5:22; 6:1-3.

22. Kodi tingakhaledi achimwemwe motani?

22 Chotero, mwachiwonekere, mkhalidwe waukulu umene tingapititse patsogolo ndiwo a·gaʹpe, chikondi cha mtundu wopanda dyera wozikidwa palamulo lamakhalidwe abwino. Ndipo palibe kukaikira kuti chikondi chenicheni chimafupa. Chotero, tidzakhala achimwemwedi ngati tipititsa patsogolo ndi kusonyeza mkhalidwewu pamlingo waukuludi kuulemerero wa Mulungu wathu wachikondi, Yehova.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi Yehova Mulungu wachisonyeza chikondi chenicheni m’njira zotani?

◻ Kodi chikondi chasonyezedwa motani ndi Yesu Kristu?

◻ Kodi mtumwi Paulo anakhazikitsa chitsanzo chotani m’kusonyeza chikondi chenicheni?

◻ Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zasonyezera chikondi?

◻ Kodi nchifukwa ninji munganene kuti chikondi chenicheni chimafupa?

[Chithunzi patsamba 16]

Chikondi cha Yehova kaamba ka anthu chinamsonkhezera kupereka Mwana wake kotero kuti tipeze moyo wosatha. Kodi mumachiyamikira chikondi chenicheni chimenecho?

[Chithunzi patsamba 18]

Chikondi chenicheni kaamba ka Yehova chidzatisonkhezera ‘kulimbikira m’pemphero’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena