Perekani Chisamaliro ku Mawu Aulosi a Mulungu!
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Petro Wachiŵiri
MAWU aulosi a Yehova, kapena uthenga, ali ngati nyali younikira m’malo amdima, ndipo Akristu owona ayenera kuwapatsa chisamaliro chachikulu. Kumeneko sikopepuka pamene aphunzitsi onyenga ayesayesa kupititsa patsogolo mpatuko. Koma kungachitidwe ndi thandizo laumulungu. Ndipo tiyenera kumamatira ku mawu a Mulungu mosagwedezeka ngati titi tidzapulumuke tsiku la Yehova lomayandikira mofulumira.
Kalata yachiŵiri youziridwa ya mtumwi Petro ingatithandize kupereka chisamaliro ku mawu aulosi a Mulungu. Petro analemba kalatayi mwinamwake ali ku Babulo pafupifupi 64 C.E. M’kalata yake iye akuchirikiza chowonadi cha Mulungu, nachenjeza okhulupirira anzake za kudza konga mbala kwa tsiku la Yehova, ndipo akuthandiza oŵerenga ake kusasochezedwa ndi mphulupulu za anthu onyalanyaza lamulo. Popeza kuti tsiku la Yehova langotsala nenene kutigwera, tingapindule mokulira kuchokera m’mawu ouziridwa a Petro.
Khulupirirani Mawu Aulosi
Monga Akristu, tifunikira kuchita mwamphamvu kusonyeza mikhalidwe yaumulungu ndipo tiyenera kupereka chisamaliro ku mawu aulosi. (1:1-21) Kuti tipeŵe kukhala ofooka kapena osabala zipatso, tifunikira ‘kuwonjezera kuchikhulupiriro chathu ukoma, chidziŵitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, chikondi cha pa abale, ndi chikondi.’ (NW) Pamene Petro anawona Yesu atasandulika ndi kumva Mulungu akulankhula za Kristu pachochitika chimenecho, mawu aulosi anatsimikiziridwa mowonjezereka. (Marko 9:1-8) Timafunika kupereka chisamaliro ku mawu ouziridwa mwaumulunguwo.
Chenjerani ndi Ampatuko
Mwakupereka chisamaliro chachikulu ku mawu aulosi a Mulungu, tingachenjere ndi ampatuko ndi anthu ena oipa. (2:1-22) Petro anachenjeza kuti aphunzitsi onyenga akaloŵerera mpingo. Komabe, Yehova akapereka chiweruzo champhamvu motsutsana ndi ampatukoŵa, mongadi momwe anaweruzira angelo osamvera, dziko losapembedza la m’tsiku la Nowa, ndi mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Aphunzitsi onyenga amanyoza ulamuliro wopatsidwa ndi Mulungu ndi kunyengerera ofooka kuti agwirizane nawo m’kuchita zoipa. Kukadakhala bwino kwa ampatuko oterowo kusazindikira ‘njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.’
Tsiku la Yehova Likubwera!
Monga opereka chisamaliro ku mawu aulosi m’masiku ano otsiriza, sitiyenera kudzilola enife kusonkhezeredwa ndi oseka omwe amanyodola uthenga wonena za kukhalapo kwa Yesu. (3:1-18) Iwo amaiŵala kuti Mulungu yemwe walinganiza kuwononga dongosolo la zinthu liripoli anawononga dziko lokhalako Chigumula chisanadze. Kuleza mtima kwa Yehova sikuyenera kuwonedwa ngati kuchedwa, popeza kuti iye akufuna kuti anthu onse alape. Dongosolo ili lidzawonongedwa ‘m’tsiku la Yehova’ ndipo lidzaloŵedwa mmalo ndi ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene mudzakhalitsa chilungamo.’ Chotero, tiyenera kuyesayesa mwamphamvu kuti tikhale ‘mumtendere, opanda banga ndi opanda chirema.’ Mmalo mosochezedwa ndi aphunzitsi onyenga, tiyeni tikuletu m’chidziŵitso cha Yesu Kristu.
Tatiyeni tilabadire mawu a Petro. Tisalephere konse kuchenjera ndi aphunzitsi onyenga. Khalani atcheru kuti tsiku la Yehova lidzabwera posachedwapa. Ndipo nthaŵi zonse perekani chisamaliro ku mawu aulosi a Mulungu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 31]
Anaponyedwa Kundende: Yehova ‘sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzidwe.’ (2 Petro 2:4) Iyi siiri Ndende yanthanthi yosonyezedwa mu Iliad ya Homer monga malo akunsi kwa nthaka kumene milungu yonama yaing’ono, Cronus ndi mizimu ina ya Titan, inamangidwako. Ndende ya m’Baibulo ndiyo mkhalidwe wonyozeka, wonga ndende mmene Mulungu anaponya angelo opandukawo m’tsiku la Nowa. (Genesis 6:1-8; 1 Petro 3:19, 20; Yuda 6) ‘Mdima waukulu’ umachititsidwa ndi kudulidwa kwawo ndi Mulungu ku kuunika kwauzimu monga opitikitsidwa m’banja lake. Pokhala osungidwira chiweruzo chake champhamvu, iwo ali kokha ndikawonekedwe ka mdima. Ndendeyi iri kalambula bwalo wa kuponyedwa m’phompho komwe Satana ndi ziŵanda zake adzayang’anizana nako Zaka Chikwi za Kulamulira kwa Kristu zisanayambe. Chiwonongeko chawo chidzachitika pambuyo pa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu.—Mateyu 25:41; Chibvumbulutso 20:1-3, 7-10, 14.
[Chithunzi]
Zeu anaponyera milungu yaing’ono m’Ndende yanthanthi
[Mawu a Chithunzi]
National Archaeological Museum, Athens, Greece