Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 1/1 tsamba 32
  • Kumasula Yomalizira ya Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumasula Yomalizira ya Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 1/1 tsamba 32

Kumasula Yomalizira ya Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa

SEPTEMBER wapita, chothetsa nzeru cha akatswiri chomwe chinakhalapo kwa zaka makumi ambiri chinagonjetsedwa. Mkangano waukulu pakati pa ophunzira Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa unawonekera kukhala utatha, ngakhale kuti mkangano watsopano ungakhale unayamba.

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inatumbidwa m’mapanga pafupi ndi Nyanja Yakufa mu 1947 ndi m’zaka zotsatirapo. Iyo inali yothandiza kwambiri m’kusonyeza kulongosoka kofunika kwa zolembedwa za Malemba Achihebri ndi kupereka chithunzi cha mikhalidwe yachipembedzo m’Palestina pamene Yesu anali padziko lapansi. (Yesaya 40:8) Pamene kuli kwakuti malembo apamanja ena anafalitsidwa mwamsanga, mu 1991 malembo apamanja pafupifupi 400 anali osafalitsidwabe ndi osapezeka kwa akatswiri ochuluka. Ambiri, mofanana ndi Profesa Ben Zion Wacholder, “anakhumudwa pamene anazindikira kuti paliŵiroli lakufalitsidwa kwa bukhuli tonsefe tidzakhala titafa pamene zolembedwa za ku Nyanja Yakufa zidzaperekedwa ku dziko.”

Koma mkhalidwewo unasintha September wapitayu. Choyamba, Profesa Wacholder ndi mnzake, Martin Abegg, analengeza kuti iwo mwamachenjera anagwiritsira ntchito kompyuta kulembanso malemba otetezeredwa mosamalitsa. Ndiyeno, Huntington Library mu San Marino, California, U.S.A., inalengeza kuti iwo anali ndi zithunzithunzi za malembo apamanja oyambirira ndipo akawapereka kwa akatswiri otchuka popanda ziletso. Mwachiwonekere, makope ojambulidwa angapo a mipukutuyo anapangidwa kuti asungike. Mipukutu yambiri ya zithunzithunzizo inasungidwa m’malo osiyanasiyana, ndipo m’kupita kwanthaŵi mpukutu umodzi unapezeka mu Huntington Library.

Katswiri wina anatcha kusintha kwa zinthu kumeneku ‘kugwetsa khoma kwa akatswiri kofanana ndi Khoma la Berlin.’ Akonzi alamulo anati kufalitsidwa kwa zolembedwa zapakompyutazo ndi kumasulidwa kwa zithunzithunzizo kunali ‘kuba.’ Mwachiwonekere, mkangano pa mwambo wa makhalidwe udzakhalapobe kwa zaka zambiri. Pakali pano, kukuwonekera kuti pomalizira pake akatswiri ena ambiri adzakhoza kukambitsirana ndi bungwe lonse la Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa.

[Chithunzi patsamba 32]

Umodzi wa Mipukutu ya Kunyanja Yakufa, woimira ndemanga ya Habakuku

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena