Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/1 tsamba 32
  • “Mkazi Wokula Naye”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mkazi Wokula Naye”
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/1 tsamba 32

“Mkazi Wokula Naye”

“CHIGOLOLO chikuwonekera kukhala chochitika cha masiku onse.” Akutero akatswiri ambiri, malinga ndi Los Angeles Times. Kodi ndemanga yotero ikukudabwitsani? Chikhalirechobe, katswiri wanthenda zamaganizo Frank Pittman akuyerekezera kuti pafupifupi 50 peresenti ya amuna okwatira ndi kuyambira pa 30 peresenti mpaka 40 peresenti ya akazi okwatiwa akhala osakhulupirika. Ngati zimenezo ziri zowona, pafupifupi theka la anthu onse okwatira amachita chigololo!

Kodi zimenezo zimatanthauza kuti chisembwere chiri chabwino? Kutalitali! Kufalikira kwa kusakhulupirika sikumachipanga kukhala chabwino​—monga momwedi kukula kwa upandu wa m’makwalala sikumapangitsa kufwamba munthu wina kukhala kwabwino. Chisembwere chimavulaza. Mwachitsanzo, mtundu wa anthu lerolino ngwokanthidwa ndi mliri wanthenda zowopsa zopatsirana mwakugonana zimene zikanachinjirizidwa mosavuta ngati anthu akanakhala odzisungira. Nthenda yakupha ya AIDS sikanafalikira motero ngati anthu akanakhala odziletsa m’zakugonana.

Ndiponso, ngakhale ophunzira ndi “achidziŵitso” kwambiri amapsinjika mtima kwambiri pamene anzawo amuukwati akhala osakhulupirika. Mchitidwe umodzi wakusakhulupirika ungachititse kusweka mtima kumene kumatenga nthaŵi yaitali yamoyo kuchira.

Komabe, mfundo yofunika koposa njakuti kupeputsa malumbiro aukwati kumanyoza Mulungu kwambiri, popeza kuti ndiye Woyambitsa wa ukwati. Baibulo limati: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse.” Ndiponso timachenjezedwa kuti: “Adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.”​—Ahebri 13:4.

Chifukwa chake, anthu anzeru amalabadira mawu ouziridwa akuti: “Ukondwere ndi mkazi wokula naye.” (Miyambo 5:18) Iwo amafunafuna chikhutiro ndi chimwemwe ndi anzawo amuukwati. Mwakutero amasungitsa thanzi lawo lakuthupi ndi lamalingaliro, ndipo chofunika koposa, amapereka ulemu kwa Woyambitsa wamkulu wa ukwati, Yehova Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena