Chowonadi Chisefukira m’Mudzi wa Madzi Ambiri
NKWACHILENDO chotani nanga! Dziko lomveka chifukwa cha madzi ake ambiri lipezeka laludzu! Dera la madzi ambiri lipezeka louma ndi losabala! Liri ludzu limene lingaphedwe kokha ndi madzi a chowonadi cha Mawu a Mulungu, Baibulo. Imeneyi ndinkhani yosimba za Rahbeh, mudzi waung’ono wa anthu 2,200, wokhala pakati pa mapiri kumpoto kwa Lebanon, pafupifupi makilomita 130 kuchokera ku Beirut.
Dzinalo Rahbeh limatanthauza “malo otakata” m’Chiluya, ndipo latengedwa kumagwero otanthauza “chachikulu, chofutukuka” lochokera ku zinenero za fuko la Semu. Moyenerera, mudziwo ngwofutukukira pazitunda ziŵiri zazikulu pafupifupi mlingo wa mamita 600 pamwamba pa mlingo wa nyanja. M’nthaŵi yachisanu ndi yangululu, chipale chofeŵa chingawoneke pamwamba pa mapiri kum’maŵa, chikumawonjezera kukongola kwake. Koma, kwakukulukulu, Rahbeh uli mudzi wa madzi ambiri. Muli akasupe aakulu ndi aang’ono 360 m’deralo, opereka madzi ofunikawo kaamba ka minda yachonde ya tirigu, maapricot, mapeyala, mapichesi, ndi mphesa m’zigwa zapafupi.
Zamakedzana ndi Zamakono Zipezeka m’Rahbeh
M’mbali zambiri zinthu m’Rahbeh zakhala zimodzimodzi chiyambire m’nthaŵi za m’Baibulo. Nyumba m’mudziwu nzomangidwa pafupipafupi. Makwalala ngopapatiza, okhotakhota, ndi odzala zoyendera—abulu ndi ng’ombe. Ngakhale kuti kuli magalimoto, zinyama ziri ndi ufulu wakugwiritsira ntchito msewu kunoko. Kaŵirikaŵiri eni ake amazisenza katundu kuminda nazitumiza kunyumba mwa izo zokha. Zimatsatira makwalala opapatiza, zikumapyola m’malo apiringupiringu, nizibwerera kunyumba kwawo. Kodi zimenezi zingakhale zofanana ndi zimene Yesaya analikuganiza pamene anati: “Ng’ombe idziŵa mwini wake, ndi bulu adziŵa pomtsekereza”?—Yesaya 1:3.
Rahbeh alinso malo amikhalidwe yosiyanasiyana. Kunoko mudzapeza omaliza maphunziro payunivesiti limodzi ndi alimi wamba amene sanapitepo kumzinda. Muli nyumba zazikulu zozunguliridwa ndi maluŵa ndi kapinga, ndipo muli tinyumba tamaudzu ndi zifuyo zomathamangathamanga. Zipangizo zamagetsi zimapezeka pafupifupi m’nyumba iriyonse, koma magetsi samapezeka nthaŵi zambiri. Kaamba ka chifukwa chimenechi, nyumba zambiri ziri ndi makina opanga magetsi. Misewu yaikulu ya m’mudziwu njokonzedwa, ngakhale kuti tinjira tambiri topita kuminda ntoŵirira ndi tokumbikakumbika. Chotero, njira yokha yonyamulira dzinthu kuchokera kuminda ndiyo zinyama zoŵeta. Mungawone ngakhale bulu atanyamula makina opanga magetsi kupita nawo kumunda kukapereka magetsi kumakina apafamu, amene amagwiritsidwa ntchito pambali pa zinyama zonyamula katundu m’minda.
Mofananamo, moyo m’mudziwu sunasinthe kwambiri. Ngati mugona m’mudziwu, mungadzutsidwe ndi atambala olira pa 2 kapena 3 koloko mbandakucha. Ntchito ya tsiku ndi tsiku ya nthaŵi zonse imayamba m’mamaŵa, choncho musadabwe ngati mumva anthu akuitanana mofuula m’mdima pokonzekeretsa zinyama. Kutacha, mungathe kuwona anthu ambiri a m’mudziwu, ndi zinyama zawo zitanyamula katundu, kupita kuminda kapena kumisika kukagulitsa katundu wawo.
Pamene dzuŵa likwera, tianyamata ndi tiasungwana timatulukira kunja kukaseŵera m’misewu ndi m’mabwalo. Kulira kwawo ndi kuseka kumadzaza mlengalenga, monga mmene zinaliri m’Yerusalemu wamakedzana wofotokozedwa ndi mneneri Zekariya kuti: “M’misewu ya mudzi mudzakhala ana amuna ndi akazi akuseŵera m’misewu yake.” (Zekariya 8:5) Mudzapezanso kuti anthu a m’mudzi ali aubwenzi kwambiri ndi okonda kufunsa. Mumayembekezeredwa kupereka moni kwa munthu aliyense amene mukumana naye, popeza amafuna kudziŵa kuti ndinu yani, kumene muchokera, chifukwa chake muli kuno, ndi kumene mukupita. Anthu amafikira pakudziŵana bwino kwambiri.
Madzi a Chowonadi Afika m’Rahbeh
M’chitaganya cha anthu ogwirizana chotero, mbiri imafalikira mofulumira. Zimenezi ndizo zinachitika pamene Asaad Younis anabwera ku Rahbeh kuchokera ku United States mu 1923. Pofuna kudziŵa ngati Asaad analemera ali ku Amereka, Abdallah Blal bwenzi lake anapita kukamuwona. Mmalo molankhula za ndalama, Asaad anampatsa kope la bukhu la Zeze wa Mulungu namuuza kuti: “Nachi chuma chenicheni.” Abdallah, yemwe anali Mprotesitanti, anaŵerenga bukhu lofotokoza Baibulo limeneli ndipo anachita chidwi kwambiri. Ngakhale kuti Asaad sanachitepo kanthu kwenikweni pa chidziŵitsocho, Abdallah anachita nthumanzi kwambiri ndi zimene anaphunzira navomereza poyera kuti anapeza chowonadi.
Pambuyo pa nthaŵi yakutiyakuti, Abdallah anasamukira ku Tripoli, mzinda waukulu kumpoto kwa Lebanon. Kumeneko, anakumana ndi Ophunzira Baibulo angapo, monga momwe Mboni za Yehova zinadziŵikira panthaŵiyo, ndipo anapanga kupita patsogolo kwambiri m’maphunziro ake a Baibulo. Pambuyo pake anabwereranso ku Rahbeh kukafalitsa mbiri yabwino imene anaphunzira. Iye ankaloŵetsa anansi ake m’makambitsirano ankhani zonga Utatu, kaya ngati munthu ali ndi moyo wosakhoza kufa, moto wa helo, unsembe, Misa, ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa mafano, akumagaŵana nawo zimene Baibulo limaphunzitsadi.
Ena a m’mudziwo anasonyeza chikondwerero. Atatu kapena anayi a iwo anagwirizana ndi Abdallah m’ntchito yolalikira. Ndiyeno anayamba kuchita misonkhano ya pa Sande. Imeneyi inaphatikizapo kumvetsera ulaliki wojambulidwa pa rekodi puleya kapena kuŵerenga Baibulo, kotsatiridwa ndi kukambitsirana zimene anali atamva kumene. Pambuyo pake, zothandizira kuphunzira Baibulo zina zinagwiritsiridwa ntchito, kuphatikizapo mabuku akuti Zeze wa Mulungu, Cuma, ndi “Mulungu Akhale Woona.” Opezekapo anali osaposa pa anthu khumi, amene ambiri a iwo anangofuna kudzawona zochitika mmalo mwakuphunzira. Ena anawoneka kukhala atabwerera kwakukulukulu chakudya choperekedwa pamapeto a msonkhano uliwonse.
M’ma 1940, Abdallah Blal anapatsidwa thayo la kuyang’anira kagulu m’Rahbeh. Anakhaladi mtumiki wa Yehova wachangu ndi wokhulupirika, akumapereka chitsanzo chabwino kwa ena. Mmodzi wa ameneŵa, Mbale Mattar, akukumbukira mmene ankachitira ntchito yawo yolalikira kuti: “Popeza kuti kunalibe galimoto panthaŵiyo, Mbale Blal ndi ine tinapita ndi miyendo kukachitira umboni m’midzi yapafupi. Ndinanyamula rekodi puleya, pamene Mbale Blal anachita mbali yakulankhula. Kaŵirikaŵiri tinkapita kwa masiku aŵiri kapena atatu tisanabwerere kunyumba.” Mbale Blal anatumikira Yehova mokhulupirika kufikira imfa yake mu 1979 ali wazaka 98 zakubadwa.
Kupita Patsogolo Kubweretsa Chitsutso
Pamene ntchitoyo inali kupita patsogolo, abale anayamba kukumana ndi chitsutso. Mu 1950, mosonkhezeredwa ndi wansembe wa m’mudziwu, mkupiti wa chizunzo unayambidwa pa abale m’Rahbeh. Wansembe anaimba abale mlandu wakunyozera tchalitchi ndi wakuchita mwano. Anthu ena a m’mudziwu anakwiya kwambiri kotero kuti anaponya miyala abale, ndipo abale ena anagwidwa naponyedwa m’ndende. Komabe, kufufuza kotsatirapo kunatsimikizira zinenezozo kukhala zonama. Ngakhale zitatero, abalewo anasungidwa m’ndende kwa masiku angapo.
Wotsutsa wina anayesa kuchititsa anthu a m’mudzi, amene ena a iwo angakhale anali osadziŵa bwino kuŵerenga, kusaina chikalata choimba abale mlandu wa zinthu zambiri, kuphatikizapo kudodometsa anthu mwakufika panyumba zawo mosalekeza. Kuti achititse anthu ambiri kusaina chikalatacho, iye anawauza kuti linali pempho la wantchito wina yemwe akasamutsidwiranso kumudziwo. Pamene anthu anadziŵa kuti chinali kwenikweni chinenezo pa Mboni, iwo anafafaniza masaini awo. Zochitika zonga chimenechi zinathandizira kuchitira umboni wabwino kwa akuluakulu a m’deralo.
Kuwonjezera pa kuyang’anizana ndi chitsutso chotheratu chimenecho, abale anayang’anizana ndi chopinga china. M’mudzi waung’ono m’mene anthu onse amadziŵana, “kuwopa anthu kutchera msampha,” monga momwe Baibulo limanenera pa Miyambo 29:25. Pamafunikira kulimba mtima kuti abale alalikire kwa anansi, mabwenzi, ndi achibale, amene amawasuliza ndi kuwaseka mosalekeza. Chotero tanthauzo lenileni limaikidwa pa mawu a Yesu pa Mateyu 10:36 akuti: “Apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.” Komabe, monga momwe mwambiwo umapitirizira kuti, “wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” Chikhulupiriro ndi chipiriro cha abale zadzetsa zotulukapo zapadera.
Chowonadi Chisefukira m’Rahbeh
M’zaka zambiri zapita anthu a m’mudziwu afikira pakuzindikira mkhalidwe wabwino wa Mboni za Yehova, ndipo ambiri alandira chowonadi. Abale anakondwera kwambiri mu 1969 pamene mpingo wachiŵiri unapangidwa m’Rahbeh. Iwo anapitiriza kugwira ntchito zolimba. Ambiri anayamba uminisitala wanthaŵi yonse, ena anasamukadi kukatumikira kumagawo ena, kuphatikizapo mzinda wa Beirut. Yehova anadalitsa ntchito yawo yamphamvuyo, ndipo mpingo wachitatu unayambidwa m’Rahbeh mu 1983. Panthaŵiyo, abale ambiri anasamukira kumizinda. Komabe, chiwonjezeko chinapitirizabe, ndipo mpingo wachinayi unapangidwa m’Rahbeh mu 1989, wotsatiridwa ndi wachisanu mu 1990.
Podzafika panthaŵi imeneyi pafupifupi banja lirilonse m’mudziwu linali ndi wachibale kapena bwenzi limene linali Mboni. Udani umene unalipo kalelo unazimiririka. Anthu anazoloŵerana bwino lomwe ndi Mboni. Kwenikweni, mawu akuti “mkulu,” “mpainiya,” “woyang’anira dera,” “msonkhano,” ndi “Armagedo” anayamba kugwiritsidwa ntchito mofala m’makambitsirano a tsiku ndi tsiku a anthu a m’mudziwu. Pazochitika zapadera, zonga kuchezetsa kwa woyang’anira dera kapena Chikumbutso, misewu ikakhala yopanda anthu ndi Nyumba Zaufumu zikadzala thothotho. Mipingo ina imaikadi zokuzira mawu m’khonde kuti anansi azimvetsera.
Tsopano muli ofalitsa Ufumu oposa 250 m’Rahbeh. Zimenezo zikutanthauza kuti pali Mboni 1 mwa anthu 8 alionse a m’mudziwu! Mpingo wina wa ofalitsa 51 uli ndi gawo la nyumba zokwanira 76, ndipo amalifola mlungu uliwonse. Tayerekezerani zimene zinachitika m’mwezi wa March ndi April chaka chatha pamene 98 mwa ofalitsa 250 anatenga ntchito ya upainiya wothandiza, limodzi ndi apainiya okhazikika 13 m’Rahbeh. Gawolo linafoledwa nthaŵi zambiri mlungu uliwonse. Sikunali kwachilendo kwa nyumba imodzi kufikiridwa kaŵiri kapena katatu ndi ofalitsa ali aŵiri aŵiri patsiku limodzi kapena ngakhale onsewo panthaŵi imodzi. Ambiri a anthu a m’mudziwu azoloŵera maulendowo. Koma pamene mwamuna wina anadandaula, wofalitsa wina anayankha naati: “Pamene mudzavomera kuti tichite nanu phunziro Labaibulo, pamenepo tidzakufikirani kamodzi kokha pamlungu.” Iwo amalankhulanso kwa aliyense amene amakumana naye m’minda—anthu olima, odzala, othirira, kapena okwera pa abulu.
Kunena zowona, chowonadi cha Baibulo chasefukira m’Rahbeh, mudzi wa madzi ambiri. Koma sizokhazo. Monga momwedi Rahbeh wakhalira magwero a madzi ŵeniŵeni kumidzi yozungulira, wagaŵiranso midziyo madzi a moyo a chowonadi cha Baibulo. Ofalitsa a m’Rahbeh amachezera anthu m’midzi yapafupi mwakuyenda ndi miyendo ndipo amalinganiza timagulu toyenda ndi galimoto kupita paulendo wa tsiku limodzi kukalalikira kumidzi yakutali. Ofalitsa ena amasamuka kukatumikira kumizinda ina. Ndi dalitso la Yehova, padzakhala chiwonjezeko chachikulu cha anthu amene adzaperekabe chitamando chachikulu kwa Atate wakumwamba, Yehova Mulungu.
[Chithunzi patsamba 26]
Mawonekedwe a khwalala m’Rahbeh