Kupereka Chidziŵitso mu Namibia
KODI ndim’zinenero zingati mmene munamva mawu akutiwo “Sindidziŵa”? “Hi nokuzuva,” anatero dona Wachiherero, atavala diresi lake lalitali lamwambo ndipo ataphimba kumutu mpango wamawonekedwe anyanga. “Nghi udite ko,” anayankha motero msungwana wafuko la Kwanyama, momwetulira. “Kandi uvite ko,” anayankha motero m’Ndonga wakumidzi, akumatukula mapewa ake. “Kapi na kuzuvha,” anatero mbusa wa mbuzi Wachikwangali.
Anthu onse amenewa anali kunena kuti, “Sindidziŵa.” Zimenezi zimasonyeza mwafanizo bwino lomwe chotani nanga kuti Mboni za Yehova m’Namibia zinayang’anizana ndi mavuto aakulu achinenero pamene zinayesa kufika kwa nzika zokwanira 1,370,000 m’gawo lalikulu kwambiri limeneli la ukulu pafupifupi makilomita 824,000 monsemonse!
Ndipo mposadabwitsa! Si anthu Achiherero ndi Anama okha komanso Aovambo, Akavango, Atswana, nzika za Caprivi, Ahimba, Abathwa, ndi Adamara, anthu aku Namibia onsewa ali ndi zinenero zawozawo. Mosiyana, Mboni zinali zitanyamula kokha Baibulo ndi mabukhu a Chingelezi ndi a Chiafrikaans. Mwachiwonekere, kuti chowonadi chimveke kwa anthu owonjezereka, ntchito yotembenuza inali yofunika. Imeneyi inayamba pamlingo wochepa kwambiri zaka zambiri zapitazo mu Windhoek, mzinda umene uli likulu la dziko limene kalelo linali kutchedwa South-West Africa.
“Mu Windhoek, munali chitsutso chadzawoneni kuntchito yathu yochitira umboni chochokera ku tchalitchi ndi apolisi,” akukumbukira motero Dick Waldron. Limodzi ndi mkazi wake, Coralie, iye anafika m’dzikoli mu 1953 monga wotsiriza maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. “Sitinali kuloledwa kulowa m’madera a anthu akuda, ndipo nthaŵi zina tinali kuthupsidwa pamene tinawonedwa tikulankhula ndi anthu akuda. Potsirizira pake tinapeza malo kumene sitinali ododometsedwa—pankhwaŵa la Mtsinje wa Gammans! Malowa anali kunja pang’ono kwa tawuni. Mobisika m’zitsamba za acacia, tinachititsa maphunziro a Baibulo kumeneko.”
Kunalinso kumeneko kumene mabukhu a Watch Tower anatembenuzidwira m’zinenero za dzikolo kwanthaŵi yoyamba. Anaphatikizapo matrakiti m’chinenero cha Kwanyama ndi kabukhu kotchedwa “Mbiri Yabwino Imeneyi Yaufumu” m’Chinama. Mbale Waldron akukumbukira chochitika choseketsa chokhudza kabuku kameneka, kamene munthu wokondwerera anali kuthandizira kutembenuza. Liwu lofanana m’Chinama silinapezeke la mawu akuti, “Adamu anali munthu wangwiro.” Chotero wokondwererayo anati: “Ingolembani kuti Adamu anali wofanana ndi pichesi wakupsa. Anthu Achinama adzazindikira kuti iye anali wangwiro.” Choncho, umu, ndimo mmene chiyambi chinaliri m’kupereka chidziŵitso cha Malemba pakati pa nzika zambiri za anthu aku Namibia.—Yerekezerani ndi Danieli 11:33.
Kufika Pachochitika Chachikulu
Chochitika chachikulu chinafikidwa kuchiyambiyambi kwa ma 1970 pamene bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya linatembenuzidwira m’Chindonga ndi Kwanyama. Izi ndizo zinenero zazikulu ziŵiri zolankhulidwa m’malo okhala anthu ambirimbiri aku Namibia mu Ovamboland, pafupifupi makilomita 700 kumpoto kwa Windhoek. Pamenepo malo okhala apainiya anayambika mu Ondangwa, malo akumidzi a Ovamboland. Kuthandiza anthu okondwerera m’dera limeneli kuti apindule ndi phunziro la Baibulo la mlungu uliwonse lochokera mu Nsanja ya Olonda, apainiya apadera otumikira ku Ovamboland anapatsidwa gawo lakutembenuzira mwachidule nkhani zophunziridwa m’chingelezi m’zinenero za Ndonga ndi Kwanyama.
“Ofesi” yotembenuza inali chipinda chowonjezeredwa pangodya ya garaji kumene makope ankhani zotembenuzidwa za Nsanja ya Olonda anasindikizidwa pa makina akale osindikizira. Sikunali kosavuta kusumika maganizo pa ntchito yodya nthaŵi kwambiri imeneyi, popeza mikhalidwe inali yachikale kwambiri ndipo kutentha kwa m’chilimwe kunali kufika pa mlingo wa pakati pa 38 ndi 44 digiri Celsius. Komabe, kunali kunoko kumene mabrosha atsopano ndi bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi zinatembenuzidwirako.
Pamene mipingo inapangidwa mu Ovamboland ndi malo ena m’Namibia, kulabadirako kunali kwakukulu kotero kuti malo okulira ndi abwinopo anali ofunika. Kuwonjezera apa, malo apakatikati anafunika kuchitira kuti chisamaliro chikaperekedwa kuzofunika m’mbali zina zadzikolo. Panthaŵiyo, udani wotsutsa ntchito yolalikira Ufumu unali utachepachepa. Chotero chilolezo chinaperekedwa chakuyamba kumanga pamalo aakulu operekedwa monga mphatso ndi mmodzi wa Mboni za Yehova mu Windhoek. Mwamsanga, oposa antchito odzifunira 40 anali kugona pamalo anyumba yatsopano amenewa, ndipo mu December 1990 maofesi a otembenuza anamalizidwa.
Tsopano, kuchokera m’maofesi abwino ndi zipinda zanyumba yamakono imeneyi, ntchito yakupereka chidziŵitso kwa ambiri ikuyenda mofulumira. Mabukhu atsopano akutembenuzidwira mosalekeza m’chinenero cha Herero ndi Kwangali. Ponena za chinenero cha Ndonga ndi Kwanyama, kope la mwezi ndi mwezi la Nsanja ya Olonda tsopano likusindikizidwa m’zinenero zogwirizana ziŵiri zimenezi m’mawonekedwe okongola. Limakhala ndi nkhani zophunziridwa zonse kudzanso nkhani zina. Ndithudi, zimenezi, nzosiyana kwambiri ndi chiyambi chochepetsetsa mkhwaŵalo zaka zambiri zapitazo.
“Sindidziŵa” tsopano amamvedwa mwa kamodzikamodzi. Mmalomwake, Mboni za Yehova zoposa 600 mu Namibia zikuyamikira kwambiri Atate wawo wakumwamba, ndipo tsopano izo zinganene kuti: “Potsegulira mawu anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.”—Salmo 119:130.
[Zithunzi patsamba 25]
Kulalikira mbiri yabwino pakati pa anthu Achiherero
Kutembenuza mabukhu Achikristu kupindulitsa anthu aku Namibia
Maofesi otembenuzira mu Namibia