Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 2/15 tsamba 7
  • Sangalalani ndi Dziko Lapansi Loyeretsedwa Mtsogolomo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sangalalani ndi Dziko Lapansi Loyeretsedwa Mtsogolomo!
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Paradaiso Kapena Dzala—Kodi Musankhapo Chiti?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kuzulamo Kuipitsa Malo Mumtima ndi m’Maganizo
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Yehova Amakonda Anthu Aukhondo
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Kodi Ukhondo Umatanthauza Chiyani Makamaka?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 2/15 tsamba 7

Sangalalani ndi Dziko Lapansi Loyeretsedwa Mtsogolomo!

TINGAKHALE achimwemwe chotani nanga kuti Yehova, Mulungu wadongosolo ndi waudongo, adzakwaniritsa chifuno chake choyambirira chakupanga dziko lapansi kukhala paradaiso wadziko lonse! (Yesaya 11:6-9) Iye akulonjeza kuti: ‘Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna.’ ‘Mulungu sakhoza kunama,’ chotero amenewa sali mawu achabechabe.​—Yesaya 55:11; Ahebri 6:18.

Tingathe kutonthozedwa m’chakuti Yehova adzaloŵerera mwachikondi anthuwo asanafike mlingo woipitsitsa umene kuwonongeka kotheratu kwa malo okhala anthu ndi zinyama kungakhale kosaletseka!​—Chivumbulutso 11:18.

Yehova adzachotsa oipitsa osalapawo, ochita dala ndi anthu amene mopanduka amanyalanyaza malamulo ake amakhalidwe abwino a dongosolo ndi ukhondo. Palibe munthu adzaloledwa kuika paupandu Paradaiso wobwezeretsedwanso.​—Miyambo 2:20-22.

Mkati mwa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, motsogozedwa ndi Kristu Yesu, anthu adzaphunzitsidwa mmene angachotsere zoputira zonse zotsala za kuipitsa malo kwakuthupi. Panthaŵiyo​—osati tsopano​—ndipamene kudzakhala kofunika kuti atumiki a Mulungu onse aphatikizidwe mwachangu m’njira zaumwini ndi zachiungwe zimene zidzathandizira kuyeretsa kwa padziko lonse kumene sikunachitikepo ndi kalelonse.​—Yerekezerani ndi Ezekieli 39:8-16.

Opulumuka mapeto adongosolo loipa liripoli la zinthu adzachirikiza programu yakuyeretsa kwakuthupi imeneyi ndi kudzipereka kumodzimodzi ndi kutenthedwa maganizo konga kumene amakhala nako pokhala ndi phande mu mkupiti wakuyeretsa kwauzimu kwa lerolino.​—Salmo 110:3.

Dziko lapansi loyeretsedwa lidzadza motsimikizirika, kalambula bwalo wake adzakhala mkupiti wakuyeretsa waukulu koposa umene sunachitikepo nthaŵi zonse, wochitidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Zizindikiro zonse zakuipitsa malo ndi mpweya zidzachotsedwa. Sipadzakhalanso zolembalemba zirizonse pamakoma. Sipadzakhala mabotolo otaidwa, zitini, matumba a plasitiki, chingamu ndi mapepala a maswiti, manyuzipepala, ndi magazini zoti mbwee pa gombe lirilonse kapena malo aparadaiso.

Sangalalani ndi dziko lapansi loyeretsedwa mtsogolomo!

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi inu mudzakhala ndi phande m’kuyeretsa kwa padziko lonse kulinkudza?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena