Kuzulamo Kuipitsa Malo Mumtima ndi m’Maganizo
YEHOVA sanachititse anthu kukhala ndi chikhumbo cha uve kapena chisokonezo. Pulaneti lawo limene lirinso kwawo linalinganizidwa kukhala paradaiso waudongo, wadongosolo, ndi wokongola. Mulungu sanalinganize kuti linyonyosoke kukhala dzala lochititsa nyansi.—Genesis 2:8, 9.
Komabe, anthu atakana chitsogozo cha Mulungu, anayamba kumanga dongosolo la iwo eni la dziko. Popanda nzeru yochokera kwa Mulungu ndi popanda chidziŵitso, iwo anakakamizidwa kuphunzira mwa kuwongolera pambuyo pakulakwa. Mbiri yadziko ikutsimikizira chowonadi cha Baibulo chakuti anthu sangathe kudzilamulira mwachipambano; kwa zaka zikwi zimbiri ‘munthu wapweteka mnzake pomlamulira.’ (Mlaliki 8:9; Yeremiya 10:23) Vuto lamakono lakuipitsidwa kwa malo, m’mipangidwe yake yonse, liri chotulukapo cha kulephera kwa munthu kulamulira.
Kulandira Lingaliro la Mulungu
Anthu okhumba kukondweretsa Mulungu amayesa mwamphamvu kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Mlengi ya ukhondo. Chotero, Mboni za Yehova zinayang’anizana ndi vuto pamene msonkhano wamitundu yonse unalinganizidwa kuchitidwira m’Prague, Czechoslovakia, chapakati pa 1991.a Pafupifupi anthu 75,000 anayembekezeredwa kufika pamsonkhanowo, khamu limene Stadium la Strahov ikakhoza kukwanira popanda vuto. Koma bwalo lamaseŵeralo silinagwiritsidwe ntchito kwa zaka zisanu. Linali mu mkhalidwe wopasuka, lowonongedwa ndi mikhalidwe yakunja. Pafupifupi Mboni za Yehova 1,500 zinathera maola oposa 65,000 kulikonzanso ndi kulipakanso utoto. Podzafika nthaŵi yamsonkhano mkupiti wakuyeretsa umenewu unali utapangitsa bwalo lamaseŵeralo kukhala malo oyenerera kulambiriramo Mulungu wowona, Yehova.
Kodi chimasokhezera Mboni za Yehova kukhala zosiyana nchiyani, pamene dziko lonse limasonyeza chiyamikiro chochepa chotero cha udongo ndi ukhondo? Kuyamikira uphungu wa Baibulo wakuti Akristu ayenera kuzula mikhalidwe yoipa, monga ngati dyera, kusalingalira ena, umbombo, ndi kupanda chikondi. ‘Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,’ Baibulo limatero. Uloŵedwe mmalo ndi ‘umunthu watsopano, umene mwachidziŵitso cholongosoka ulikupangidwa kukhala watsopano mogwirizana ndi chifanefane cha Uyo amene anaulenga,’ Umunthu wodziŵika ndi kukonda kwake udongo, ukhondo, ndi kukongola ulibe malo akukhala ndi zikhoterero zoipitsa.—Akolose 3:9, 10; 2 Akorinto 7:1; Afilipi 4:8; Tito 2:14.
Umunthu watsopano umafuna kuti Akristu akhale odera nkhaŵa ndi kuipitsidwa kwa malo, osati kukhala oipitsa osasamala kapena mosamvera onyalanyaza malamulo oletsa kuipitsa amene maboma amapereka. Umathandiza Akristuwo kupeŵa kukhala ndi kaimidwe kamaganizo kotayataya zinthu, dyera, ndi ulesi kamene kamatsogolera kukuipitsa malo ndi zinyalala. Mwakukulitsa ulemu wa zinthu za ena umaletsa kugwiritsira ntchito kulembalemba pamakoma monga njira yosonyezera malingaliro anu ndi ziganizo, monga kuseŵera wamba, kapena monga mchitidwe wina wakujambula mwaluso. Umafuna kuti nyumba, magalimoto, zovala, ndi matupi zisungidwe ziri zoyera.—Yerekezerani ndi Yakobo 1:21.
Ponena za anthu osafuna kuvala umunthu watsopano umenewu, kodi Mulungu angapezedwe ndi mlandu posawalola kupeza moyo m’Paradaiso wake alinkudza? Kutalitali. Aliyense amene adakali ndi zikhoterero zakuipitsa ziri zobisika mu mtima mwake kapena maganizo akadodometsa kukongola kwa paradaiso wobwezeretsedwa pa pulaneti iri lokongola Dziko Lapansi, kukumachititsa chisoni anthuwo okhala ndi chikhumbo chakuwusamalira. Chosankha cha Mulungu cha ‘kuwononga iwo akuwononga dziko lapansi’ chiri ponse paŵiri cholungama ndi chachikondi.—Chivumbulutso 11:18; 21:8.
Kodi Tikhalemo ndi Phande Mwachangu?
Komabe, kodi izi zitanthauza kuti, Akristu afunikira kupititsa patsogolo michitidwe yotsutsa kuipitsa malo kapena yoyeretsa?
Mwachiwonekere kuipitsa malo nkwaupandu kuthanzi ndi chisungiko cha anthu onse. Yehova ali ndi nkhaŵa yoyenerera yokhudza nkhani zotere, monga momwe tingawonere kuchokera m’malamulo amene anawapereka kwa Aisrayeli. (Eksodo 21:28-34; Deuteronomo 22:8; 23:12-14) Koma palibe nthaŵi iriyonse pamene anawauza kusonkhezera anthu ena pankhani za chisungiko cha anthu onse; ndiponso Akristu a m’zaka za zana loyamba sanauzidwe kuchita motero.
Lerolino, nkhani zokhudza malo okhala zingathe kukhala mosavuta mikangano ya ndale zadziko. Kwenikweni, zipani zina za ndale zadziko zapangidwa kwenikweni ndi cholinga cha kuthetsa mavuto okhudza malo okhala. Mkristu amene akudzilola kusonkhezeredwa kutenga mbali mochirikiza ziganizo za ndale zadziko salinso wachete kundale zadziko. Yesu anapereka kwa ophunzira ake lamulo lamakhalidwe abwino lakuti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.” Mkristu amene amanyalanyaza chofunika chimenecho akudziika paupandu wakukhala wochirikiza “akulu anthaŵi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa.”—Yohane 17:16; 1 Akorinto 2:6.
Yesu sanayese kuthetsa mavuto onse amakhalidwe a anthu a m’tsiku lake; ndiponso sanauze ophunzira ake kuchita motero. Lamulo lake kwa iwo linali lakuti: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza . . . , kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’ Iye sanawapatse malamulo okhudza malo okhala.—Mateyu 28:19, 20.
Akumafotokoza zimene ziyenera kukhala zoyambirira m’moyo wa Mkristu, Kristu anati: ‘Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.’ (Mateyu 6:33) Pamene Yehova, kupyolera mwa Ufumu Waumesiya, akakamiza malamulo ake amakhalidwe abwino olungama pamlingo wa dziko lonse, mavuto amalo okhala adzakhala atathetsedwa kwachikhalire ndi mokhutiritsa onse.
Chotero, Mboni za Yehova zimachita mosapambanitsa. Chifukwa cha zimene Aroma 13:1-7 amanena, kuli koyenerera kuti iwo mwachikumbumtima amvere malamulo aboma amene amalamulira malo okhala. Kuwonjezera apa, chikondi chaumulungu cha pamnansi chimawasonkhezera kusonyeza ulemu zinthu za ena—za anthu onse kapena za aliyense payekha—mwakusaziwononga ndipo mwakusataya zinyalala paliponse. Koma iwo samalamulidwa mwachindunji kuti atsogolere m’zochitika zakuyeretsa zadziko. Iwo moyenerera amaika kulalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu pachiyambi, akumazindikira kuti iyi ndiyo njira yochitira zabwino zokhalitsa.
Kuyeretsa Kwauzimu
Aisrayeli akale anachenjezedwa mobwerezabwereza za zotulukapo ngati anaipitsa dziko lapansi mwa kukhetsa mwazi, mwakuloŵa m’njira yamoyo ya chisembwere, kapena mwakusasonyeza ulemu zinthu zopatulika. (Numeri 35:33; Yeremiya 3:1, 2; Malaki 1:7, 8) Kwakukulukulu, iwo anatsutsidwa chifukwa cha kuipitsa kumeneku kwauzimu, osati kuipitsa kulikonse kwakuthupi kumene angakhale analinso nako liwongo.b
Chifukwa chake, kuli kuipitsa kwauzimu kapena chidetso chimene Mkristu lerolino amayesayesa kwambiri kupeŵa. Iye amachita izi mwakuvala “umunthu watsopano,” umene umazula zikhoterero zakuipitsa mu mtima ndi m’maganizo. Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni anayi zikupindula ndi kuyeretsa kwauzimu kumeneku, zikumapeza pakati pawo chiyero chachipembedzo ndi chamakhalidwe, kuphatikizapo udongo wakuthupi wowonekera bwino lomwe.—Aefeso 4:22-24.
Tsopano iri nthaŵi yamkupiti wakuyeretsa kwauzimu. M’nthaŵi yokwanira mkupiti wakuyeretsa kwakuthupi wapadziko lonse lapansi udzatsatira ndipo udzapulumutsa malo athu okhala kuti asakhale dzala la dziko lonse mwakulipangitsa kukhala malo opanda zoipitsa amene limayenerera.—Mlaliki 3:1.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze lipoti lonse lonena za mpambo umenewu wamisonkhano Kummaŵa kwa Yuropu, wonani Galamukani! wa December 8 1991.
b Aisrayeli anali ozoloŵerana ndi m’chitidwe wakusungunula zitsulo. M’mabwinja mwapezeka ina yamigodi yawo yamkuwa, ndipo mkuwa unasungunulidwa kukonzera milimo ya pakachisi (Yerekezerani ndi 1 Mafumu 7:14-46.) Kukuwonekera kukhala kosatheka kuti mchitidwe wakusungunula zitsulo umenewo ungakhoze kukhala utachitidwa popanda kuchititsa mlingo waung’ono wakuipitsa mu mpangidwe wa utsi, zitoto, ndi nthale, mwinamwake limodzi ndi ziyambukiro zina zosafunika. Komabe, Yehova mwachiwonekere anali wofunitsitsa kulekerera kumlingo waung’ono kuipitsidwa kwa maloŵa akutali okhalidwa mwa patalipatali.