Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 3/15 tsamba 19-22
  • Chifukwa Chake Mkhalidwe Wamoyo wa Wodandaula Suli Wachimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Mkhalidwe Wamoyo wa Wodandaula Suli Wachimwemwe
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Madandaulo Enieni
  • Lingaliro la Mulungu pa Odandaula
  • Kugonjetsa Mzimu Wakudandaula
  • Kodi Kudandaula Konse Nkoipa?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Pewani Kudandaula
    Nsanja ya Olonda—2006
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupewa Mtima Wodandaula?
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Madalitso Kapena Matemberero—Zitsanzo kwa Ife Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 3/15 tsamba 19-22

Chifukwa Chake Mkhalidwe Wamoyo wa Wodandaula Suli Wachimwemwe

CHIKONDWERERO chinali chitasandulika kugwiritsidwa mwala m’masabata ochepekera chabe. Chisangalalo choyamba cha Aisrayeli chifukwa cha ufulu wawo wopezedwa chatsopano kuchokera ku ukapolo wa Igupto chinali chitasandulika kukhala kung’ung’udza kopanda pake pa chakudya. Mkati mwa mwezi wachiŵiri pambuyo pakutuluka mu Igupto, mtundu wosakhutirawo unanena kuti ukasankha mkhalidwe wa ukapolo kuposa moyo wovutikira wam’chipululu. M’miyezi imene inatsatira, mzimu wakudandaula umenewu unafooketsa chitsimikizo chawo chakumvera Yehova ndipo unawononga ziyembekezo za mtunduwo zakuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.​—Eksodo 16:1-3; Numeri 14:26-30.

Ndithudi, kudandaula sikunakhale pa mbadwo umodzi wokha kapena anthu amodzi okha. Kodi ndani amene panthaŵi zina samadandaula za ntchito, chakudya, mkhalidwe wakunja, ana, anansi, kapena kukwera kwa mitengo? Kukuwonekera ngati kupanda ungwiro kwaumunthu kumachititsa munthu kukhala ndi chikhoterero chakudandaula.​—Aroma 5:12; Yakobo 3:2.

Kodi nchifukwa ninji timafulumira choncho kudandaula? Mwinamwake timakhala okhwethemulidwa maganizo, ogwiritsidwa mwala, kapena odwala. Kudandaula kungakhale njira yothetsera kugwiritsidwa kwathu mwala, kapena kungakhale njira yosakhala yachindunji yakunenera kuti: “Ndikachita ntchitoyo bwinopo!” Nthaŵi zina madandaulo amasonkhezeredwa ndi kusiyana kwa maumunthu. Ndiyenonso, pamakhala zodandaulitsa zenizeni.

Chirichonse chimene chingakhale chifukwacho, monga momwe chitsanzo chotchulidwacho cha Aisrayeli chimasonyezera, kudandaula kungathe kukhala kowononga ngati kupitirizabe. Munthuyo angafikire kukhala wodandaula wosaleka, ngakhale kung’ung’udza ponena za njira za Yehova zochitira zinthu. Kodi nchifukwa ninji zimenezo ziri zaupandu kwambiri? Ndipo kodi ndimotani mmene madandaulo enieni angasamaliridwire moyenerera?

Madandaulo Enieni

Ngati dandaulo liri laling’ono, funso loyamba limene tiyenera kufunsa nlakuti, Kodi ndingalinyalanyaze m’chikondi? Ndithudi, tingakhale ndi chifukwa chabwino cha kudandaula motsutsana ndi munthu wina, mwinamwake ngakhale wokhulupirira mnzathu. Angakhale atatichitira mopanda chifundo kapena mopanda chilungamo. Komabe, kodi kudandaula kwa ena zakuchitiridwa mosalungama kudzawongolera zinthu? Kodi Baibulo limavomereza kuti tiyenera kuchitanji? Akolose 3:13, NW amati: “Pitirizanibe kupirirana ndi kukhululukirana mwaufulu ngati aliyense ali ndi chifukwa chodandaulira ndi wina. Monganso Yehova mwaufulu anakukhululukirani, teroni inunso.” Chotero ngakhale pamene dandaulo lingakhale lolungamitsidwa, Malemba amavomereza mkhalidwe wakukhululukirana mmalo mwa mzimu wakudandaula.​—Mateyu 18:21, 22.

Bwanji ngati nkhaniyo iri yaikulu koposa yosakhoza kunyalanyazidwa? Pangakhale chifukwa chabwino chakutulutsira dandaulo. Pamene “mfuu yodandaula” yoyenerera inamveka kwa Yehova yonena za Sodomu ndi Gomora, iye anachitapo kanthu kuthetsa mkhalidwe woluluza m’mizinda yachisembwere imeneyo. (Genesis 18:20, 21) Chifukwa china choyenerera chakudandaulira chinabuka mwamsanga pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E. Pamene chakudya chinali kugaŵiridwa kwa akazi amasiye osoŵa, tsankho linali kusonyezedwa moyanja akazi olankhula Chihebri. Pachifukwa chabwino, izi zinapangitsa dandaulo pakati pa akazi amasiye olankhula Chigiriki. Potsirizira pake, dandaulo linafika kwa atumwi, ndipo iwo mwamsanga analinganiza kagulu ka amuna osenza thayo kulungamitsa vutolo.​—Machitidwe 6:1-6.

Mofananamo, akulu Achikristu oikidwa lerolino sayenera kuzengereza kuchitapo kanthu pamene nkhani zazikulu ziperekedwa kwa iwo. Miyambo 21:13 imati: “Wotseka makutu ake polira waumphaŵi, nayenso adzalira, osamvedwa.” Mmalo mwakunyalanyaza dandaulo lenileni, akulu ayenera kumvetsera momvera chisoni. Kumbali ina, tonsefe tingathe kuchita mogwirizana mwakulunjikitsa madandaulo athu aakulu kwa akulu, mmalo mwakuwadandaulira kwa munthu aliyense amene adzamvetsera.

Komabe, unyinji wa ife ukavomereza mosaŵiringula kuti pali nthaŵi zina pamene kupanda ungwiro kwaumunthu kumatichititsa kudandaula mosafunikira. Kupenda kosamalitsa mkhalidwe wa Aisrayeli m’chipululu kudzatithandiza kuwona upandu wakulola kung’ung’udza kwa nthaŵi ndi nthaŵi kukula kufikira kukhala mzimu wodandaula.

Lingaliro la Mulungu pa Odandaula

Kung’ung’udza kwa Aisrayeli ponena za chakudya kumavumbula maupandu obadwa nawo aŵiri m’kudandaula. Choyamba, kudandaula kumayambukira ena. Cholembedwacho chimanena kuti ‘khamu lonse la ana Aisrayeli linadandaulira Mose ndi Aroni m’chipululu.’ (Eksodo 16:2) Mwachiwonekere, anali ochepekera amene anayamba kudandaula zakupereŵera kwa chakudya, ndipo pasanapite nthaŵi yaitali munthu aliyense anali kudandaula.

Chachiŵiri, kaŵirikaŵiri wodandaula amakulitsa vutolo ndi malovu. M’nkhaniyi, Aisrayeli anatsimikizira kuti mkhalidwe wawo ukakhala wabwinopo mu Igupto, kumene akanadya mkate wochuluka ndi nyama zambiri monga momwe anafunira. Iwo anadandaula kuti anatsogozedwa m’chipululu kokha kuti akafe ndi njala.​—Eksodo 16:3.

Kodi mkhalidwe wa Aisrayeli amenewa unalidi woipa motero? Mwinamwake zakudya zawo zinali kuchepachepa, koma Yehova anali atawoneratu vutolo, ndipo m’nthaŵi yokwanira anagaŵira mana kukhutiritsa zosoŵa zawo zakuthupi. Madandaulo awo okulitsidwa ndi malovu anasonyeza kusadalira kotheratu Mulungu. Pamene anali m’Igupto moyenerera anali atadandaula za mikhalidwe yankhalwe. (Eksodo 2:23) Koma pamene Yehova anawamasula kuukapolo, iwo anayamba kudandaula za chakudya. Kumeneko kunali kung’ung’udza kosalungamitsidwa. “Simuli kudandaulira ife koma Yehova,” anachenjeza motero Mose.​—Eksodo 16:8.

Mzimu wodandaula umenewu wa Aisrayeli unasonyezedwa mobwerezabwereza. Mkati mwa chaka chimodzi mana anafikira kukhala chifukwa chodandaulira. (Numeri 11:4-6) Mwamsanga pambuyo pake lipoti loipa lochokera kwa Aisrayeli 10 mwa 12 linachititsa mfuu yonena za maupandu onenedwawo ophatikizapo kugonjetsedwa kwa Dziko Lolonjezedwa. Anthu anafikira ngakhale pakunena kuti: ‘Mwenzi tikadafa m’dziko la Aigupto; kapena mwenzi tikadafa m’chipululu muno!’ (Numeri 14:2) Nkupanda chiyamikiro kwakukulu chotani nanga! Mposadabwitsa, kuti Yehova anati kwa Mose: “Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira?” (Numeri 14:11) Odandaula osayamikira amenewo anatsutsidwira kukupupulikapupulika m’chipululu kwa zaka 40 kufikira mbadwo umenewo unatha psiti.

Mtumwi Paulo akutikumbutsa za chitsanzo chimenechi. Iye akuchenjeza Akristu anzake kusafanana konse ndi Aisrayeli amenewo amene anakhala ong’ung’udza, nawonongekera onse m’chipululu. (1 Akorinto 10:10, 11) Mwachiwonekere, kung’ung’udza kosalungamitsidwa ndi mzimu wakudandaula zingathe kufooketsa chikhulupiriro chathu ndi kutsogolera ku mkwiyo wa Yehova.

Komabe, Yehova ngwoleza mtima ndi atumiki ake amene panthaŵi ina amadandaula chifukwa cha mikhalidwe yolefula. Pamene Eliya anathaŵira ku Phiri la Horebe chifukwa cha chizunzo chochitidwa ndi Yezebeli Mkazi wa Mfumu, iye anali wokhutira kuti ntchito yake monga mneneri inali itatha. Molakwa anayerekezera kuti anali wolambira yekha wa Yehova wotsala m’dzikolo. Kulimbikitsa chikhulupiriro cha Eliya, Mulungu anampatsa chitsanzo cha mphamvu Yake yaumulungu. Pamenepo mneneri anauzidwa kuti panali chikhalirebe atumiki okhulupirika a Yehova 7,000 mu Israyeli ndi kuti panali ntchito yambiri yakuti aichite. Chifukwa chake, Eliya anaiŵala madandaulo ake napita patsogolo ndi nyonga yatsopano. (1 Mafumu 19:4, 10-12, 15-18) Pamene akulu Achikristu asonyeza luntha, mofananamo iwo angalankhule motonthoza kwa okhulupirikawo, akumawathandiza kuwona mbali yawo m’kuchitidwa kwa chifuno cha Mulungu.​—1 Atesalonika 5:14.

Kugonjetsa Mzimu Wakudandaula

Kodi mzimu wakudandaula ungagonjetsedwe motani? Eya, awo amene apatsidwa umboni wachivulazo chimene fodya amachita m’thupi ali ndi chifukwa champhamvu chosonkhezera kusiya kusuta fodya. Mofananamo, kuzindikira chifukwa chake mzimu wodandaula uli wovulaza kwambiri kungatisonkhezere kusiya chizoloŵezi chirichonse cha kudandaula.

Kodi ndimapindu otani amene amakhalapo kwa ogonjetsa mzimu wodandaula? Phindu limodzi lofunika limene opeŵa kudandaula amakhala nalo nlakuti angawone nkhani mogwirizana ndi Malemba ndipo motsimikizira kwambiri. Sikaŵirikaŵiri kuti wodandaula aime kaye kuganiza mogwirizana ndi lingaliro la Yehova ponena za vutolo. Aisrayeli odandaula anaiŵala kuti Yehova Mulungu anawamasula kuukapolo ndikuti anawalekanitsira mozizwitsa madzi a Nyanja Yofiira. Kuganiza kwawo kosatsimikiza kunawachititsa kusawona mphamvu ya Mulungu ndipo kunalanda chisangalalo chawo. Chotulukapo chake, chinali chakuti chidaliro chawo mwa Yehova chinatha.

Ndiponso, munthu amene angathe kupenda mavuto ake motsimikizira amazindikira pamene zophophonya za iyemwini zakhala magwero a mavuto ake. Mwachiwonekere iye samapanganso cholakwa chofananacho. Yeremiya anachenjeza Aisrayeli anzake kusadandaula za mavuto amene iwo anali kutsagana nawo pambuyo pa chiwonongeko cha Yerusalemu. Kuvutika kwawo kunali chotulukapo chachindunji cha machimo a iwo eni, ndipo chimenecho chinali kanthu kena kamene iwo anafunikira kumvetsetsa kuti alape ndi kubwerera kwa Yehova. (Maliro 3:39, 40) Mofananamo, wophunzira Yuda anatsutsa “amuna osapembedza” amene anakana chitsogozo cha Yehova ndipo anali ‘odandaulira kosatha mkhalidwe wawo m’moyo.’​—Yuda 3, 4, 16.

Monga momwe Mfumu Solomo wanzeru nthaŵi zina ananenera, ‘mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.’ (Miyambo 17:22) Mzimu wodandaula umatifooketsa mwamaganizo ndipo umatilanda chimwemwe chathu. Umasonyeza kupanda chiyembekezo, osati kukhala ndi chiyembekezo. Koma awo amene amaphunzira kuganiza ndi kulankhula za ‘zinthu zotamandidwa’ ali ndi mtima wachisangalalo, umene ungawapangitsedi kumva bwino.​—Afilipi 4:8.

Mosakaikira, miyoyo yathu idzakhala yolemerera kwambiri ngati tiwona maubwino a anthu mmalo mwa zolephera zawo. Tidzakhala otsitsimulidwa ngati tichita zothekera kukondwera m’nthaŵi za mavuto kuposa kung’ung’udza za mikhalidwe yathu yakulephera. Ngakhale mayesero angathe kukhala magwero achisangalalo ngati tiwawona monga mpata wakulimbikitsa chikhulupiriro chathu ndi kuchirikiza chipiriro chathu.​—Yakobo 1:2, 3.

Kulinso kofunika kukumbukira kuti pamene ting’ung’udza, sitiri kudzivulaza ife chabe. Mwakudandaula mosalekeza, tingakhale tikufooketsa chikhulupiriro cha ena. Lipoti loipa la azondi khumi Achiisrayeli linachititsa mtundu wonse kuwona lingaliro lakugonjetsa Dziko Lolonjezedwa kukhala chochitika chosatheka. (Numeri 13:25–14:4) Panyengo ina, Mose analefulidwa kwambiri chifukwa chakung’ung’udza kosatha kwa anthuwo kotero kuti anapempha Yehova kuti amuphe. (Numeri 11:4, 13-15) Kumbali ina, ngati tilankhula nkhani m’njira yolimbikitsa, tingalimbikitse chikhulupiriro cha ena ndi kuthandizira chisangalalo chawo.​—Machitidwe 14:21, 22.

Ngakhale kuti tingayesedwe kudandaula motsutsana ndi antchito anzathu, mabwenzi athu, banja lathu, kapena ngakhale akulu ampingo, Yehova amafuna anthu ake ‘kukhala ndi chikondano chachikulu.’ Chikondi chotero chimatisonkhezera kukwirira zophophonya za ena mmalo mwakukulitsa zolakwa zawo. (1 Petro 4:8) Tiyamikira kuti, Yehova amakumbukira kuti tiri fumbi chabe ndipo samayang’ana mphulupulu zathu. (Salmo 103:13, 14; 130:3) Ngati tonsefe tinayesa kutsatira chitsanzo chake, mosakaikira tikadandaula mocheperapo kwambiri.

Pamene anthu abwezeretsedwa kuungwiro, palibe munthu amene adzakhala ndi chifukwa chodandaulira za mkhalidwe wake m’moyo. Kufikira pamene nthaŵiyo ifika, tifunikira kukaniza chiyeso chakudandaula za ena kapena za mikhalidwe yathu yopereka chiyeso. Kuti tisonyeze kuti timadalira Yehova ndi kukondadi okhulupirira anzathu, tiyeni tichite ‘zonse popanda madandaulo.’ (Afilipi 2:14) Izi zidzakondweretsa Yehova ndipo zidzatipindulitsa kwambiri. Pamenepa, chifukwa cha ubwino wathu ndi ubwino wa ena, tisaiwale kuti mkhalidwe wa moyo wa wodandaula ngwopanda chimwemwe.

[Chithunzi patsamba 20]

Ngakhale mana ochokera kwa Mulungu ogaŵiridwa mwakakonzedwe kozizwitsa anali chodandaulitsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena