Kupeza Chuma Chenicheni mu Hong Kong
HONG KONG ali malo kumene ndalama zochuluka zingapezedwe m’nthaŵi yaifupi—ngati zonse zofunika ziripo. M’zaka 40 kapena chapompo zapitazo, dziko lolamulidwa ndi Britain limenelo lachoka pakukhala doko lokhala ndi zochitika zochepa kufikira pakukhala dziko lolingaliridwa kukhala lamphamvu m’zachuma osati kokha ku Southeast Asia komanso pazochitika zamalonda zapadziko lonse.
Msonkho wake wotsika umakopa makampani akunja oikiza chuma ndi kupereka chisonkhezero kwa ogwira ntchito opezeka pakati pa nzika mamiliyoni asanu ndi imodzi za Hong Kong. Okondekanso, ndiwo malo ake onga khomo pakati pa chigawo chakummwera kwa China ndi chigawo cha Asia ndi Pacific ndi mbali zina. Pokhala ndi njira zamakono zoyendetsera katundu, zakukambitsirana, za kuwodetsa ndi kugulitsa malonda, Hong Kong ngwokonzekera kuloŵa mosavuta m’malonda apadziko lonse.
Chipambano cha chuma chapatsa Hong Kong umodzi wa miyezo ya umoyo wapamwamba kwambiri m’dziko. Komabe, kodi kulemera konse kwakuthupi kwadzetsa chikhutiro ndi chimwemwe chokhalitsa kunzika za Hong Kong? Ayi, koma ena afunafuna ndi kupeza chuma cha mtundu wabwino kwambiri.
Anapeza Chuma Chauzimu
Pakati pa awo amene apeza chuma chauzimu chosayerekezera chimenechi pali Alfred mbadwa ya ku Hong Kong. Iyeyu anali ndi ntchito yodzisankhira yachipambano monga mkulu wa mgwirizano wamabizinesi wapadziko lonse wokhala ndi malikulu ku Britain. Mofanana ndi anthu ena ambiri mu Hong Kong, chonulirapo chake m’moyo chinali cha kupeza ndalama zambiri, kukhala ndi nyumba ya iye mwini, kudya bwino, ndi kukhala ndi moyo wabwino. Pokhala ndi malo ake abwino antchito ndi ndalama, iye anawonekera kukhala atapeza zinthu zonsezo. Koma kodi anali wachimwemwe? “Ndinaphunzira mwa chokumana nacho kuti ndalama ziridi ndi malire ake odzetsera chimwemwe,” anadandaula motero Alfred. Iye anali kuvutika maganizo mosalekeza ponena zakuti ndalama zake zikakhala kwa utali wotani ntchito yake itatha. Pamene anawonjezera nthaŵi ya kugwira ntchito yake, m’banja munayamba kubuka mavuto. Mkazi wake, Emily, anapsinjika maganizo pamene mwana wawo wamwamuna anafa mwadzidzidzi. “Ndinafuna kudziŵa kumene iye anali kotero kuti ndichite kanthu kena komthandiza,” iye anatero. Popeza kuti sakanachita kanthu kalikonse, iye anakhala wotsenderezeka maganizo kwambiri.
Justina anaferedwa ndi atate wake ali wamng’ono kwambiri. Koma mwakulimbikira anamaliza maphunziro pa Yunivesite ya Hong Kong yotchuka. Zimenezi zinamtheketsa kupeza ntchito m’boma. M’Chicantonese kumeneku kumatchedwa kuti gum fan woon, mbale ya mpunga yagolidi—chisungiko cha ntchito ndi malipiro abwino. Komabe, Justina sanali wachimwemwe kapenanso wokhutiritsidwa. Kaŵirikaŵiri ankadabwa ndi chimene chili chifuno cha moyo ndi zimene zili mtsogolo. Mwamuna wake, Francis, nayenso analingalira kuti moyo unali wopanda chifuno. Anadziwona monga munthu wopanda pake, wosanunkha kanthu, wokhala mumkhalidwe wonyong’onyeka kosatha.
Ndiyeno pali Ricky, manijala wa bizinesi. Ngakhale kuti anali kupeza ndalama zambiri, anayamba kuwona mbali ina ya moyo—mpikisano wa wafawafa pakati pa ogwira nawo ntchito ndi mavuto muukwati. Ndalama sizinathe kumthandiza kuthetsa mavuto ameneŵa. Kwa mkazi wake, Wendy, ntchito yolemekezeka, ndalama zambiri, ndi kukhala ndi moyo m’chitaganya cha ndale zadziko chokhazikika kunatanthauza chisungiko. Koma kodi moyo wakewo wowoneka kukhala wachisungiko ukakhala nthaŵi yaitali motani? Zimenezo zinamuvutitsa maganizo chifukwa chakuti kutsimikizirika kwa imfa kunamchititsa kulingalira kuti moyo wake unali wopanda tanthauzo ndi wopanda chifuno.
David nayenso ali ndi nkhani yake. Maphunziro ake a ku yunivesite anampatsa ntchito yabwino ndi chisungiko cha chuma, koma sanapeze chikhutiro. Chifukwa ninji? Anali atadziloŵetsa kwambiri m’nthathi za chisinthiko ndi nzeru zakudziko, ndipo anakhulupirira kuti palibe moyo wina woposa umene tili nawo. David analingalira kuti panalibe choti ayembekezere mtsogolo, ndipo chuma chake chonse chakuthupi sichinamtetezere m’kulingalira kwake kukhala wosoŵa thandizo.
Ngakhale kuti anthu ameneŵa anali ndi chiyambi chosiyana, iwo anali ofanana pachinthu chimodzi. Onsewo anali atapeza chimene analingalira kuti chikawapatsa moyo wachimwemwe ndi chikhutiro. Komabe, pamene anafika pamlingo umene analingalira kuti ziyembekezo zawo zikakwaniritsidwa, miyoyo yawo inali yopanda kanthu.
Kukhala Wolemera kwa Mulungu
Mkhalidwe wa Alfred, Justina, ndi ena amene angotchulidwa kumenewo unali wofanana kwambiri ndi uja wa munthu wachuma m’fanizo la Yesu. Iyeyu ‘anadzikundikira chuma koma sanali wolemera kwa Mulungu.’ (Luka 12:21) Komabe, mwachimwemwe, iwo anapeza kanthu kena kabwino kwambiri—moyo wodzazidwa ndi chuma chenicheni. Awo amene amakhumba chimwemwe chowona ndi chikhutiro ayenera ‘kusayembekezera chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira kuti tikondwere nazo.’ (1 Timoteo 6:17) Inde, kudziŵa Mulungu wowona, Yehova, ndi kuika mwa iye chidaliro chawo kunachita mbali yaikulu m’moyo wa anthu ameneŵa. Tiyeni tiwone mmene zonsezi zinachitikira.
Alfred ndi Emily anakhwethemuka maganizo pamene mwana wawo wamwamuna anafa mwadzidzidzi, ndipo chuma chawo chonse sichinaziziritse kupwetekedwa mtima kwawo. Anamka kutchalitchi koma anamvabe kukhala opanda pake ndi osakhutira. Ndiyeno mmodzi wa Mboni za Yehova anafika pakhomo pawo ndi kufunsa kuti: “Kodi chiyembekezo cha munthu cha mtsogolo nchotani?” Alfred anayankha mogwirizana ndi zimene anali atauzidwa kutchalitchi ponena za kumwamba ndi helo. Komabe, anasonyezedwa m’Baibulo kuti “akufa sadziŵa kanthu bi” ndipo awo amene ali m’chikumbukiro cha Mulungu ali m’manda akumayembekezera chiukiriro. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 5:28, 29) Zimenezi zinamvekera kukhala zenizeni ndi zanzeru kwa Alfred. Tsopano anazindikira kuti mwana wakeyo sanali kuvutika kumalo ena koma kuti anali mtulo ta imfa, mwinamwake ndi chiyembekezo cha kudzagwirizananso ndi a banja lake pachiukiriro. Ndimpumulo wotonthoza chotani nanga umenewo! M’kupita kwa nthaŵi, Alfred ndi mkazi wake analandira phunziro la Baibulo la panyumba naloŵa panjira yogwirira zolimba pachuma chenicheni chimene Baibulo limapereka.
Justina anathedwa nzeru pamene analephera kupeza mzimu wothandiza ena pakati pa anzake ogwira nawo ntchito. Monga Mkatolika wodzipereka, iye analefulidwa pamene anawona kuti wansembe ankasuta ndi kumka kokavina, mongofanana ndi anthu ena. Ndiyeno anawonana ndi Mboni za Yehova nayamba kupeza mayankho okhutiritsa a Malemba pamafunso ambiri. Wansembeyo sanampatse kanthu kalikonse kusiyapo za m’mutu mwake, ndipo anali asanaŵerenge Baibulo m’zaka 16, ngakhale kuti anali kupita kutchalitchi nthaŵi zonse ndipo anali wantchito wamba kwa zaka 10.
Pamene Mbonizo zinali kuphunzira Baibulo ndi Justina ndi mwamuna wake, Francis, mwamunayo anakopeka ndi umodzi wawo wapadziko lonse m’chikhulupiriro ndi ntchito. Francis anafikira pakukhutiritsidwa maganizo kuti Mulungu ndiweniweni. Zinthu zonse zitalingaliridwa, ndi Mulungu wamoyo yekha ndi wowona amene angasonkhezere motero gulu lapadziko lonse la anthu. Okwatirana ameneŵa ngokondwa chotani nanga kuti apeza chuma chenicheni!
Ricky ndi Wendy anadziŵa kuti anafunikira kuchitapo kanthu kena pamene anawona kuti anali kumira mwapang’onopang’ono m’mavuto awo. Popeza kuti onse aŵiriwo anali kumakambitsirana ndi Mboni za Yehova kalelo, iwo, aliyense payekha, anayamba kuzifunafunanso. Mwakuyesayesa kwakhama, Ricky ndi Wendy anapeza osati zothetsera mavuto awo zopindulitsa zokha komanso chuma checheni muunansi wawo waumwini ndi “Mulungu wachimwemwe,” Yehova.—1 Timoteo 1:11, NW.
Moyo wa Davide nawonso unasintha pamene Mboni za Yehova zinamfikira. Iye anavomereza kuti zibwerenso komatu anali ndi cholinga cha kudzavumbula zolakwa zawo. Komabe, m’kupita kwanthaŵi, maso ake anatseguka, pakuti anayamba kuwona kuti Baibulo nlolondola ponena za sayansi, za mbiri yakale, ndi m’njira zina zambiri. Zonsezi zinathandiza Davide kuwona Baibulo kukhala buku la chowonadi limene linampatsa chifuno chenicheni m’moyo. Kunali kusintha kokondweretsa ndi kokhutiritsa chotani nanga kwa iye!
Kuthandiza Ena Ambiri Kupeza Chuma Chenicheni
Mwa anthu ochuluka mu Hong Kong, Alfred, Emily, Justina, Francis, ndi ena otchulidwa muno angokhala chabe anthu oŵerengeka a awo amene apeza chuma chenicheni cha chowonadi cha Baibulo ndi kukhulupirira Yehova Mulungu. Mu 1992 Mboni za Yehova 2,600 zinathera chiwonkhetso cha maola pafupifupi 900,000 zikumafikira anthu mu Hong Kong ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba oposa 3,800. Komabe, moyo mu Hong Kong ngwofulumira, ndipo anthu ngotanganitsidwa. Chifukwa chake, kuwonjezera pakufikira anthu kunyumba ndi nyumba, olengeza Ufumu akupeza chipambano m’kuchitira umboni wa m’khwalala. Amakambitsirananso ndi anthu kumalo awo antchito mwa kufikira anthu ogwira ntchito muofesi, ogulitsa m’sitolo, alimi, ndi anthu ochokera kuulendo wokasodza ku South China Sea.
Kunganenedwedi kuti “zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka” mu Hong Kong. (Mateyu 9:37) Pakali pano, chiŵerengero cha Mboni za Yehova kwa anthu m’dzikolo chili pa 1 kwa 2,300. Pozindikira kufulumira kwa ntchito yotuta, pafupifupi 600 mwa ofalitsa Ufumu 2,600 ndiwo apainiya kumeneko, kapena ofalitsa anthaŵi yonse a mbiri yabwino. Mboni za Yehova mu Hong Kong, mofanana ndi ena kwina kulikonse, zimazindikira kuti “madalitso a Yehova alemeretsa.” (Miyambo 10:22) Chifukwa chake, izo zimagwira ntchito zolimba kuti zithandize anthu ena ambiri m’chitaganya chotukukacho kupeza chuma checheni.
[Mapu patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
SOUTH CHINA SEA
CHINA
Hong Kong
Makilomita
Mamailosi
15
15