Yehova Asanduliza Nthaŵi ndi Nyengo mu Romania
KUSINTHA kwakukulu kunachitika Kum’maŵa kwa Ulaya mu 1989. M’miyezi yoŵerengeka yokha, maboma amene anali ngati malinga osakhoza kugonjetsedwa anagwetsedwa limodzi motsatizana ndi linzake. Kusintha kwazandaleko kunadza ndi kusintha kwa kakhalidwe ka anthu, chuma, ndipo, chosangalatsa kwambiri kwa Mboni za Yehova, kusintha kwachipembedzo. M’dziko limodzi pambuyo pa linzake, Mboni za Yehova zinazindikiridwa mwalamulo, ndipo zinabwezeredwa ufulu wakuchita ntchito yawo yachipembedzo.
Koma zinthu zinawoneka kuti zikakhala zosiyana mu Romania. Boma linali ndi mphamvu yaikulu pa anthu kotero kuti kunawonekera monga ngati kuti kusinthako kungakhale ndi chiyambukiro chochepa. Pamene Mboni za Yehova kumeneko zinamva zimene zinali kuchitika m’maiko ena a Kum’maŵa kwa Ulaya, izo zinadzifunsa kuti, ‘Kodi tidzakhala okhoza konse kulambira mwaufulu Armagedo isanafike?’ Mitima yawo inalakalaka nthaŵi imene adzasonkhana pamisonkhano Yachikristu ndi abale ndi alongo awo auzimu, kulalikira mbiri yabwino poyera, ndi kuphunzira mabuku awo ofotokoza Baibulo poyera, popanda kuwabisa nthaŵi zonse. Zonse zinawoneka ngati loto.
Ndiyeno lotolo linachitikadi! Zinachitika mu December 1989. Modabwitsa aliyense, ulamuliro wa Ceauşescu unagwetsedwa mwadzidzidzi. Mwadzidzidzi, Akristu amenewo anapeza mpumulo. Pa April 9, 1990, Mboni za Yehova zinavomerezedwa mwalamulo monga gulu lachipembedzo m’Romania. Yehova anali atasanduliza nthaŵi ndi nyengo kwa Mboni 17,000 zokangalika za kumeneko.—Yerekezerani ndi Danieli 2:21.
Mbiri Yaitali
Mu 1911, Carol Szabo ndi Josif Kiss anabwerera ku Romania kuchokera ku United States, kumene anaphunzira chowonadi cha Baibulo ndipo anapatulira miyoyo yawo kwa Yehova kuchita chifuniro chake. Iwo anafuna kufotokozera mbiri yabwino anthu a m’dziko lawo. Atafika ku Romania, iwo anayamba kulalikira nthaŵi yomweyo. Pamene Nkhondo Yadziko I inaulika, iwo anagwidwa chifukwa cha zimene anali kuchita. Komabe, mbewu za Ufumu zimene anali atafesa zinayamba kubala. Pofika 1920, pamene ntchitoyo inalinganizidwanso, panali pafupifupi ofalitsa Ufumu 1,800 m’Romania.
Panthaŵiyo mzimu wakugalukira boma umene unayambika ku Balkans unayamba kufika kwambiri m’Romania, ndipo munali ziwawa zambiri. Mosasamala kanthu za nthaŵi zovutazo, abale athu auzimu anapitiriza ntchitoyo. Mu 1924 Watch Tower Society inatsegula ofesi pa 26 Regina Maria Street ku ClujNapoca kuti isamalire ntchito m’Romania, Hungary, Bulgaria, Yugoslavia, ndi Albania.
Komabe, mkhalidwe wandale unaipa kwambiri ndipo kuwonjezera pamavuto ochokera kwa olamulira, munali mavuto mkati mwa gululo. Lipoti la mu 1930 Year Book limati: “Chifukwa cha kusakhulupirika kwa munthu amene Sosaite inatumiza kumeneko, mabwenziwo abalalitsidwa ndipo chidaliro chawo chagwedezeka kwakukulu. Sosaite yakhala ikufunafuna mpata wa kuyambitsanso ntchito m’dziko limenelo, koma olamulira akumeneko akuletsa zinthu zonse, ndipo tiyenera kudikira kufikira Ambuye atatsegula njira yabwino koposa.” Ndiyeno, mu 1930, Martin Magyarosi, Mboni ya ku Romania imene inabatizidwa mu 1922, anaikidwa kukhala mtumiki wanthambi watsopano, ndipo pambuyo pake ofesi inasamutsidwira ku 33 Crişana Street, Bucharest. Pambuyo pa kumenyera nkhondo kwa nthaŵi yaitali, pomalizira pake Sosaite inalembetsedwa monga gulu lalamulo m’Romania mu 1933.
Mavuto Apitirizabe
Ziyeso zazikulu zinapitirizabe kufika pa Mboni m’Romania. Lipoti la mu 1936 Year Book limati: “Mosakayikira palibe mbali ina ya dziko lapansi kumene abale amagwira ntchito ndi mavuto aakulu kuposa ku Rumania.” Mosasamala kanthu za nsautso zonsezo, malipoti autumiki a 1937 anasonyeza mipingo 75 yokhala ndi ofalitsa 856 m’Romania. Pa Chikumbutso, panafika okwanira 2,608.
Pamene Nkhondo Yadziko II inayamba, Romania anayambukiridwa. Mu September 1940, Kazembe Ion Antonescu analanda ulamuliro waboma nayamba kulamulira mofanana ndi Hitler. Nkhanza zinali zofala. Mazana ambiri a abale athu anagwidwa, kumenyedwa, ndi kuzunzidwa. Mbale Magyarosi anagwidwa mu September 1942, koma anali wokhozabe kugwirizanitsa ntchito ya Transylvania ali m’ndendemo.
Chizunzo chinapitirizabe pamene magulu ankhondo a Hitler analoŵa m’dzikomo mu 1944. Lipoti lochokera ku Bucharest linafotokoza mikhalidweyo muulamuliro wa Nazi kuti: “Mboni za Yehova m’dziko lino zinazunzidwa kowopsa. Zinaikidwa m’ndende ndi ochilikiza Chikomyunizimu, kunenezedwa mlandu ndi atsogoleri achipembedzo ochilikiza Hitler kukhala zoipa kwambiri kuposa ochilikiza Chikomyunizimu, ambiri a ife tinaweruzidwa kukhala m’ndende zaka 25, kapena kwa moyo wonse, kapena kuphedwa.”
Pomalizira pake nkhondoyo inatha, ndipo pa June 1, 1945, ofesi ya Sosaite ku Bucharest inapitiriza kugwira ntchito. Mosasamala kanthu kuti kunali kovuta kupeza mapepala, antchito odzipereka anasindikiza timabuku toposa 860,000 ndi makope a Nsanja ya Olonda oposa 85,000 m’Chiromania ndi Chihungary. Yehova anadalitsa kugwira ntchito kwawo zolimbako. Pofika 1946, achatsopano okwanira 1,630 anabatizidwa. Chochitika chapadera cha chaka chimenecho chinali msonkhano wamitundu umene unachitidwira ku Bucharest pa September 28 ndi 29. Atsogoleri achipembedzo anayesayesa mwamphamvu kudodometsa ndi kuletsa msonkhanowo, koma analephera, ndipo pafupifupi anthu 15,000 anafika pankhani yapoyera. Inali nthaŵi yoyamba imene abale a m’Romania anali okhoza kuchita msonkhano woterowo.
Sosaite inatumiza Mbale Alfred Rütimann wochokera ku nthambi ya Switzerland kupita ku Romania. Mu August 1947 iye anali wokhoza kulankhula ndi abale oposa 4,500 m’malo 16, kuwalimbikitsa kaamba ka zimene zinali kutsogolo. Posakhalitsa zitsenderezo zinafikanso pa Mbonizo, panthaŵiyi kuchokera kwa olamulira Achikomyunizimu. Mu February 1948 olamulirawo analetsa ntchito yathu yakusindikiza ndi kulalikira. Ndiyeno, mu August 1949, ofesi ya ku 38 Alion Street inafunkhidwa. Pambuyo pake abale ambiri, kuphatikizapo Mbale Magyarosi, anagwidwa. Panthaŵiyi, akumanenezedwa kukhala ochilikiza boma la atsamunda, ndipo anatumizidwa kundende kapena misasa yachibalo. Kwa zaka 40 zotsatirapo, ntchitoyo inali yoletsedwa, ndipo Mbonizo zinavutika kwambiri. Mavuto oyambitsidwa ndi adani mkati mwa gulu anawonjezera nsautsoyo. Pomalizira pake, ulamuliro wa Ceauşescu unagwetsedwa mu 1989, ndipo zinamasuka! Kodi tsopano izo zikachita chiyani ndi ufulu wawo?
Kulalikira Poyera Kachiŵirinso
Mboni sizinataye nthaŵi iliyonse. Izo zinayamba nthaŵi yomweyo kulalikira kunyumba ndi nyumba. Komatu zimenezi sizinali zokhweka kwa awo amene kwa zaka zambiri anachita ntchitoyi molimba mtima koma mobisa mwakulalikira mwamwaŵi. Iwo tsopano akuchita kuwopa ngati angakhoze kulalikira poyera. Ambiri a iwo anali asanachitepo zimenezi ndi kale lonse, ndipo nthaŵi yomaliza imene ena a iwo analalikira kunyumba ndi nyumba inali kumapeto kwa ma 1940. Kodi iwo akulandira zotulukapo zotani? Tiyeni tiwone.
Malo abwino oyambirako ndiwo malikuluwo, Bucharest, umene uli ndi nzika 2.5 miliyoni. Zaka ziŵiri zapitazo, mumzindawu munali mipingo inayi yokha. Tsopano muli mipingo khumi, ndipo oposa 2,100 anafika pa phwando la Chikumbutso la mu 1992. Popeza kuti maphunziro a Baibulo apanyumba opita patsogolo akuchititsidwa, mwinamwake mipingo ina yatsopano ingapangidwe posachedwapa.
Mzinda wa Craiova wokhala ndi nzika 300,000, uli kum’mwera koma chakumadzulo kwa dzikolo. Kufikira 1990, kunali Mboni 80 zokha m’mzinda wonsewo. Ndiyeno mzimu wa upainiya unayambika, ndipo ntchito inapita patsogolo. Mu 1992 mokha, anthu 74 anabatizidwa, ndipo maphunziro a Baibulo oposa 150 akuchititsidwa. Pokhala ndi ofalitsa oposa 200, iwo akufunafuna mwakhama malo oyenera omangapo Nyumba Yaufumu.
Ku Tirgu-Mures, Mboni yaikazi ndi abale aŵiri anapita kwa wansembe wa tchalitchi cha Orthodox kukafafanizitsa maina awo pandandanda ya tchalitchi. Atadziŵa chifuno cha ulendo wawo, wansembeyo anawaitana kuloŵa m’nyumba, ndipo anakhala ndi makambitsirano abwino. Ndiyeno wansembeyo anati: “Ndikukuchitirani nsanje koma osati nsanje yoipa. Tiyenera kuchita ntchito imene mukuchita. Nzomvetsa chisoni kuti Tchalitchi cha Orthodox changokhala tchalitchi chachikulu koma chaulesi”! Iye analandira brosha lakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? ndi kope la Nsanja ya Olonda. Mlongoyo ngwachimwemwe kuti salinso chiŵalo cha “tchalitchi chachikulu koma chaulesi.”—Chivumbulutso 18:4.
Nkwachiwonekere kuti ambiri amene akuphunzira chowonadi lerolino ndianthu achichepere. Chifukwa? Mwachiwonekere iwo anayembekezera zochuluka pamene boma linasintha, koma anagwiritsidwa mwala. Iwo ngachimwemwe kuphunzira kuti Ufumu wa Yehova wokha ndiwo ungabweretse yankho lokhalitsa la mavuto athu.—Salmo 146:3-5.
Zinthu Zazikulu Zikuchitika m’Malo Aang’ono
Ocoliş ndimudzi waung’ono kumpoto kwa Romania. Mu 1920 munthu wina wotchedwa Pintea Moise anabwerera kuchoka kugulu lankhondo la Russia, kumene anatengedwa monga msilikali wandende. Panthaŵi ina iye anali Mkatolika, koma asanabwerere anakhala wa Baptist. Milungu itatu pambuyo pake, Ophunzira Baibulo, monga momwe Mboni za Yehova zinkadziŵikira panthaŵiyo, anamfikira. Pambuyo pa ulendo umenewo, iye ananena kuti: “Tsopano ndapeza chowonadi cha Mulungu!” Pofika mu 1924 kunali gulu la anthu 35 ku Ocoliş.
Lerolino, pakati pa anthu okwanira 473 akumaloko, pali ofalitsa Ufumu 170. Wofalitsa aliyense anagaŵiridwa nyumba ziŵiri monga gawo lake, ndipo amapitanso kumidzi yapafupi. Komabe, iwo ali ndi chiyembekezo. Iwo angomanga kumene Nyumba Yaufumu yokongola yokhalamo anthu 400. Ntchito yonse inachitidwa ndi Mboni zakumaloko.
Mbale Szabo ndi Kiss anakhala ku Valea Largă mu 1914. Mu 1991, pakati pa nzika 3,700 zakumeneko, panali mipingo isanu ndi itatu ndi ofalitsa Ufumu 582. Pa Chikumbutso cha mu 1992, panafika 1,082—pafupifupi munthu 1 mwa anthu 3 a m’chigwa chimenechi.
Apainiya Apadera Alambula Njira
Apainiya apadera amachita mbali yaikulu m’kufikitsa mbiri yabwino kwa anthu okhala kumadera akutali. Mwamsanga pamene ufulu wa kulalikira unaperekedwa, Ionel Alban anayamba kugwira ntchito m’mizinda iŵiri, akumathera masiku aŵiri mlungu uliwonse ku Orşova ndi masiku asanu ku Turnu-Severin.
Pamene Ionel anafika ku Orşova nkuti kulibe Mboni. Mlungu woyamba, anayambitsa phunziro la Baibulo ndi mnyamata wazaka 14 zakubadwa. Mnyamatayo anapanga kusintha kwakukulu m’miyezi iŵiri kotero kuti bwenzi lake ndi mnansi anayambanso kuphunzira. Mnansiyo, Roland, yemwe anali Mkatolika, anapanga kupita patsogolo kodabwitsa. Pambuyo pa mwezi umodzi wokha ndi theka, iye anatsagana ndi Ionel m’ntchito yolalikira, ndipo anabatizidwa patapita miyezi isanu. Anayamba utumiki wanthaŵi yonse panthaŵi yomweyo. Amake anayambanso kuphunzira ndipo anabatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wa 1992 wa “Onyamula Kuunika.” Tsopano ku Orşova kuli ofalitsa khumi, ndipo akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 30.
Munthu woyamba kulandira chowonadi ku Turnu-Severin anali munthu wolandira alendo kuhotela kumene Ionel anakhala. Pambuyo pa miyezi iŵiri mwamunayo anakhala wofalitsa wosabatizidwa, ndipo anabatizidwa patapita miyezi itatu. Tsopano iye ali mmodzi wa ofalitsa 32 kumeneko amene onse pamodzi akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 84.
Mpainiya wina wapadera, Gabriela Geica, anatumikira monga mpainiya wokhazikika ngakhale pamene ntchito yathu inali yoletsedwa. Chikhumbo chake chinali chakugwira ntchito kumene kusoŵa kunali kokulira. Anagaŵiridwa gawo lalikulu kwambiri. Nthaŵi zina anayenda makilomita 100 mpaka 160 kukafikira anthu okondwerera. Mzinda wina umene anagwirako ntchito unali wa Motru, kumene kunali Mboni zinayi zokha. Iye akusimba kuti: “Chifukwa cha kuwonjezeka kwa ntchito ku Motru, ansembe ndi magulu ena achipembedzo anayamba kutitsutsa. Iwo anasonkhezera meya ndi apolisi kuika chitsenderezo pamabanja amene anandipatsa malo ogona. Anandithamangitsa chotero pafupifupi mwezi uliwonse, ndinayenera kufuna malo okhala.”
Gabriela anayambitsa phunziro ndi munthu wosakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu wa ku Orşova, amene ananena kuti sanali wokondweretsedwa ndi chipembedzo kapena Baibulo. Koma pambuyo pophunzira miyezi inayi yokha, mkaziyo anayamba kuchilikiza Baibulo. Ngakhale kuti mwamuna wake anamkaniza kuloŵa m’nyumba usiku ndi kumuwopseza kuti adzamsudzula kapena kumupha, iye anasungabe umphumphu wake. Ngakhale pamene anali asanabatizidwe, iye anali kuchititsa maphunziro a Baibulo khumi.
Ziyembekezo Zabwino Koposa Zamtsogolo
Mu August 1992, Romania anafikira chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 24,752 m’mipingo 286. Ofika pa Chikumbutso anali oposa 66,000. Paofesi yanthambi yaing’ono ya ku Bucharest, pali antchito 17 amene akuchita zimene angathe kusamalira zosoŵa zauzimu za abale awo. Iwo akuyembekezera kuyamba kumanga nthambi yaikulu posachedwapa.
Mboni za Yehova m’Romania sizingathe kuleka kudabwa ndi kusintha konse kwakukulu kumene kwachitika m’zaka zoŵerengeka zapitazo. Izo zikuyamikira Yehova Mulungu kuti zili mbali ya mpingo wapadziko lonse umene uli ndi dzina lake ndipo ukutsogoza anthu kuchidziŵitso cholongosoka chonena za iye ndi chifuno chake chosasintha. Pambuyo pa zaka zambiri za mavuto ndi chizunzo, izo nzoyamikira chotani nanga kwa Yehova kuti iye wasandulizadi nthaŵi ndi nyengo mu Romania!
[Mapu patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
HUNGARY
ROMANIA
Bucharest
Cluj-Napoca
Craiova
Tirgu-Mures
Orşova
Turnu -Severin
Motru
Turda
BULGARIA
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
1. Pafupifupi Mboni 700 zinasonkhana m’nkhalango mu 1947
2. Handibilu ya nkhani yapoyera mu 1946
3. Msonkhano waposachedwapa ku Romania
4. Kulalikira ku Cluj-Napoca lerolino
5. Nyumba Yaufumu pafupi ndi Turda
6. Banja la Beteli m’Bucharest