Kodi Nkuti Kumene Mungapeze Chitsogozo Chodalirika?
“INU YEHOVA, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.”—Yeremiya 10:23, 24.
Wolemba Baibulo Yeremiya analemba mawu amenewo pafupifupi zaka mazana 25 zapitazo. Mkhalidwe woipa wa mtundu wa anthu pambuyo pa zaka zikwi zambiri za kugwiritsira ntchito chitsogozo chaumunthu wasonyezadi kuwona kosakanika kwa mawu ameneŵa. Koma inu mungafunse kuti, ‘Kodi nkuti kumene chitsogozo chodalirika chingapezeke?’
Lemba logwidwa mawu pamwambapolo limasonya kumagwero a chitsogozo ndi njira yodalirika zimene zili zapamwamba kwambiri koposa za munthu—Mlengi wa munthu, Yehova Mulungu. Ndithudi palibe amene amadziŵa bwino kwambiri mpangidwe wa munthu ndi zosoŵa zake kuposa Mlengi wathu. Komabe, kodi Mulungu ngwokondweretsedwa m’kutipatsa chitsogozo ndi njira yotero? Kodi amachita zimenezo motani? Kodi izo nzopindulitsa m’nthaŵi yathu?
Opangidwa ndi Nzeru ya Kulandira Chitsogozo Chaumulungu
Nkwachidziwikire kuti kusiyana kwakukulu kolekanitsa munthu ndi nyama kuli pa maumbidwe, kukhoza, ndi kagwiridwe ka ntchito ka ubongo wa munthu. Munyama pafupifupi kagwiridwe ka ntchito konse ka ubongo nkolinganizidwiratu m’chimene chafikira kutchedwa nzeru yolinganizidwiratu. Zimenezi nzosiyana ndi anthu.—Miyambo 30:24-28.
Mosiyana ndi ubongo wa nyama, mbali yaikulu ya nzeru za ubongo wa munthu ili yosalinganizidwiratu. Mulungu anapatsa anthu nzeru ya kudzisankhira, kuwakhozetsa kupanga zosankha zanzeru ndi kusonyeza mikhalidwe yapamwamba, yonga chikondi, kuwoloŵa manja, kusadzikonda, chilungamo, ndi luntha.
Kodi nkwanzeru kuganiza kuti Mulungu akalenga munthu ndi nzeru ya maganizo yotero popanda kupereka mtundu wina wa chitsogozo wonena za mmene ingagwiritsiridwire ntchito bwino lomwe? Mulungu anapereka chitsogozo chachindunji kwa anthu oyamba. (Genesis 2:15-17, 19; 3:8, 9) Ngakhale pamene munthu anagwera muuchimo, Yehova anapitirizabe kutsogolera amuna ndi akazi okhulupirika, kwakukulukulu kupyolera m’Mawu ake ouziridwa, Baibulo. (Salmo 119:105) Zimenezi zaloleza anthu kulimbana ndi mavuto a moyo watsiku ndi tsiku mwachipambano pamene akugwiritsira ntchito kudzisankhira kwawo mwanzeru.
Kulembedwa Mwaumulungu kwa Baibulo
Kodi nchiyani chimene chimapangitsa Baibulo kukhala magwero odalirika a chitsogozo? Choyamba, limapereka chidziŵitso chimene ndi Mlengi yekha akanapereka. Limasimba mwatsatanetsatane mbiri ya zochitika zimene zinachitika kalekale munthu asanakhaleko. Mwachitsanzo, limasimba mbiri ya mmene dziko lapansi linakonzedwera m’masitepe olondolana kufikira pamene linakhala loyenera kuchirikiza moyo wa munthu. (Genesis, machaputala 1, 2) Ngakhale kuti zimenezi zinalembedwa m’Baibulo zaka zoposa 3,000 zapitazo, zili zogwirizana ndi zikhulupiriro za sayansi ya makono.
Kalekalelo anthu asanavomereze kuti dziko lapansi nlobulungika, Baibulo linalengeza kuti “[Mulungu] ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.” (Yobu 26:7) Ndiponso, Baibulo limavumbula kuti “ndiye Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala.” (Yesaya 40:22) Ndi Mulungu yekha, Mlengi, amene angapereke umboni umenewu.
Kukhoza kwa kuoneratu zamtsogolo sikuli mphatso imene yapatsidwa kwa munthu. Mmalo mwake, Mlengi amaneneratu zamtsogolo kupyolera m’Baibulo. Mulungu anauzira mneneri Yesaya kulemba za Iye kuti: “Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe.”—Yesaya 46:9, 10.
Baibulo lasonyeza kuti likhoza kuneneratu za chimaliziro kuyambira pachiyambi ndi kulunjika kodabwitsa. Mwachitsanzo, linaneneratu za kubuka, kugwa, ndi mikhalidwe ya maulamuliro aakulu adziko mkati mwa zaka mazana ambiri a mbiri ya munthu. Maulosi apadera ameneŵa analembedwa zaka mazana ambiri kukwaniritsidwa kwawo kusanachitike, m’zochitika zina zaka zikwi zambiri pasadakhale. Motero Baibulo limaneneratu molondola za zochitika zamakono, ndiponso zotulukapo zake zotsiriza. Baibulo lilinso lapadera chifukwa chakuti limasonyeza njira ya chipulumutso m’nthaŵi ya chiwonongeko cha maboma opanda ungwiro a anthu pa Armagedo, “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” Ufumu wa Mulungu m’manja mwa Mwana wake, Yesu Kristu, udzakwaniritsa chochita chachikulu chimenecho.—Chivumbulutso 16:14, 16; 17:9-18; Danieli machaputala 2, 8.
Lopindulitsa Nthaŵi Zonse—Losavulaza
Nzeru wamba yaumunthu njopanda ungwiro; chifukwa chake, uphungu waumunthu suli wopindulitsa nthaŵi zonse, ngakhale ngati ungaperekedwe ndi cholinga chabwino. Zimenezi nzosiyana ndi uphungu wa Baibulo. Mulungu mwiniyo amati: “Ine ndine Yehova, . . . amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:17, 18.
Chithandizo chaumulungu chimatithandiza kuika zinthu zoyambirira poyamba ndi kumamatira kumakhalidwe apamwamba m’moyo. Pamene kuli kwakuti chitaganya chamakono chimagogomezera pa zipambano ndi zonulirapo zakuthupi, Baibulo limagogomezera za mmene kulili kwaphindu kwa ife “[kupenyerera, osati pa, NW] zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthaŵi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.” (2 Akorinto 4:18) Mwanjira imeneyi timalimbikitsidwa kukhala ndi zonulirapo zabwino kwambiri m’moyo, ndiko kuti, zonulirapo zauzimu mogwirizana ndi kuchita chifuniro cha Mulungu, chonulirapo chotsiriza chikumakhala chija cha moyo wosatha m’dongosolo latsopano labwino.
Pamene Mkristu amenya nkhondo mwamphamvu kulondola zonulirapo zapamwamba zimenezi, uphungu wa Baibulo umamthandiza kukhala ndi moyo wabwino kopambana monga momwe angathere m’dongosolo lino loipa la zinthu. Nzeru yaumunthu ya makono imakonda kulimbikitsa lingaliro la kugwira ntchito pang’ono ndi kulandira malipiro ambiri. Kumbali inayo, Baibulo limatiuza kuti “wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa.” Mtumwi Paulo analembera Akristu Achihebri kuti: “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse.”—Miyambo 10:4; Ahebri 13:18.
Baibulo limaperekanso uphungu wopindulitsa pakakonzedwe kabanja. Limafotokoza mwapadera malo a mwamuna ndi mkazi yemwe m’kakonzedwe kaukwati, ndiponso limafotokoza njira yoyenera yolelera ndi kuphunzitsira ana. Ilo limati: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. . . . Ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziwopa mwamuna. Ananu, mverani akukubalani, . . . atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Kutsatira uphungu wapamwamba wa Mlengi kumachirikiza kwambiri bata ndi chimwemwe za mabanja.—Aefeso 5:21–6:4.
Mtsogolo Mosungika kwa Awo Amene Amatsatira Chitsogozo cha Mulungu
Mawu a Mulungu olembedwa amasonyeza chothetsera mavuto onse a mtundu wa anthu chimene Mulungu ali nacho. Posachedwapa Yehova Mulungu adzachotsa dongosolo la zinthu lilipoli, limodzi ndi mavuto ake onse, chisalungamo ndi kuvutika, ndipo mmalo mwake adzaloŵetsamo dongosolo lake lolungama latsopano. Baibulo limafotokoza zimenezi pa 2 Petro 3:7-10, likumawonjeza pa vesi 13 kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” Zimenezi zimapanga mbiri yabwino kopambana iliyonse imene ingaperekedwe kumtundu wa anthu. Ndiwo uthenga weniweniwo umene Baibulo limapereka ndi umene Mboni za Yehova zimalalikira m’maiko oposa 200 ndi zisumbu za m’nyanja.
Pamene chifuniro cha Mulungu chidzakhala chikuchitidwa padziko lonse lapansi, banja lonse laumunthu lidzapindula mwa kutsatira chitsogozo chabwino kwambiri cha Mlengi wawo, Yehova. Sipadzakhalanso mavuto a umphaŵi, upandu, ndi a mankhwala. Mtundu wa anthu sudzavutikanso ndi matenda, ukalamba, ndi imfa. Banja laumunthu lidzatukulidwira kuungwiro umene makolo athu oyamba anali nawo asanapandukire chitsogozo cha Mulungu.
Mmene limafotokozera bwino mwachidule nanga buku la Baibulo lotsiriza ponena za mikhalidwe yosangalatsa ya awo amene amaika chidaliro chawo m’chitsogozo chaumulungu! Pa Chivumbulutso 21:4, 5 pamati: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Mlengi wathu anatsimikizira zimenezi, akumati: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” Ndipo akuwonjezera kuti: “Mawu awa ali okhulupirika ndi owona.”
Ngati titi tilandire madalitso ameneŵa, kodi Mulungu akuyembekezeranji kwa ife? Mtumwi Paulo akufotokoza kuti chifuniro cha Mulungu nchakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira chowonadi.” (1 Timoteo 2:4) Mboni za Yehova zikukupemphani mwachikondi kudzapeza chidziŵitso cholongosoka chimenecho cha chowonadi kupyolera m’phunziro losamalitsa la Baibulo. Mwa kuphunzira mosamalitsa za chifuniro cha Mulungu, nanunso mungazindikire kupyolera m’chokumana nacho kuti nzeru yaumulungu njodalirika kwambiri m’nthaŵi zino zowopsa. Kufulumira kwa nthaŵi kumapangitsa zimenezi kukhala zofunika kwambiri kuzitsatira koposa ndi kale lonse!