Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 4/15 tsamba 19-21
  • Kodi Nkubadi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkubadi?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndalamazo Nzayani?
  • Kukongola Kapena Kuba?
  • Kudalira Mulungu
  • Mtumwi Amene Anafikira Kukhala Mbala
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Usakhale Wakuba!
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?
    Galamukani!—2015
  • Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 4/15 tsamba 19-21

Kodi Nkubadi?

ABIODUN anali woperekera chakudya wamkulu mu hotelo ina yaikulu mu Nigeria. Pamene anali kutseka chipinda china chodyera usiku wina, anapeza thumba la ndalama zokwanira $1,827 za ku United States. Mofulumira iye anakapereka ndalamazo, zimene pambuyo pake zinafunsidwa ndi mwiniwake, mlendo wina wa m’hoteloyo. Akuluakulu a hotelo anafupa Abiodun mwa kumkweza pantchito kukhala woyang’anira ndi kumpatsa mphotho ya “wantchito wabwino kopambana wa pachaka.” Nayenso mwini ndalamayo anamufupa.

Maganizi amomwemo otchedwa Quality, anasimba nkhaniyo, akumatcha Abiodun “Msamariya Wachifundo.” Pamene anafunsidwa ndi Quality ngati anayesedwapo ndi chikhumbo cha kusunga ndalamazo, Abiodun anati: ‘Ine ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. Chotero pamene ndipeza kanthu kalikonse kamene sikali kanga, ndimakapereka kwa mwini wake.’

Ambiri a m’chitaganyacho anadabwa ndi mchitidwe wowona mtima wa Abiodun. Mboni zinzake za Abiodun zinakondwera ndi zimene zinachitika, koma izo sizinadabwe. Padziko lonse lapansi Mboni za Yehova zili zodziŵika chifukwa cha malamulo awo a mkhalidwe apamwamba. Pakati pawo kuwona mtima nkofunika kwambiri; ndiko lamulo, mbali yofunika ya Chikristu chowona.

Komabe, mwakamodzikamodzi, mikhalidwe ingaonekere kukhala yovuta kusiyanitsa pakati pa kuwona mtima ndi zimene sizili kuwona mtima. Talingalirani za mkhalidwe uwu. Festus, amene anali kusamalira zopereka ndi maakaunti ampingo wa Mboni za Yehova ku West Africa, analoŵa m’vuto lalikulu la kusoŵa ndalama.a Mkazi wake adafunikira kuchitidwa opaleshoni yaikulu imene madokotala ake anamuuza kuti siyenera kuchedwetsedwa. Kuchipatala adafuna theka la ndalamazo pasadakhale.

Festus anasoŵa ndalama. Pamene anafikira anthu angapo kuti amkongoze ndalama, iwo anakana. Ndiyeno anaganiza za ndalama zimene anali kusunga nati mumtima, ‘Kodi nkwabwino kwa ine kuti ndilekerere mkazi wanga kufa pamene kuli kwakuti ndikhoza kuchita kanthu kena kuti imfayo isachitike? Bwanji “ndingokongola” ndalama za mpingozi? Ndidzazibwezera anthu akadzandipatsa ngongole zanga.’

Festus anagwiritsira ntchito ndalama zimene sizinali zake kulipirira chipatala. Kodi kulingalira kwakeko kunali kolondola? Kodi mchitidwe wake unali wolungama polingalira za mkhalidwe wangozi umene anayang’anizana nawo?

Kodi Ndalamazo Nzayani?

Popenda mafunso ameneŵa, tiyeni mwachidule tipende mfundo zingapo ponena za magwero ndi chifuno cha ndalama zonga zimene Festus anatenga. Ndalamazo zimakhalapo kupyolera m’zopereka zochitidwa ndi ziŵalo za mpingo zimene zimafuna kupititsa patsogolo kulambira koyera kwa Yehova. (2 Akorinto 9:7) Sizimagwiritsiridwa ntchito kulipirira anthu malipiro, popeza kuti palibe aliyense amene amalipidwa chifukwa cha zimene amachita mumpingo. Mosiyana ndi zimenezo, ndalama zoperekedwazo zimagwiritsiridwa ntchito kwakukulukulu kupezera ndi kusamalira malo osonkhanira, kaŵirikaŵiri Nyumba Yaufumu. Imeneyi imapereka malo oyenera ndi abwino kumene anthu​—achichepere ndi achikulire, olemera ndi osauka​—angasonkhaneko kaamba ka malangizo a m’Baibulo.

Kodi ndalamazo nzayani? Nzampingo wonse. Palibe chiŵalo chilichonse pachokha chimene chimasankha chokha mmene ndalamazo ziyenera kugwiritsiridwira ntchito. Pamene kuli kwakuti bungwe la akulu limayang’anira zolipiriridwa zanthaŵi zonse za mpingo, pamene kanthu kena kayenera kulipiliridwa, akuluwo amapereka nkhaniyo kumpingo wonse kaamba ka chivomerezo.

Kukongola Kapena Kuba?

Chifukwa cha kulinganiza kwake za kubwezera ndalamazo mofulumira monga momwe akanathera, Festus anaona mchitidwe wakewo monga kukongola. Komabe, Webster’s New Dictionary of Synonyms imagwiritsira ntchito mawu ena ponena za “kutenga ndi kuchotsa chinthu chamwini kaŵirikaŵiri mwa kuba kapena popanda kudziŵa munthuyo ndipo nthaŵi zonse mosavomerezedwa naye.” Mawu ake ndiwo “kuba” ndi “mbala.” Popanda chilolezo kapena lamulo, Festus anatenga ndalama zimene zinali za mpingo. Chotero, inde, anali ndi liwongo la kuba. Iye anali mbala.

Zowonadi, pali milingo yosiyanasiyana ya malingaliro osonkhezera kuba. Tikhoza kuona zimenezo m’chitsanzo cha Yudase Isikariote, amene anaikiziridwa thayo la kusamalira ndalama zimene zinali za Yesu ndi atumwi ake okhulupirika. Baibulo limati: “[Yudase] chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.” (Yohane 12:6) Posonkhezeredwa ndi mtima woipa ndi dyera lapoyera, Yudase anachoka pakuipa kumka pakuipitsitsa. Potsirizira pake anadziloŵetsa m’kupereka Mwana wa Mulungu​—kaamba ndalama 30 zasiliva.​—Mateyu 26:14-16.

Komabe, Festus, anasonkhezeredwa ndi nkhaŵa ya mkazi wake wodwala kwambiriyo. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti iye analibe liwongo? Kutalitali. Talingalirani za chimene Baibulo limanena ponena za kuba mumkhalidwe wina wovuta mwachionekere: “Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala; koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kaŵiri; idzapereka chuma chonse cha m’nyumba yake.” (Miyambo 6:30, 31) M’mawu ena, itagwidwa, mbalayo iyenera kuyang’anizana ndi chilango chonse cha lamulo. Malinga ndi kunena kwa Chilamulo cha Mose, mbala inafunikira kubwezera zinthu kaamba ka mlanduwo. Chotero mmalo mwa kulimbikitsa kapena kulungamitsa kuba, Baibulo limachenjeza kuti ngakhale m’mikhalidwe yovuta yadzidzidzi, kuba kungachititse kutayikiridwa ndi chuma, kuchititsidwa manyazi, ndipo chinthu chowopsa kwambiri, kutayikiridwa ndi chivomerezo cha Mulungu.

Monga Mboni za Yehova, Akristu onse owona, makamaka awo amene aikiziridwa mathayo mumpingo, ayenera kukhala achitsanzo chabwino, “opanda chifukwa.” (1 Timoteo 3:10) Festus sanalandire ndalama zake zangongole zimene anali kuyembekezera, ndipo motero anali wosakhoza kubwezera ndalama zimene anatenga. Zimene anachita zinadziŵika. Kodi nchiyani chimene chinamchitikira? Iye akanakhala mbala yosalapa, akanathamangitsidwa mumpingo woyera Wachikristu. (1 Petro 4:15) Koma iye anagwidwa ndi chisoni chachikulu ndipo analapa. Chifukwa chake, iye anakhalabe mumpingo, ngakhale kuti anatayikiridwa ndi mwaŵi wake wautumiki.

Kudalira Mulungu

Mtumwi Paulo anachenjeza kuti kuba kochitidwa ndi munthu amene amanena kuti amatumikira Yehova kungatonzetse dzina la Mulungu ndi anthu ake. Paulo analemba kuti: “Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu.”​—Aroma 2:21, 24.

Aguri, mwamuna wanzeru wanthaŵi zakale, ananena mfundo imodzimodziyo. M’pemphero lake iye anapempha kuti ‘asasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wake pachabe.’ (Miyambo 30:9) Onani kuti munthu wanzeruyo anavomereza kuti kusauka kungadzetse mikhalidwe imene ingayese ngakhale munthu wolungama kuti abe. Inde, nthaŵi zovuta zingayese chikhulupiriro cha Mkristu pakukhoza kwa Yehova kusamalira zosoŵa za anthu ake.

Komabe, Mboni zokhulupirika za Yehova, kuphatikizapo izo zimene zili zosauka, zili ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu “ali wobwezera mphoto iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Zimadziŵa kuti Yehova amafupa okhulupirika ake mwa kuwathandiza kupeza zosoŵa zawo. Yesu anafotokoza zimenezo momvekera bwino mu Ulaliki wake wa pa Phiri, akumati: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? . . . Pakuti Atate wanu wa kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”​—Mateyu 6:31-33.

Kodi ndimotani mmene Mulungu amagaŵirira osoŵa mumpingo Wachikristu? M’njira zambiri. Njira imodzi ili kupyolera mwa okhulupirira anzathu. Anthu a Mulungu amasonyezana chikondi chowona. Amaona mwamphamvu chilangizo cha Baibulo chakuti: “Iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosoŵa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’chowonadi.”​—1 Yohane 3:17, 18.

Kuzungulira dziko lonse, m’mipingo yoposa 73,000, Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni anayi ndi theka zimayesayesa mwakhama kutumikira Mulungu mogwirizana ndi malamulo ake a mkhalidwe olungama. Zimadziŵa kuti Mulungu sadzasiya konse okhulupirika ake. Awo amene atumikira Yehova kwazaka zambiri amakweza mawu awo mogwirizana ndi Mfumu Davide, amene analemba kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.”​—Salmo 37:25.

Nkwabwino kwambiri chotani nanga kuika chikhulupiriro mwa Mulungu amene anauzira mawu amenewo, mmalo mwa kudzilola kuyesedwa kuba ndipo mwinamwake kutayikiridwa ndi chiyanjo cha Mulungu kosatha!​—1 Akorinto 6:9, 10.

[Mawu a M’munsi]

a Dzinalo lasinthidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena