Tayani Nkhaŵa Yanu Yonse pa Yehova
“Dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.”—1 PETRO 5:6, 7.
1. Kodi ndimotani mmene nkhaŵa ingatiyambukirire, ndipo kodi ndimotani mmene zimenezi zingachitiridwire fanizo?
NKHAŴA ingayambukire moyo wathu mopambanitsa. Ingayerekezeredwe ndi phokoso limene nthaŵi zina limadodometsa nyimbo yokoma yomvedwa pa wailesi. Ngati mphepo ya pa wailesi sinadodometsedwe, nyimbo zokoma zimasangalatsa ndipo zimatonthoza mtima. Komabe, phokoso lingawononge nyimbo yokometsetsadi, likumatikwiyitsa ndi kutigwiritsa mwala. Nkhaŵa ingakhalenso ndi chiyambukiro chofananacho pa bata lathu. Ingatilemetse kwambiri kwakuti sitingathe kusamalira nkhani zina zofunika. Zoonadi, “nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu.”—Miyambo 12:25.
2. Kodi nchiyani chimene Yesu Kristu ananena ponena za “zosamalira za moyo uno”?
2 Yesu Kristu analankhula za ngozi ya kukhala wocheukitsidwa ndi nkhaŵa yopambanitsa. Mu ulosi wake wonena za masiku otsiriza, iye analimbikitsa kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) Monga momwe madyaidya ndi kuledzera zingachititsire mkhalidwe wa kuganiza moziya, choteronso kulemetsedwa ndi “zosamalira za moyo uno” kungatitayitse kuganiza bwino, limodzi ndi zotulukapo zatsoka.
Chimene Nkhaŵa Ili
3. Kodi ndimotani mmene “nkhaŵa” yafotokozedwera, ndipo kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimaichititsa?
3 “Nkhaŵa” yafotokozedwa monga “kusakhazikika kwa maganizo kopweteka kapena kodetsa mtima kaŵiri[kaŵiri] kochititsidwa ndi nsautso yoyandikira kapena yoyembekezeredwa.” Ndiko “kutekeseka kapena mantha” ndiponso ndiwo “mkhalidwe wachilendo ndi wothetsa mphamvu wa kuwopa ndi kuda mtima wosonyezedwa kaŵirikaŵiri ndi zizindikiro zakuthupi (zonga ngati kutuluka thukuta, kupsinjika maganizo, ndi kugunda kwa mtima kowonjezereka), ndi kukayikira chiwopsezo ndi mkhalidwe wake, ndi mwa kudzikayikira kuti sukhoza kulimbana nacho.” (Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary) Chotero nkhaŵa ingakhale vuto locholoŵana. Pakati pa zochititsa zake zambiri pali matenda, kukalamba, kuwopa upandu, kuchotsedwa ntchito, ndi kuvutika mtima kaamba ka ubwino wa banja la munthuwe.
4. (a) Kodi nchiyani chimene chili chabwino kukumbukira ponena za anthu ndi nkhaŵa zawo? (b) Ngati tili ndi nkhaŵa, kodi nchiyani chimene chingachitidwe?
4 Mwachionekere, nkhaŵa zili zosiyanasiyana mu ukulu wake, monga momwe mikhalidwe imene ingaziyambitse ilili yosiyanasiyana. Anthu samachita ndi mkhalidwe m’njira yofanana. Chifukwa chake, tifunikira kuzindikira kuti ngakhale ngati kanthu kena sikativutitsa maganizo, iko kangachititse nkhaŵa yaikulu kwa olambira Yehova anzathu ena. Kodi nchiyani chimene chingachitidwe ngati nkhaŵa yafika pakuti sitingathe kusumika maganizo pa choonadi cha Mawu a Mulungu chogwirizana ndi chokondweretsa? Bwanji ngati tikanthidwa ndi nkhaŵa kwakuti tili osakhoza kusumika chisamaliro pa nkhani za ulamuliro wa Yehova ndi umphumphu Wachikristu? Mwina sitingakhoze kusintha mikhalidwe yathu. M’malo mwake, tifunikira kupenda mfundo za m’Malemba zimene zidzatithandiza kulimbana ndi nkhaŵa yosayenerera yochititsidwa ndi mavuto osautsa a moyo.
Thandizo Lilipo
5. Kodi tingachite motani mogwirizana ndi Salmo 55:22?
5 Pamene Akristu afunikira thandizo lauzimu ndi pamene ali olemetsedwa ndi nkhaŵa, angapeze chitonthozo m’Mawu a Mulungu. Iwo amapereka chitsogozo chodalirika ndi kutilimbikitsa kwambiri kuti sitili tokha monga atumiki okhulupirika a Yehova. Mwachitsanzo, wamasalmo Davide anaimba kuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Kodi ndimotani mmene tingachitire mogwirizana ndi mawu ameneŵa? Mwa kusenzetsa Atate wathu wachikondi wakumwamba nkhaŵa zathu zonse, zovutitsa maganizo, mantha, ndi zogwiritsa mwala. Zimenezi zidzatithandiza kumva tili osungika ndi mtima wa bata.
6. Malinga ndi kunena kwa Afilipi 4:6, 7, kodi pemphero lingatichitirenji?
6 Pemphero lanthaŵi zonse la mtima wonse nlofunika ngati titi tisenze Yehova zolemetsa zathu, kuphatikizapo nkhaŵa yathu. Zimenezi zidzatidzetsera mtendere wamkati, pakuti mtumwi Paulo analemba kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) “Mtendere wa Mulungu” wosayerekezereka umenewo ndiwo bata losaonekaoneka limene lili ndi atumiki odzipatulira a Yehova ngakhale mkati mwa mikhalidwe yoyesa kwambiri. Limakhalapo chifukwa cha unansi wathu wolimba ndi Mulungu. Pamene tipempherera mzimu wake woyera ndi kuulola kutisonkhezera, mavuto athu onse a moyo sachotsedwa pa ife, koma timalandira chipatso cha mzimu cha mtendere. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Sitimalemetsedwa ndi nkhaŵa, pakuti timadziŵa kuti Yehova amachititsa anthu ake onse okhulupirika ‘kukhala m’chisungiko’ ndipo sadzalola kanthu kalikonse kuchitika kamene kangativulaze moyo wonse.—Salmo 4:8, NW.
7. Kodi ndi mbali yotani imene ingachitidwe ndi akulu Achikristu m’kutithandiza kulimbana ndi nkhaŵa?
7 Komabe, bwanji ngati nkhaŵa yathu ipitirizabe kukhalapo, ngakhale ngati tikusinkhasinkha Malemba ndi kuchita khama m’pemphero? (Aroma 12:12) Akulu oikidwa mu mpingo alinso chogaŵira cha Yehova kutithandiza mwauzimu. Iwo angatitonthoze ndi kutithandiza mwa kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu ndi mwa kupemphera nafe ndi kutipempherera. (Yakobo 5:13-16) Mtumwi Petro anadandaulira akulu anzake kuŵeta gulu la Mulungu mwaufulu, mofunitsitsa, ndi mwa chitsanzo chabwino. (1 Petro 5:1-4) Amuna ameneŵa amatifunira zabwino koposa ndipo amafuna kukhala othandiza. Zoonadi, kuti tipindule mokwanira ndi thandizo la akulu ndi kuchita bwino mwauzimu mu mpingo, tonsefe tifunikira kugwiritsira ntchito uphungu wa Petro wakuti: “Anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”—1 Petro 5:4, 5.
8, 9. Kodi ndi chitonthozo chotani chimene chingapezedwe mu 1 Petro 5:6-11?
8 Petro anawonjezera kuti: “Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu. Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire; ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko. Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kuloŵa ulemerero wake wosatha mwa Kristu, mutamva zoŵaŵa kanthaŵi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu. Kwa Iye kukhale mphamvu ku nthaŵi za nthaŵi. Amen.”—1 Petro 5:6-11.
9 Nkotonthoza chotani nanga kuzindikira kuti tingathe ‘kutaya nkhaŵa zathu zonse pa Mulungu pakuti iye asamalira ife’! Ndipo ngati zina za nkhaŵa zathu zikhalapo chifukwa cha zoyesayesa za Mdyerekezi za kuwononga unansi wathu ndi Yehova mwa kubweretsa chizunzo ndi mavuto ena pa ife, kodi sikwabwino kwambiri kudziŵa kuti zinthu zonse zidzayendera bwino osunga umphumphu? Inde, titavutika kanthaŵi, Mulungu wa chisomo chonse adzamaliza maphunziro athu ndipo adzatilimbitsa.
10. Kodi 1 Petro 5:6, 7 amakhudza mikhalidwe itatu iti imene ingatithandize kuchepetsa nkhaŵa?
10 Petro Woyamba 5:6, 7 amakhudza mikhalidwe itatu imene ingatithandize kulimbana ndi nkhaŵa. Umodzi ndiwo kufatsa, kapena “kudzichepetsa.” Vesi 6 limatha ndi mawu akuti “panthaŵi yake,” likumapereka lingaliro la kufunika kwa kuleza mtima. Vesi 7 limasonyeza kuti ife tingataye nkhaŵa yathu yonse pa Mulungu ndi chidaliro ‘pakuti iye asamalira ife,’ ndipo mawu amenewo amalimbikitsa kukhulupirira Yehova kotheratu. Chotero tiyeni tione mmene kufatsa, chipiriro, ndi kukhulupirira Mulungu kotheratu zingathandizire kuchepetsa nkhaŵa.
Mmene Kufatsa Kungathandizire
11. Kodi ndimotani mmene kufatsa kungatithandizire kulimbana ndi nkhaŵa?
11 Ngati tili ofatsa, tidzavomereza kuti malingaliro a Mulungu ali apamwamba kuposa a ife eni. (Yesaya 55:8, 9) Kufatsa kumatithandiza kuzindikira kufinimpha maganizo kwathu poyerekezera ndi malingaliro akuya a Yehova. Iye amaona zinthu zimene sitidziŵa, monga momwe nkhani ya munthu wolungamayo Yobu imasonyezera. (Yobu 1:7-12; 2:1-6) Mwa kudzichititsa kukhala ofatsa “pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu,” timavomereza malo athu otsika poyerekezera ndi a Mfumu Yam’mwambamwamba. Zimenezi nazonso, zimatithandiza kulimbana ndi mikhalidwe imene iye amalola. Mitima yathu ingakhumbe kupeza mpumulo panthaŵi yomweyo, koma popeza kuti mikhalidwe ya Yehova njolinganizika bwino kwambiri, amadziŵa bwino lomwe nthaŵi ndi mmene adzachitirapo kanthu kaamba ka ife. Pamenepo, ife mofanana ndi ana, tiyeni tigwiritsitse zolimba mkono wa Yehova wamphamvuwo modzichepetsa, tili ndi chidaliro chakuti iye adzatithandiza kulimbana ndi nkhaŵa zathu.—Yesaya 41:8-13.
12. Kodi nchiyani chimene chidzachitikira nkhaŵa ya chisungiko cha zachuma ngati tigwiritsira ntchito mofatsa mawu a Ahebri 13:5?
12 Kufatsa kumaphatikizapo kufunitsitsa kugwiritsira ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu, umene kaŵirikaŵiri ungachepetse nkhaŵa. Mwachitsanzo, ngati nkhaŵa yathu yakhalapo chifukwa cha kuloŵa mwakuya m’kulondola zinthu zakuthupi, kungakhale bwino kwa ife kulingalira za uphungu wa Paulo wakuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti [Mulungu] anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Mwa kugwiritsira ntchito modzichepetsa uphungu wotero, ambiri adziwonjola pa nkhaŵa yaikulu ya chisungiko cha zachuma. Ngakhale kuli kwakuti mkhalidwe wawo wa ndalama sunawongokere, zimenezi sizimalamulira malingaliro awo kuti ziwaloŵetse m’ngozi yauzimu.
Mbali ya Kuleza Mtima
13, 14. (a) Ponena za kupirira moleza mtima, kodi ndi chitsanzo chotani chimene munthuyo Yobu anapereka? (b) Kodi kuyembekezera Yehova moleza mtima kungatichitirenji?
13 Mawu akuti “panthaŵi yake” pa 1 Petro 5:6 amapereka lingaliro la kufunika kwa kupirira moleza mtima. Nthaŵi zina vuto limapitirizabe kwanthaŵi yaitali, ndipo zimenezo zingawonjezere nkhaŵa. Pamenepo mpamene makamaka timafunikira kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Yobu anatayikiridwa ndi chuma, anatayikiridwa ndi ana khumi mu imfa, anadwala nthenda yonyansa, ndipo anaimbidwa mlandu molakwa ndi otonthoza onyenga. Ndithudi pangakhale nkhaŵa mwachibadwa m’mikhalidwe yotero.
14 Mulimonse mmene zinalili, Yobu anali chitsanzo chabwino cha kupirira moleza mtima. Ngati tili pansi pa chiyeso chachikulu cha chikhulupiriro, mwina tingafunikire kuyembekezera mpumulo, monga momwedi iye anachitira. Koma Mulungu anachitapo kanthu m’malo mwake, potsirizira pake akumachotsera Yobu mavuto ake ndi kumfupa moŵirikiza. (Yobu 42:10-17) Kuyembekezera pa Yehova moleza mtima kumakulitsa chipiriro chathu ndi kusonyeza kuya kwa kudzipereka kwathu kwa iye.—Yakobo 1:2-4.
Kukhulupirira Yehova
15. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhulupirira Yehova kotheratu?
15 Petro anadandaulira okhulupirira anzake ‘kutaya nkhaŵa yawo yonse pa Mulungu pakuti asamalira iwo.’ (1 Petro 5:7) Chotero ife tingathe ndipo tiyenera kukhulupirira Yehova kotheratu. Miyambo 3:5, 6 imati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” Chifukwa cha zokumana nazo zakale, ena amene ali ndi nkhaŵa yaikulu amaona kukhulupirira anthu ena kukhala kovuta. Koma ife tilidi ndi chifukwa cha kukhulupirira Mlengi wathu, Magwero enieniwo a moyo ndi Mchirikizi wake. Ngakhale ngati tikayikira zimene tiyenera kuchita pa nkhani ina yake, nthaŵi zonse tingadalire Yehova kuti adzatipulumutsa m’masoka athu onse.—Salmo 34:18, 19; 36:9; 56:3, 4.
16. Kodi nchiyani chimene Yesu Kristu ananena ponena za kudera nkhaŵa ndi zinthu zakuthupi?
16 Kukhulupirira Mulungu kumaphatikizapo kumvera Mwana wake, Yesu Kristu, amene anaphunzitsa zimene anaphunzira kwa Atate wake. (Yohane 7:16) Yesu analimbikitsa ophunzira ake ‘kudzikundikira chuma m’mwamba’ mwa kutumikira Yehova. Koma bwanji za zosoŵa zakuthupi zophatikizapo chakudya, zovala, ndi pogona? “Musadere nkhaŵa,” Yesu analangiza motero. Iye anasonyeza kuti Mulungu amadyetsa mbalame. Amaveka maluŵa mokongola. Kodi atumiki aumunthu a Mulungu sali oposa zimenezi? Ndithudi iwo ali otero. Chifukwa chake, Yesu analimbikitsa kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” Yesu anapitiriza kuti: “Chifukwa chake musadere nkhaŵa za maŵa; pakuti maŵa adzadzidera nkhaŵa iwo okha.” (Mateyu 6:20, 25-34) Inde, timafunikira chakudya, chakumwa, zovala, ndi pogona, koma ngati tikhulupirira Yehova, sitidzakhala ankhaŵa mopambanitsa ponena za zinthu zimenezi.
17. Kodi tingafanizire motani za kufunika kwa kufuna Ufumu choyamba?
17 Kuti tithange tafuna Ufumu, tiyenera kukhulupirira Mulungu ndi kuika zinthu zathu zoyamba m’dongosolo loyenera. Munthu woloŵa pamadzi wopanda chiwiya chopumira angapite pansi akumafunafuna oyster yokhala ndi ngale mkati mwake. Imeneyi ndiyo njira yosamalirira banja lake. Ndithudi, zimenezo nzofunika kwambiri! Komano kodi nchiyani chimene chili chofunika kwambiri? Mpweya! Iye ayenera kuvuuka pamadzipo nthaŵi ndi nthaŵi kudzakoka mpweya woloŵetsa m’mapapu ake. Mpweya ndiwo chinthu choyambirira chachikulu koposa. Mofananamo, ife mwinamwake tingafunikire kukhala ophatikizidwa pang’ono m’dongosolo ili la zinthu kuti tipeze zofunika za moyo. Komabe, zinthu zauzimu ziyenera kudza pamalo oyamba chifukwa chakuti moyo weniweniwo wa banja lathu umadalira pa zinthu zimenezi. Kuti tipeŵe nkhaŵa yopambanitsa ya zosoŵa zakuthupi, tiyenera kukhulupirira Mulungu kotheratu. Ndiponso, ‘kukhala akuchuluka mu ntchito ya Ambuye’ kungatithandize kuchepetsa nkhaŵa chifukwa chakuti “chimwemwe cha Yehova” chimakhaladi linga lathu.—1 Akorinto 15:58; Nehemiya 8:10.
Pitirizanibe Kutaya Nkhaŵa Yanu pa Yehova
18. Kodi ndi umboni wotani umene ulipo wakuti kutaya nkhaŵa zathu zonse pa Yehova kungatithandizedi?
18 Kuti tikhalebe osumika bwino maganizo mwauzimu, tiyenera kupitirizabe kutaya nkhaŵa yathu pa Yehova. Nthaŵi zonse kumbukirani kuti iye amasamaladi atumiki ake. Mwachitsanzo: Chifukwa cha kusakhulupirika kwa mwamuna wake kwa iye, nkhaŵa ya mkazi wina Wachikristu inawonjezereka kufikira pakuti kunali kosatheka kwa iye kugona. (Yerekezerani ndi Salmo 119:28.) Komabe, ali pakama, iye ankataya nkhaŵa yake yonse pa Yehova. Iye ankatsanulira mtima wake kwa Mulungu, akumamuuza za mavuto amene iyeyo ndi ana ake aŵiri aang’ono aakazi anasauka nawo. Atalira kuti apeze mpumulo m’pemphero laphamphu, nthaŵi zonse ankakhoza kugona, pakuti anakhulupirira kuti Yehova adzasamalira iye ndi ana ake. Mkazi wosudzulidwa mwa Malembayu tsopano ngwokwatiwa mwachimwemwe ndi mkulu wina.
19, 20. (a) Kodi ndi njira zina ziti zimene tingalimbanire ndi nkhaŵa? (b) Kodi nchiyani chimene tiyenera kupitirizabe kuchita ndi nkhaŵa yathu yonse?
19 Monga anthu a Yehova, ife tili ndi njira zosiyanasiyana zolimbanira ndi nkhaŵa. Makamaka kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu nkothandiza. Tili ndi chakudya chopatsa thanzi chauzimu choperekedwa ndi Mulungu kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kuphatikizapo nkhani zothandiza ndi zotsitsimula mtima zofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! (Mateyu 24:45-47) Tili ndi thandizo la mzimu woyera wa Mulungu. Mapemphero anthaŵi zonse ndi aphamphu amatipindulitsa kwambiri. Akulu Achikristu oikidwa ali okonzekera ndi ofunitsitsa kupereka thandizo ndi chitonthozo chauzimu.
20 Kufatsa kwa ife eni ndi kuleza mtima nzothandiza kwambiri polimbana ndi nkhaŵa imene ingatisautse. Makamaka chofunika kwambiri ndicho kukhulupirira Yehova kotheratu, pakuti chikhulupiriro chathu chimakulitsidwa pamene tilandira thandizo ndi chitsogozo chake. Ndiponso, chikhulupiriro mwa Mulungu chingatitetezere pa kukhala ovutika mtima mopambanitsa. (Yohane 14:1) Chikhulupiriro chimatisonkhezera kufuna Ufumu choyamba ndi kukhala otanganitsidwa m’ntchito yosangalatsa ya Ambuye, zimene zingatithandize kulimbana ndi nkhaŵa. Ntchito yotero imatichititsa kukhala osungika pakati pa awo amene adzaimba zitamando za Mulungu ku umuyaya wonse. (Salmo 104:33) Chotero tiyeni tipitirizebe kutaya nkhaŵa zathu zonse pa Yehova.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nkhaŵa ingafotokozedwe motani?
◻ Kodi ndi njira zina ziti zimene tingalimbanire ndi nkhaŵa?
◻ Kodi kufatsa ndi kuleza mtima kungathandize motani kuchepetsa nkhaŵa?
◻ Polimbana ndi nkhaŵa, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukhala ndi chikhulupiriro chotheratu mwa Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupitirizabe kutaya nkhaŵa yathu yonse pa Yehova?
[Chithunzi patsamba 24]
Kodi mukudziŵa chifukwa chake Yesu ananena kuti, “Musadere nkhaŵa”?