“Chipangano Chakale” Kapena “Malemba Achihebri”—Ziti?
LEROLINO uli mwambo wofala m’Dziko Lachikristu kugwiritsira ntchito mawu akuti “Chipangano Chakale” ndi “Chipangano Chatsopano” pofotokoza mbali za Baibulo za chinenero cha Chihebri/Chiaramaiki ndi Chigiriki. Koma kodi pali maziko alionse a m’Baibulo ogwiritsirira ntchito mawu ameneŵa? Ndipo ndi kaamba ka zifukwa ziti zimene Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimapeŵera kuwagwiritsira ntchito m’zofalitsidwa zawo?
Zoona, 2 Akorinto 3:14, malinga ndi King James Version limodzinso ndi matembenuzidwe ena akale, onga Septembertestament Yachijeremani, matembenuzidwe oyambirira a Martin Luther (1522), angaoneke kukhala akuchirikiza mwambo umenewu. Mu King James Version, vesi limeneli limati: “Koma maganizo awo anachititsidwa khungu: pakuti kufikira tsikuli padakali nsalu yochinga imodzimodziyo yosachotsedwa pa kuŵerengedwa kwa chipangano chakale; nsalu yochinga imene ichotsedwa mwa Kristu.”
Komabe, kodi mtumwiyo panopa akulankhula za mabuku 39 amene amatchedwa ndi ambiri kuti “Chipangano Chakale”? Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “chipangano” panopa ndi di·a·theʹke. Insaikulopediya ya zaumulungu yotchuka Yachijeremani Theologische Realenzyklopädie, pothirira ndemanga pa 2 Akorinto 3:14, imanena kuti ‘kuŵerengedwa kwa di·a·theʹke wakale’ m’vesi limenelo nkumodzimodzi ndi ‘kuŵerengedwa kwa Mose’ m’vesi lotsatira. Chifukwa chake, imanena kuti, ‘di·a·theʹke wakale’ amaimira Chilamulo cha Mose, kapena makamaka Pentatuke. Ndithudi samaimira Malemba onse ouziridwa a m’nyengo ya Chikristu chisanakhale.
Mtumwiyo akutchula mbali ina chabe ya Malemba Achihebri, pangano lakale la Chilamulo, limene linalembedwa ndi Mose m’Pentatuke; sakutchula za Malemba onse Achihebri ndi Achiaramaiki. Ndiponso, sakutanthauza kuti zolemba zouziridwa Zachikristu za m’zaka za zana loyamba C.E. zili “chipangano chatsopano,” pakuti mawu ameneŵa samapezeka kulikonse m’Baibulo.
Kuyenera kudziŵidwanso kuti liwu Lachigirikilo di·a·theʹke limene Paulo anagwiritsira ntchito panopa kwenikweni limatanthauza “pangano.” (Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezera onani New World Translation of the Holy Scriptures—With References, Appendix 7E, tsamba 1585, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., 1984.) Chifukwa chake matembenuzidwe ambiri amakono amanena molondola kuti “pangano lakale” m’malo mwa “chipangano chakale.”
Mogwirizana ndi zimenezi, “National Catholic Reporter” inati: “Mawuwo ‘Chipangano Chakale’ mosapeŵeka amachititsa mkhalidwe wa kusanunkha kanthu ndi kuguga.” Koma Baibulo ndi buku limodzi ndithu, ndipo palibe mbali yake imene ili yoguga, kapena “yakale.” Uthenga wake ndi umodzi kuyambira buku loyamba m’mbali Yachihebri mpaka buku lomaliza m’mbali Yachigiriki. (Aroma 15:4; 2 Timoteo 3:16, 17) Chotero tili ndi zifukwa zomveka zopeŵera mawu ameneŵa amene ali ozikidwa pa malingaliro olakwika, ndipo timakonda kugwiritsira ntchito mawu olondola kwambiriwo “Malemba Achihebri” ndi “Malemba Achigiriki Achikristu.”