Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 4/1 tsamba 9
  • Kulalikira m’Nyengo Yovuta

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira m’Nyengo Yovuta
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Zipatala—Mutakhala Wodwala
    Galamukani!—1991
  • Lankhulani Ponena za Ulemerero wa Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kuchezetsa Wodwala—Mmene Mungathandizire
    Galamukani!—1991
Nsanja ya Olonda—1995
w95 4/1 tsamba 9

Olengeza Ufumu Akusimba

Kulalikira m’Nyengo Yovuta

MTUMWI Paulo analosera kuti “masiku otsiriza [zikafika] nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Mawu amenewo akhala oona chotani nanga! Anthu a ku El Salvador ku Central America kwanthaŵi yaitali akumana ndi nthaŵi zovuta zimenezi. Kwa zaka zoposa khumi, dziko limenelo linali pankhondo ya chiŵeniŵeni imene inasautsa ndi kupha anthu zikwizikwi. Nkhondoyo tsopano inatha, koma kuvutika kukalipobe. Upandu wachuluka kwambiri kuyambira pamene nkhondoyo inatha. Muulutsi wina wakomweko wa pawailesi ya kanema posachedwapa anati: “Chiwawa ndi kuba zakhala chakudya chathu tsopano.”

Mboni za Yehova nazonso zakhudzidwa ndi upandu umenewu. Mbala zathyola Nyumba Zaufumu zambiri ndi kuba zokuzira mawu. Panthaŵi zingapo timagulu ta anyamata onyamula zida taloŵa m’Nyumba Zaufumu misonkhano Yachikristu ili mkati, ndi kuba ndalama, mawatchi, ndi zinthu zina zamtengo wake kwa opezekapo. Ngakhale pochita ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku, Mboni zambiri zaphedwa ndi mbala.

Ngakhale kuti pali zopinga zimenezi, Mboni za Yehova ku El Salvador zikupitiriza kugwira ntchito mwamphamvu kulalikira uthenga wabwino. Zikuchita zimenezi momvera lamulo la Malemba: “Uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) M’dziko limeneli mudakali ambiri amene akulakalaka chiyembekezo cha Ufumu chimene Baibulo limapatsa, ndipo Mbonizo zikuyesayesa kufikira aliyense wa iwo. Umboni wamwamwaŵi uli njira yogwira mtima yolalikirira.

Pamene Mboni ina inali kulandira chithandizo cha mankhwala m’chipatala, inagwiritsira ntchito mpata uliwonse kuuza odwala ena za malonjezo a Mulungu a mtsogolo, opezeka m’Baibulo. Munthu wina wodwala kwambiri anadandaula momvetsa chisoni: “Ndidzafa posachedwapa!” Koma kupanda chiyembekezo kwa wodwalayo sikunaletse Mboniyo kumuuza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. M’malo mwake, inaŵerengera mwamunayo momveka buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Pambuyo pa masiku angapo, Mboniyo inachoka m’chipatala, ili ndi chisoni kuti mwamunayo anali kuyembekezera kufa.

Patapita zaka zinayi Mboniyo inapita kukalandira chithandizo cha mankhwala kuchipatala china. Ili komweko, munthu wina wodwala anadza kwa iye nati: “Kodi mukundikumbukira?” Ameneyo anali mwamuna uja yemwe anakumana naye zaka zinayi zapitazo, mwamuna yemwe anati anali kufa! Anadabwa kwambiri nakondwera pamene mwamunayo anamfungatira nawonjezera kuti: “Tsopano nanenso ndine mmodzi wa Mboni za Yehova!” Mwamunayo analandira chiyembekezo cha m’Baibulo cha mtsogolo, anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, napatulira moyo wake kwa Yehova. Iye sanali chabe Mboni komanso anali kale mu utumiki wanthaŵi yonse monga mpainiya wokhazikika kwa pafupifupi zaka ziŵiri.

M’chochitikachi, mbewu za choonadi zimene zinabzalidwa mwamwaŵi zinaloŵa mumtima womvera. Mwaŵi umenewu wa kuthandiza anthu kudziŵa choonadi umasonkhezera Akristu oona kupitiriza m’ntchito yolalikira ngakhale kuti zino ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena