Mboni za Yehova Padziko Lonse—Sweden
SWEDEN ali kumbali ya kummaŵa kwa ndomo ya Scandinavia ndipo amakwera kupyola pa Arctic Circle. Iye ali wotchuka chifukwa cha nkhalango zake zobiriŵira nthaŵi zonse, ndiponso nyanja zake ndi mapiri, Sweden ali limodzi la maiko a ku Ulaya a anthu okhalirana patalipatali. Chikhalirechobe, Mboni za Yehova zakhoza kupeza okonda choonadi kumeneko chiyambire kumapeto kwa ma 1800. Tangolingalirani za chitsanzo chaposachedwapa.
Mkazi wina anaphunzira Baibulo ndi Mboni, koma mwamuna wake sanakonde zimenezi. Anauza mkazi wake kuleka kuphunzirako, ndipo mkaziyo anatero. Mwamuna ameneyu ankagwira ntchito m’nyumba yosungiramo zinthu zophikira moŵa. Tsiku lina woyendetsa lole wina anafika panyumbapo ndi mdzukulu wake wamwamuna wazaka khumi. Gogo wachimunayo anapempha mwamunayo kuti ayang’anire mnyamatayo pamene anali kupachira katundu mu lole yake. Kuti ayambe kucheza, mwamunayo anafunsa mnyamatayo kuti anapatsidwa mphatso yotani pa tsiku lake la kubadwa laposachedwapa. Mwamunayo anadabwa pamene mnyamatayo anamuuza kuti iyeyo ndi a m’banja lawo samakondwerera masiku akubadwa chifukwa chakuti ali Mboni za Yehova. Mnyamatayo anamuuzanso kuti amalandira mphatso panthaŵi zina m’chaka ndipo samasoŵa kanthu, popeza kuti ali ndi banja labwino ndi lachikondi kwambiri. Palibe mphatso imene inali yamtengo wapatali kuposa imeneyo, iye anawonjezera motero.
Mnyamatayo anafikanso pamalopo ndi agogo ake aamuna kangapo konse. Panthaŵi iliyonse, mwamunayo anali kufunsa mnyamatayo mafunso ambiri, ndipo iye anachita chidwi kwambiri ndi mmene mnyamatayo ankaperekera mayankho oona ndi olunjika, popanda kukayikira kulikonse. Iye anachitanso chidwi ndi kudziŵa makhalidwe abwino kwa mnyamatayo. Usiku wina mwamunayo ataonerera programu ina ya pa wailesi yakanema imene inasonyeza mikhalidwe yomvetsa chisoni m’dziko, anazindikira kuti anafunikira kupenda zinthu zauzimu mwamphamvu. Iye anaimbira telefoni Mboni yachikazi imene inaphunzira ndi mkazi wake ndi kuipempha kufikanso. Posapita nthaŵi, mwamunayo anali kuchititsidwa phunziro ndi Mboni ina yachimuna ndipo anapita patsogolo mofulumira. Anabatizidwa pa April 10, 1994. Mkazi wake nayenso tsopano ndi wobatizidwa.
Chifutukuko Chifunikiritsa Nyumba
Sweden ndi malo a othaŵa kwawo, ndipo Mboni Zachiswidishi zakhala ndi zotulukapo zabwino m’kulalikira kwawo. M’zochitika zambiri ntchitoyo yachitidwa mwachipambano kwakuti Nyumba Zaufumu zakhala zofunika kuti zithandize pa chifutukukocho. Kuyambira 1986 kukafika 1993, Nyumba Zaufumu 37 zinamangidwa ndi njira yomangira nyumba yofulumira, pamene kuli kwakuti nyumba 8 zinakuzidwa ndi kukonzedwanso. Mu 1994 mokha, Nyumba Zaufumu zisanu ndi ziŵiri zinamangidwa, ndipo zitatu zinakonzedwanso.
Pakali pano, pali mipingo 65 imene ikuyembekezera thandizo la kumanga Nyumba Zaufumu zatsopano kapena kukulitsa kapena kukonzanso zimene ali nazo. Antchito odzifunira 2,500 amathandiza pantchito zomanga zotero, ndipo mipingo imayamikira kwambiri thandizo lawo lachikondilo.
Mbali ya kumpoto kwa Sweden, imene imapyola pa Arctic Circle, nthaŵi zina imatchedwa kuti dziko la dzuŵa la pakati pa usiku. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti mkati mwa mbali ina ya chilimwe dzuŵa silimaloŵa kumeneko. Komabe, mu Sweden monse, kuunika kwa choonadi kukupitirizanso kuŵala kwambiri. Limodzi ndi dalitso la Yehova, kuunika kwauzimu kumeneko sikudzazima koma kudzapitirizabe kuŵaliraŵalirabe.
[Bokosi patsamba 8]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO
Chaka Chautumiki cha 1994
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 24,246
KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 326
OFIKA PA CHIKHUMBUTSO: 40,372
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 2,509
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 11,306
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 850
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 358
OFESI YA NTHAMBI: ARBOGA
[Chithunzi patsamba 9]
Ofesi ya nthambi ndi Nyumba ya Beteli ku Arboga
[Chithunzi patsamba 9]
Mboni zoyambirira ku Hjo zinagwiritsira ntchito minibasi iyi kufola gawo la mtunda wa makilomita 5,000 monsemonse